Okhalako Chifukwa cha Tsoka
KODI kukhala wothaŵa kwawo kumamveka bwanji? Yesani kuyerekezera kuti mukukhala mumtendere, ndiyeno mwadzidzidzi mkhalidwe wanu usintha. Usiku umodzi wokha, anansi anu asanduka adani anu. Asilikali akubwera kudzafunkha ndi kutentha nyumba yanu. Muli ndi mphindi khumi zokha kuti mulonge zinthu ndi kuthaŵa kupulumutsa moyo wanu. Zimene mungathe kunyamula ndi kathumba kamodzi kakang’ono basi, pakuti mudzakanyamula makilomita ambiri. Kodi mudzaikamo chiyani?
Mukuchoka mfuti ndi mizinga zikulira. Mukugwirizana ndi ena amenenso akuthaŵa. Masiku akupita; mukupupulikapupulika muli wanjala, waludzu, ndi wotopa kwambiri. Kuti mupulumuke, muyenera kudzikakamiza ngakhale kuti mwatopa. Mugona pansi. Mukufunafuna chakudya m’thengo.
Mukufika kudziko lotetezereka, koma alonda akumalire sakukulolani kudutsa. Iwo asanthula m’matumba mwanu ndi kutengamo chilichonse cha mtengo wapatali. Mukupita pamalo ena a alonda ndi kudutsa malirewo. Akukuikani mumsasa wauve wa othaŵa kwawo, wotchingidwa ndi waya waminga. Ngakhale kuti mwazingidwa ndi ena amene mukuvutika nawo, mukumva kukhala wotayika ndi wosokonezeka maganizo.
Mukulakalaka kukhala ndi banja lanu ndi mabwenzi. Mukupeza kuti mukudalira kotheratu chithandizo chakunja. Kulibe ntchito ndi chilichonse chochita. Mukulimbana ndi kuthedwa nzeru, kutaya mtima, ndi mkwiyo. Mukudera nkhaŵa za mtsogolo mwanu, podziŵa kuti kukhala kwanu mumsasawo kungakhale kwakanthaŵi. Ndi iko komwe, msasawo si nyumba—uli ngati chipinda chongoyembekezeramo kapena nyumba yosungiramo anthu amene aliyense sakuwafuna. Mukukayikira ngati sadzakuumirizani kubwerera kumene munachokera.
Zimenezi zikuchitikira anthu mamiliyoni ambiri lerolino. Malinga ndi United Nations High Commissioner for Refugees (UNHCR), anthu 27 miliyoni padziko lonse athaŵa nkhondo kapena chizunzo. Anthu enanso 23 miliyoni amalandidwa malo m’maiko mwawo. Zonse zitalingaliridwa, timapeza kuti 1 mwa anthu 115 alionse padziko lapansi athamangitsidwa. Ochuluka ndiwo akazi ndi ana. Pokhala akuthaŵa nkhondo ndi tsoka, othaŵa kwawo amangopupulika m’dziko limene silimawafuna, dziko limene limawakana, osati chifukwa cha umunthu wawo, koma chifukwa cha mkhalidwe wawo.
Kukhalapo kwawo ndiko chizindikiro chakuti padziko lonse pali chipolowe chachikulu. UNHCR ikuti: “Othaŵa kwawo ndiwo chizindikiro chosatsutsika chakuti chikhalidwe cha anthu chikunyonyotsoka. Iwo ali umboni womaliza, wooneka kwambiri wa zochitika ndi zochititsa zake zimene zimasonyeza ukulu wa kunyonyotsoka kwa chikhalidwe cha anthu ndi ndale. Titayang’ana padziko lonse, iwo ali chizindikiro chosonyeza mkhalidwe umene kutsungula kwaumunthu kwafikapo.”
Akatswiri akunena kuti vutolo silinakhalepo lalikulu choncho ndipo likukulirakulira kosaleka. Kodi chimene chachititsa mkhalidwe umenewu nchiyani? Kodi pali chothetsera chake? Nkhani zotsatira zidzayankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Chithunzithunzi cha U.S Navy
Mnyamata kulamanzere: UN PHOTO 159243/J. Isaac