Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 10/8 tsamba 22-24
  • Lamulirani Moyo Wanu Tsopano!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lamulirani Moyo Wanu Tsopano!
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Lingaliro la Baibulo Nlotani?
  • Thandizo Labwino Koposa Limene Lilipo
  • “Mawu a Mulungu Ngamoyo Ndipo Amapereka Mphamvu”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Muli ndi Vuto Ndinu Kapena Chibadwa Chanu?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
    Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
  • Mmene Mungasinthire Amene Muli
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 10/8 tsamba 22-24

Lamulirani Moyo Wanu Tsopano!

KUFUFUZA kwa sayansi pa khalidwe ndi kusonkhezereka kwa munthu kwatipindulitsa m’njira zambiri. Mwinamwake kwatithandiza kulimbana ndi matenda ena ake mwa kutiphunzitsa zambiri ponena za iwo. Panthaŵi imodzimodziyo, nkwanzeru kukhala wochenjera ponena za malingaliro ochititsa chidwi kwambiri, makamaka aja amene amaoneka kuti akutsutsa mapulinsipulo odziŵika kwambiri.

Pankhani ya majini ndi khalidwe, pali mafunso akuti: Kodi tiyenera kukana zimene tachita ndi kusavomera mlandu uliwonse pa zochita zathu? Kodi tiyenera kukana kapena ngakhale kupatsa winawake kapena chinthu china mlandu wa cholakwa chilichonse, motero tikumagwirizana ndi anthu omawonjezereka mu mbadwo uno wa “sindine”? Kutalitali. Anthu ochuluka mwaufulu amalandira thamo pa chipambano chilichonse m’moyo, chotero kodi amalekeranji kuvomerezanso mwaufulu mlandu wa zolakwa zawo?

Chotero, tingafunse kuti, Kodi Mawu a Mulungu, Baibulo Loyera, amanenanji ponena za amene kapena chimene chimalamulira moyo wathu lerolino?

Kodi Lingaliro la Baibulo Nlotani?

Choyamba chimene tiyenera kuzindikira ndicho chakuti tonsefe timabadwira mu uchimo umene tinalandira kwa makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava. (Salmo 51:5) Ndiponso, tikukhala m’nthaŵi yapadera, yotchedwa “masiku otsiriza,” pamene anthu akuyang’anizana ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa zovuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1, NW) Zimenezi zikutanthauza kuti, kunena mwachisawawa, timavutika kwambiri kuti tilamulire bwino moyo wathu kuposa mmene makolo athu akale anachitira.

Ngakhale zili choncho, anthu onse ali ndi ufulu wa kudzisankhira, ndipo angapange zosankha zawo zaumwini. Pa zimenezo iwo amalamulira moyo wawo. Zimenezi zakhala choncho chiyambire nthaŵi zakale ndipo zingaonedwe m’mawu a Yoswa kwa mtundu wa Israyeli kuti: “Mudzisankhire lero amene mudzamtumikira.”—Yoswa 24:15.

Baibulo limanena kuti Satana Mdyerekezi waponyedwa kuchokera kumwamba ndipo tsopano, kuposa ndi kale lonse, akusonkhezera mwamphamvu fuko lonse la anthu kuti achite zoipa. Limatiuzanso kuti ngakhale m’masiku a mtumwi Yohane, dziko lonse linali kugona m’mphamvu ya woipayo. (1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9, 12) Komabe, monga momwe Mulungu Wamphamvuyonse samalamulira zochita zathu zonse kapena kuikiratu mapeto athu odziŵa iye yekha, sitiyenera kuika mwachindunji pa Satana mlandu wa cholakwa kapena kulephera kwathu konse. Choonadi cholinganiza cha m’Malemba ndicho chakuti “munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo.” (Yakobo 1:14, 15) Mtumwi Paulo analemba mawuwa ouziridwa kuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”—Agalatiya 6:7.

Chotero Yehova Mulungu amatiŵerengera aliyense payekha mlandu wa zochita zathu. Tiyenera kusamala kuti sitikuyesa kukana mlandu chifukwa cha mkhalidwe wathu wa majini ndi choloŵa cha kupanda ungwiro. Mulungu anaŵerengera mlandu anthu achiwawa ndi amathanyula a ku Sodomu ndi Gomora wakale pa zochita zawo zoipa. Mwachionekere, sanaone okhala mmenemo monga zolengedwa zatsoka zochititsa chifundo zimene chifukwa cha kulakwika kolinganizidwiratu m’majini sizikanapeŵa kukhala zoipa. Mofananamo, anthu omwe ankakhala m’masiku a Nowa anali ndi zisonkhezero zambiri zoipa zowazinga; komabe, anafunikira kupanga chosankha, chosankha chaumwini, ngati anafuna kupulumuka Chigumula chimene chinali pafupi kuchitika. Oŵerengeka anapanga chosankha chabwino. Ambiri sanachite motero.

Mneneri wachihebri Ezekieli akutsimikizira kuti kudzilamulira nkofunika ngati tikufuna kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu: “Ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako.”—Ezekieli 3:19.

Thandizo Labwino Koposa Limene Lilipo

Komabe, tonsefe timafuna thandizo kuti tizidzilamulira m’moyo wathu wa masiku onse, ndipo kwa ambiri a ife, zimenezi nzovuta kwambiri. Koma tisataye mtima. Ngakhale kuti zikhoterero zathu zauchimo zacholoŵa sizili zovomerezeka kwa Mulungu, ngati tikufuna kukonza khalidwe lathu, iye adzatipatsa thandizo labwino koposa limene lilipo—mzimu wake woyera ndi choonadi chake chouziridwa. Mosasamala kanthu za mkhalidwe uliwonse wa majini umene tingakhale nawo ndi zisonkhezero zakunja zilizonse zimene zingatikhudze, ‘tingavule munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndi kudziveka watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye.’—Akolose 3:9, 10.

Akristu ambiri mumpingo wa ku Korinto anasintha khalidwe lawo kwambiri. Mbiri youziridwa imatiuza kuti: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa mzimu wa Mulungu wathu.”—1 Akorinto 6:9-11.

Chotero ngati tikulimbana ndi zikhoterero zathu, tisazigonjere. Akristu ambiri amakono atsimikizira kuti pokhala ndi thandizo la Yehova, anatha ‘kukhala osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wawo ndi kuzindikira chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa ndi changwiro.’ Iwo amadyetsa malingaliro awo zinthu zilizonse zoona, zolungama, zoyera, zokongola, zokoma mtima, zachitamando; ndipo ‘amazilingirira izi.’ Iwo amadya chakudya chotafuna chauzimu ndipo mwa kuchigwiritsira ntchito anazoloŵeretsa zizindikiro zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.—Aroma 12:2; Afilipi 4:8; Ahebri 5:14.

Nkolimbikitsa kudziŵa za kulimbikira kwawo, kulephera kwawo nthaŵi zina, ndi chipambano chawo m’kupita kwa nthaŵi mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Mulungu akutitsimikizira kuti kusintha khalidwe lathu kaŵirikaŵiri kumaloŵetsamo mtima ndi chikhumbo chake pamene akuti: “Pakuti nzeru idzalowa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa.”—Miyambo 2:10-12.

Chotero, ngati mukufuna kuika moyo wosatha kukhala chonulirapo chanu—moyo wopanda mavuto a dziko loipa ndipo wopanda zikhoterero zofooketsa—‘yesetsani’ kulamulira moyo wanu tsopano ndipo nzeru yakumwamba ikutsogolereni. (Luka 13:24) Gwiritsirani ntchito thandizo la mzimu woyera wa Yehova kotero kuti mubale chipatso cha kudziletsa. Kugwirizanitsa moyo wanu ndi malamulo a Mulungu kukhale chikhumbo cha mtima wanu, ndipo mverani uphungu wakuti: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Kugwira “moyo weniweniwo” m’dziko latsopano la Mulungu—limene Yehova Mulungu adzawongoleramo kupereŵera konse kwa majini pa maziko a chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu Kristu—nkofunika kuyesayesa konse kumene mukuchita kuti mulamulire moyo wanu m’dziko lino!—1 Timoteo 6:19; Yohane 3:16.

[Chithunzi patsamba 23]

Kuphunzira Baibulo kungatipatse nyonga yogonjetsera zofooka zovuta kwambiri

[Chithunzi patsamba 23]

Kuphunzira Baibulo kungatithandize kumamatiradi ku miyezo ya Mulungu ya makhalidwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena