Kuchotsa—Makonzedwe Achikondi?
“WOYERA, woyera, woyera, [Yehova, NW] Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 4:8) Mogwirizana ndi malongosoledwe amenewo, Yehova ndiye Magwero a miyezo yoyera. Imeneyi yalembedwa mu “malembo opatulika,” ndipo Akristu ayenera kutsatira zitsogozo zimenezi. Ndithudi, ayenera kupeŵa chilichonse chimene chili chodetsedwa pamaso pa Yehova.—2 Timoteo 3:15; Yesaya 52:11.
Baibulo limalamula momveka bwino kuti: “Monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:15, 16) Chiyambire pamene mpingo Wachikristu unakhalapo zaka mazana 19 zapitazo, Akristu oona amenya nkhondo zolimba kuutetezera pa chidetso chauzimu ndi chamakhalidwe.—Yuda 3.
Chifukwa Chake Chitetezero Chili Chofunika
Atumiki onse a Mulungu amayang’anizana ndi chitokoso cha kudzisunga ali oyera mwamakhalidwe ndi mwauzimu. Ndi cholinga chimenecho, ayenera kulimbana ndi adani atatu amphamvu—Satana, dziko lake, ndi zikhoterero zathu zauchimo za thupi. (Aroma 5:12; 2 Akorinto 2:11; 1 Yohane 5:19) Dziko la Satana lingakuyeseni kukhala amakhalidwe oipa, lingakusonkhezereni kutengera njira zake, ndipo lingakulonjezeni chuma, kudziŵika, malo, kutchuka, ndi mphamvu. Koma awo amene ali otsimikiza kulondola kulambira koona amakana zimene Satana amawalonjeza ndi kukhalabe “osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amafuna kukhala pansi pa chisamaliro chotetezera ndi chachikondi cha gulu loyera la Yehova.—Yakobo 1:27; 1 Yohane 2:15-17.
Yehova wapereka thandizo kwa chiŵalo chilichonse cha mpingo Wachikristu chimene chigwera m’ngozi ya mayesero a Satana chifukwa cha kufooka kwa umunthu. Akulu okhoza bwino mwauzimu aikidwa kutetezera mpingo ndi kuthandiza mwachikondi ochimwa kulapa machimo awo ndi kusintha kuti achire. Mkristu aliyense amene aloŵa m’cholakwa ayenera kuthandizidwa moleza mtima kuti alape ndi kusintha njira zake.—Agalatiya 6:1, 2; Yakobo 5:13-16.
Mmene Kuchotsa Kulili Kwachikondi
Atumiki a Yehova obatizidwa amene amatsata mwadala njira yoipa ndi kukana kusintha ayenera kuonedwa monga osalapa ndipo motero osayenerera mayanjano Achikristu. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 2:19.) Anthu otero samaloledwa kukhala mumpingo woyera Wachikristu akumaudetsa. Ayenera kuthamangitsidwa.
Kuyenera kwa kuthamangitsa awo amene amachita ntchito zoipa kungafanizidwe ndi mkhalidwe wotsatirawu: Chifukwa cha kuwonjezereka kwa ziukiro ndi maupandu achiwawa pa ophunzira, sukulu zina zayamba kugwiritsira ntchito njira imene “imafuna kuchotseratu ophunzira amene amagwiritsira ntchito chida kapena kuwopseza nacho ena,” ikusimba motero The Globe and Mail, nyuzipepala ya ku Toronto, Canada. Kuthamangitsako kumachitidwa kuti atetezere ophunzira amene akufuna kupindula ndi programu ya maphunziro popanda kuukiridwa.
Kodi nchifukwa ninji kuthamangitsa wolakwa wosalapa mumpingo kuli kwachikondi? Kuchita motero ndiko chisonyezero cha kukonda Yehova ndi njira zake. (Salmo 97:10) Mchitidwe umenewu umasonyeza kukonda awo amene amalondola njira yolungama chifukwa chakuti umachotsa munthu amene angapereke chisonkhezero choipa pakati pawo. Umatetezeranso chiyero cha mpingo. (1 Akorinto 5:1-13) Ngati mkhalidwe woipa kwambiri kapena chidetso chauzimu ziloledwa mumpingo, ungaipitsidwe ndipo ungakhale wosayenerera kupereka utumiki wopatulika kwa Yehova, amene ali woyera. Ndiponso, kuthamangitsidwa kwa wochita cholakwa kungamthandize kuona kuwopsa kwa njira yake ya mphulupuluyo, kulapa, ndi kupanga masinthidwe oyenera ndi kubwezeretsedwanso mumpingo.
Chiyambukiro pa Ena
Pamene chiŵalo cha mpingo chichita cholakwa chachikulu, monga ngati chigololo, icho sichimakondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Mkristu aliyense amene amagonjera kuchisembwere ndithudi samaganiza monga momwe Yosefe anachitira pamene mkazi wa Potifara anayesa kumchititsa kugonana naye. Yankho la Yosefe linali lakuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:6-12) Yosefe analemekeza miyezo yoyera ya Yehova ndi kuthaŵa kuchoka pamalowo. Komanso, wochita chigogolo amaoneka kukhala wopanda chikondi chokwanira cha pa Mulungu cha kupeŵa kukhutiritsa chilakolako chake chathupi.—Agalatiya 5:19-21.
Munthu wobatizidwa amene amaswa malamulo a Mulungu samasonyeza nkhaŵa ponena za chivulazo ndi kuvutika mtima kumene iye adzabweretsa pa achibale ake okhulupirira. Kuvutika mtimako kumakhala kosapiririka ndi ena. Atadziŵa kuti mwana wake wamwamuna anali wamakhalidwe oipa, mkazi wina Wachikristu anadandaula kuti: “Ndi abale ndi alongo oŵerengeka okha, ngati alipo nkomwe, amene akukhala ngati akumvetsa mmene tikusautsidwira. . . . Ndife osweka mtima.” Mbiri ya banja lonse ingaipitsidwe. Kupsinjika mtima ndi kumva kukhala waliwongo kungavutitse ziŵalo zokhulupirika za m’banja. Motero njira yoipa ya wochita cholakwayo imachititsa kuŵaŵidwa mtima m’banja.
Thandizo Lachikondi la Ziŵalo za Banja
Ziŵalo za banja zokhulupirika Zachikristu za anthu othamangitsidwa zifunikira kukumbukira kuti kuchotsako kuli kwachikondi ndiponso kotetezera. Kuyesayesa kulikonse kumapangidwa kuthandiza wochita cholakwayo. Koma ngati asonyezadi kukhala wosamvera Mulungu ndipo ali wosalapa mouma khosi, mpingo ufunikira kutetezeredwa ndipo sungachitire mwina koma kuchita mogwirizana ndi mmene Mawu a Mulungu amalangizira: “Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” (1 Akorinto 5:13) Zili monga momwe Mboni ina inanenera, “kuchotsa kuli nkhani ya kukhulupirika kulinga kwa Yehova.”
Pamene chiŵalo cha banja chichotsedwa, achibale Achikristu amavutika mtima. Chotero akulu oikidwa ayenera kuchita momwe angathere kuwatonthoza mwauzimu. (1 Atesalonika 5:14) Akulu angawapempherere ndi kupemphera nawo. Kaŵirikaŵiri kumakhala kotheka kuchezera Akristu okhulupirika ameneŵa ndi kukambitsirana nawo malingaliro omangirira a Malemba. Abusa a gulu la nkhosa ayenera kugwiritsira ntchito mpata uliwonse kulimbitsa okondedwa ameneŵa mwauzimu misonkhano Yachikristu isanayambe ndi pambuyo pake. Chilimbikitso chowonjezereka chingaperekedwe mwa kutsagana nawo mu utumiki wakumunda. (Aroma 1:11, 12) Abusa auzimu afunikira kusonyeza chikondi ndi nkhaŵa imene atumiki a Yehova okhulupirika ameneŵa amafunikira.—1 Atesalonika 2:7, 8.
Njira yauchimo ya munthu siili chifukwa chonyalanyazira aliyense wa m’banja lake amene ali wokhulupirika kwa Yehova. Mfumu yoipa ya Israyeli Sauli anakanidwa ndi Mulungu, koma Davide sanalole kuti zimenezi zidodometse kukonda kwake mwana wa Sauli, Jonatani. Kwenikweni, chikondi cha Davide ndi Jonatani chinakhala champhamvu kwambiri. (1 Samueli 15:22, 23; 18:1-3; 20:41) Chotero onse mumpingo ayenera kukhala ochirikiza ndi achikondi kwa Akristu amene achibale awo amachimwira Yehova.
Kungakhale kupanda chikondi kotani nanga kunyalanyaza kapena kukhala ankhanza kwa okhulupirika otero! Ziŵalo za banja zokhulupirika zifunikira kwambiri kulimbikitsidwa. Zingaone ngati kuti zili zokhazokha ndipo zinthu zingakhale zovuta kwambiri kwa iwo. Mwinamwake mungakambitsirane nawo za kanthu kena kauzimu kapena chokumana nacho cholimbikitsa pa telefoni. Ngati munthu wothamangitsidwayo ayankha telefoni, ingopemphani kulankhula ndi wachibale Wachikristu. Mungaitane ziŵalo zokhulupirikazo za m’banjalo kumacheza kapena kudzadya nanu chakudya kunyumba kwanu. Ngati mukumana nawo pogula zinthu, mungagwiritsire ntchito nyengoyo pa kuyanjana nawo komangirira. Kumbukirani, Akristu okhulupirika amene ali ndi achibale ochotsedwa akali mbali ya gulu loyera la Yehova. Angadzipatule mosavuta ndi kulefulidwa. Chotero, khalani maso kuwakomera mtima ndi kuwasonyeza chikondi. Pitirizani kuchita zabwino ‘kwa iwo onse a pa banja la chikhulupiriro.’—Agalatiya 6:10.
Yamikirani Makonzedwe a Yehova
Ndife othokoza chotani nanga kuti Yehova Mulungu amasonyeza chisamaliro chachikondi kwa aliyense wa ife m’banja la padziko lonse la olambira ake. Kupyolera m’gulu lake iye mwachikondi wapanga makonzedwe otithandiza kuyenda pamaso pake m’njira yolungama. Ngakhale ngati chiŵalo cha banja chichita tchimo mwadala ndipo chifunikira kuthamangitsidwa mumpingo, pali njira ya kubwerera ngati chilidi cholapa. Zimenezi zasonyezedwa ndi chitsanzo chotsatirachi:
Akulu anayesa kuthandiza munthu wina amene tidzamutcha kuti Anna, koma anayamba kusuta fodya, kumwa, ndi anamgoneka. Anali wosalapa ndipo anachotsedwa mumpingo. Komabe, posapita nthaŵi, Anna anayamba kulakalaka mayanjano achikondi a mpingo woyera wa Yehova ndipo anapemphera kwa iye kaamba ka thandizo. Akuvomereza kuti sanazindikire mokwanira ponena za chisamaliro cha akulu kwa awo amene amapambuka. Anna anayamba kufika pamisonkhano kachiŵirinso, ndipo zimenezi zinamchititsa kulapa. Pambuyo pake, anabwezeretsedwa mumpingo wachikondi ndi wotetezera. Kachiŵirinso, Anna akuchirikiza miyezo yapamwamba ya makhalidwe ya Yehova. Iye ngwoyamikira chikondi chimene anasonyezedwa ndi akulu ndiponso akuti: “Simungadziŵe bwino mmene zofalitsa Zachikristu zandithandizira. Yehova amasamaliradi zosoŵa zathu.”
Inde, Mulungu walinganiza njira ya kubwereranso kwa awo amene athamangitsidwa mumpingo komano pambuyo pake nalapa. Taona kuti ngakhale kuchotsa kwenikweniko kuli makonzedwe achikondi. Komatu nkwabwino kwambiri chotani nanga kupeŵa chochitika chomvetsa chisoni chimenechi mwa kumamatira nthaŵi zonse ku njira zolungama za Mulungu wathu woyera! Tikhaletu othokoza nthaŵi zonse kaamba ka mwaŵi wa kutamanda Yehova monga mbali ya gulu lake loyera, lachikondi, ndi lotetezera.
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi mukusonyeza chikondi kwa achibale a awo othamangitsidwa mumpingo?