Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 5/8 tsamba 12-15
  • Aids mu Afirika Kodi Dziko Lachikristu Lili ndi Mlandu Waukulu Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aids mu Afirika Kodi Dziko Lachikristu Lili ndi Mlandu Waukulu Motani?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chipembedzo—Kodi Chinathandizira Kufalikira Kwake?
  • Mmene Afirika Anakhalira “Wachikristu”
  • Kuloŵerera kwa Zosangulutsa Zakumadzulo
  • Mankhwala a Vutolo
  • Kodi Nchifukwa Ninji Afirika Akuvutika Kwambiri Chotero?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Aids Yafalikira Kwambiri Motani mu Afirika?
    Galamukani!—1992
  • Kuthandiza Awo Amene Ali ndi AIDS
    Galamukani!—1994
  • AIDS—Vuto la Azaka Zapakati pa 13 ndi 19
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 5/8 tsamba 12-15

Aids mu Afirika Kodi Dziko Lachikristu Lili ndi Mlandu Waukulu Motani?

Yolembedwa ndi mtolankhani wa Galamukani! mu Afirika

Malinga ndi mmene lagwiritsidwira ntchito m’nkhani ino, liwulo “Dziko Lachikristu” likunena za Chikristu chapakamwa chabe, chosiyana ndi Chikristu cha m’Baibulo.

Christendom (Dziko Lachikristu)

“Madera a dziko kumene anthu ake ochuluka amati chipembedzo chawo ndi Chikristu.”—Webster’s New World Dictionary.

AIDS

‘Nthenda yochita kuitenga ya kuchepa kwa mphamvu yoletsa matenda imene imachititsa maselo oletsa matenda kuloŵedwa ndi retrovirus.’—Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary.

AIDS ndi mliri wapadziko lonse. Anthu ngati 17 miliyoni aloŵedwa kale ndi HIV, vairasi imene imachititsa AIDS. Ndipo ikufalikira mofulumira.

Pamene kuli kwakuti anthu asumika maganizo kwambiri pa nkhani za mankhwala, ndale, ndi zokhudza mtima zogwirizana ndi mliriwu, pakambidwa zochepa kwambiri ponena za nkhani zachipembedzo zophatikizidwa. Tsopano lingaliro lakuti chipembedzo chili ndi mbali m’kufalikira kwa AIDS lingaoneke kukhala lapatali kwambiri kwa oŵerenga ena. Komatu silopanda pake pamene mulingalira za mkhalidwe umene wakhalako m’kontinenti ya Afirika.

AIDS yasakaza Afirika kwambiri.a Ena amati m’kontinentiyi mumapezeka 67 peresenti ya odwala AIDS padziko lonse. Ku Chad chiŵerengero chochitidwa lipoti cha odwala ake pazaka zisanu zapitazo chaŵirikiza nthaŵi 100. Komabe, kukuyerekezedwa kuti limodzi lokha la magawo atatu a odwala ake onse ndilo lachitidwa lipoti. Malinga ndi lipoti la World Bank, AIDS yakhala chochititsa imfa chofala koposa pakati pa achikulire ambiri m’matauni a m’Afirika.

Chipembedzo—Kodi Chinathandizira Kufalikira Kwake?

Ndithudi, Chikristu—chipembedzo chimene Yesu Kristu anaphunzitsa—sichingapatsidwe mlandu wa tsoka limeneli. Komabe, monga momwe pakusonyezera pansipa, liwulo “Dziko Lachikristu” limaphatikiza pamodzi maiko aja kumene anthu amati ndi Akristu. Ndipotu Dziko Lachikristu lilidi ndi mlandu mosakayikira konse. Sikuti matchalitchi ndiwo anapanga vairasi ya AIDS kapena kuifalitsa. Koma AIDS yafalikira mu Afirika makamaka chifukwa cha kugonana kwauchiwerewere kwa amuna ndi akazi.b Chifukwa chake AIDS ingatchedwe vuto la makhalidwe ndipo motero, ikubutsa mafunso ovuta achipembedzo. Ndi iko komwe, “Chikristu” cha mu Afirika chinachita kubwera kuchoka kumaiko Akumadzulo. Atsogoleri a matchalitchi anayamba kutembenuzira Aafirika ku chipembedzo chawo, akumati chinapereka moyo woposa njira zamwambo zachiafirika. Kodi mphamvu ya Dziko Lachikristu inawongoleradi makhalidwe a anthu ake atsopano? Vuto la AIDS likusonyeza bwino lomwe kuti zimene zinachitika nzosiyana kwambiri ndi zimenezo.

Mwachitsanzo, talingalirani za dziko la Chad. Pa mizinda yake yaikulu inayi, itatu ili ndi “Akristu” ochuluka. Winawo uli ndi Asilamu ochuluka. Komabe, mizinda itatuyo “yachikristu” ndi imene ikusakazidwa ndi vairasiyo! Ndi mmenenso zilili m’kontinenti yonse. Pakati ndi kummwera kwa Afirika, madera amene mwa dzina ali achikristu, kuli odwala ochuluka kwambiri kuposa ku North Africa, kumene kuli Asilamu ochuluka.

Mmene Afirika Anakhalira “Wachikristu”

Kodi nchifukwa ninji vairasi imeneyi yafalikira kwambiri pakati pa anthu amene amati ndi otsatira a Kristu? Kwenikweni, ngakhale kuti Aafirika ambiri amadzitcha Akristu, ali oŵerengeka kwambiri amene amatsatira miyezo ya makhalidwe yachikristu, yopezeka m’Baibulo. Zimenezi zikuoneka kuti zakhalapo chifukwa cha njira imene amishonale a Dziko Lachikristu anatsatira “potembenuza” anthu achiafirika.

M’zaka za zana la 18 ndi 19, zikhulupiriro zamwambo za Dziko Lachikristu zinakayikiridwa. Maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo anakhala otchuka, akumaluluza Baibulo m’maso mwa ambiri kukhala buku wamba lakale. Chiphunzitso cha chisinthiko nachonso chinayamba kulandiridwa, ngakhale ndi atsogoleri achipembedzo. Mbewu za chikayikiro zinafesedwa. Chikhulupiriro m’Malemba Oyera chinakayikiridwa. Mumkhalidwe umenewu nkosadabwitsa kuti kulimbikira kwa Dziko Lachikristu “kutembenuza” Aafirika kunasumikidwa makamaka pankhani zadziko. Amishonale atchalitchi analalikira uthenga wa kakhalidwe, akumagogomezera kwambiri ntchito zothandiza anthu m’malo mwa kuthandiza otembenuka kutsatira miyezo ya Baibulo ya makhalidwe. Mwinamwake mosadziŵa, amishonale kwenikweni anathandizira kuwononga makhalidwe omwe analipo.

Mwachitsanzo, mitala kwa nthaŵi yaitali inali mwambo m’zitaganya zambiri za Afirika. Komabe, uchiwerewere sunali kuchitikachitika popeza mafuko ambiri anali ndi malamulo okhwima oletsa chigololo. Joseph Darnas, mphunzitsi wopuma pantchito, amene ali wodziŵika m’Chad, anauza Galamukani! kuti amishonale atchalitchi asanadze, “anthu anakhulupirira kuti chigololo chimadzetsa tsoka.” Chotero, “ochimwawo anali kulangidwa kowopsa—nthaŵi zambiri ndi imfa chifukwa cha kuika mudzi pangozi.” Kuwopa malodza kodi? Inde, koma zikhulupiriro zotero zinaletsadi uchiwerewere.

Tsono panafika amishonale a Dziko Lachikristu. Iwo analetsa mitala koma anachita zochepa kusungitsa miyezo ya Baibulo ya makhalidwe. Ngakhale kuti Baibulo limati adama ndi achigololo osalapa apitikitsidwe mumpingo wachikristu, matchalitchi a Dziko Lachikristu amalanga ochimwa awo mwakamodzikamodzi. (1 Akorinto 5:11-13) Mpaka lero, andale ambiri omveka a mu Afirika ali ndi mbiri yoipa ya uchiwerewere wawo, komabe amawaonabe ngati anthu atchalitchi akaimidwe kabwino. Kukhulupirika mu ukwati nkwakamodzikamodzi pakati pa odzitcha Akristu mu Afirika.

Ndiyeno pali chitsanzo choipa choperekedwa ndi atsogoleri achipembedzo ambiri. M’chitaganya chokonda banja chimenechi, nkwachibadwa kukwatira ndi kukhala ndi ana ochuluka. Mwinamwake ndicho chifukwa chake ansembe ochuluka kwambiri achikatolika samadzimva amlandu pakuswa zoŵinda zawo za chiyero ndi umbeta. The New York Times ya May 3, 1980 inati: “M’madera ambiri akumidzi, . . . ansembe ndi mabishopu ngamitala.”

Monga mudziŵa, maukwati otero samalembetsedwa, ndipo “akaziwo,” kwenikweni, amangokhala akazi amseri. Sitingakankhire pambali khalidwe lauchimoli kuti nlaling’ono. Malinga ndi Times, “mtsogoleri wachipembedzo womveka wachikatolika” akuvomereza kuti “wansembe wa mu Afirika amachita ulamuliro, amachita ufumu m’malo mwa kukhala mtumiki wa Yesu Kristu.” “Olamulira” ameneŵa amachita monga ngati akunena kuti, “Muzichita zimene ndinena osati zimene ndichita.”

Kuloŵerera kwa Zosangulutsa Zakumadzulo

Zimenenso sitiyenera kuiŵala ndizo zosangulutsa zachisembwere zochuluka zimene zaloŵa mu Afirika posachedwapa. Ku Chad malo osayang’aniridwa oonetsera mavidiyo kwa onse osonyeza zosangulutsa zimenezo ali ponseponse—m’nyumba za anthu, m’magalaja, ndipo nthaŵi zambiri, m’mabwalo usiku. Mafilimu ameneŵa ngotchipa, amalipira ndalama zokwanira 25 francs (5 senti ya United States). Ana aang’ono amapita kumeneko. Kodi zimenezi zimachokera kuti? Zochuluka zimachokera ku United States—dziko lomwe limati ndi la Akristu ambiri!

Koma kodi kuloŵereraku kwa makhalidwe Akumadzulo kwakhudza openyerera mwanjira iliyonse? Mmishonale wina wa Mboni za Yehova, amene wakhala mu Central Africa zaka 14, akuti: “Anthu kuno sadziŵa zochuluka za maiko Akumadzulo kusiyapo zimene amaona pa mavidiyokaseti. Iwo amafuna kukhala ngati anthu Akumadzulo amene amaona m’mafilimu ameneŵa. Sindinapeze maumboni olembedwa otsimikiza zimenezi, koma zili zachionekere kwa anthu akuno ochuluka kuti zosangulutsa zotero zimasonkhezera chisembwere.”

Nzodabwitsa kwambiri chotani nanga kuti pamene kuli kwakuti madokotala akuyesayesa mothedwa nzeru kuti aletse kukula kwa matenda opatsana mwa kugonana, maiko otchedwa achikristu akutulutsa nkhani zochuluka zochirikiza makhalidwe oipa angozi! Pamene kuli kwakuti matchalitchi achita zochepa kuletsa vuto limeneli kwawo kapena kunja kwa dziko lawo, maboma ena a mu Afirika, monga la Chad ndi Cameroon, ayesa kuletsa kapena kuchepetsa kuloŵa kwa zithunzithunzi zaumaliseche m’maiko mwawo. Koma zoyesayesa zawo zalephera nthaŵi zambiri.

Chifukwa cha zimenezi makhalidwe anyonyotsoka kwambiri pakati pa “Akristu” a mu Afirika. Mikhalidwe yoipa ya zachuma yakhalanso ndi zotulukapo zoipa. Chifukwa cha kusoŵa kwa ntchito, amuna nthaŵi zambiri amakakamizika kusiya mabanja awo kwa miyezi yambiri kupita kukafuna ntchito. Amuna otero ndi omwe mahule akumaloko samavutika kupeza. Komanso, chimene chimachititsa mahule ochuluka kukhala choncho ndi umphaŵi. Chochititsa chinanso ndicho makolo omwe amafuna malowolo okwera kwambiri. Amuna ambiri samakwatira chifukwa satha kupeza ndalama zofunika kulipirira malowolo. Motero ena amangokhala ndi moyo wachiwerewere. Mumkhalidwe wotero wa chikhalidwe ndi zachuma, AIDS yafalikira mofulumira kwambiri.

Mankhwala a Vutolo

Mwachionekere, vuto la AIDS mu Afirika silili mlandu wa Dziko Lachikristu lokha. Koma umboni womwe ulipo wakuti ndilo lili ndi mlandu waukulu ngwomvetsa chisoni kwambiri. Zimenezi zili ndi zotulukapo zowopsa kwa aja ofuna kukhala pakati pa amene Yesu anatcha “olambira oona.”—Yohane 4:23.

Mosasamala kanthu za mlanduwo, kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuletsa mliri wa AIDS? Maboma a mu Afirika achita mikupiti yoletsa AIDS, akumalimbikitsa kugwiritsira ntchito makondomu. Koma Dr. Samuel Brew-Graves, woimira Nigeria ku World Health Organization, anavomereza mosapita m’mbali kuti: “Munthu ayenera kukhala ndi moyo wodzisunga . . . , pamene banja liyenera . . . kupeŵa uchiwerewere.”

Kale kwambiri anthu asanadziŵe AIDS, Baibulo linatsutsa uchiwerewere ndi kulimbikitsa chiyero, kudziletsa, ndi kukhulupirika muukwati. (Miyambo 5:18-20; 1 Akorinto 6:18) Mboni za Yehova zikwi mazana mu Afirika zimapereka umboni wamphamvu wakuti kutsatira mapulinsipulo ameneŵa kumatetezera munthu kwambiri kuti asatenge AIDS ndi matenda ena opatsana mwa kugonana. Kutsatira kwawo miyezo ya Baibulo kuli maziko enieni ozengerapo mlandu Dziko Lachikristu. Akristu oona ameneŵa aikanso chiyembekezo chawo m’dziko latsopano likudzalo mmene ‘mudzakhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Kwa amuna achikhulupiriro, ameneŵa ndiwo mankhwala okha a vuto la AIDS.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mufuna kudziŵa zambiri, onani nkhani yakuti “AIDS mu Afirika—Kodi Idzatha Motani?” m’kope la August 8, 1992.

b Nthendayo ingafalikirenso mwa kuika mwazi ndi kubwerekana majekeseni obayira anamgoneka m’mitsempha. Akristu ena opanda chifukwa atenga nthendayo kwa anzawo a muukwati amene anachita chisembwere kapena kugwiritsira ntchito anamgoneka.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“M’madera ambiri akumidzi, . . . ansembe ndi mabishopu ngamitala.”—The New York Times

[Chithunzi patsamba 14]

Chitsanzo choipa cha atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu chasonkhezera mliri wa uchiwerewere mu Afirika

[Chithunzi patsamba 15]

Achichepere amaonerera zosangulutsa zachisembwere zotumizidwa ndi maiko “achikristu”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena