Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 11/8 tsamba 32
  • Chakudya Chokwanira kwa Onse!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chakudya Chokwanira kwa Onse!
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chakudya Chochuluka kwa Onse
  • Kodi Mumadya Bwino Mwauzimu?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Chakudya Chanu Nchomanga Thupi Motani?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Kusowa kwa Chakudya Masiku Ano?
    Nkhani Zina
  • Munthu Aliyense Adzakhala Nacho Chakudya Chosakayikitsa
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 11/8 tsamba 32

Chakudya Chokwanira kwa Onse!

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRAZIL

NKOTHEKA kupeza chakudya chambiri, chabwino kwambiri nkukhalabe wosakondwa. Kuti tikhale ndi chimwemwe chenicheni chokhalitsa, kanthu kenakake nkofunika—chakudya chauzimu. Yesu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”—Mateyu 4:4.

Komano, kukana Mawu a Mulungu kumadzetsa njala yauzimu, monga momwe kunanenedweratu pa Amosi 8:11: “Ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” Komabe, matenda a njala yauzimu angapeŵedwe. Yesu analengeza kuti: “Odala ali osauka mumzimu;  . . . Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.” (Mateyu 5:3, 6) Monga momwe chakudya chopatsa thanzi choperekedwa mu unyinji woyenera chimalimbitsira thupi lathu, chakudya chauzimu chabwino chimalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi chiyembekezo chathu cha mtsogolo. Kodi tingayembekezere dziko lotani?

Chakudya Chochuluka kwa Onse

Tangoganizirani za dziko lokhala ndi chakudya chabwino chochuluka ndi chokoma. Dziko lopanda nkhondo, masoka, kapena nsautso imene imadzetsa njala kapena matenda a njala, amene amafooketsa anthu kapena kuwapsinja. Sipadzakhalanso anthu osoŵa pokhala kapena malova odalira pa kupatsidwa chakudya kapena zopereka, ndiponso kukwera mitengo kwa chakudya sikudzaumiriza anthu kungodya chilichonse kuti akhute. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; Zipatso zake zidzati waa.” (Salmo 72:16) Koma kodi zonsezi zidzachitika motani? Kodi ndani amene adzathetsa vuto la matenda a njala?

Mlengi wathu adzapereka chisamaliro chachikondi kwa anthu pa chakudya choyenera chimene amafuna. Ngakhale mkhalidwe wa dziko lapansi udzalamuliridwa, zikumatanthauza kuti mbewu sizidzalepheranso kumera. “Yehova adzapereka zokoma; ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.” (Salmo 85:12) Ndiponso, ngakhale kuti dziko lapansi lili lokhoza kupatsa chakudya chokwanira, ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetsa umbombo ndi kuponderezana, zinthu zimene zimachititsa kupereŵera kwa zinthu zogaŵiridwa, matenda a njala, ndi nsautso.

Inde, boma lakumwamba la Yehova lidzatsimikira kuti madongosolo alionse a ulimi ndi a mtengatenga okhalako adzachititsa kuti chakudya chabwino chiperekedwe kumene anthu akuchifuna. Kuyendetsa zinthu kwa Ufumuwo sikudzalemeretsa anthu oŵerengeka chabe ndi kusiya unyinji ukumavutika ndi moyo. M’malo mwa kuthedwa nzeru ndi kupanda chiyembekezo, madalitso a Ufumuwo adzabweretsa chimwemwe chosonyezedwa m’phwando lalikulu la zinthu lonenedweratu pa Yesaya 25:6 kuti: “M’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha.”

Tsopano, tayerekezerani kuti mkhalidwe wampikisano, wochititsa tondovi, wouma mtima wamakonowu watheratu. Palibe amene adzakhala wopereŵera chakudya kapena wodwala. Chotero, ngati mukufunadi kudzasangalala ndi moyo m’dziko latsopano limenelo, labadirani mawu a Yesu akuti: “Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha.”—Yohane 6:27.

Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena