Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 10/8 tsamba 17-18
  • “Si Mlandu Wanga”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Si Mlandu Wanga”
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Si Lingaliro Latsopano Kwenikweni
  • Kodi Muli ndi Vuto Ndinu Kapena Chibadwa Chanu?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Majini Athu Amaikiratu Zamtsogolo Mwathu?
    Galamukani!—1996
  • Kodi ndi Mlandu wa Yani?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa za Kukhulupirira Choikidwiratu?
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 10/8 tsamba 17-18

“Si Mlandu Wanga”

KODI ndi kangati pamene mumamva winawake akunena kuti, ‘Pepani. Ndi mlandu wanga. Ndinedi ndachititsa zimenezi!’? Kuona mtima kosavuta kumeneku sikumamvekamvekanso. Kwenikweni, nthaŵi zambiri, ngakhale pamene munthu avomera mlandu, amayesetsa kukankhira mlanduwo pa wina kapena pa mikhalidwe yovuta imene wolakwayo anena kuti sanathe kuilamulira.

Ena amaimba mlandu ngakhale majini awo! Koma kodi zimenezi nzoona? Buku lakuti Exploding the Gene Myth likayikira zolinga ndi phindu lake la mbali zina za kufufuza majini. Mtolankhani wa ku Australia Bill Deane, pa kupenda kwake bukulo, akunena zotsatirazi pambuyo pa kusinkhasinkha: “Okhulupirira kuti makhalidwe a anthu ngoikidwiratu akuoneka kuti posachedwapa ayamba kukhulupirira kuti apeza umboni wosatsutsika kwenikweni wochirikiza malingaliro awo akuti palibe amene ayenera kuimbidwa mlandu pa zochita zawo: ‘Palibe chimene akanachita kuti asadule m’mero wa mkaziyu, Wolemekezekanu—zili m’majini ake.’”

Si Lingaliro Latsopano Kwenikweni

Pokhala ndi mbadwo uno umene mofulumira ukukhala zimene wolemba wina amatcha kuti mbadwo wa “sindine,” lingaliro limeneli lingaoneke kuti likufala. Komabe, mbiri yolembedwa ikusonyeza kuti kukankhira mlandu pa ena, mwa kuŵiringula kuti “Si mlandu wanga,” kwakhalapo kuchokera pachiyambi cha munthu. Zimene Adamu ndi Hava anachita pambuyo pa tchimo lawo loyamba, kudya chipatso chimene Mulungu anawaletsa, zinali chitsanzo chapadera cha kukankhira mlandu pa ena. Nkhani ya mu Genesis imasimba za kukambitsirana kumene kunachitika, pamene Mulungu anali woyamba kulankhula kuti: “Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye? Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya. Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.”—Genesis 3:11-13.

Kuyambira pa nthaŵi imeneyo, anthu asema mitundu yosiyanasiyana ya zikhulupiriro ndipo afunafuna zifukwa zosiyanasiyana zachilendo zimene zingawachotsere mlandu uliwonse pa zochita zawo. Chodziŵika kwambiri pakati pa zimenezi chinali chikhulupiriro chakale cha choikidwiratu. Mkazi wina wachibuda amene moona mtima ankakhulupirira Karma anati: “Ndinkalingalira kuti sikunali kwanzeru kuvutika chifukwa cha chinthu chimene ndinabadwa nacho komano chimene sindinali kudziŵa. Ndinangochivomereza monga choikidwiratu.” Posonkhezeredwa ndi chiphunzitso cha kuikiratu zamtsogolo chophunzitsidwa ndi John Calvin, kukhulupirira choikidwiratu nkofalanso m’Dziko Lachikristu. Kaŵirikaŵiri atsogoleri achipembedzo amauza achibale olira maliro kuti ngozi yakutiyakuti inali chifuno cha Mulungu. Ndiyenonso, Akristu ena oona mtima amapatsa Satana mlandu pa chilichonse chimene chilakwika m’moyo wawo.

Tsopano, tayamba kuona khalidwe limene amati lilibe mlandu limene malamulo ndi anthu akulivomereza. Tikukhala m’nyengo pamene zoyenera za anthu zikuchuluka ndi pamene kupatsa munthu mlandu kukuzimiririka.

Kufufuza za khalidwe la munthu kwatulutsa zimene amati ndi umboni wa sayansi umene ena amalingalira kuti udzapereka ufulu wa khalidwe losiyanasiyana kuyambira pa chisembwere kufika pa mbanda. Zimenezi zikusonyeza chikhumbo cha anthu cha kukankhira mlandu pa chilichonse kapena wina aliyense koma osati pa munthuwe.

Tikufuna mayankho a mafunso onga aŵa: Kodi nchiyani kwenikweni chimene sayansi yapeza? Kodi khalidwe la munthu limadalira kotheratu pa majini athu? Kapena kodi khalidwe lathu limalamuliridwa ndi zinthu zamkati ndi zakunja zomwe? Kodi nchiyani kwenikweni chimene umboni umasonyeza?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena