Kuvuta Akazi—Vuto Lapadziko Lonse
NTCHITO inali chizunzo kwa kalaliki wachichepere wotchedwa Rena Weeks. Inde, kampani ya maloya imene inamlemba ntchito inali yotchuka ndipo inali ndi maofesi m’maiko oposa 24. Koma iye anali kugwirira ntchito mwamuna wina amene, malinga ndi kunena kwake, sanali kusiya kumgwiragwira ndi kumkhudza. Kuvutidwa konyazitsako kunaphatikizapo mawu otukwana ndi onyansa.
Zaka zapitazo, akazi okhala m’mikhalidwe yonga imeneyi analibe kokadandaula—mwina kusiyapo kuleka ntchito. ‘Mawu a mkazi oimba mlandu mwamuna’ sakanakhutiritsa amanijala. Ndipo ngakhale aja okonda kukhulupirira zonena za mkazi mwinamwake akanangokankhira pambali vutolo mwa kunena kuti, ‘Kodi ndiyo nkhani yokwiya nayo?’ Komatu zinthu zasintha. Rena Weeks sanangokwiya ndi kuchoka ntchito. Anapitanso kukhoti.
Oweruza a ku United States anampatsa $50,000 monga malipo kaamba ka kupsinjika mtima kwake, limodzi ndi $225,000 imene analipitsa amene kale anali mkulu wake wa ntchito. Ndiyeno, akumachita zimene zinadabwitsa amabizinesi ndiponso makampani a maloya padziko lonse, oweruzawo analamula kampani ya maloyayo kumlipira ndalama zochuluka zokwana $6.9 miliyoni monga malipo chifukwa cholephera kuthetsa vutolo!
Mlandu wa a Weeks sindiwo wokha umene wakhalako. Mlandu wina waposachedwapa unakhudza bungwe la masitolo (ku United States) ochita maselo. Wantchito wotchedwa Peggy Kimzey ananena kuti kapitao wake anamuuza mawu ochuluka otukwana a zakugonana. Mu 1993, Peggy Kimzey analeka ntchito nampitira kukhoti. Anapatsidwa $35,000 ponyazitsidwa ndi pozunzika maganizo limodzinso ndi $1 yoimira malipiro ake otayika. Oweruza anagamulanso kuti omlemba ntchito ake apapitapo anachititsa malo antchito kukhala oipa mwa kulekerera vutolo. Chilango chake? Anawalipitsa $50 miliyoni!
Magazini a Men’s Health akuti: “Milandu ya kuvuta akazi yakhala ikuwonjezeka monga mliri. Mu 1990, EEOC [Equal Employment Opportunity Commission] inasamalira madandaulo otero okwana 6,127; podzafika chaka chatha [1993] chiwonjezeko cha pachaka chinaŵirikiza pafupifupi kaŵiri kukhala 11,908.”
Kugwiritsira Ntchito Mphamvu Molakwa
Pamene kuli kwakuti ndalama zochuluka zimene oweruza amalipitsa anthu zimakhala mitu ya nkhani, choonadi nchakuti ndi milandu ingapo chabe imene imapita kukhoti. Ochuluka amene amavutidwa amangovutikira mumtima ndi kunyazitsidwa kwawoko—amangokhala zoseŵeretsa m’maseŵero onyansa a mphamvu ndi kuwopseza amene amachitikira m’maofesi, m’makwalala, m’mabasi, pakaunta ya chakudya cha masana, ndi m’mafakitale. Nthaŵi zina, ena ayesa kuwaumiriza kugona nawo. Komabe, nthaŵi zambiri amawavuta mwamachenjera, komanso mopanda manyazi ndi monyansa: kuwakhudza iwo asakufuna kapena posayenera, mawu osonyeza chilakolako choipa, kuwayang’anitsitsa kolakalaka zoipa.
Zoona, ena amakana kunena kuti khalidwe lotero nkuvutitsa wina, akumatsutsa kuti langokhala kuyesa kwa amuna ena mothedwa nzeru kukopa akazi. Koma ambiri, monga mlembi Martha Langelan, amakana zoyesayesa zimenezo za kulungamitsa khalidwe loipalo. Iye akulemba kuti: “Sindilo chibwenzi chongoyesa, kapena chibwenzi chopanda manyazi, kapena chibwenzi chongoseŵera, kapena chibwenzi ‘chotengedwa molakwa.’ Cholinga chake sindicho kukopa akazi; lili khalidwe limene cholinga chake nchina. Monga kugwirira chigololo, cholinga cha kuvuta akazi ndicho kuwakakamiza, osati kuwakopa. . . . [Ndiko] kusonyeza mphamvu.” Inde, nthaŵi zambiri kuvuta kotero kwangokhala njira ina yankhanza imene “wina apweteka [nayo] mnzake pomlamulira.”—Mlaliki 8:9; yerekezerani ndi Mlaliki 4:1.
Kaŵirikaŵiri akazi samakondwa kuvutidwa ndi amuna, m’malo mwake amamva mosiyanasiyana mwina kuipidwa ndi kukwiya kapena kuchita tondovi ndi manyazi. Mkazi wina akukumbukira kuti: “Mkhalidwewo unandiwononga. Ndinataya chidaliro changa, kulimba mtima kwanga, kudzilemekeza, ndi zonulirapo zanga pantchito. Umunthu wanga unasintha kwambiri. Ndinali munthu wosawopa kanthu. Ndiyeno ndinakhala wokwiya, wosafuna kulankhula ndi munthu, ndi wamanyazi.” Ndipo ngati wovutitsayo ndi mwini ntchito kapena wina amene ali ndi ukumu, kuvutidwa kumeneko kumakhala kosautsa kwambiri.
Nchifukwa chake makhoti ayamba kulanga amaliwongowo ndi kulipira ovutidwawo. Kuyambira pamene Bwalo Lapamwamba la United States linafotokoza kuvuta ena kumeneko kukhala kuswa zoyenera za munthu, nthaŵi ndi nthaŵi malamulo owonjezereka afuna kuti olemba ntchito azisunga malo awo a ntchito opanda “udani kapena chiwawa.”
Makampani amene amalola kuvuta akazi angapeze kuti antchito awo sakukondwanso ndi ntchito, olova akuchuluka, ntchito siikugwirika kwambiri, ndi kuti ali ndi atsopano ochuluka otenga malo a ochoka ntchito—kuphatikizapo kutaya ndalama zambiri ngati ovutidwawo asankha kupita kukhoti.
Kodi Nkofala Motani?
Koma kodi kuvuta akazi nkofala motani? Kufufuza kukusonyeza kuti oposa theka la akazi ogwira ntchito ku United States anavutidwapo. Chotero buku lina likuti: “Kuvuta akazi ndi vuto lofala. Kumachitikira akazi ogwira ntchito zamtundu uliwonse kaya ogwira ntchito ya uweta kapena yoyang’anira pakampani. Kumachitika pakati pa akulu alionse a kampani ndi m’mabizinesi alionse ndi maindasitale.” Komabe, vutolo silili ku United States kokha. Buku lakuti Shockwaves: The Global Impact of Sexual Harassment, lolembedwa ndi Susan L. Webb, likusonyeza ziŵerengero zotsatirazi:a
CANADA: “Kufufuza kwina kunasonyeza kuti akazi 4 pa akazi 10 anasimba kuti anavutidwapo ndi amuna kuntchito.”
JAPAN: “Kufufuza kwa m’August 1991 kunasonyeza kuti 70 peresenti ya akazi amene anafunsidwa anakumana” ndi vutolo kuntchito. Okwanira “90 peresenti anati anavutidwapo ndi amuna popita kuntchito ndi pobwerako.”
AUSTRIA: “Kufufuza kwa mu 1986 kunasonyeza kuti pafupifupi 31 peresenti ya akazi anasimba kuti vutolo linawachitikirapo kowopsa.”
FRANCE: “Mu 1991 ofufuza . . . anapeza kuti 21 peresenti ya akazi 1,300 amene anafunsidwa ananena kuti iwo eni anavutidwapo ndi amuna.”
NETHERLANDS: Kufufuza kunasonyeza kuti “58 peresenti ya akazi oyankha [pakufufuzako] anati iwo eni anavutidwapo ndi amuna.”
Chizindikiro cha Nthaŵi
Inde, kuvutana pantchito sikwachilendo. Akazi—ndipo nthaŵi zina amuna—anavutidwa mofananamo ngakhale m’nthaŵi za Baibulo. (Genesis 39:7, 8; Rute 2:8, 9, 15) Koma zikuoneka kuti kupulupudza kumeneko kwafala kwambiri lerolino. Chifukwa ninji?
Choyamba, m’zaka zaposachedwapa akazi ochuluka aloŵa ntchito. Chotero akazi ambiri amapezeka m’mikhalidwe imene nsautso zotero zingachitike. Komanso, zatanthauzo koposa ndi zimene Baibulo linalosera kalelo kuti: “Kumbukirani izi! Kudzakhala nthaŵi zovuta m’masiku otsiriza. Anthu adzakhala odzikonda, aumbombo, odzitukumula, ndi onyada; adzakhala akumachita chipongwe . . . ; adzakhala osakoma mtima, opanda chifundo, oneneza, achiwawa, ndi aukali.” (2 Timoteo 3:1-3, Today’s English Version) Kufalikira kwa kuvuta akazi kwangokhala umboni wina wamphamvu wakuti mawu ameneŵa akukwaniritsidwa lerolino. Zili bwinonso kudziŵa kuti magazini akuti Men’s Health anati “kuwonjezeka kwa madandaulo a akazi ovutidwa ndi amuna kwatsatizana ndi kutayiratu ulemu kwa anthu ambiri. Makhalidwe oipa ali ponseponse.”
Kufalikira kwa kuvuta akazi kulinso umboni wa “makhalidwe atsopano,” amene anawanda padziko lonse m’ma 1960. Kuwonongeka kwa mwambo wa makhalidwe kwachititsa kunyalanyaza moipa zoyenera za ena ndi malingaliro awo. Kaya chochititsa chikhale chotani, kuvuta akazi ndiko mkhalidwe wowopsa umene ukupezekadi kuntchito. Kodi amuna ndi akazi angachitenji kuti adzitetezere? Kodi pali nthaŵi imene malo a ntchito sadzakhalanso ndi vutolo?
[Mawu a M’munsi]
a Ziŵerengero zimasiyana chifukwa ofufuza amagwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana zofufuzira ndipo amamasulira kuvuta akazi mosiyanasiyana.
[Bokosi patsamba 4]
Kuvuta Akazi—Zonama ndi Zoona
Zonama: Kuvuta akazi kumasimbidwa mopambanitsa. Kwangokhala mkhalidwe wa kanthaŵi chabe, umene aulutsi amaukuza mwa kukambapo kwambiri chifukwa cha kutengeka mtima kwawo.
Zoona: Kaŵirikaŵiri, mkazi amavutika kwambiri ndipo palibe zimene amapeza ngati wanena kuti mwamuna akumvuta. Kunena zoona, ndi akazi oŵerengeka chabe (22 peresenti malinga ndi kufufuza kwina) amene amauza wina aliyense kuti mwamuna wina akhala akuwavuta. Mantha, manyazi, kudzimva wamlandu, kusokonezeka, ndi kusadziŵa zoyenera zawo zalamulo kumawakhalitsa chete akazi ambiri. Chotero akatswiri ambiri akhulupirira kuti vutolo silimachitidwa lipoti kwambiri!
Zonama: Akazi ambiri amakonda zimenezo. Aja amene amanena kuti amuna akhala akuwavuta ali chabe ndi mtima wapachala.
Zoona: Kufufuza nthaŵi zonse kumasonyeza kuti akazi amakwiya pochitidwa mopanda ulemu chonchi. Pakufufuza kwina, “akazi oposa aŵiri mwa asanu alionse ananena kuti ananyansidwa nazo ndipo pafupifupi mmodzi mwa atatu alionse ananena kuti zinawakwiyitsa.” Ena anasimba kuti anada nkhaŵa, kupwetekedwa mtima, ndi kuchita tondovi.
Zonama: Amuna nawonso amavutidwa kwambiri monga akazi.
Zoona: Ofufuza a National Association of Working Women (U.S.) akusimba kuti “milandu ngati 90 peresenti ya kuvutidwa imakhala ya amuna amene avuta akazi, 9 peresenti ya amuna ovutana okhaokha kapena akazi ovutana okhaokha . . . , ndipo 1 peresenti chabe imakhala ya akazi ovuta amuna.”
[Chithunzi patsamba 5]
Kuvuta akazi sikuli chabe pa zakugonana