Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/15 tsamba 3-4
  • Achimwemwe M’dziko Lopanda Chimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achimwemwe M’dziko Lopanda Chimwemwe
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mwala m’Matope”
  • Kuvumbula Zoipa za Nazi
    Galamukani!—1995
  • Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Umboni wa Chikhulupiriro Chawo
    Galamukani!—1996
  • Sitinachirikize Nkhondo ya Hitler
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/15 tsamba 3-4

Achimwemwe M’dziko Lopanda Chimwemwe

“NZOIPA kwambiri, zaka za zana lino zakhala za Satana,” inayamba motero nkhani ina mu The New York Times ya January 26, 1995. “Palibe nyengo ina kumbuyoku imene anthu asonyeza luso, ndi chikhumbo, cha kupha anthu ena mamiliyoni ambiri pa zifukwa za fuko, chipembedzo kapena gulu la m’chitaganya.”

Chaka cha 50 cha kukumbukira chimasuko cha anthu osalakwa oikidwa m’ndende m’misasa ya imfa ya Nazi chinasonkhezera kulembedwa kwa nkhani zonga ili pamwambayo. Komabe, kupha kwankhanza kwa mtundu umodzimodziwo kukuchitikabe m’mbali zina za Afirika ndi Eastern Europe.

Kupha anthu ochuluka kolinganizidwa, kuyeretsa fuko, kuphana kwamafuko​—mulimonse mmene amakutchulira​—kumabweretsa chisoni chachikulu. Komabe, pakati pa kusakazana kumeneku pali mfuu yamphamvu yachimwemwe. Mwachitsanzo, tiyeni tione zimene zinachitikira Germany m’ma 1930.

Pofika April wa 1935, Mboni za Yehova zinali zitaletsedwa ndi Hitler ndi chipani chake cha Nazi kugwira ntchito m’boma. Mbonizo zinagwidwanso, kuikidwa m’ndende, ndi kutumizidwa kumisasa yachibalo chifukwa cha kusakhalira mbali kwawo kwachikristu. (Yohane 17:16) Kumapeto kwa August wa 1936, Mboni za Yehova zambiri zinagwidwa. Zikwi za iwo zinatumizidwa kumisasa yachibalo, kumene ambiri anakhala kufikira 1945 ngati anapulumuka. Komabe, kodi Mbonizo zinachita motani pankhanza imene zinakumana nayo m’misasamo? Modabwitsa, zinali zokhoza kusunga chimwemwe chawo ngakhale kuti zinali mumkhalidwe wosakondweretsa.

“Mwala m’Matope”

Wolemba mbiri wachibritishi Christine King anafunsa mkazi wina wachikatolika amene anali m’misasamo. “Anagwiritsira ntchito mawu ena amene sindinaiwale,” anatero Dr. King. “Anasimba zambiri ponena za moyo woopsawo, mikhalidwe yonyansa imene anakhalamo. Ndipo anati ankadziŵa Mboni, ndipo Mboni zimenezo zinali ngati mwala m’matope. Malo olimba m’thope lonselo. Iye anati iwo anali anthu okha amene sananyansidwe pamene alonda anadutsa. Ndiwo anthu okha amene sanalimbane ndi mkhalidwewo mwa udani koma ndi chikondi ndi chiyembekezo ndi lingaliro lakuti panali chifuno chake.”

Kodi nchiyani chimene chinatheketsa Mboni za Yehova kukhala ngati ‘miyala m’matope’? Chikhulupiriro chosagwedezeka mwa Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu. Chotero, zoyesayesa za Hitler zinalephera kuletsa chikondi chawo chachikristu ndi chimwemwe.

Mvetserani pamene opulumuka aŵiri akusimba zochitikazo patapita zaka makumi asanu chiyambire pamene anakumana ndi chiyeso cha chikhulupiriro chimenechi mwachipambano. Mmodzi akuti: “Ndimadzazidwa ndi chimwemwe podziŵa kuti ndinali ndi mwaŵi wapadera wa kusonyeza chikondi changa ndi chithokozo kwa Yehova pansi pa mikhalidwe yankhanza koposa. Palibe anandiumiriza kuchita zimenezi! Komano, anthu amene anayesa kutiumiriza anali adani athu amene anayesa kutipangitsa kumvera Hitler koposa Mulungu mwakutiwopseza​—koma mosaphula kanthu! Ndili wachimwemwe osati panthaŵi ino yokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima chabwino, ndinali wachimwemwe ngakhale pamene ndinali m’ndende.”​—Maria Hombach, wazaka 94.

Mboni ina ikunena kuti: “Ndimakumbukira za masiku anga a m’ndende mwachithokozo ndi mwachimwemwe. Zaka zimene ndinathera m’ndende za Hitler ndi m’misasa yachibalo zinali zovuta ndi za mayeso ochuluka. Koma sindikanakonda kuziphonya, pakuti zinandiphunzitsa kudalira pa Yehova kotheratu.”​—Johannes Neubacher, wazaka 91.

“Kudalira pa Yehova kotheratu”​—chimenecho ndicho chimene chinali chinsinsi cha chimwemwe chimene Mboni za Yehova zinali nacho. Motero, izo nzachimwemwe, ngakhale kuti zazingidwa ndi dziko lopanda chimwemwe. Chimwemwe chawo chinali choonekera pa Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” m’miyezi yapitayi. Tiyeni tipendenso mwachidule za misonkhano imeneyi yachimwemwe.

[Chithunzi patsamba 4]

Maria Hombach

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena