Kodi Nkusinthiranji?
NDIOCHEPA aife amene timakonda kuvomera kuti tiri ndi zifooko zazikulu. Ngowona motani nanga mawu a wolemba ndakatulo wa ku Scotland Robert Burns akuti: “Ha, ngatitu panali mphamvu yotipatsa luso lakudziwona tokha monga momwe ena amatiwonera!” Inde, kumatikhalira kosavuta kupeza zolakwa mwa ena ndipo tingakhale ofulumira kupereka uphungu wosonyeza mmene angawongokere. Koma lingaliro lirilonse limene ifeyo timafunikira kuti tisinthe khalidwe lathu lingatikwiitse. Kodi likakukwiitsani?
Tiyeni tiime kwakamphindi ndi kuyerekezera dziko langwiro m’mene aliyense ngwaudongo, wathanzi, wachimwemwe, ndi wowona mtima; m’mene ngakhale okhala ndi ulamuliro ngachifundo ndi olingalira, okondweretsedwa kuchitira ena zabwino; m’mene mulibe umbombo, ndipo palibe amene amadyera mnzake masuku pamutu; m’mene ana ngomvera makolo okoma mtima ndi osamala; m’mene mulibe kunyanyuka ndi mkwiyo—mulibe chiwawa, mulibe upandu, mulibe chisembwere; m’mene anthu ngokhulupirirana ndipo ngokoma mtima mwachibadwa; m’mene moyo ungasangalalidwe ndi lingaliro la chisungiko ndi mkhalidwe wabwino.
Kodi mukhoza kudziwona kukhala woyenerera dziko longa limenelo, ngati dziko loyerekezera lamtendere loterolo lingakhalekodi? Eya, mbiri yabwino yochokera m’Baibulo njakuti dziko loterolo likubwera pompano padziko lapansi posachedwapa. Tsopano funso lofunika nlakuti: Kodi muli ndi mikhalidwe yakudzisungira iriyonse imene ikakuletsani kuyenerera m’chitaganya chamtendere wokhutiritsa chimenecho? Kodi mukuganiza kuti nkoyenerera kuyesayesa kovuta motani, kuti muyeneretsedwe kaamba ka moyo m’paradaiso woteroyo?—Yesaya 65:17-25; 2 Petro 3:13.
Ngakhale tsopanoli, dziko latsopano loterolo lisanadze, kodi moyo wanu ungawongokere ngati mukachitapo kanthu ponena za khalidwe lanu ndi maganizo? Ngati nditero, bwanji osasintha? Nkotheka kuchita zimenezo. Kumbukirani, ziyambukiro zakutizakuti zinalinganiza ndi kuumba khalidwe lanu poyamba, choncho mwakukhala ndi kudzilamulira kwakukulu ndi chikondwerero, nkotheka kwa inu kusinthanso khalidwe lanu ngakhale tsopano.
Komabe, mungatsutsebe kuti: ‘Koma kodi ndingasinthedi? Ndinayesapo kale, nthaŵi zambiri, ndipo ndinalephera. Ine ndiri choncho basi, ndipo palibe chimene ndingachite ponena za icho!’
Talingalirani Paulo, mtumwi wa Yesu Kristu. (Aroma 7:18-21) Paulo anasintha umunthu wachiwawa, wotsutsa Akristu wodzilungamitsa, ndipo anakhala Mkristu iyemwini. Iye anasintha chifukwa chakuti anafunadi kutero. Sanaleke chifukwa cha kulefulidwa kapena zisonkhezero zamajini. Iye sanakhulupirire kuti umunthu wake wakale unali wosakhoza kusintha. Zinalira kuti iye achite kuyesayesa kwamphamvu. Koma analandira chithandizo chochuluka.—Agalatiya 1:13-16.
Kodi chithandizo chimenechi chinachokera kuti?