Kodi Luso Nchiyani?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SPAIN
KODI chinthu chokongola koposa chimene munaonapo nchiyani? Kodi kunali kuloŵa kwa dzuŵa kumadera otentha, mapiri okhala ndi chipale chofeŵa pamwamba pake, munda wa maluŵa m’chipululu, maonekedwe osiyanasiyana a nkhalango posakasa?
Ambiri a ife timakumbukira nthaŵi ina yabwino pamene tinakopedwa ndi kukongola kwa dziko lapansi. Timakonda kuthera tchuthi chathu m’malo onga ngati paradaiso, ngati tingathe, ndipo timayesa kujambula maonekedwe apadera kwambiri.
Nthaŵi yotsatira pamene muyang’anitsitsa kukongola kosaipitsidwa kumeneku, pali mafunso amene mungalingalirepo. Kodi simukanamva kuti kanthu kena kake kanali kusoŵeka ngati chithunzi chilichonse m’malo osungiramo zithunzi chinalembedwapo kuti “Wosadziŵika”? Ngati munasonkhezeredwa maganizo ndi mtengo wa zithunzizi ndi kukongola kwake pachisonyezero, kodi simungakonde kudziŵa munthu waluso amene anazipanga? Kodi tiyenera kukhutira ndi kusinkhasinkha za zinthu zambiri zodabwitsa za dziko koma nkunyalanyaza munthu Waluso amene anazilenga?
Zoonadi, pali anthu amene amanena kuti kulibe chotchedwa luso m’chilengedwe—kuti luso limafuna luntha la kulenga laumunthu ndi kuligwiritsira ntchito. Komabe, tanthauzo limeneli la luso nlosakwanira. Motero kodi luso kwenikweni nchiyani?
Kutanthauzira Luso
Tanthauzo la luso limene lingakhutiritse aliyense mwachionekere nlosatheka. Koma tanthauzo labwinopo limapezeka mu Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary, limene limanena kuti luso ndilo “kugwiritsira ntchito moganizira luntha ndi nzeru ya kulenga makamaka pa kupanga zinthu zokongola.” Pa maziko ameneŵa tinganene kuti munthu waluso ayenera kukhala ndi zonse ziŵiri luntha ndi nzeru ya kulenga. Atagwiritsira ntchito zinthu ziŵirizi, angapange chinthu chimene ena angaone kukhala chosangalatsa kapena chokongola.
Kodi nzeru ndi luntha zimangosonyezedwa ndi ntchito zaluso za munthu? Kapena kodi zimaonekeranso m’chilengedwe chotizungulira?
Mitengo yaitali ya redwood ku California, mitandaza yaikulu ya makorali m’Pacific, mathithi amphamvuwo a m’nkhalango ya mvula, ndi zinyama zokongolazo za m’madera a m’Afirika opanda mitengo yambiri zili zofunika kwambiri kwa anthu m’njira zosiyanasiyana kuposa chithunzithunzi cha “Mona Lisa.” Kaamba ka chifukwa chimenecho, UNESCO (United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization) yasankha Redwood National Park U.S.A.; Iguaçú Falls Argentina/Brazil; Great Barrier Reef, Australia; ndi Serengeti National Park, Tanzania monga mbali ya “Choloŵa cha Dziko” cha anthu.
Chuma cha chilengedwe chimenechi chimaphatikizidwa pa zinthu zachikumbukiro zopangidwa ndi manja a munthu. Chifukwa ninji? Chifuno chake ndicho kusunga chilichonse chokhala ndi “phindu lapadera la padziko lonse.” UNESCO ikunena kuti kaya kukongola kwake kukhale kuja kwa Taj Mahal, India, kapena kwa Grand Canyon, U.S.A., kumafunika kutetezeredwa kaamba ka mibadwo ya mtsogolo.
Koma simufunikira kupita ku paki kuti mukaone luntha la kulenga. Chitsanzo chabwino kwambiri ndicho thupi lanu. Osema a m’Girisi wakale anaona kapangidwe ka munthu monga chitsanzo cha luso labwino koposa, ndipo anayesayesa kukajambula bwino kwambiri monga mmene akanathera. Ndi chidziŵitso chathu chamakono cha mmene thupi limagwirira ntchito, tingamvetsetse ngakhale mokulirapo za mphamvu yopambana imene inafunika kuti lilengedwe.
Bwanji ponena za nzeru za kulenga? Tayang’anani mapangidwe okongola a nthenga za peacock, duŵa losansuka bwino la rose, kapena kuuluka kwaliŵiro kwa kambalame konyezima ka hummingbird. Indedi, limenelo linali luso ngakhale lisanajambulidwe pamanja kapena ndi kamera. Mlembi wina wa National Geographic, atachita chidwi ndi duŵa lofiirira la tacca lily, anafunsa wasayansi wina wachichepere chimene chifuno chake chili. Yankho lake lalifupi linali lakuti: “Zimavumbula malingaliro a Mulungu.”
Luntha ndi nzeru za kulenga sizinangochuluka m’zachilengedwe chotizungulira komanso zasonkhezera anthu aluso nthaŵi zonse. Auguste Rodin, wosema Wachifrenchi wotchuka, anati: “Munthu waluso ali bwenzi la chilengedwe. Maluŵa amalankhula naye mwa kuŵerama kwake kokongola ndi maonekedwe ogwirizana bwino a masamba ake.”
Aluso ena anavomereza poyera kusafikapo kwawo poyesayesa kujambula kukongola kwa chilengedwe. “Ntchito yeniyeni yaluso ili chabe chithunzithunzi cha ungwiro waumulungu,” anavomereza motero Michelangelo, woonedwa kukhala mmodzi wa anthu aluso opambana koposa.
Asayansi, pamodzinso ndi aluso, angatengeke maganizo ndi kukongola kwa chilengedwe. Profesa wa mathematical physics, Paul Davies, m’buku lake lakuti The Mind of God, akufotokoza kuti “ngakhale okana Mulungu olimba kwambiri nthaŵi zambiri amakhala ndi chimene chatchedwa ulemu pa chilengedwe, kuzizwa ndi kulemekeza kuya kwake ndi kukongola ndi kucholoŵana kwake, zimene zili zofanana ndi mantha a chipembedzo.” Kodi zimenezi ziyenera kutiphunzitsa chiyani?
Lusolo ndi Mwini Wake
Wophunzira luso amaphunzira za mwini wake wa lusolo kuti amvetsetse ndi kuyamikira luso lake. Iye amadziŵa kuti ntchito ya waluso imasonyeza umunthu wa mwini luso. Luso la chilengedwe nalonso limasonyeza umunthu wa myambitsi wa chilengedwe, Mulungu Wamphamvuyonse. “Zaoneka bwino zosaoneka zake . . . ndi zinthu zolengedwa,” anafotokoza motero mtumwi Paulo. (Aroma 1:20) Ndiponso, Mpangi wa dziko lapansi sali wosadziŵika ayi. Monga momwe Paulo anauzira afilosofi a ku Atene a m’nthaŵi yake, “[Mulungu] sakhala patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27.
Luso m’chilengedwe cha Mulungu silili lopanda chifuno ndipo silinakhaleko mwangozi. Kuwonjezera pa kusangalatsa moyo wathu, limavumbula luntha, malingaliro, ndi ulemerero wa Waluso wamkulu koposa, Mlinganizi wa Chilengedwe Chonse, Yehova Mulungu. Nkhani yotsatira idzafotokoza mmene luso limeneli lingatithandizire kumdziŵa bwinopo Waluso Wamkulu ameneyu.
[Mawu a Chithunzi patsamba 19]
Musei Capitolini, Roma