Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 7/8 tsamba 3-4
  • Kudziŵa Amene Inuyo Mulidi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudziŵa Amene Inuyo Mulidi
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Majini Amachita Mbali Yaikulu
  • Bwanji Ponena za Zakudya, Utenda, ndi Malo Okhala?
  • Kodi Chipembedzo Chimachita Mbali Yanji?
  • Mmene Mungasinthire Amene Muli
    Galamukani!—1991
  • Kodi Nkusinthiranji?
    Galamukani!—1991
  • Kulera Mwana Wovuta Monga Kholo
    Galamukani!—1994
  • Lamulirani Moyo Wanu Tsopano!
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 7/8 tsamba 3-4

Kudziŵa Amene Inuyo Mulidi

MUTAYANG’ANA m’kalirole, kodi mumawonanji? Chithunzi chanu chenichenicho. Koma kodi chimenecho chimakuuzani amene inuyo mulidi? Kodi icho chimakuuzani mmene ena amakuwonerani monga munthu? Kodi mumadziŵadi amene muli? Kodi mumadziŵa mmene khalidwe lanu linayambira? Inde, kodi ndimotani mmene umunthu wanu, ndiko kuti inuyo, unayambira?

Mutaima kuti mupende mbali zonse zimene zinaumba umunthu wanu, mungawone kuti ziyambukiro zambiri zaperekedwa pa inu—kaya ndi anthu ena kapena ndi zinthu zina. Mkati mwa zaka zathu zoyambirira zakukula, ambirife tinalibe zambiri zochita kuti tikhazikitse zizoloŵezi ndi njira zathuzathu. Chotero tiyeni tiwone zina za ziyambukiro zoumba umunthu zimenezi zomwe zinaperekedwa pa inu—zina za izo zochitika kale kwambiri inuyo musanakhale ndi mwaŵi wakuchitapo kanthu pa khalidwe lanu.

Majini Amachita Mbali Yaikulu

Kodi majini akuyambukirani mokulira chotani? Magwero a DNA, opezeka m’machromosome omwe amapatsira mikhalidwe yachibadwa, ali ndi mpangidwe ndi malangizo oikidwa mwadongosolo a munthu aliyense. Chotero kodi khalidwe lanu panokha limayambukiridwa mokulira chotani mwa zamajini? Kukuwoneka kuti padakali vuto kufotokoza kugwirizana kulikonse kotsimikizirika pakati pa majini ndi umunthu. Komabe, pali mfundo zina zomwe zimawonekera kukhala zowona. Mwachitsanzo, ingapo ya mikhalidwe yanu yachibadwa yakuthupi imasonkhezera mwachindunji khalidwe lanu. Chifukwa chake, anthu ena amakhala ndi makhalidwe achete, pamene ena ngomasuka mwachibadwa.

Mkazi wapathupi akhoza kupindulitsa kapena kuvulaza mwana wake wosabadwa mwa machitidwe ake, maganizo, ndi malingaliro. Kodi pamene munali m’mimba mwa amanu, munapatsidwa mtendere wochuluka motani kapena kuvutitsidwa kotani? Kodi munaphunzira zochuluka motani mwakumvera mawu a makolo anu, nyimbo zimene anamvetsera? Kodi munayambukiridwa motani ndi chakudya chimene amayi anu anadya? Pamene iwo anamwa moŵa kapena mankhwala oledzeretsa, iwo anayambukiridwa motani? Podzafika nthaŵi imene munabadwa, zikhoterero zanu zambiri zinakhazikitsidwa kale ndipo mwina nzovuta kuzisintha tsopano.

Bwanji Ponena za Zakudya, Utenda, ndi Malo Okhala?

Pamene munkakula kuubwana, zinthu zina m’chakudya chanu zingakhale zinali ndi chiyambukiro pa khalidwe lanu. Zinthu zozuna, zosintha mtundu zongopanga, ndi zokoleretsa—zonsezo zingakhale ndi chiyambukiro chosawoneka pa khalidwe lanu. Kukangalika kopambanitsa, kukwinjika kowonjezereka, kukwiya, kupweteka kwa mitsempha, ndi machitidwe opambanitsa ndi osalamulirika zangokhala zina za zotulukapo. Kuipitsa kochititsidwa ndi utsi wa magalimoto, zoipa zotaidwa m’maindasitale, ndi zapaizoni zina m’malo okhala zimaumbanso khalidwe. Kapena inuyo, monga munthu payekha, mungakhale ndi utenda umene umakuyambukirani mowopsa koma umene sungakhale ndi chiyambukiro kwa aja okhala nanu pafupi.

Kuwonjezera pa ziyambukiro zimenezi, khalidwe la makolo anu, zimene amakonda ndi zimene samakonda limodzinso ndi malingaliro awo atsankho amene mwina mwakhala nawo kuyambira kuubwana wanu, zakhala ndi chiyambukiro pa inu ndipo zaumba umunthu wanu kuukulu winawake. Chotulukapo nchakuti njira zanu zambiri ndi lingaliro lanu lachisawawa la moyo zangokhala chithunzi cha zawo. Mumayedzamira pa kukwiya ndi zinthu zimene zimawakwiitsa. Mumakhoterera kulekerera zinthu zimene amalekerera. Ndipo simumawona kuti mumatengera khalidwe lawo kufikira pamene wina amakuuzani kuti mumachita mofananadi ndi abambo anu kapena amayi anu. Mkhalidwe wawo wazachuma ndi wamayanjano umakuyambukiraninso, monga momwe malo kumene mumakhala ndi malo akusukulu anachitira. Mabwenzi anu ndi anzanu akhalanso ndi chiyambukiro chachikulu pa inu. Mwinamwake ngozi yoipa (kwa inu kapena kwa bwenzi lapamtima), tsoka lakwanuko, kapena ngakhale zochitika zadziko zovutitsa maganizo zakuyambukirani. Kapena zingakhale kuti tsoka linalake, monga ngati chisudzulo kapena matenda aakulu, anasiya chipsera pa umunthu wanu.

Kodi inuyo, mwakulingalira, mukhoza kudziŵa chirichonse cha ziyambukiro zoterozo?

Kodi Chipembedzo Chimachita Mbali Yanji?

Mogwirizana ndi zophunziridwa, chipembedzo chiyenera kukuthandizani kukhala munthu wabwinopo, kuwongolera mkhalidwe wanu wakudzisungira, miyezo, ndi njira ya moyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Kodi ndi ingati ya miyezo yanu yamakhalidwe ndi machitidwe imene yayambukiridwa ndi chipembedzo? Pamene kuli kwakuti chipembedzo chiyenera kuchita monga choletsa khalidwe loipa, lakuchita upandu, anthu ambiri amayambukiridwa ndi chipembedzo mwanjira yosiyana. Iwo amawona chinyengo chachikulu ndi chigogomezo choikidwa pa zinthu zakuthupi mmalo mwa makhalidwe abwino auzimu m’matchalitchi ndipo amakwiya nazo. Iwo angaleke kupembedza, kufwambidwa mkhalidwe wauzimu ndi chiyembekezo.

Inu mungathe kuganiza za ziyambukiro zina zakunja zimene zimaumba khalidwe. Tangotherani mphindi zoŵerengeka mukulingalira pa chirichonse cha zinthu zimene zingakhale zakuyambukirani kufikira tsopano. Kodi mungandandalitse zina za izo? Sikokhweka kuganiza mopanda tsankhu ndi kulingalira mwa njirayi, koma nkoyenerera kuyesayesa ndipo kungakhale kothandiza kwa inuyo. Motani?

Eya, ngati mungadziŵe chisonkhezero chakutichakuti kapena chifukwa chochititsa chizoloŵezi choipa m’khalidwe lanu, ngati mungachiike pachokha, mudzakhala m’malo abwinopo akuchilamulira, mwinamwake ngakhale kuchisintha. Ngati mungathe kuchilamulira, kapena ngakhale kuchichotsa chisonkhezero chosafunidwacho, mukhoza kukhala munthu wosiyana, ndi wakhalidwe labwinopo kulinga kwa ena.

Ndithudi, chimenecho nchitokoso. Koma popeza kuti zisonkhezero zambiri zaperekedwa pa khalidwe lanu kuchokera kwa anthu ena kapena mikhalidwe imene simukatha kuilamulira, bwanji osayamba kuchitapo kanthu ponena za mkhalidwewo kaamba ka ubwino wanu? Ngati zikafuna kuwongokera, bwanji osasintha amene muli?

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Machitidwe ndi malingaliro a mkazi wapathupi angayambukire mwana wosabadwayo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena