Miyambo ya m’Madera Osiyanasiyana ndi Mapulinsipulo Achikristu—Kodi Nzogwirizana?
STEPHEN, Mboni ya Kumpoto kwa Ulaya, anatumidwa monga mmishonale kudziko lina mu Afirika. Poyenda pamsewu m’tauni ndi mbale wakomweko, anadabwa pamene mbaleyo anamgwira dzanja.
Kuyenda pamsewu wa anthu ambiri atagwirana m’manja ndi mwamuna mnzake inali nkhani yachilendo kwa Stephen. Pachikhalidwe chakwawo, amene ali ndi chizoloŵezi chimenecho ndi anthu amathanyula. (Aroma 1:27) Komabe kwa mbale wa mu Afirika, kugwirana manja kunali kungosonyeza ubwenzi basi. Kukana kugwirana manja kukanatanthauza kukananso ubwenzi wawo.
Kodi nchifukwa chiyani tiyenera kulingalira za kusiyana kwa miyambo? Makamaka nchifukwa chakuti anthu a Yehova amafunitsitsa kukwaniritsa ntchito yawo imene Mulungu anawapatsa ya ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19) Kuti achite ntchito imeneyi, ena asamuka kukatumikira kumene kukufunikira atumiki ambiri. Kuti ziwayendere bwino kumalo awo atsopanowo, afunikira kuzindikira miyambo yosiyanasiyana imene amaipeza kenako kusintha malinga ndi miyamboyo. Akatero, atha kugwira ntchito mogwirizana ndi abale awo ndi alongo, komanso kukhala ogwira mtima kwambiri mu utumiki wapoyera.
Ndiponso, m’dziko lino lamavuto, anthu ambiri athaŵa kwawo kumene kuli mavuto andale kapena achuma ndipo apita kukakhala kumaiko ena. Choncho zingatheke kuti polalikira kwa anansi atsopano ameneŵa, nkupezana ndi miyambo yatsopano. (Mateyu 22:39) Poyamba titapezana ndi miyambo yosiyana ingatisokoneze.
Mbali Zodziŵikiratu
Mwambo ndiwo maziko a chikhalidwe cha anthu. Ndiye chifukwa chake kungakhale kosathandiza mpang’ono pomwe ‘kupambanitsa kukhala wolungama’ ndi kufufuza kamwambo kalikonse pofuna kuona ngati kakugwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo!—Mlaliki 7:16.
Komanso tifunikira kudziŵa miyambo yakwathu imene mosakayikira imaswa mapulinsipulo aumulungu. Nthaŵi zambiri, zimenezo nzosavuta kuchita, pakuti Mawu a Mulungu alipo kuti ‘akonze’ zinthu. (2 Timoteo 3:16) Mwachitsanzo, kumaiko ambiri kuli mwambo wokhala ndi akazi ambiri, koma lamulo la m’Malemba kwa Akristu oona limati mwamuna akhale ndi mkazi mmodzi yekha wamoyo.—Genesis 2:24; 1 Timoteo 3:2.
Momwemonso miyambo ina ya maliro imene cholinga chake ndicho kupitikitsa mizimu yoipa, kapena imene ilipo chifukwa chokhulupirira kuti mzimu sufa, njosaloleka kwa Akristu oona. Anthu ena amapereka nsembe kapena mapemphero kwa akufa kuti apitikitse mizimu yoipa. Ena amachezera pamaliro kapena kuika maliro kachiŵiri ncholinga choti athandize wakufayo kukonzekera moyo wa ‘kudziko lina.’ Komabe, Baibulo limaphunzitsa kuti munthu akamwalira, “sadziŵa kanthu bi,” chotero sangachite chabwino kwa munthu aliyense kapena kumvulaza.—Mlaliki 9:5; Salmo 146:4.
Inde, ilipo miyambo yambiri yogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Zimakhala zotsitsimula chotani nanga pamene tifika kumalo kumene kudakali mzimu wochereza alendo, kumene mwambo umafuna kuti ngakhale mlendo apatsidwe moni waubwenzi ndi kuti, ngati kuli kofunika, alandiridwe m’nyumba! Mutakumana ndi zimenezi nthaŵi yoyamba, kodi sizimakusonkhezerani kutsanzira chitsanzo chimenechi? Ngati zimatero, zidzakuthandizani kuwongolera umunthu wanu wachikristu.—Ahebri 13:1, 2.
Ndani wa ife amakonda kungokhala akuyembekezera? M’maiko ena zimenezi sizichitikachitika chifukwa kusunga nthaŵi nkofunika kwambiri. Baibulo limatiuza kuti Yehova ali Mulungu wadongosolo. (1 Akorinto 14:33) Chifukwa chake, waika ‘tsiku ndi nthaŵi’ yothetsa kuipa, ndipo amatitsimikizira kuti zimenezi ‘sizizengereza.’ (Mateyu 24:36; Habakuku 2:3) Miyambo imene imalimbikitsa kusunga nthaŵi imatithandiza kukhala adongosolo ndi kulemekeza anthu ena ndi nthaŵi yawo, zimene zili zogwirizanadi ndi mapulinsipulo a m’Malemba.—1 Akorinto 14:40; Afilipi 2:4.
Bwanji Nanga za Miyambo Yosalakwika?
Pamene miyambo ina mosakayikira ili yogwirizana ndi moyo wachikristu, ina sili. Nanga bwanji za miyambo imene sitinganene kuti njabwino kapena njoipa? Miyambo yambiri si yolakwika, ndipo tingaonetse kuti ndife okhazikika mwauzimu mwa njira imene timaonera miyamboyo.
Mwachitsanzo, moni uli m’mitundu yambiri—kugwirana chanza, kugwada, kupsompsona, kapena ngakhale kukumbatira. Palinso miyambo yosiyanasiyana yokhudza khalidwe pachakudya. M’maiko ambiri anthu amadyera m’mbale imodzi. Kumaiko ena kugeya ndi khalidwe lololeka—ngakhale lokhumbirika—loonetsera kuyamikira, pamene kumaiko ena nkosaloleka ndipo amakuyesa kupandiratu khalidwe.
M’malo mosankha kuti mumakonda miyambo yakuti osati yakuti mwa miyambo yosalakwika imeneyi, yesetsani kukhala ndi maganizo abwino pamiyamboyo. Uphungu wosasintha wa m’Baibulo umatilimbikitsa kuti ‘tisachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.’ (Afilipi 2:3) Mofananamo, Eleanor Boykin, m’buku lake lakuti This Way, Please—A Book of Manners, anati: “Choyamba chimene mufunikira ndicho kukoma mtima.”
Kudzichepetsa kumeneku kudzatiletsa kusuliza miyambo ya ena. Tidzayamba ndife kuphunzira mmene anthu ena amakhalira, kugwirizana nayo miyambo yawo ndi kulaŵa zakudya zawo m’malo mozipeŵa kapena kukayikira zilizonse zooneka ngati zosiyana. Mwa kukhala womasuka ndi wokonzeka kuyesa zatsopano, timalemekeza mwininyumba kapena anansi athu achilendo. Timapindulanso ifeyo pamene ‘tifutukula’ mtima wathu ndi chidziŵitso.—2 Akorinto 6:13, NW.
Ngati Mwambo Ukuletsa Kupita Patsogolo Kwauzimu
Bwanji ngati tipeza miyambo imene simatsutsana ndi Malemba, komano yosathandiza munthu kupita patsogolo kwauzimu? Mwachitsanzo, anthu kumaiko ena angakonde kwambiri kuzengereza. Moyo wokhweka umenewu ungachepetse kupsinjika, koma ungativutitsire zinthu kwambiri moti nkulephera ‘kukwaniritsa’ utumiki wathu.—2 Timoteo 4:5.
Kodi tingaŵalimbikitse motani ena kupeŵa kuika pambali zinthu zofunika kudikirira “maŵa”? Kumbukirani kuti “choyamba chimene mufunikira ndicho kukoma mtima.” Posonkhezeredwa ndi chikondi, tingapereke chitsanzo ndiyeno kufotokoza mokoma mtima ubwino wa kusasiya zimene ziyenera kuchitidwa lero kuti tikazichite maŵa. (Mlaliki 11:4) Komanso tiyenera kusamala kuti tisawononge kukhulupirirana pofuna kuti zinthu ziyende. Ngati ena sagwiritsa ntchito maganizo athu nthaŵi yomweyo, tisawaumirize kapena kuwakwiyira. Chikondi nthaŵi zonse chizikhala choyamba osati nkhani yakuyendetsa zinthu bwino.—1 Petro 4:8; 5:3.
Kulingalira za Chizoloŵezi cha Kumaloko
Tiyenera kuonetsetsa kuti maganizo alionse amene tikupereka ali otsimikizika ndi kuti sitikungoyesa kuumiriza ena kuti akonde zimene timakonda. Mwachitsanzo, kavalidwe kamasiyana kwambiri. Kumadera ambiri mwamuna wolalikira uthenga wabwino ayenera kuvala tayo, koma kumaiko ena otentha, angaone zimenezo kukhala zonyanyira. Kulingalira za chizoloŵezi cha kumaloko ponena za kavalidwe koyenera ka munthu wantchito amene amaonana ndi anthu kumathandiza nthaŵi zambiri. ‘Kudziletsa’ kumafunika kwambiri pankhani yovuta kwambiri ya kavalidwe.—1 Timoteo 2:9, 10.
Bwanji ngati mwambo wina sutikondweretsa? Kodi tiyenera kuukana kamodzinkamodzi? Osati kwenikweni. Mwambo wogwirana manja amuna okhaokha, wotchulidwa poyamba, unali wololeka m’dzikolo la mu Afirika. Pamene mmishonale uja anaona kuti amuna ena anali kuyenda atagwirana manja, anamasuka.
Mtumwi Paulo, pamaulendo ake aatali aumishonale, anachezera mipingo imene anthu ake anali a mafuko osiyanasiyana. Mosakayikira, pankakhala kusiyana miyambo nthaŵi zambiri. Ndiye chifukwa chake Paulo analandira miyambo iliyonse imene anatha pamenenso anamamatira zolimba pamapulinsipulo a Baibulo. “Ndakhala zonse kwa anthu onse,” anatero, “kuti paliponse ndikapulumutse ena.”—1 Akorinto 9:22, 23; Machitidwe 16:3.
Mafunso angapo oyenerera angatithandize kusankha zimene tingachite titakumana ndi miyambo yatsopano. Mwa kulandira mwambo wakuti—kapena kuukana—kodi timapereka chithunzi chotani kwa oonera? Kodi iwo adzakopeka ndi uthenga wa Ufumu chifukwa choona kuti tikuyesa kutengera chikhalidwe chawo? Komanso, ngati titengera mwambo wakumaloko, kodi ‘utumiki wathu unganenezedwe?’—2 Akorinto 6:3.
Ngati tikufuna ‘kukhala zonse kwa anthu onse,’ mwina tingafunikire kusintha maganizo athu amphamvu ponena za choyenera ndi chosayenera. Nthaŵi zambiri njira “yabwino” kapena “yolakwika” yochitira zinthu imangodalira ndi kumene tikukhala. Ndiye chifukwa chake, kudziko lina kugwirana manja amuna okhaokha ndi umboni wa ubwenzi wawo, pamene kumaiko ena ambiri kungalepheretse ena kulandira uthenga wa Ufumu.
Komabe, ilipo miyambo ina imene ili yololeka kumadera ambiri imenenso ingakhale yoyenera kwa Akristu; koma tizisamala.
Samalani Kuti Musadutse Malire
Yesu Kristu anatero kuti ngakhale kuti ophunzira ake sakanawachotsa m’dziko, anafunikirabe ‘kusakhala a dziko lapansi.’ (Yohane 17:15, 16) Koma nthaŵi zina zimavuta kuzindikira malire ake pakati pa dziko la Satana ndi mwambo wamba. Mwachitsanzo, pafupifupi fuko lililonse lili ndi nyimbo ndi mavinidwe ake, ngakhale kuti m’maiko ena zimenezi zimakhala zofunika kwambiri.
Ife tingafulumire kugamula—malinga ndi kumene tinachokera m’malo mwa zifukwa za m’Malemba. Alex, mbale wachijeremani, anatumizidwa ku Spain. Kwawo, kuvina sikunali kotchuka kwambiri, koma ku Spain kuvina ndi chikhalidwe chawo. Nthaŵi yoyamba imene anaona mbale ndi mlongo akuvina mwamphamvu gule wakwawo, anadabwa. Kodi gule ameneyo anali wolakwika kapena mwina anali wadziko? Kodi akanakhala akunyalanyaza malamulo ake ngati akanatengera mwambo umenewo? Alex anadzadziŵa kuti ngakhale kuti nyimbozo ndi mavinidwe ake zinali zosiyana ndi zakwawo, panalibe chifukwa choganizira kuti abale ndi alongo achispanyawo anali kunyalanyaza malamulo achikristu. Anadabwa chifukwa miyambo inasiyana.
Koma Emilio, amene amakonda mavinidwe achispanya, akudziŵa kuti pali ngozi zake. “Ndimaona kuti mavinidwe ambiri amafuna kuti mwamuna ndi mkazi aziyandikana kwambiri,” akutero. “Pokhala wosakwatira ineyo, ndikudziŵa kuti zimenezi zingakhudze mtima wa mmodzi wa ovinawo. Nthaŵi zina, munthu angatengerepo mwayi pakuvina kuti aonetse chikondi pa wina amene wakopeka naye. Kuonetsetsa kuti nyimbozo zili bwino ndi kuti achepetse kukhudzana zingawateteze. Komabe, ndikuvomereza kuti pamene abale ndi alongo osakwatira komanso achinyamata apita kukavinira limodzi, nzovuta kwambiri kuti pakhale mkhalidwe wateokrase.”
Inde, sitikufuna kugwiritsa ntchito miyambo yathu monga mpata wotsatirira khalidwe ladziko. Aisrayeli ankaimba ndi kuvina malinga ndi chikhalidwe chawo, ndipo pamene anapulumutsidwa kwa Aigupto pa Nyanja Yofiira, chikondwerero chawo chinaphatikizapo kuimba ndi kuvina. (Eksodo 15:1, 20) Komabe, nyimbo zawo ndi mavinidwe zinali zosiyana ndi zija za mitundu yachikunja yowazinga.
Zachisoni nzakuti pamene ankayembekezera Mose kuchokera m’Phiri la Sinai, Aisrayeli anataya mtima, napanga mwana wa ng’ombe wagolidi, ndipo atadya ndi kumwa ‘anauka kuseŵera.’ (Eksodo 32:1-6) Pamene Mose ndi Yoswa anamva maimbidwe awo, zinawadabwitsa nthaŵi yomweyo. (Eksodo 32:17, 18) Aisrayeli anali atadutsa “malire” aja, ndipo maimbidwe ndi mavinidwe awo tsopano anafanana ndi mitundu yachikunja yowazinga.
Momwemonso lero, nyimbo ndi kuvina zingakhale zololeka kwa ambiri m’dera lathu ndipo mwina sizingakhumudwitse chikumbumtima cha ena. Koma ngati mphamvu ya magetsi ichepetsedwa nkuchita kamdima, kenako nkuyatsa magetsi angwephingwephi, kapena kuikapo nyimbo za maliridwe osiyana, zimene poyamba zinali zololeka zingakhale ndi mzimu wa dziko tsopano. “Umenewu wangokhala mwambo wathu,” tingatero. Aroni anagwiritsa ntchito chifukwa chonga chimenecho pamene anavomereza kusanguluka ndi kulambira kwachikunja, akumazifotokoza molakwika kukhala “madyerero a Yehova.” Chifukwa chimenecho chinali chosamveka. Ndipotu khalidwe lawo linali ‘lowatonzetsa kwa adani awo.’—Eksodo 32:5, 25.
Mwambo Uli ndi Malo Ake
Poyamba miyambo yachilendo ingatidabwitse, koma sikuti yonse kwenikweni ili yosaloleka. Mwa ‘kuzoloŵeretsa zizindikiritso’ zathu, titha kuona miyambo imene imagwirizana ndi mapulinsipulo achikristu ndi imene simagwirizana nawo. (Ahebri 5:14) Pamene tionetsa kukoma mtima ndi chikondi chachikulu kwa anzathu, tidzachita moyenera tikapezana ndi miyambo yosalakwika.
Pamene tilalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu m’dera lathu kapena kutali, kukhala ndi maganizo abwino pamiyambo yosiyanasiyana kudzatithandiza kukhala “zonse kwa anthu onse.” Ndipo mosakayikira tidzapeza kuti pamene tilandira miyambo yosiyanasiyana, zidzatithandiza kukhala ndi moyo watanthauzo ndi wosangalatsa.
[Chithunzi patsamba 20]
Moni wachikristu ungaperekedwe moyenerera m’njira zambiri
[Chithunzi patsamba 23]
Kukhala ndi maganizo abwino pamiyambo yosiyanasiyana kungatipatse moyo watanthauzo ndi wosangalatsa