Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 12/8 tsamba 31
  • Krisimasi—Chiyambi Chake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Krisimasi—Chiyambi Chake
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Krisimasi—kodi Nchifukwa Ninji Iri Yotchuka Kwambiri M’japani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chiyambi cha Krisimasi Yamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Chifukwa Chake Krisimasi Siiri ya Akristu
    Galamukani!—1991
  • Kodi Akhristu Ayenera Kukondwerera Khirisimasi?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 12/8 tsamba 31

Krisimasi—Chiyambi Chake

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ITALY

MASIKU atatu chabe Krisimasi ya 1993 isanafike, Papa John Paul II anavomereza kuti kukondwerera Krisimasi si kozikidwa m’Baibulo. Ponena za deti la December 25, papayo anavomereza kuti: “Kale patsiku limenelo m’chikunja, kubadwa kwa ‘Dzuŵa Losagonjetseka’ kunali chikondwerero chogwirizana ndi winter solstice.” Motero, kodi Krisimasi inayamba motani? Papa anapitiriza kuti: “Kunaoneka kwanzeru ndi kwachibadwa kwa Akristu kutenga phwando la Dzuŵa loona lokha, Yesu Kristu, ndi kuliika m’malo mwa chikondwerero chimenecho.”

“M’mawu ena,” analemba motero mtolankhani Nello Ajello mu La Repubblica, “munthu wina analengeza kubadwa kwa Yesu padeti longoganizira, lopeka, labodza.” Kodi kupeka kumeneku kunachitika liti? Chofalitsidwa china cha Vatican chinati: “Dzoma la Krisimasi linakhalapo kwa nthaŵi yoyamba mu 354 [C.E.].”

Bwanji ponena za January 6, Epifano, limene lili chikumbukiro cha kubwera kwa Anzeru kudzachezera Yesu wobadwa chatsopanoyo? “Umboni wochuluka umatichititsa kukhulupirira kuti kusankha January 6, monga kuja kwa December 25 kaamba ka tchuthi cha Chiroma chokondwerera kubadwa kwa Yesu, kunasonkhezeredwanso ndi kukumbukira za tsiku la chochitika china chachikunja,” chinapitiriza motero chofalitsidwacho. “Kwenikweni ku Alexandria, pa usiku wa pakati pa January 5 ndi 6, akunja anali kukumbukira kubadwa kwa mulungu Aeon (mulungu wa nthaŵi ndi umuyaya). . . . Kukuoneka kuti Tchalitchi chinafuna kupanga phwando limeneli kukhala Lachikristu.”

Yesu sanalamulirepo otsatira ake kusanganiza kulambira koona ndi miyambo yachikunja. M’malo mwake, anawauza kuphunzitsa “zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Ndiponso, pamene anakumana ndi atsogoleri achipembedzo a m’tsiku lake, Yesu anawafunsa kuti: “Mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?” (Mateyu 15:3) Funso limodzimodzilo lingafunsidwenso ponena za otchedwa Akristu amene amalimbikira miyambo yachikunja lerolino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena