Kodi Chakudya Chanu Nchomanga Thupi Motani?
NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRAZIL
Kodi mumasankha motani chakudya chanu? Pogula chakudya, kodi ndi zinthu ziti zimene zimakusonkhezerani? Kodi ndi mapaketi ake okongola? Mtengo? Kusavuta kukonza? Mawu okopa onenedwa posatsa malonda? Kapena maonekedwe a chakudyacho ndi kukoma kwake basi? Kupanga zosankha zoyenera kungasonyeze kaya ngati mumadya chakudya chomanga thupi kapena chosamanga thupi, kapena ngati thanzi lanu limalimbitsidwa kapena kuwonongedwa.
UMPHAŴI ndiwo chochititsa chachikulu cha kutupirana. Pamene kuli kwakuti anthu ambiri azoloŵera kukhala ndi chakudya, ena miyandamiyanda samadya kaŵirikaŵiri chakudya chomanga thupi. “M’nyumba muno timadya zilizonse zimene tingapeze,” anatero woumba njerwa wina ku Brazil, tate wa ana asanu ndi mmodzi. Nthaŵi zambiri zimenezo ndizo mkate wofumuka ndi khofi wosukuluka kapena mpunga ndi nyemba. Kwenikweni, malinga ndi lipoti la Food and Agriculture Organization ya United Nations, 20 peresenti ya anthu a padziko lonse akuvutika ndi njala. Pamene kuli kwakuti m’maiko ena a m’Afirika muli njala yaikulu, ku Asia kuli anthu ochulukirapo anjala. Ngakhale ku United States, 12 peresenti ya anthu, kapena anthu 30 miliyoni, akunenedwa kuti alibe chakudya chokwanira.
Kudya zosayenera sikuli koipa chabe komanso kumapha. “Kutupirana kochititsidwa ndi kadyedwe kosayenera ka ana kumapha miyoyo yambiri kuposa njala yeniyeni kuŵirikiza nthaŵi 10,” akutero wofufuza William Chandler. “Limodzi ndi kutha madzi m’thupi chifukwa cha kutseguka m’mimba, kutupirana kuli wakupha wamkulu padziko.” UNICEF (United Nations Children’s Fund) ikusimba: “Palibe mliri, kusefuka kwa madzi, ngakhale chivomezi chilichonse kapena nkhondo zimene zapha miyoyo 250,000 ya ana mumlungu umodzi wokha.” Koma malinga ndi kunena kwa bungwe lina la United Nations, chimenecho ndicho chiŵerengero cha ana amene akufa padziko lonse chifukwa cha kutupirana ndi matenda amene kumadzetsa. Kwenikweni, kusakaza kwa kutupirana nkosaneneka: Luso la kuphunzira limachepa, antchito amachepa mphamvu, zinthu zopangidwa pantchito ndi mkhalidwe wake zimatsika.
Komabe, kudya zakudya zoyenera zokwanira kungathetse kuchepa kwa chakudya m’thupi ndi ziyambukiro zake zonga kuchepa mwazi m’thupi ndi matenda ena. Chithandizo cha boma chonga chakudya cha masana cha kusukulu ndi malo othandiza osauka ndi chakudya zingachepetse kutupirana m’madera ena, koma malinga ndi akuluakulu a UNICEF, pakufunikira $25,000,000,000 pachaka kuchepetsera imfa za ana zochititsidwa ndi kutseguka m’mimba, chibayo, ndi chikuku. ‘Zimenezo ndi ndalama zambiri,’ ena angatero. Koma kwanenedwa kuti zimenezo nzimene Amereka amatayira pa nsapato za maseŵero ndi zimene anthu a ku Ulaya amatayira pa vinyo m’chaka chimodzi. Vuto lina ndilo la kuchepetsa zinthu zowonongedwa. Ngakhale kuti Abrazil onga ngati 32 miliyoni ali ndi njala, Unduna wa Zaulimi wa Brazil ukusimba “kuti kuwonongedwa kwa zokolola [za ndalama $1,500,000,000] pozinyamula kapena pamene zikusungidwa kumatayitsa 18 mpaka 20 peresenti ya zolimidwa za dzikolo.” Pali mavuto aakulu a zaulimi, kuthirira, kasungidwe ka zakudya, ndi kanyamulidwe kake m’maiko ambiri; komabe, dziko lapansi likhozabe kutulutsa zochuluka kaamba ka onse. Chotero kodi mungathetse motani vuto la kudyetsa banja lanu?
Ndalama Zokha Sizokwanira
M’maiko osatukuka anthu kaŵirikaŵiri amakhoza kudyetsa mabanja awo mwa kukhala ndi ntchito ziŵiri kapena zitatu. M’Brazil anthu 1.5 miliyoni pachaka amasiya mabanja kapena mabwenzi awo nasamukira kumizinda yaikulu kukafuna ntchito ndi chakudya. Ngakhale kuti thanzi kwakukulukulu limadalira pa zimene anthu amadya, ndalama zawo zambiri zimapita ku zovala, nyumba, ndi kayendedwe.
Chosangalatsa nchakuti, zakudya zofala, zonga mpunga, nyemba, chimanga, mbatata, chinangwa, nthochi, limodzinso ndi nyama ndi nsomba pang’ono, zili magwero aakulu a zomanga thupi ku mabanja onse padziko lonse. Katswiri wa chakudya chomanga thupi wa ku Brazil José Eduardo de Oliveira Dutra anati: “Nyemba ndi mpunga ndi msanganizo umene uli ndi zomanga thupi zambiri. Ndi chakudya wamba ndi chosakwera mtengo chimenecho, nkotheka kuthetsa njala [m’dzikoli].” Inde, chakudya chosakwera mtengo ndi chomanga thupi chingapezeke kumene mumakhala. Kapena mungalime chakudya chanu china.
Ngakhale ngati mungakhale ndi ndalama zokwanira, kodi mumagula nazo chakudya chomanga thupi kaamba ka banja lanu? Kapena kodi mumagula zozuna kapena chakudya chosamanga thupi chifukwa cha kukopeka ndi kusatsa malonda kopanda pake ndi kopitiriza, motero mukumanyalanyaza kufunika kwa maproteni, maminero, ndi mavitameni? Kodi mumakonda kukoma kwake kuposa phindu lake? The World Book Encyclopedia ikuti: “Kuti apeze ndi kusunga thanzi labwino, anthu ayenera kukhala ndi chidziŵitso choyambirira cha thupi la munthu ndi mmene limagwirira ntchito. Mpokhapo pamene angadziŵe zimene zingathandizire thanzi lawo kapena kusalithandizira kapena zimene zingaliwononge. Kuphunzira za thanzi kuyenera kukhala mbali ya maphunziro a munthu aliyense.”
Zoona, sitimangokhalira moyo kudya, koma chakudya chili mbali yofunika pa moyo wathu. Baibulo limanena za kudya bwino monga mphotho ya ntchito yakhama, kuti: “Munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Kodi mumaona chakudya chabwino kukhala chopindulitsa ndi chofunika? Ngati ndi choncho, chonde ŵerengani nkhani yotsatira yonena za mmene kudya zoyenera kungapindulire inu ndi banja lanu.