Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 3/8 tsamba 5-7
  • Mmene Chakudya Choyenera Chingawongolere Thanzi Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Chakudya Choyenera Chingawongolere Thanzi Lanu
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuikiza Kwanzeru
  • Kodi Nkudyeranji Zakudya Zamitundumitundu?
  • Lingaliro Loyenera la Chakudya ndi Thanzi
  • Kodi Chakudya Chanu Nchomanga Thupi Motani?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Pagona Vutoli Mpati, Nanga Kuipa Kwake N’kotani?
    Galamukani!—2003
  • Chakudya Chopatsa Thanzi N’chosasoŵa
    Galamukani!—2002
  • Kodi Mumadya Bwino Mwauzimu?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 3/8 tsamba 5-7

Mmene Chakudya Choyenera Chingawongolere Thanzi Lanu

NKOSANGALATSA chotani nanga kuona mwana wodyetsedwa bwino! Komabe, sizimangochitika kuti mwana wathanzi akhaleko. “Chakudya wamba koma chomanga thupi chinali choyamba nthaŵi zonse m’banja lathu osati chabe chifukwa chakuti zochuluka za ndalama zathu zinali zogulira chakudyacho komanso chifukwa cha nthaŵi imene inatheredwa pa kuchikonza ndi kuchidya tili pamodzi,” akukumbukira Kate, Mkanada wokhala ku Brazil. “Popeza amayi sankagwira ntchito kwina, tinali kufika panyumba tsiku lililonse kuchokera kusukulu fungo lokoma likumamveka la chakudya cha madzulo chimene anali kukonza kapena la pie kapena keke imene anaphika.”

Komabe, m’malo mochirikizidwa ndi chakudya choyenera, “anthu pafupifupi 780 [miliyoni] m’maiko osauka, mmodzi mwa asanu a anthuwo, samapeza chakudya chokwanira,” ikutero The Economist. “Anthu ofika pa 2 biliyoni amene amapeza chakudya chokwanira kuthetsa njala yawo amasoŵabe mavitameni ndi maminero ofunikira.” Wakudya zosakwanira samangofooka komanso sangathandize ena kwambiri. Chifukwa chake, ponena za ana odya zosakwanira, katswiri wa zachuma Eduardo Giannetti da Fonseca wa pa São Paulo University, Brazil, anagwidwa mawu kuti: “[Kuwonongedwa kwa chuma cha anthu] kumeneku nkoipa kwambiri kuposa kanthu kalikonse. . . . Ndikhulupirira kuti pakati pa ana ameneŵa pali maluso ndi nzeru zimene zimangobisika chifukwa cha umphaŵi. Pakati pawo, m’mikhalidwe yosiyana, pakanakhala munthu wonga Albert Einstein.” Magazini a Veja akuti: “Dzikoli likutaya mphamvu zimene zikuwonongeka chifukwa cha kudya zosayenera ndipo likutaya amene akanakhala nkhokwe ya nzeru, luso la kupanga zinthu, ndi nyonga.” Chifukwa chake, ngakhale kuti pali kukwera kwa mitengo, makolo anzeru amayalira ana awo maziko olimba mwa kuikiza m’chakudya chomanga thupi.

Kuikiza Kwanzeru

“Kuikiza” kumatanthauza “kugwiritsira ntchito chinthu kaamba ka mapindu kapena maubwino a mtsogolo.” Kodi ndimotani mmene mungaikizire m’zakudya? Ngati mufunikira kusankha, kodi mudzapeŵa zakudya zosafunikira kwenikweni kapena zinthu zapamwamba ndi kugwiritsira ntchito ndalama zanu zochepa kugulira chakudya choyenera?

“Sikuti mphamvu za thupi zimakhala zosagwira ntchito kufikira zitasonkhezeredwa pa kubadwa; umboni umasonyeza kuti mphamvu za thupi zimagwira ntchito kubadwa kusanachitike nkomwe,” ikutero The New Encyclopædia Britannica. Chotero, njira yabwino yoyambira kudyetsa mwana ndiyo kukhala nakubala wakudya bwino. Chinthu chotsatira—pambuyo pa kubadwa—nchakuti khandalo liziyamwa bere, popeza kuti mkaka wa munthu umapereka chakudya chokwanira ndiponso umaletsa matenda ofala. Facts for Life, chofalitsa cha United Nations, chimati: “M’miyezi yoŵerengeka yoyamba ya moyo wa khanda, mkaka wakubere wokha ndiwo chakudya ndi chakumwa chokha chabwino koposa. Makanda amafunikira zakudya zina, kuwonjezera pa mkaka wakubere, atakwanitsa miyezi inayi kufikira isanu ndi umodzi.”

Pamene kuli kwakuti thupi la munthu limasintha malinga ndi mkhalidwe, siliyenera kuchitiridwa mosasamala. Nkofunika kuliumba ndi chakudya choyenera poyamba m’moyo. The World Book Encyclopedia imati: “Pofika nthaŵi imene munthu ali ndi zaka 6, ubongo umakhala utakwana pa kulemera kwake kwenikweni kwa pafupifupi mapaundi 3 (makilogramu 1.4). Pakubadwa ochuluka a maselo a ubongo amakhala alipo kale, choncho kuwonjezereka kwa kulemerako kumachitika makamaka chifukwa cha kukula kwa maselowo. M’nyengo ya zaka zisanu ndi chimodzi imeneyi, munthu amaphunzira ndi kukhala ndi khalidwe latsopano mofulumira koposa m’moyo.” Chifukwa chake, ngakhale ngati mwana amadya chakudya chokwanira chaka chake chachisanu ndi chimodzi chitapita, ndi maselo owonjezera oŵerengeka chabe a ubongo amene amapangika. Kate akuti: “Chakudya choyenera, chomanga thupi chili ina ya mphatso zazikulu koposa zimene makolo angapatse ana awo. Ngakhale ngati zotchedwa zofunika za moyo, zimene kaŵirikaŵiri zimangokhala zosangulutsa chabe, sizingaperekedwe, makolo amene amaikiza m’thanzi la maganizo ndi la kuthupi la ana awo amawapatsa chiyambi cha moyo kuyambira pa ukhanda chimene chili chamtengo wapatali.”

Kodi Nkudyeranji Zakudya Zamitundumitundu?

Mwana amafunikira chakudya chokhala ndi maproteni ochuluka kuti akule kuthupi ndi maganizo. Kudya zosayenera kumalepheretsa kukula kwa maganizo a mwana kusukulu, ndipo mwanayo angakhale wamphwayi ndi wotopa, wosakhoza kumvetsera mosamalitsa kapena kukumbukira zimene zikuphunzitsidwa. Osachepera pa matenda 25 osiyanasiyana a kupereŵera kwa zinthu zina amadzetsedwa ndi kusoŵa chimodzi cha zomanga thupi zazikulu—proteni, mavitameni, mafuta ofunika, kapena zinthu zina zomanga thupi.

Talingalirani nkhani ya Joaquim. “Banja lathu linali losauka,” iye akutero. “Koma tinali ndi dimba limene tinkalimako pafupifupi zonse zimene tinkadya. Pachakudya chilichonse tinali ndi chimanga ndi mkate wophikidwa ndi ufa wa rye wosapuntha, ndipo zimenezo zinathandizira pa kudya zoyenera. Pafupifupi tsiku lililonse amayi ankaphika supu wosanganiza ndi ndiwo zamasamba zamitundumitundu, kuphatikizapo nyemba, ndipo zimenezi zinatipatsa zomanga thupi zambiri zofunikira. Sitinali kudya nyama yambiri, koma nsomba zokha tinkadya, makamaka masaladinya, cod, ndi matemba.” Akuwonjezera: “Amayi anali ndi ana asanu, ndipo sindikukumbukira kuti aliyense wa ife anadwalapo kusiyapo kukhala ndi chifuŵa ndi chimfine. Ndikhulupirira kuti chakudya chathu choyenera ndicho chinachititsa zimenezo.” Nakubala wina wa ana asanu ndi aŵiri akufotokoza: “Tinafunikira kukhala ndi chakudya chomanga thupi pa mtengo wotsika. Chotero tinalima dimba la ndiwo zamasamba, limene, ngakhale kuti linali laling’ono, linapatsa zochuluka zokwanira zosoŵa zathu.” Iye akuwonjezera: “Ana athu sanadwalepo kwambiri ndipo nthaŵi zonse anali kupambana kusukulu.”

Thupi lanu limafuna zomanga thupi 22 mwa makhemikolo 103 ovomerezedwa mwa lamulo. Ngakhale kuti nkovuta kudziŵa mlingo weniweni wa mavitameni, maminero, ndi maproteni amene mufunikira panokha, chakudya choyenera chidzakupatsani zosoŵa zanu. Buku lina linati: “Mfungulo ya kudya zoyenera ndiyo zakudya zamitundumitundu zimene zimaphatikizapo zomanga thupi zonse.”

Bwanji nanga ngati ana anu samakonda zakudya zina, zonga ndiwo zamasamba oŵaŵa? Malinga ndi kunena kwa munthu wina wodziŵa kuphika, makolo ayenera kupereka “ndiwo zamasamba zonse zimene zimapezeka kwawoko. Achikulire ambiri samadya ndiwo zamasamba chifukwa chakuti sanazidziŵe pamene anali ana. Popeza kuti ndiwo zamasamba zimapatsa fiber ndi mavitameni ambiri amene timafunikira ndipo nzotsika mtengo, makolo nthaŵi zonse ayenera kukhala nazo kaamba ka ana awo.” Chotero bwanji osaphunzira maphikidwe atsopano amene amafuna ndiwo zamasamba zaziŵisi ndi zipatso, mwina mwake zoikidwa mu soufflé kapena msuzi wokoma? Ponena za zotchedwa zakudya za ma calorie zopanda zomanga thupi, iye akuti: “Makolo sayenera kukhala ndi maswiti m’nyumba kusiyapo panthaŵi zapadera. Ngati [ana] sakhala nawo, sadzawadya.”

Ngakhale kuti kudya chakudya choyenera chokwanira kumachepetsa ngozi ya kutupirana, anthu ena amadzitengera mavuto mwa kudyetsa. Kudyetsa ma calorie oposa amene thupi lifunikira kungachititse kunenepetsa, kumene amati kumadzetsa nthenda ya shuga ndi ya mtima.a Popeza mankhwala ngakhale machitachita akuthupi sangaloŵe m’malo mwa kadyedwe koyenera, lingaliro labwino ndilo kuchepetsa kudya mafuta, maswiti, mchere, ndi kumwa moŵa. Ndiponso, insaikulopediya ikuti, “njira ziyenera kutengedwa kuchepetsa njala, kusungulumwa, kuchita tondovi, kunyong’onyeka, mkwiyo, ndi kutopa, zimene chilichonse cha izo chingachititse kudyetsa.”

Lingaliro Loyenera la Chakudya ndi Thanzi

Baibulo silili buku la kadyedwe; komabe, limatithandiza kukhala ndi lingaliro loyenera pa nkhani za thanzi. Mtumwi Paulo anachenjeza za awo amene amalamula ena ‘kusiya zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.’ (1 Timoteo 4:3) Mulungu amafuna kuti tikhale okhutira ndi kugwiritsira ntchito bwino zimene zilipo. “Zapang’ono, ulikuwopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.”—Miyambo 15:16.

Lerolino palibe aliyense amene ali ndi thanzi langwiro. Chotero bwanji osadekha, m’malo mwa kukhala wosasamala kapena woda nkhaŵa kwambiri? Kufunitsitsa kwathu kosalamulirika kapena kotengeka maganizo kudziŵa za kadyedwe kapena za thanzi kungatitayitse kukhazikika kwathu.

Mosasamala kanthu za zoyesayesa za kusamalira thanzi lathu, malinga ndi mmene zinthu zilili tsopano, timakalamba ndi kufa m’kupita kwa nthaŵi. Komabe, chokondweretsa nchakuti Baibulo limatitsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa kutupirana ndi matenda. Ngakhale kuti zolinganiza za anthu za kuthetsa njala zalephera, tingayang’ane kutsogolo ku dziko limene lidzakhala ndi chakudya chochuluka chomanga thupi kaamba ka onse.—Salmo 72:16; 85:12.

[Mawu a M’munsi]

a “Akatswiri ena amakhulupirira kuti mumakhala wonenepetsa ngati muposa ndi 20 peresenti kulemera ‘koyenera’ . . . kolingana ndi kutalika kwanu, kaumbidwe ka thupi ndi usinkhu.”—The American Medical Association Family Medical Guide, tsamba 501. Onaninso Galamukani! wa May 8, 1994, “Achichepere Akufunsa Kuti . . . “Kodi Ndingachepetse Motani Thupi?” ndi June 8, 1989, “Kodi Kutaya Kulemera Kuli Nkhondo Yosagonjetseka?”

[Bokosi patsamba 7]

MALINGALIRO OTHANDIZA ANA ANU KUKHALA NDI KADYEDWE KABWINO

◻ Perekani chitsanzo chabwino.

◻ Musalole ana kudya zimene amafuna.

◻ Peŵani kukhala ndi chakudya chosamanga thupi kapena maswiti panyumba.

◻ Phunzitsani ana kukonda zakudya zosiyanasiyana.

◻ Khalani ndi nthaŵi yoikika ya chakudya, kuphatikizapo mfisulo.

◻ Musalole kusatsa malonda kwa pa TV kulamulira zimene mumadya.

◻ Musalole ana kudzitengera okha zakudya m’firiji.

◻ Phunzitsani ana kuthandiza kukonza chakudya.

◻ Kulitsani chiyamikiro kaamba ka zakudya za tsiku ndi tsiku.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena