Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 9/8 tsamba 29-30
  • Chifukwa Chake Kuchotsa Kuli Makonzedwe Achikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Kuchotsa Kuli Makonzedwe Achikondi
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumachirikiza Dzina la Mulungu
  • Kumachititsa Mpingo Kukhala Wosungika
  • Chitetezo cha Aliyense
  • Bwererani kwa Mulungu
  • Kuchotsa Anthu Osalapa Kumathandiza
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Chilango Chimene Chingabale Chipatso cha Mtendere
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Landirani Chilango cha Yehova Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kuchotsa—Makonzedwe Achikondi?
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 9/8 tsamba 29-30

Lingaliro la Baibulo

Chifukwa Chake Kuchotsa Kuli Makonzedwe Achikondi

KUTULUTSA—lingaliro lake chabe limachititsa malingaliro ambiri osiyanasiyana pakati pa anthu achipembedzo.a Anthu ambiri amavomereza kuti zipembedzo zimafunika kukhala ndi chilango china chake. Koma ambiri amaona kutulutsa monga mchitidwe wachikale—chilango chaukali chimene chimawakumbutsa za kulanga anthu opanda mlandu ndi zochitika za inquisition.

Chokulitsa vutolo ndicho chisonkhezero chosokeretsa cha dziko. Chotero, zipembedzo zambiri za Dziko Lachikristu zatenga kaonedwe kolekerera uchimo kwambiri. Nchifukwa chake mtumiki wina wa Episkopo anati: “Kutulutsa kuli mbali ya mwambo wathu, koma ndiganiza kuti sitikukugwiritsira ntchito m’zaka za zana lino.”

Komabe, anthu ambiri angadabwe kudziŵa kuti pakati pa Mboni za Yehova, kuchotsa (kolingana ndi kutulutsa) ndi nkhani yaikulu. Kunena zoona, ndi chinthu chovuta kuchichita, koma ndi makonzedwe achikondi. Motani?

Kumachirikiza Dzina la Mulungu

Yehova ndi Mulungu woyera. Samalekerera tchimo ladala la awo omwe amati amamulambira. Mtumwi Petro analembera Akristu kuti: “Khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:15, 16) Chotero kuchotsa ochimwa osalapa kumachirikiza dzina loyera la Mulungu; kumasonyeza chikondi cha pa dzinalo.—Yerekezerani ndi Ahebri 6:10.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ngati Mkristu wakhala ndi chifooko kapena wachita tchimo lalikulu, amangochotsedwa mumpingo? Kutalitali! Yehova si wolamulira wopondereza wopanda chifundo. Iye ngwachifundo ndipo amamvetsetsa. Amakumbukira kuti ndife opanda ungwiro. (Salmo 103:14) Yehova amadziŵa kuti “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Mulungu wapanga makonzedwe a thandizo lauzimu mumpingo kotero kuti ngati Mkristu ‘alakwa’ kapena ngakhale kuchita tchimo lalikulu, ‘angabwezedwe’ mwachikondi mumzimu wa chifatso. (Agalatiya 6:1) Mwa kulandira uphungu wochokera m’Mawu a Mulungu ndi kusonyeza chisoni chochokera mumtima ndi kulapa kwenikweni, munthu amene wapatuka panjira yachilungamo ‘angachiritsidwe’ mwauzimu.—Yakobo 5:13-16.

Komano bwanji ngati Mkristu wobatizidwa wachita tchimo lalikulu ndipo zoyesayesa zonse za kumubweza zalephera? M’mawu ena, bwanji ngati akana mouma khosi kuwongolera njira yake yauchimo?

Kumachititsa Mpingo Kukhala Wosungika

Baibulo limalamula Akristu kuti: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi.”—1 Akorinto 5:11.

Kodi lamulo la Baibulo limeneli ndi lankhanza ndi loluluza? Tangolingalirani izi: Pamene mpandu wouma mutu aponyedwa m’ndende chifukwa cha kuswa lamulo, kodi zimenezo zimaonedwa monga nkhanza kapena kupanda chifundo? Ayi, chifukwa chakuti anthu ayenera kutetezera mtendere ndi chisungiko cha chitaganya. Kwenikweni, pamene mpanduyo ali m’ndende amakhala wochotsedwa m’chitaganya cha omvera malamulo.

Mofananamo, mpingo wachikristu uyenera kuchotsa olakwa osalapa pakati pawo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mpingo uyenera kukhala malo osungika opanda anthu a khalidwe loipa ndi ena ochimwira dala.

Pozindikira kuti “wochimwa mmodzi awononga zabwino zambiri,” mtumwi Paulo analamula okhulupirira anzake kuti: “Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” (Mlaliki 9:18; 1 Akorinto 5:13) Mchitidwe umenewu umaletsa wochimwayo kuwanditsa kuipa mumpingo, ndipo umatetezera dzina labwino la mpingo.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 3:15.

Chitetezo cha Aliyense

Kuchotsa kumatetezeranso aliyense mumpingo. Tiyeni tifanizire: Yerekezerani kuti mwadzutsidwa pa tulo ndi phokoso lalikulu la hutala kapena alamu ya galimoto. Phokoso lopyozalo nlovuta kulinyalanyaza; kwenikweni, likukudzidzimutsani! Mofananamo, pamene wina achotsedwa mumpingo, mchitidwewu umagalamutsa aliyense wa m’gulu la nkhosa. Umasokoneza maganizo awo. Sunganyalanyazidwe. Kodi zimenezi zingakhale chitetezo motani?

“Nthaŵi yoyamba pamene ndinamva ku Nyumba ya Ufumu kuti wina anachotsedwa, ndinachita mantha choyamba,” ikutero Mboni ina. “Ndiyeno zinandichititsa kudzichepetsa. Zinandichititsa kuzindikira kuti inenso ndikhoza kugwa.” Monga mmene mawu ake akusonyezera, kuchotsa kungasonkhezere ena kusanthula makhalidwe awo.—1 Akorinto 10:12.

Mwa kudzifunsa ife eni mafunso onga akuti ‘Kodi pali mbali zilizonse m’moyo wanga zimene ndili wofooka mwauzimu?’ tingathandizidwe kusanthula kaimidwe kathu ndi Mulungu. Mwa njira imeneyi tingapitirizebe ‘kugwira ntchito yake ya chipulumutso chathu ndi mantha, ndi kunthunthumira.’—Afilipi 2:12.

Bwererani kwa Mulungu

“Ngakhale kuti chinali chovuta,” anatero Mkristu wina amene anachotsedwapo nthaŵi ina, “chilangocho chinali choyenera ndi chofunika kwambiri, ndipo chinakhaladi chopulumutsa moyo.” Zimenezi zikusonyeza mbali inanso yofunika ya kuchotsa. Kungasonkhezere amene anali ochimwa osalapa kuyambanso kubwerera kwa Mulungu.

Mtumwi Paulo anati: “Iye amene [Yehova, NW] amkonda amlanga.” (Ahebri 12:6) Ndipo pamene kuli kwakuti nzoona kuti “chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu choŵaŵa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”—Ahebri 12:11.

Zimenezo ndi zimene zinachitikira Richard. Atachotsedwa kwa zaka pafupifupi ziŵiri, analapa, kuwongolera khalidwe lake losalemekeza Mulungu, ndipo anamlandiranso mumpingo wachikristu. Akamakumbukira, amanena za chochitikacho kuti: “Ndikuzindikira kuti ndinafunikira kuchotsedwa ndi kuti ndinayeneradi kulandira zimenezo. Kunalidi kofunika ndipo kunandithandiza kuona mmene njira yanga inalilidi yoipa ndi kufunika kwa kufunafuna chikhululukiro cha Yehova.”

Kupirira chilango kungakhale kovuta. Kuchilandira kumafuna kudzichepetsa, koma awo amene amatengapo phunziro amatuta zipatso zochuluka.

Chotero, kuchotsa kuli makonzedwe achikondi chifukwa chakuti kumachirikiza dzina loyera la Mulungu ndipo kumatetezera mpingo ku chisonkhezero choipa cha uchimo. Ndiponso, kumasonyeza chikondi pa wochimwayo mwa kumlimbikitsa kulapa ndi ‘kubwerera kuti afafanizidwe machimo ake, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Yehova.’—Machitidwe 3:19.

[Mawu a M’munsi]

a Kutulutsa ndi chilango cha kuchotsedwa m’chipembedzo.

[Mawu a Chithunzi patsamba 29]

The New Testament: A Pictorial Archive from Nineteenth-Century Sources, yolembedwa ndi Don Rice/Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena