Mboni za Yehova Zothandiza Kuwongolera Opaleshoni ya Mtima
DAILY NEWS ya ku New York ya August 27, 1995, inalemba nkhani ya mutu wakuti, “Opaleshoni Yopanda Mwazi.” Iyo inanena kuti Hospital-Cornell Medical Center ya ku New York inali “kudzavumbula njira yatsopano yochitira opaleshoni ya coronary bypass—opaleshoni imodzimodzi imene posachedwapa inafunika kwa amene kale anali Bwanamkubwa David Dinkins—popanda kutayapo ngakhale dontho la mwazi.”
“Atasonkhezeredwa ndi zosankha za Mboni za Yehova,” nyuzipepalayo inatero, “zotulukapo za njira yatsopanoyi . . . zidzaonekera pa kusawononga ndalama zikwi mazana a madola za zipatala ndi kuchepetsa kwenikweni ngozi ya kuika mwazi woipa mwa odwala.” Dr. Todd Rosengart, mkulu wa programu ya chipatalacho ya opaleshoni yopanda mwazi, anati: “Tsopano tikhoza kuchepetsa unyinji wa mwazi wofunika kuikidwa mkati mwa opaleshoni imeneyi kuchokera pa mabotolo aŵiri mpaka anayi a masiku onse pa wodwala mmodzi kufika pa chabe.”
Dr. Karl Krieger, dokotala wa chipatalacho wa opaleshoni ya mtima, amene anathandiza kupeza njirayo, anati: “Mwa kuchotsapo chifuno cha mwazi woperekedwa ndi anthu ena ndi zinthu zopangidwa ndi mwazi, tikuchepetsanso matenda ena a pambuyo pa opaleshoni amene nthaŵi zambiri amachititsidwa ndi kuikidwa mwazi.”
Akatswiri ena akunena kuti “opaleshoni ya bypass yopanda mwazi imachepetsa nthaŵi imene munthu amakhala mu pa chisamaliro chapadera pambuyo pa opaleshoni—kuchoka pa maola 24 kapena kuposapo kufika pa maola asanu ndi limodzi okha. Odwala pa amene zimenezi zinayesedwapo anakhoza kukhalanso bwino mwamsanga ndi kutuluka m’chipatala m’maola 48.” Zimenezi zikutanthauza kusataya ndalama zambiri za zipatala, boma, ndi makampani a inshuwalansi. Dr. Rosengart anayerekezera kuti “opaleshoni imeneyi ingathandize kusataya pafupifupi $1,600 pa wodwala mmodzi.”
Nkhani ya mu Daily News ikupitiriza kuti:
“Chodabwitsa nchakuti, opaleshoni yatsopanoyi siinasonkhezeredwe ndi mkhalidwe wa zachuma kapena kufulumira kwa zamankhwala, koma ndi kudzipereka kwa chipembedzo. Gulu la Mboni za Yehova—limene zikhulupiriro zawo zimaletsa kuikidwa mwazi—linali kufuna chithandizo kaamba ka anzawo achikulire amene akudwala matenda a mtima. . . .
“Posonkhezeredwa ndi gulu la Mboni za Yehova, madokotala anasanganiza maluso awo osungira mwazi ndi mankhwala atsopano. Iwo anapezanso njira yatsopano yogwiritsira ntchito makina awo akale a heart and lung ogwiritsiridwa ntchito kusunga odwala ali moyo powachita opaleshoni ya mtima.
“Kuwonjezera pa odwala 40 a Mboni za Yehova amene anasankhidwa kaamba ka kuyesa opaleshoni yopanda mwazi, miyezi isanu ndi umodzi yapitayo kagulu ka New York-Cornell kanayambitsa opaleshoniyo kwa odwala ena onse. ‘Kuyambira pamenepo, iwo achita maopaleshoni 100 a bypass opanda mwazi otsatizana ndipo sipanakhale akufa,’ anatero Krieger. Imfa za opaleshoni ya bypass yanthaŵi zonse zili pafupifupi 2.3%.”
Kuzungulira dziko lonse lapansi zipatala 102 zayamba programu ya kuchita opaleshoni yopanda mwazi m’zipatalazo, zikumachititsa njira za opaleshoni zabwino zimenezi kupezeka kwa odwala ena onse padziko lonse lapansi.