Ufulu wa Kulankhula Panyumba—Kodi ndi Mkhalidwe Wangozi?
NGATI wina akuwa monama kuti “Moto!” m’nyumba ya maseŵero yodzaza anthu ndipo pothaŵa mopanikizika kuti atuluke ena apondedwa mpaka kufa, kodi amene wakuwayo sayenera kupatsidwa mlandu wa imfa ndi ngozi zimene zachitika? Pamene wina anena kuti, “Sindivomerezana ndi zimene ukunena, koma ndidzachirikiza kuyenera kwako kwa kuzinena,” kodi ndiye kuti wapatsidwa ufulu wakuchita chilichonse chimene ukufuna, ufulu wopanda malire, wa kulankhula poyera zilizonse zimene ukufuna, mosasamala kanthu za zotulukapo zake? Alipo amene amaganiza choncho.
Mwachitsanzo, ku France, pamene oimba nyimbo za rap analimbikitsa kupha apolisi ndipo apolisi anaphedwa ndi ena amene anamvetsera nyimbozo, kodi oimbawo anayenera kukhala ndi mlandu chifukwa cha kusonkhezera kwawo chiwawa? Kapena kodi ayenera kutetezeredwa ndi mpambo wa zoyenera za munthu? Pamene aulutsi apawailesi ndi wailesi yakanema ndi makampani a makompyuta apanga zithunzi zosabisa zosonyeza chiwawa ndi zaumaliseche kuti ana azione, ena mwa iwo amene amatsatira zochitika zimenezi akumadzipweteka okha ndi kupwetekanso ena, kodi ofalitsa zinthu zimenezi ali ndi mlandu?
Kufufuza kochitidwa ndi American Psychological Association “kwapeza kuti mwana wamba, amene amapenyerera TV kwa maola 27 mlungu umodzi, amaona mbanda 8,000 ndi zochitika zachiwawa 100,000 kuyambira pazaka 3 kufika pazaka 12,” anatero magazini a U.S.News & World Report. Kodi moonadi makolo anganyalanyaze zimenezi akumati zilibe chiyambukiro chenicheni pa ana awo? Kapena kodi zingakhale ndi “ngozi yachionekere imene ilipo”? Kodi apa ndipo payenera kuikidwa malire kapena malire kuikidwa pa ufulu wa kulankhula?
Kufufuza kwina kochitidwa ndi akatswiri apayunivesite kunasonyeza kuti pamene zidole za “ngwazi zomenyana nkhonya” zinasonyezedwa nthaŵi zonse ku gulu lina la ana a zaka zinayi ndipo “zidole zodekha ndi zosakondweretsa” ku gulu linanso, awo amene anaona zidole zochita nkhonya anali okhoza kumenya ndi kuponya zinthu pambuyo pake. Ziyambukiro za chiwawa cha pa TV sizimatha ngakhale pambuyo pa ubwana. Kufufuza kwinanso kwa payunivesite, pambuyo pa kuyang’anira ana 650 kuyambira mu 1960 kufika mu 1995 ndi kupenda kupenyerera kwawo wailesi yakanema ndi makhalidwe awo, kunapeza kuti awo amene ankapenyerera wailesi yakanema yachiwawa koposa pamene anali ana anakula nakhala achikulire amakhalidwe aukali, kuphatikizapo kumenya anzawo a muukwati ndi kuyendetsa galimoto ali oledzera.
Pamene kuli kwakuti ana ena sangavomere kuti wailesi yakanema ndi mafilimu zimawayambukira, ena amavomereza. Mu 1995, Children Now, gulu la ku California lopereka chichirikizo, linafunsa ana 750 azaka 10 mpaka 16. Kufufuzako kunasonyeza kuti asanu ndi mmodzi mwa ana khumi ananena kuti kugonana kwa pa TV kumasonkhezera ana kuyamba kugonana akali aang’ono kwambiri.
Ena angatsutse akumanena kuti chiwawa cha pawailesi yakanema ndi m’mafilimu sichimaonedwa kukhala chenicheni ndi ana ndi kuti mafilimu ochititsa mantha onsewo samawayambukira. “Ngati zili choncho,” inatero nyuzipepala ya ku Britain “kodi nchifukwa ninji akuluakulu a sukulu chapakati pa America anauza zikwi za ana kuti m’mipope yopitamo madzi a m’chimbudzi ya kumaloko munalibe ma Teenage Mutant Ninja Turtles? Anawo okonda ma Turtle anali kukwaŵira m’mipopemo kuwafunafuna, ndiye chifukwa chake.”
Lerolino pali mkangano waukulu ponena za zimene ena amayesa kusiyana koonekera bwino pakati pa kulankhula mwaufulu ndi chiwawa chochititsidwa ndi zonena za otsutsa kuchotsa mimba m’malo ambiri ku United States. Otsutsa kuchotsa mimba amadandaula poyera kuti madokotala ndi antchito a m’makiliniki amene amathandiza kuchotsa mimba ali ambanda ndipo sayenera kukhala ndi moyo iwo eniwo. Achangu angapo akufuna kuti madokotala ameneŵa ndi athandizi awo aphedwe. Azondi amaikidwa kuti atenge manambala a magalimoto a oterewa, ndipo maina awo ndi makeyala awo amaperekedwa. Chotero, madokotala ndi antchito a m’makiliniki aomberedwa mfuti ndi kuphedwa.
“Imeneyi si nkhani ya kulankhula mwaufulu,” anatero pulezidenti wa Planned Parenthood Federation of America. “Zimenezi zangofanana ndi kukuwa kuti ‘Moto!’ m’nyumba ya maseŵero yodzaza anthu. Tili ndi nyumba ya maseŵero yodzaza anthu; tangoonani chiŵerengero chachikulu cha mbanda m’makiliniki m’zaka zingapo zapitazi.” Awo amene amasonkhezera chiwawa chimenechi amanena kuti iwo akungogwiritsira ntchito choyenera chawo choperekedwa ndi America’s First Amendment—ufulu wa kulankhula. Zimatero basi. Nkhondo zomenyera choyenera chimenechi zidzapitirizabe kumenyedwa m’zolankhulira za onse, ndipo makhoti adzayenera kuthetsa nkhaniyo, mwatsoka lake, mosakondweretsa onse.
Zimene Makolo Angachite
Nyumba ziyenera kukhala malo achisungiko kwa ana, osati malo kumene angakhale pangozi mosavuta kwa aja ofuna kuwalima pamsana ndi kuwachitira nkhanza kapena kumene maumunthu abata angasonkhezeredwe kusintha makhalidwe awo kukhala achiwawa. “Mungakhale wotsimikizira kuti mwana wanu sadzakhala wachiwawa mosasamala kanthu za kupenyererera kwake chiwawa nthaŵi zonse pa TV,” anatero profesa wina wa payunivesite wa ku United States polankhula ndi makolo. “Koma simungatsimikizire kuti mwana wanu sadzaphedwa kapena kulemazidwa ndi mwana wa munthu wina, amene amapenyerera zofananazo.” Ndiyeno analimbikitsa kuti: “Kuletsa ana kupenyerera chiwawa pa TV kuyenera kukhala mbali ya programu ya umoyo wa anthu onse, mofanana ndi mipando yotetezera m’galimoto, zipeŵa zotetezera panjinga, katemera ndi zakudya zabwino.”
Ngati simungalole mlendo kubwera m’nyumba mwanu ndi kugwiritsira ntchito mawu otukwana ndi kulankhula zonyansa kwa mwana wanu ponena za kugonana ndi chiwawa, pamenepo musalole wailesi ndi wailesi yakanema kukhala mlendoyo. Dziŵani pamene muyenera kuizima kapena kusintha siteshoni. Dziŵani zimene mwana wanu akupenyerera, pawailesi yakanema ndi pakompyuta pomwe, ngakhale m’chipinda chake. Ngati akudziŵa mogwiritsirira ntchito kompyuta ndi mmene angadzilunzanitsire ku makompyuta ena, mungadabwe kwambiri kudziŵa zimene amaloŵetsa m’maganizo mwake usiku uliwonse. Ngati simukuvomereza zimene mwana wanu amapenyerera, mungonena kuti ayi ndi kufotokoza chifukwa chake. Sadzamwalira ngati aletsedwa.
Chomalizira, phunzitsani ana anu kutsatira mapulinsipulo aumulungu ndipo osati makhalidwe a dongosolo la zinthu loipali—ndi malankhulidwe ndi machitidwe ake onyansa ndi achiwawa. (Miyambo 22:6; Aefeso 6:4) Mtumwi Paulo anapatsa Akristu uphungu wina wapanthaŵi yake umene tonsefe tiyenera kutsatira. “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.”—Aefeso 5:3, 4.
[Chithunzi patsamba 10]
Maprogramu ena a pa TV angasonkhezere chiwawa ndi chisembwere