Kodi Chothetsera Chake Nchiyani?
MKHALIDWE wa othaŵa kwawo suuli wopandiratu chiyembekezo. Kuzungulira dziko lonse, magulu othandiza anthu amayesetsa kuthandiza aja othaŵa chifukwa cha nkhondo ndi mavuto ena. Njira yaikulu imene amawathandizira ndiyo mwa kuthandiza othaŵa kwawowo kubwerera kumaiko akwawo.
Othaŵa kwawo amenewo amasiya nyumba, chitaganya, ndi dziko chifukwa chakuti amawopa kuphedwa, kuzunzidwa, kugwiriridwa chigololo, kuponyedwa m’ndende, kugwidwa ukapolo, kuberedwa, kapena kufa ndi njala. Chotero othaŵa kwawo asanabwerere kwawo bwinobwino, mavuto amene anawachititsa kuthaŵa ayenera kuthetsedwa. Ngakhale pamene nkhondo itheratu, kusoŵeka kwa bata ndi mtendere kaŵirikaŵiri kumaletsa anthu kubwerera kwawo. Agnes, wothaŵa kwawo ku Rwanda ndiponso mayi wa ana asanu ndi mmodzi, akunena kuti: “Kutibwezera ku Rwanda kungakhale ngati kukatiika m’manda athu.”
Ngakhale zili choncho, kuyambira mu 1989, othaŵa kwawo oposa mamiliyoni asanu ndi anayi abwerera kwawo. Pafupifupi 3.6 miliyoni mwa ameneŵa abwerera ku Afghanistan kuchokera ku Iran ndi Pakistan. Othaŵa kwawo enanso 1.6 miliyoni amene anali m’maiko asanu ndi limodzi anabwerera ku Mozambique, dziko losakazidwa ndi nkhondo yachiŵeniŵeni yazaka 16.
Kubwerera nkovuta. Nthaŵi zambiri maiko amene othaŵa kwawowo amabwererako amakhala osakazidwa—midzi itakhala mabwinja, maulalo atawonongedwa, ndipo m’misewu ndi m’minda atatcheramo mabomba okwirira. Chotero, othaŵa kwawo obwererawo ayenera kuyambiranso osati moyo wawo wokha komanso kumanga nyumba zawo, sukulu, zipatala, ndi zina zilizonse.
Komabe, ngakhale pamene nkhondo zitha kudera lina, ndi kulola othaŵa kwawo kubwerera, zimaulikanso kwina, kuyambitsanso othaŵa kwawo ena. Chifukwa chake, kuthetsa vuto la othaŵa kwawo kumafuna kuthetsa mavuto okuchititsa a nkhondo, kutsendereza, chidani, chizunzo, ndi zinthu zina zimene zimachititsa anthu kuthaŵa kuti apulumutse moyo wawo.
The State of the World’s Refugees 1995 ikuvomereza kuti: “Choonadi chosakanika . . . nchakuti chothetsera [vuto la othaŵa kwawo] chimadalira kwambiri pa zandale, zankhondo ndi zachuma zimene magulu othandiza anthu sakhoza kulamulira.” Malinga ndi kunena kwa Baibulo, gulu lililonse la padziko lapansi, lothandiza anthu kapena lina lililonse, silingathe kupeza chothetsera chake.
Dziko Lopanda Othaŵa Kwawo
Komabe, chothetsera chake chilipo. Baibulo limasonyeza kuti Yehova Mulungu amasamala za aja amene asiya nyumba zawo ndi mabanja. Mosiyana ndi maboma a dziko lapansi, iye ali ndi mphamvu ndi nzeru yothetsera mavuto aakulu koposa omwe anthu akuyang’anizana nawo. Adzatero mwa Ufumu wake—boma lakumwamba limene posachedwapa lidzalamulira zinthu padziko lapansi.
Ufumu wa Mulungu udzatenga malo a maboma onse aumunthu. M’malo mwa kukhala ndi maboma ambiri padziko lapansi, onga omwe tili nawo tsopano, padzakhala boma limodzi lokha, limene lidzalamulira pulaneti lonseli. Baibulo limalosera kuti: “Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Muyenera kuti mukulidziŵa pemphero la chitsanzo lopezeka m’Baibulo pa Mateyu 6:9-13. Mbali ina ya pempherolo imati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” Mogwirizana ndi pemphero limenelo, Ufumu wa Mulungu posachedwapa ‘udzadza’ kudzachita chifuno cha Mulungu padziko lapansi.
Mu ulamuliro wachikondi wa Ufumu wa Mulungu, mudzakhala mtendere ndi chisungiko kwa onse. Sikudzakhalanso chidani kapena kumenyana kwa anthu ndi mitundu ya padziko lapansi. (Salmo 46:9) Sikudzakhalanso mamiliyoni a othaŵa kwawo ofuna kupulumutsa moyo wawo kapena omazunzika m’misasa.
Mawu a Mulungu amalonjeza kuti Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Kristu Yesu, “adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”—Salmo 72:12-14.
[Chithunzi patsamba 10]
Posachedwapa onse adzakhala monga abale ndi alongo