Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 5/8 tsamba 30-31
  • Kodi Akristu Ayenera Kuvina?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akristu Ayenera Kuvina?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuvina Kuli Kulankhulana
  • Kuvina—Kwabwino ndi Koipa
  • Koipa Kapena Kwabwino—Mmene Mungadziŵire
  • Kodi N’kulakwa Kupita ku Malo Ovinira a Achinyamata?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Ndizichita Zosangalatsa Zotani?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Miyambo ya m’Madera Osiyanasiyana ndi Mapulinsipulo Achikristu—Kodi Nzogwirizana?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Tinapeza Chinachake Chabwino Koposa
    Galamukani!—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 5/8 tsamba 30-31

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Ayenera Kuvina?

“SINDINGAPENYERERE zimenezi. Ndikutuluka,” ananong’oneza motero mwamuna wina kwa mkazi wake akumanyamuka pampando wake ndi kutuluka m’chipindacho kukawongola miyendo panja pozizirira bwino usiku. Iye anachita manyazi.

Iyeyo ndi mkazi wake anali ataitanidwa ndi mabwenzi ku phwando. Eni phwandolo anasankha kukhala ndi akazi atatu ovina. Openyerera ena onse sanavutike nazo. Kodi mwamunayo anali wonyumwa mopambanitsa? Kodi ovinawo sanali kungosonyeza malingaliro awo ndi kusangalala ndi ufulu wa kuvina? Tiyeni tiyese kumvetsa kuvina m’lingaliro lachikristu.

Kuvina Kuli Kulankhulana

Imodzi ya njira zolankhulirana za anthu ndiyo mwa majesicha kapena mayendedwe. Mwachitsanzo, pamene ali kudziko lina, alendo ambiri adabwa kudziŵa kuti kayendedwe kamene iwo anakaona kukhala kabwinobwino kali ndi tanthauzo lina kumeneko—mwinamwake loipa. Amene kale anali mmishonale ku Solomon Islands, Malaysia, ndi Papua New Guinea anati: “M’madera ena malingaliro a kugonana amagwirizanitsidwa ndi mayendedwe ena a thupi. Mwachitsanzo, pamene mkazi akhala pansi, kumakhala kosayenera kwa mwamuna kulumpha miyendo yake. Mofananamo, nkopanda nzeru kwa mkazi kudutsa kutsogolo kwa mwamuna amene wakhala pansi. M’zochitika zonse ziŵiri malingaliro akugonana amaperekedwa pomwepo.” Kaya tikudziŵa za zimenezo kapena ayi, mayendedwe a thupi lathu amalankhula. Motero siziyenera kutidabwitsa kuti m’mbiri yonse kuvina kwagwiritsiridwa ntchito monga njira ina ya kulankhulana.

Kuvina kungasonyeze malingaliro osiyanasiyana—kuyambira pa chimwemwe ndi kusangalala kwambiri kwa paphwando kufika ku ulemu wa padzoma ndi mwambo wachipembedzo. (2 Samueli 6:14-17; Salmo 149:1, 3) The New Encyclopædia Britannica imati: “Wovina amalankhula ndi openyerera m’njira ziŵiri zapadera, kaya mwa kusonyeza malingaliro kupyolera m’thupi limodzinso ndi nkhope kapena mwa chilankhulo chocholoŵana choyerekezera kulankhula ndi majesicha.” M’mavinidwe ena kulankhulana kumamveka bwino lomwe. M’mitundu ina ya mavinidwe, chilankhulo chake chingamvedwe kokha ndi anthu angapo ochidziŵa. Mwachitsanzo, m’gule wa ballet wa nyimbo za classic dzanja loikidwa pachifuŵa limatanthauza chikondi, pamene kuloza chala chachinayi cha dzanja lamanzere kumatanthauza ukwati. M’maseŵero achitchaina kuyenda mozungulira kumatanthauza ulendo, pamene kuzungulira bwalo la maseŵero atanyamula mkwapulo mopingasa kumatanthauza kukwera kavalo; mbendera yakuda yokokedwa pabwalo la maseŵero ndiwo mkuntho, pamene ya bluu imasonyeza kamphepo kayaziyazi. Motero m’mavinidwe ndi majesicha, thupi limalankhula. Koma kodi uthengawo nthaŵi zonse umakhala wabwino?

Kuvina—Kwabwino ndi Koipa

Kuvina kungakhale mtundu wabwino wa kusanguluka ndi maseŵero olimbitsa thupi. Kungakhale njira yabwino ndi yosabisa kanthu, yosonyeza chimwemwe ndi thupi chifukwa cha kukondwa kwenikweni pokhala ndi moyo kapena kuyamikira ubwino wa Yehova. (Eksodo 15:20; Oweruza 11:34) Magule ena a kagulu ndi a makolo athu angakhale osangalatsa. Yesu, m’fanizo lake la mwana woloŵerera, anatchulapo ngakhale za gulu la ovina, mwachionekere linali gulu la ovina loitanidwa, monga mbali ya phwando. (Luka 15:25) Motero, momvekera bwino, Baibulo silimatsutsa kuvina ayi. Komabe, limachenjeza za kusonkhezera malingaliro ndi zikhumbo zolakwika. Apa mpamene mavinidwe ena amakhala oipa, ngakhale angozi pa mkhalidwe wauzimu wa munthu. (Akolose 3:5) Kuyambira kale kuvina nthaŵi zina kwakhala kodzutsa chikhumbo cha kugonana ndipo kwagwiritsiridwa ntchito pa zifuno zoipa.—Yerekezerani ndi Mateyu 14:3-11.

Mdani wathu, Satana Mdyerekezi, amadziŵa kuti msanganizo wa mavinidwe ena ndi malingaliro oipa chili chida champhamvu chimene ali nacho. (Yerekezerani ndi Yakobo 1:14, 15.) Iye amadziŵa bwino lomwe za mmene kagwedezedwe kathupi kangasonkhezerere chilakolako chathupi ndi mmene kangasonkhezerere malingaliro a kugonana. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti Satana ngwofunitsitsa kutinyenga kotero kuti ‘maganizo athu aipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.’ (2 Akorinto 11:3) Talingalirani za mmene Mdyerekezi angasangalalire ngati mwa kupenyerera kapena kuvina nawo mavinidwe oipa tilola malingaliro athu kukoledwa ndi malingaliro achisembwere. Angasangalalenso kwambiri ngati zikhumbo zathu zosalamulirika tizigwiritsira ntchito ndipo tikoledwa m’zotulukapo zoŵaŵa za khalidwe loipa. Kalelo anagwiritsira ntchito kagwedezedwe ka thupi ndi kuvina m’njira imeneyo.—Yerekezerani ndi Eksodo 32:6, 17-19.

Koipa Kapena Kwabwino—Mmene Mungadziŵire

Momwemonso, kaya gule akuvinidwa ndi gulu, aŵiriaŵiri, kapena ndi munthu mmodzi yekha, ngati kavinidwe kake kakukudzutsirani malingaliro oipa, ndiye kuti kavinidweko nkoipa kwa inu, ngakhale ngati sizingakhale choncho kwa ena.

Ena aona kuti m’mavinidwe ambiri amakono ovina samagwirana nkomwe. Komabe, kodi nkhani ili pa kugwirana? Britannica imamaliza nkhaniyo mwa kunena kuti “chotulukapo chake nchimodzimodzi—chisangalalo chathupi pa kuvina ndi kukhumbira wovina naye, kaya atamkupatira kapena asakumpenyetsetsa kwenikweni.” Kodi “kukhumbira wovina naye” nkwanzeru kunja kwa ukwati? Osati malinga ndi mawu a Yesu akuti “yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.”—Mateyu 5:28.

Kaya musankha kuvina kapena ayi nchosankha chanu. Kuganizira pa mafunso otsatirawa kungakuthandizeni kupanga chosankha chanzeru. Kodi cholinga cha kuvinaku nchiyani? Kodi anthu amakuona motani? Kodi mavinidwewa amatanthauzanji? Kodi akusonkhezera maganizo ndi malingaliro otani mwa ineyo? Kodi akusonkhezera zikhumbo zotani mwa mnzanga wovina naye kapena mwa amene akupenyerera? Indetu, munthu ayenera kuchitapo kanthu malinga ndi chikumbumtima chake, monga momwe anachitira mwamuna wokwatira pachiyambi chathu cha nkhaniyi, mosasamala kanthu za zimene ena akuchita.

Baibulo limasonyeza kuti Mlengi amafuna kuti tisangalale ndi mphatso za kukongola, nyimbo, ndi kagwedezedwe ka thupi. Inde, sangalalani nazo—koma kumbukirani kuti pamene mukuvina, thupi lanu likulankhula. Kumbukirani zitsogozo za Paulo pa Afilipi 4:8: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Picture Fund/Ndi Chilolezo cha, Museum of Fine Arts, Boston

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena