Kodi ndi Mlandu wa Yani?
MUNTHU woyamba, Adamu, anayamba zimenezo. Atachimwa anati kwa Mulungu: “Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.” Kwenikweni, iye anali kunena kuti: “Si mlandu wanga!” Mkazi woyamba, Hava, nayenso anachita chimodzimodzi pamene anati: “Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.”—Genesis 3:12, 13.
Motero chitsanzo cha kukana kwa anthu kuvomereza mlandu wa machitidwe awo chinakhazikitsidwa m’munda wa Edene. Kodi munachitapo cholakwa chimenechi? Pamene mavuto afika, kodi mumakankhira mwamsanga mlanduwo kwa ena? Kapena kodi mumapenda mkhalidwewo ndi kuona amene alidi ndi mlandu? M’moyo wa tsiku ndi tsiku, kuli kopepuka kwambiri kugwera mumsampha wa kuimba mlandu ena pa zolakwa zathu ndi kunena kuti, “Si mlandu wanga!” Tiyeni tione mikhalidwe yofala ndi kuona zimene anthu ena amakonda kuchita. Chofunika kwambiri, lingalirani pa zimene mukanachita m’mikhalidwe yoteroyo.
Vuto la Ndalama
“Si mlandu wanga—ndi mkhalidwe wa chuma, anthu amalonda osaona mtima, kudula kwa zinthu,” ena anganene zimenezo pamene aloŵa m’vuto lalikulu la ndalama. Koma kodi zinthu zimenezi zilidi zoyenera kuimbidwa mlandu? Mwinamwake mikhalidwe ina inawatsogolera m’malonda okayikitsa ndi osaonekera bwino. Nthaŵi zina umbombo umaphimba kulingalira kwabwino, ndipo anthu amakhala mikhole yosavuta kwa amalonda osaona mtima. Iwo amaiŵala chenjezo lakuti, “Ngati zikumvekera zoona koposa, kaŵirikaŵiri sizoona.” Iwo amafunafuna uphungu umene angakonde kumva, koma pamene vuto la ndalama lifika poipitsitsa, iwo amafunafuna munthu wina wakuti amuimbe mlandu. Mwatsoka, zimenezi zimachitika nthaŵi zina ngakhale mumpingo Wachikristu.
Ena akoledwa m’malonda opanda pake ndipo ngakhale achinyengo, monga ngati kugula madiamondi achinyengo, kulipirira maprogramu a pawailesi yakanema oonekera kukhala okhupuka koma amene anazimiririka mwamsanga, kapena kuchirikiza ntchito yofutukula chuma cha munthu imene ndalama zake zinatha. Chikhumbo chosadziletsa cha chuma chingakhale chitawaiŵalitsa uphungu wa Baibulo wakuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, . . . nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:9, 10.
Kuwononga ndalama kosadziletsa kungaloŵetse wina m’vuto la ngongole zochuluka. Ena amafuna kuoneka monga anthu a m’magazini atsopano amafashoni, amapita kutchuthi chofuna ndalama zambiri, amakadyera m’malesitilanti okongola kwambiri, ndi kugula “zoseŵeretsa” za achikulire zatsopano—galimoto zosangulukira, mabwato, makamera, mawailesi a stereo. Chikhalirechobe, m’kupita kwa nthaŵi ena angakhoze kukhala ndi zinthu zimenezi kupyolera m’makonzedwe anzeru ndi kusunga ndalama. Komabe, awo amene amathamangira kukhala nazo amagwera m’ngongole zazikulu. Ngati atero, kodi ndi mlandu wa yani? Mwachionekere iwo amanyalanyaza uphungu wanzeru wa Miyambo 13:18 wakuti: “Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa.”
Kugwiritsidwa Mwala ndi Ana
“Ndi akulu amene anachititsa kuti ana anga asiye choonadi,” makolo ena angatero. “Iwo sanapereke chisamaliro chokwanira kwa ana anga.”
Akulu ali ndi thayo la kuŵeta ndi kusamalira nkhosa, koma bwanji ponena za makolo iwo eniwo? Kodi iwo akupereka chitsanzo chabwino cha kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu m’zochita zawo zonse? Kodi phunziro la Baibulo la banja linali kuchitidwa mokhazikika? Kodi makolowo ankasonyeza changu mu utumiki wa Yehova ndi kuthandiza anawo kuukonzekera? Kodi iwo anali osamala za mayanjano a ana awo?
Mofananamo, nkwapafupi kwa kholo kunena za maphunziro a kusukulu kuti: “Ndi aphunzitsi amene achititsa kuti mwana wanga asapambane mayeso. Sankamkonda mwana wanga. Ndipo mlingo wa kaphunzitsidwe ka sukulu ija ngwotsika kwambiri.” Koma kodi kholo linkalankhulana kaŵirikaŵiri ndi akusukulu? Kodi khololo linkafunitsitsa kudziŵa za maphunziro a mwanayo? Kodi homuweki yake inali ndi ndandanda, ndipo kodi thandizo linkaperekedwa pamene linafunikira? Kodi vuto lenileni lingakhale mkhalidwe wa maganizo kapena ulesi wa mwanayo kapena kholo?
M’malo mwakuti makolo aimbe mlandu sukulu, kungakhale kothandiza kwambiri ngati achitapo kanthu kutsimikizira kuti ana awo ali ndi mkhalidwe wamaganizo wabwino ndi kuti akugwiritsira ntchito njira zothandiza kuphunzira zimene zilipo pasukulu.
Kulephera Kupita Patsogolo Mwauzimu
Nthaŵi ndi nthaŵi timamva wina akunena kuti: “Bwenzi ndili wolimba mwauzimu, koma si mlandu wanga. Akulu samadera nkhaŵa za ine kwenikweni. Ndilibe mabwenzi alionse. Mzimu wa Yehova suli pampingo umenewu.” Panthaŵi imodzimodziyo, ena mumpingo ali ndi mabwenzi, ali achimwemwe, ndipo akupita patsogolo mwauzimu; ndipo mpingo wadalitsidwa ndi chiwonjezeko ndi kupita patsogolo kwauzimu. Chotero nchifukwa ninji ena ali ndi mavuto?
Ndi anthu oŵerengeka amene amafuna kumayanjana kwambiri ndi awo amene amasonyeza mzimu woipa ndi wodandaula. Lilime lakuthwa ndi lodula ndi kudandaula kosalekeza zingakhale zolefulitsa maganizo kwambiri. Posafuna kusabwezedwa m’mbuyo mwauzimu, ena angachepetse mayanjano awo ndi anthu oterowo. Poona zimenezi kukhala kupanda chikondi kwa mpingo, wina angayambe kusamukasamuka, choyamba akumapita kumpingo wina, ndiyeno ku wina, ndi ku winanso. Monga nsambi za nyama za m’madambo a mu Afirika zimene nthaŵi zonse zimafunafuna msipu, Akristu “osamukasamuka” ameneŵa nthaŵi zonse amakhala akufunafuna mpingo wabwino. Iwo akanakhala achimwemwepo chotani nanga ngati akanayang’ana pa zabwino mwa anthu ena ndi kulimbikira kusonyeza mokwanira zipatso za mzimu wa Mulungu m’miyoyo yawo!—Agalatiya 5:22, 23.
Ena amachita zimenezo mwa kupanga kuyesayesa kwa kulankhula ndi munthu wina pamsonkhano uliwonse pa Nyumba Yaufumu ndi kumuthokoza moona mtima pamfundo ina yabwino. Ingakhale ponena za ana ake odzisungira bwino, kufika pamisonkhano Yachikristu mokhazikika, mayankho okonzekeredwa bwino pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, kuchereza kwake mwa kupereka nyumba yake kaamba ka Phunziro Labuku Lampingo ndi kukumana kwa utumiki wakumunda, ndi zina zotero. Mwa kuchipanga kukhala cholinga chanu kuona zoposa pa kupanda ungwiro, ndithudi mudzapeza mikhalidwe yabwino mwa abale ndi alongo anu Achikristu. Zimenezi zidzakuchititsani kukhala wokondedwa nawo, ndipo mudzapeza kuti simukusoŵa mabwenzi okhulupirika.
Chodzikhululukira Chotsirizira
“Ndi chifuniro cha Mulungu.” “Ndi mlandu wa Mdyerekezi.” Mwinamwake chodzikhululukira chotsirizira ndicho kuimba mlandu Mulungu kapena Mdyerekezi kaamba ka zolephera zathu. Nzoona kuti Mulungu kapena Satana angasonkhezere zochitika zina m’miyoyo yathu. Komabe, ena amakhulupirira kuti chinthu chilichonse, chabwino kapena choipa m’moyo wawo, chimachititsidwa ndi Mulungu kapena Satana. Zili monga ngati kuti palibe chinthu chimene chinawachitikirapo monga chotulukapo cha zochita zawo. “Ngati Mulungu afuna kuti ndikhale ndi galimoto latsopano lija, adzandichititsa kukhala nalo.”
Oterowo kaŵirikaŵiri amakhala ndi miyoyo yosasamala, akumapanga zosankha za ndalama ndi zina mwa kulingalira kuti Mulungu adzawapulumutsa. Ngati machitidwe awo opanda nzeru achititsa tsoka, la chuma kapena mwa njira ina, iwo amaimba mlandu Mdyerekezi. Kuchita chinthu mwaphuma popanda choyamba ‘kuŵerengera mtengo’ ndiyeno nkuimba mlandu Satana kaamba ka kulepherako, kapena choipirapodi, kuyembekezera kuti Yehova adzaloŵererapo, sindiko kudzitukumula chabe komanso kutsutsana ndi Malemba.—Luka 14:28, 29.
Satana anayesa kuchititsa Yesu kulingalira mwa njira imeneyo ndi kukana mlandu wa machitidwe Ake. Ponena za chiyeso chachiŵiri, Mateyu 4:5-7 amasimba kuti: “Mdyerekezi anamuka naye ku mzinda woyera; namuika iye pamwamba pa chimbudzi cha kachisi, nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzauza angelo ake za iwe, ndipo pa manja awo adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala.” Yesu anazindikira kuti sakayembekezera Yehova kuloŵererapo ngati iye akatenga njira yopusa ndi yodzipha imeneyo. Chifukwa chake, anayankha kuti: “Kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.”
Awo okhala ndi chikhoterero cha kuimba mlandu Mdyerekezi kapena Mulungu kaamba ka machitidwe awo okayikitsa ali ofanana kwambiri ndi okhulupilira kupenda nyenyezi, amene amaika nyenyezi m’malo mwa Mulungu kapena Mdyerekezi. Pokhala okhutiritsidwa kotheratu kuti iwo alibe mphamvu pa kanthu kalikonse kamene kamachitika, amanyalanyaza lamulo la mkhalidwe lomvekera bwino lotchulidwa pa Agalatiya 6:7 lakuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”
Kuyang’anizana ndi Zenizeni
Palibe amene angatsutse chenicheni chakuti tikukhala m’dziko lopanda ungwiro. Mavuto ofotokozedwa panopa ndithudi ali enieni. Anthu amatinyenga pa nkhani za ndalama. Olemba ntchito ena adzachita mopanda chilungamo. Mabwenzi angasonkhezere ana athu m’njira zoipa. Aphunzitsi ena ndi sukulu amafunikira kuwongolera. Akulu nthaŵi zina angakhale achikondi kwambiri ndi odera nkhaŵa. Koma tiyenera kuzindikira chiyambukiro cha kupanda ungwiro ndi kuti, monga momwe Baibulo limasonyezera, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Motero sikumakhala kuyang’anizana ndi zenizeni kuyembekezera kuti njira yathu ya moyo idzakhala yosavuta nthaŵi zonse.—1 Yohane 5:19.
Kuwonjezerapo, tiyenera kuzindikira kupanda ungwiro ndi zolephera zathu ndi kudziŵa kuti nthaŵi zambiri mavuto athu amachititsidwa ndi kupusa kwathu. Paulo analangiza Akristu ku Roma kuti: “Ndiuza munthu ali yense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa.” (Aroma 12:3) Uphungu umenewo umagwira ntchito mofananamo kwa ife lerolino. Pamene chinthu china chilakwika m’miyoyo yathu, sitiyenera kufulumira kutsatira makolo athu akalewo Adamu ndi Hava ndi kunena kuti: “Si mlandu wanga!” M’malo mwake, tidzifunse kuti, ‘Kodi ndikanachita chiyani mosiyana kotero kuti ndikanapeŵa chotulukapo chosakondweretsa chimenechi? Kodi ndagwiritsira ntchito kulingalira kolama pankhaniyi ndi kufuna uphungu wochokera ku magwero anzeru? Kodi ndinachotsa chikayikiro pa winayo kapena enawo, ndikuwapatsa ulemu?’
Ngati tilondola malamulo a mkhalidwe Achikristu ndi kusonyeza kulingalira kolama, tidzakhala ndi mabwenzi ambiri ndi mavuto oŵerengeka. Zothetsa nzeru zina zosafunikira m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku zidzathetsedwa. Tidzapeza chimwemwe m’zochita zathu ndi ena ndipo sitidzavutitsidwa ndi funso lakuti: “Kodi ndi mlandu wa yani?”
[Zithunzi patsamba 28]
Makolo angathandize kwambiri ana awo kupita patsogolo mwauzimu