Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 11/8 tsamba 17-18
  • Kuchokera ku Mabotolo Kukhala Mkanda Wokongola

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchokera ku Mabotolo Kukhala Mkanda Wokongola
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupanga Mkanda ku Bida
  • Kuphunzira Lusolo
  • Uthenga Wabwino Malinga ndi Akatswiri
    Nsanja ya Olonda—1996
Galamukani!—1995
g95 11/8 tsamba 17-18

Kuchokera ku Mabotolo Kukhala Mkanda Wokongola

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU NIGERIA

MUKUFULUMIRA. Mukutenga botolo pa thebulo, komano likupulumuka m’manja mwanu, ndi kugwera pansi, niliphwanyika. Mukuusa mtima, kusesa mabotolowo, ndi kukawataya motayiramo zinyalala. Malinga ndi mmene mukudziŵira, uku ndiko kutha kwake.

Ngati munali kukhala ku Bida, Nigeria, kumeneko kukanakhala chiyambi chabe. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti pakati pa anthu Achinupe amene amakhala kumeneko, amisiri ake angathe kutenga botolo lophwanyika ndi kupangamo mkanda wokongola. Limeneli ndi luso limene laperekeredwa ku mibadwo yosiyanasiyana—limene langosintha pang’ono m’zaka mazana angapo zapitazo.

Kupanga Mkanda ku Bida

Chipala chake ndicho kanyumba kozungulira kopanga ndi dothi. Pakati pake pali uvuni yadothi. Mu uvunimo, amisiri amaikamo nkhuni, zimene amayatsa ndi moto. Motowo umakupizidwa ndi mvukuto wa manja nukhala wa malaŵi. Pamene nkhuni zinanso ziwonjezeredwa, malaŵi ofiira amalilima pamwamba pa uvuniyo. Botolo loikidwa pa kandodo amalilenjeketsa pa uvuniyo, ndipo posakhalitsa galasilo limafeŵa ndi kusungunuka.

Wopanga mkandayo amapanga umodziumodzi. Amaika kandodo kena kosongoka pamotopo pafupi ndi kandodo kamene galasi lalenjekekapo. Pamene nsonga ya kandodoko ifiira, amaiika pa galasi losungunukalo. Ndiyeno, mwa kutembenuza kandodoko ndi zala zake, amazengenezapo mlingo wa ukulu wa mkanda wa galasi losungunukalo.

Kenako, amapalapala magalasiwo kuti akhale mkanda ndi mpeni wautali waphanthiphanthi. Ngati ali katswiridi, iye amagwiritsira ntchito magalasi amaonekedwe osiyanasiyana, akumasakaniza mitundu yosiyanasiyana pa mkanda uliwonse umene akupanga. Potsirizira pake, amagwiritsira ntchito mpeniwo kupululira mkandawo m’chiwaya cha phulusa mmene umazizira. Tsopano mkandawo umakhala utatha kukonzedwa. Chiboo chopangidwa ndi kandodocho chimakhala choloŵetseramo chingwe cha mkandawo. Chotsalira ndicho kutsuka mkandawo ndiyeno kuutunga kuti ukhale wovala m’khosi.

Kuphunzira Lusolo

Kodi munthu amaphunzira bwanji luso la kupanga mkanda? Ana Achinupe amayamba mwa kuonerera. Pamene afika usinkhu wa zaka khumi, amathandiza kufunafuna nkhuni ndi kuzidula.

Sitepe yotsatira ndiyo kudziŵa kukupiza ndi mvukuto. Mvukutowo ndiwo matumba aŵiri opangidwa ndi nsalu, lililonse lomangiriridwa ku kamtengo. Kuti munthu akupize ndi mvukuto, ‘wokupizayo’ ayenera kugwira kamtengo kalikonse m’manja ndi kumavukuta mofulumira. Amafunikira nyonga ndi kuchita mogwirizana kwa manja akenso. Ayenera kukhala wamphamvu mokwanira kuti azivukuta mosalekeza mvukutowo panyengo yonse yopanga mkandayo, ndipo nyengoyo ingatenge maola ambiri!

Ayeneranso kukupiza mogwirizana bwino kuti makupizidwewo akhalebe ofulumira ndi osasintha, akumakupiza ndi mvukutowo mothamanga bwino. Ngati avukutira mochedwa kwambiri, kutentha kwa motowo sikudzafeŵetsa galasi mokwanira kuti aligwiritsire ntchito. Ngati avukutira mofulumira kwambiri, kutentha kumene kungatuluke kungachititse galasilo kugwera pamoto kuchokera pakandodopo.

Kwenikweni, wophunzira kupanga mkanda amagwiritsira ntchito mvukuto kwa zaka zisanu. Potsirizira pake, amaphunzira mmene angapangire mkanda. Mbali ina yovuta ya ntchitoyo ndiyo kuphunzira kupirira kutentha kwa moto, kumene ngati kuwonjezeredwa pa kutentha kwa m’malo a dzuŵa lotentha, kungakhale kovuta.

Munthuyo amaphunzira pang’onopang’ono. Wophunzirayo atathandizira mmisiri wopanga mkanda kugwiritsira ntchito tindodo, amaphunzira kupanga mkanda wamba waung’ono. Pamene nthaŵi ipita, amaphunzira kupanga mkanda wokulirapo ndi mkanda wokongoletsedwa ndi galasi la maonekedwe ena. Amisiri opanga mkanda amachititsa ntchitoyo kuoneka ngati yosavuta, koma pamafunika nthaŵi kuti munthu adziŵe umisiri wofunikira kupangira mitundu yosiyanasiyana ya mkanda, umodziumodzi, wonse wa ukulu wofanana, maumbidwe, ndi mtundu.

Kupanga mkanda ndi luso losangalatsa. Opanga mkanda amakondwera pamene aona anthu ochokera m’dziko lonselo atavala mkanda wawo wokongola—mkanda waung’ono wovalidwa ndi ana, mkanda wopangidwa mwaluso wovalidwa ndi akazi, ndi mkanda wolemera wamwambo wovalidwa ndi amuna. Anthu amasangalalanso panthaŵi ya phwando pamene amasonkhana mozinga chipala chake kudzaimba ndi kuvina mogwirizana ndi mayendedwe a mvukuto.

Buku lakuti History of West Africa likunena kuti: “Zopangapanga za luso la Anupe za . . . magalasi . . . zikali zinthu zina zabwino koposa za mu kontinentiyi.” Ena akuvomereza. Mmishonale wina Wachikristu anati: “Tinagula mkanda wa ku Bida ndiponso wa kumalo ena kuti tikapatse mabwenzi athu ndi achibale pamene tinamka kutchuthi. Pamene tinafika ku United States, mabwenzi athu anasankha mkanda wa ku Bida nthaŵi zonse!”

[Chithunzi patsamba 17]

Kutentha galasi pa uvuni

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena