Amgubuduza Tubzi a mu Afirika pa Ntchito Yopulumutsa!
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA
ZAKA mazana aŵiri zapitazo, pamene kwa nthaŵi yoyamba ng’ombe zinabweretsedwa ku Australia, ndani akanadziŵiratu mavuto aakulu amene adzakhalako m’dzikomo?
M’kupita kwa nthaŵi, msipu unaphimbidwa ndi ndoŵe za ng’ombe, zikumaletsa kumera kwa udzu m’malo ena kapena kupangitsa udzuwo kukhala wosakhoza kudyedwa ndi ng’ombe. Miyulu ya ndoŵezo m’kupita kwa nthaŵi inakhala malo obadwirapo ntchentche zovutitsa. Ndipo, malinga ndi nkhani ya m’magazini a Africa—Environment & Wildlife, m’ma 1970 vutolo linafika “pamlingo waukulu kwambiri wokhoza kuwononga chuma ndi zamoyo ndi malo awo okhala.” Kunaŵerengeredwa kuti “mahekitala oposa mamiliyoni aŵiri [maekala mamiliyoni asanu] a mabusa amaleka kubala chaka chilichonse . . . , nitrogen yambiri siinali kubwerera kunthaka chifukwa cha ndoŵe zosafotseredwa, ndipo chiŵerengero cha ntchentche chinali kukwera kufikira pa kukhala mliri.”
Kodi nchiyani chinalakwika? Mu Afirika amgubuduza tubzi mwachibadwa amayeretsa minda bwinobwino mwamsanga. Ndoŵe zofotseredwazo, zimatupitsa nthaka ndi kuichititsa kukhala yatidziboo tambiri, motero ikumachititsa zinthu kumera bwino. M’njira imeneyi, mitundu yowononga yantchentche imachepetsedwa ndipo mazira ake amawonongedwa, zikumaletsa kufala kwa matenda ochititsidwa ndi mabakiteriya.
Komabe, zimene okhala mu Australia oyamba sanadziŵe zinali zakuti amgubuduza tubzi a ku Australia amagwira ntchito pa ndoŵe zazing’ono, zolimba, zobulungira za nyama za kumeneko chabe ndipo sangachite ndi ndoŵe zochuluka ndi zaziŵisi za ng’ombe.
Kodi anafunikira kuchitanji? Kuitanitsa amgubuduza tubzi kuchokera ku maiko ena! Mtundu wa mu Afirika, mwachitsanzo (imene ili pafupifupi mitundu 2,000), umachita ndi ndoŵe zochuluka kwambiri zaziŵisi, zonga zija zosiyidwa ndi njovu. Kwa amgubuduza tubzi ameneŵa, kufotsera ndoŵe zang’ombe nkwapafupi kwambiri. Komatu pamafunika chiŵerengero chachikulu kwambiri cha amgubuduza tubzi kuti ntchitoyo ichitike! Africa—Environment & Wildlife ikunena kuti m’paki imodzi, “amgubuduza tubzi 7 000 anaŵapeza pa mulu umodzi wa ndoŵe za njovu,” ndipo m’paki inanso, “22 746 . . . anatengedwa kuchokera pa mulu wa 7 kg wa ndoŵe za njovu m’maola 12.” Tangolingalirani unyinji wa amgubuduza tubzi amene akufunika kuti athetse vuto la Australia lochititsa tsokalo!
Mwamwaŵi, zinthu pakali pano zikuwongokera kwambiri—zonsezo chifukwa cha amgubuduza tubzi a mu Afirika.