Mmene Mungasinthire Amene Muli
KODI nchiyani chimene chakhala chikusoŵeka m’njira zokhazikitsira khalidwe ndi zosinthira zomwe zafotokozedwazo? Zikhumbo zake za munthu ndi kugwiritsira ntchito kutsimikiza mtima kwake kwamphamvu! Kugwiritsira ntchito ufulu wodzisankhira mwa chosankha chake chodziŵidwa bwino. Mwachidule, ulamuliro waumwini ukusoŵeka!
Akatswiri ochiritsa khalidwe apeza kuti iwo ali ndi mwaŵi wokulirapo wakupeza zipambano zokhalitsa ngati munthu wothandizidwayo ali ndi mphamvu yakupanga chosankha chomalizira pokhazikitsa zonulirapo zake zakhalidwe. Vance Packard analemba m’bukhu lake lakuti The People Shapers kuti: “Mwachiwonekere atapatsidwa uphungu waung’ono, munthu wochenjera aliyense angakhale wosintha khalidwe la mwini yekha.” Kumeneku kumatchedwa kudziyendetsa. M’mawu ena, pamene kudzilamulira kumagwiritsiridwa ntchito, pamawonedwa kuwongokera kwakukulu.
Akristu ali ndi mwaŵi pamene kudzilamulira kukhala kofunika, popeza kuti iwo aphunzira kukugwiritsira ntchito monga chimodzi cha zipatso zisanu ndi zinayi za mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Ichi chikutanthauza kuti mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu Wamphamvuyonse ingachititsidwe kusonkhezera kusintha kwa khalidwe lanu ndi kukuthandizani kupambana.
Chotero, kodi mufuna kuchitanji ponena za khalidwe lanu? Kodi mumafunadi kusintha? Ngati ndichoncho, kuleka kukhala wotani? Ndiyeno nkukhala wotani? Ndipo chifukwa ninji? Kodi mungaudalire ulamuliro wanu? Kodi nkuti kumene mungapeze chithandizo chimene chimapereka mapindu okhaokha?
Tiyeni tiyang’ane pa zina za njira ndi mbali zofunika kaamba ka kusintha mikhalidwe.
Sitepe 1: Pezani Amene Inuyo Mulidi
Inuyo ndinu milimo yomangira amene mufuna kukhala. Inu watsopano ayenera kumangidwa mwakusintha inu wakale. Chotero muyenera kudzidziŵa molongosoka. Kodi mungazilongosole mbali za khalidwe lanu zimene mungakonde kusintha?
Popeza kuti nkovuta kupenda khalidwe lanulanu, mufunikira kusanthula muyezo wolemekezedwa ndi wodalirika. Baibulo Lopatulika likuvomerezedwa kukhala muyezo umenewo. Gwiritsirani ntchito Baibulo, ndipo mudzapeza lingaliro la inu mwini limene mwinamwake simunakhalepo nalo. Mwinamwake simungakonde zimene mukupeza, koma mungakhale wotsimikiza kuti nchithunzi cholondola.
Baibulo lafananizidwa ndi kalirole, ndipo anthu amalimbikitsidwa kupenyamo. ‘Ngati munthu ali wakumva mawu, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole; pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, naiŵala pompaja anali wotani. Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiŵala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.’ (Yakobo 1:23-25) Baibulo, litamvetsetsedwa ndi kugwiritsiridwa ntchito moyenera, liri ndi mphamvu yakuya, yopenda ndi yosonkhezera imene sidzangokusonyezani amene inuyo muli monga munthu koma ngakhale kuvumbula zolinga zanu ndi kaimidwe ka maganizo. Chifukwa chake, Paulo analemba kuti: ‘Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.’ Mawu a Mulungu amaposa ngakhale pamenepo mwakupereka chitsogozo chonena za chimene chiridi chabwino ndi choipa.—Ahebri 4:12; 5:14.
Baibulo litha kukuchitirani zinthu zonsezi chifukwa chakuti ilo ndilo Mawu a Yehova, Mulungu wanzeru weniweniyo. Mogwirizana ndi Salmo 139, Mulungu amakufufuzani ndikupanga masanthulidwe olongosoka a amene inu muli. Monga momwe vesi 1 limanenera kuti: ‘Munandisanthula, Yehova, nimundidziŵa.’ Mulungu wakhala akukuyang’anirani kuyambira pamene amayi anu anatenga pathupi panu. Iye amakudziŵani kotheratu. Iye wachititsa kulembedwa kwa ndemanga za moyo wa anthu m’Baibulo m’mitundu yonse yothekera. Mudzadzipeza mukufotokozedwa kwinakwake m’masamba ake, kaya moyanjidwa kapena motsutsidwa.
Chotero, mungapeze amene inuyo mulidi—ngati mumafuna kutero.
Sitepe 2: Sankhani Amene Mufuna Kukhala
Ngati mudzasintha, tsimikizirani kuti kusinthako kuli koyenerera. Tsimikizirani kuti ndikumene mumakufuna ndikuti nkwabwinopo kuposa amene muli tsopano. Kodi nzonulirapo za khalidwe zowongoleredwa zotani zimene muyenera kukhazikitsa? Kodi nkuti kumene mungapeze chilangizo cholondola cha mikhalidwe imene mumakhumba? Kachiŵirinso, Baibulo likuvomerezedwa kaamba ka chimenechi.
Baibulo limakufulumizani kusintha kukhala wabwinopo, kuvala “umunthu watsopano.” Paulo analangiza kuti: “Muyenera kuvula umunthu wakale umene umagwirizana ndi njira yanu yakale ya khalidwe ndi umene uli kumaipitsidwa mogwirizana ndi zikhumbo zake zonyenga; koma . . . muyenera kupangidwa kukhala atsopano mwa mphwamvu yosonkhezera maganizo anu, ndipo muyenera kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.” (Aefeso 4:22-24, NW) Baibulo limakusonyezani zimene makhalidwe abwino ameneŵa ali. Kodi mukulikumbukira dziko langwiro lolongosoledwa poyambapo? Ngati mukufuna kukhala mbali ya dziko limenelo, muyenera kukuwona kufunika kwa kukulitsa mikhalidwe yolongosoledwa pa Akolose 3:12-17, mikhalidwe monga chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima, kukhululukira, chikondi, mtendere, ndi kuyamikira.
Chotero pambuyo pakufufuza Baibulo lanu, khazikitsani zonulirapo zanu. Zilembeni. Ikani chonulirapo chimodzi ndi chimodzi patsogolo. Chitanipo kanthu pa chimenecho!
Sitepe 3: Funani Zitsanzo Zoyenera
Mbali yaikulu ya khalidwe lanu inakhazikitsidwa mwa kutengera kwanu anthu ena—mabwenzi, anzanu, makolo, aphunzitsi apasukulu.
Pamenepo, pambuyo posankha zonulirapo za khalidwe zimene mumazikhumba, bwanji osafunafuna winawake yemwe amadzisungira mwa njira imene mukhumba kutengera? Ndiyeno funani chithandizo cha munthuyo. Mwambi wa m’Baibulo umanena mwanzeru kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.”—Miyambo 13:20.
Baibulo liri ndi nkhani ya moyo wa chitsanzo chabwino koposa kwa tonsefe, Yesu Kristu mwiniyo. Ŵerengani mmene anachitira pansi pa mikhalidwe yonse, mayendedwe ake amakhalidwe, luntha lake ndi nzeru, ulemu wake, kulingalira kwake ndi kukoma mtima kodabwitsa ndi nkhaŵa kaamba ka anthu anzake. Iye amamveka wotonthoza motani nanga pamene akunena kuti: ‘Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka’!—Mateyu 11:28-30.
Mamiliyoni a anthu m’maiko onse atembenukira kale kwa Kristu Yesu monga chitsanzo chawo ndi kuchita zomwe angathe kutsatira mapazi ake, monga momwe iyenso, anayendera m’njira yolangizidwa ndi Atate wake wakumwamba, Yehova Mulungu. Mamiliyoni ameneŵa, pokhala anakhuta khalidwe loipa la dziko mwachisawawa lerolino, atembenukira ku mpingo wakumaloko wa Mboni za Yehova kaamba ka chithandizo ndi malangizo ndipo sanagwiritsidwe mwala. Pa Nyumba zawo Zaufumu, zitsanzo zabwino koposa zonga Kristu nzambiri, ndipo chithandizo chochuluka chaperekedwa kaamba ka ofuna kusintha khalidwe lawo kukhala anthu abwinopo. Ndithudi, Mboni ziri ndi zifooko zofala kwa anthu onse opanda ungwiro; koma izo zirinso ndi mphamvu yabwino yauzimu yosonkhezera maganizo.—Aefeso 4:23.
Sitepe 4: Pezani Nyonga Imene Muifunikira Kuti Mupambane
Kudziŵa kuti chithandizo chiripo kungakhale kotonthoza kwa amene akukhumba kusintha njira zawo. “Umunthu watsopano” ukulongosoledwa kukhala ‘ukulengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.’ (Aefeso 4:24, NW) Ichi chimatsimikizira kuti chithandizo chopambana chaumunthu chiripo chochokera kwa Mulungu mwiniyo kaamba ka ochikhumba. Kodi ndimotani mmene mungapezere chithandizo cha Yehova Mulungu?
Chimodzi cha zithandizo zofunika koposa ndicho pemphero laumwini. Pemphero limatheketsa kukambirana kofunika koposa ndi Magwero a mphamvu yoyenera kuti musinthe njira zanu. Pemphero limakulolani kulankhula mwaufulu ndi momasuka panthaŵi iriyonse, ngakhale mkati mwa mavuto. Njira yoteroyo yomkira kwa Mulungu weniweni ndi wosamala imapambana kutalitali njira yofunira chithandizo chaumunthu ndipo imagwira ntchito mofulumira. Chifukwa chake, mtumwi Yohane akulemba kuti: ‘Uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.’ (1 Yohane 5:14) Ndipo mawu a mneneri Yesaya amatilimbikitsa kuti: ‘Funani Yehova popezeka iye, itanani iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti iye adzakhululukira koposa.’—Yesaya 55:6, 7.
Phunziro Labaibulo limaperekanso nyonga, kukupatsani mpumulo, kukukhozetsani kulingaliranso tsiku ndi tsiku pa zonulirapo zanu. Baibulo limagaŵira kulimbika kwabwino pamene mukukalamira chandamale cha khalidwe chimene mwasankha. Ndiponso, chimatsitsimula lingaliro la kunyansidwa ndi njira zanu zakale. Kuphunzira chidziŵitso cha Baibulo tsiku ndi tsiku ndi zamkati mwake kudzatumikiranso kusoŵetsa malo a mabodza omwe angaloŵerere kuchokera ku nkhani zoulutsidwa za dziko ndi madongosolo ake a zamaphunziro.
Misonkhano Yachikristu pa Nyumba Yaufumu yakumaloko ya Mboni za Yehova simagaŵira maphunziro pa miyezo ya Baibulo yokha komanso imapereka chichirikizo ndi kufulumizana kukhala ndi khalidwe lowongoleredwa. Chichirikizo chimenechi choperekedwa kupyolera mumpingo chathandiza ambiri kukhala achipambano m’kusintha khalidwe. Bwanji osakambitsirana ponena za chithandizo choterocho ndi munthu amene munapezako magazini ano?
Sitepe 5: Lakani Kubwevuka
Ambiri ayesa kuwongolera njira zawo koma alefulidwa ndi kubwevuka kumene kungakhale kosapeŵeka. Chotsatirapo chakhala chakuti ena alekeratu. Kaŵirikaŵiri oterowo amaganiza kuti ngati chimene anachilingalira kukhala chiyembekezo chawo chokha chalephera tsopano, palibenso chiyembekezo chirichonse. Pamenepo iwo amadzipereka ku ziyambukiro za dziko. Kaŵirikaŵiri amaipirapo kuposa pamene anayesa kusintha.
Pitirizanibe kumadzikumbutsa kuti njira yakale iriyonse yosafunidwa iyenera kuithaŵa. Mtumwi Paulo anatchula khalidwe lake lakale ndi njira yamoyo kukhala zapadzala, kapena zinyatsi. (Afilipi 3:8) Chotero ngati inuyo, popanga kusintha, mupunthwitsidwa ndi chopinga kapena kubwevuka, dzukaninso, ndipo pitirizanibe kumka kutsogolo. Pitirizanibe! Menyanibe nkhondoyo! Idzakhala yoyenerera!
Kumbukirani, zambiri za njira zanu ndi makhalidwe zinaikidwa pa inu ndi zisonkhezero zakunja zosakhoza kulamuliridwa ndi chosankha chanu kapena mphamvu zanu panthaŵiyo. Zisonkhezero zimenezi zikugwirabe ntchito. Kodi mudzazilola kukupanikizani m’chikombole chake? Ayi? Pamenepo musaleke konse!
Anthu mamiliyoni a miyambo yosiyanasiyana—ngakhale apandu ndi anthu omwerekera m’makhalidwe achisembwere—asintha mwachipambano khalidwe lawo. Iwo asunga miyezo yawo yowongoleredwa kufikira lero, ena kwa zaka makumi ambiri, akumamatira ku njira zawo zabwinopo ndi umphumphu wodzifunira wokhumbirika. Koma iwo amayamika Mulungu kaamba ka nyonga ndi chisonkhezero chowatheketsa kutero. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera kuti: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:13.
Iwo akupambana nkhondo yakuchita chimene chiri chabwino. Nanunso mungasinthe ngati mufunadi kutero, ndipo mutha kusangalala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu.—Salmo 37:29; 2 Petro 3:13.
[Chithunzi patsamba 7]
Sitepe 1: Pezani amene inuyo mulidi
[Chithunzi patsamba 8]
Sitepe 2: Sankhani amene mufuna kukhala
[Chithunzi patsamba 8]
Sitepe 3: Funani zitsanzo zoyenera
[Chithunzi patsamba 9]
Sitepe 4: Pezani nyonga imene muifunikira kuti mupambane
[Chithunzi patsamba 9]
Sitepe 5: Lakani kubwevuka
[Chithunzi patsamba 10]
Amene amasintha angalowenso m’dziko lapansi losinthidwa