Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 10/8 tsamba 6-8
  • Kuyesayesa Kuthetsa Upandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyesayesa Kuthetsa Upandu
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Lingaliro Limeneli ndi Lonyanyitsa?
  • Maboma Akuyesa
  • Kutaya Chidaliro
  • Kulimbana ndi Upandu Kukulephereka
    Galamukani!—1998
  • Kodi Apolisi Ali ndi Tsogolo Lotani?
    Galamukani!—2002
  • Nchifukwa Ninji Pali Upandu Wochulukira Chotero?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Lili Kuti Dziko Lopanda Upandu?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 10/8 tsamba 6-8

Kuyesayesa Kuthetsa Upandu

“ACHICHEPERE Akuti Kusukidwa Ndiko Chochititsa Upandu wa Ana Chachikulu,” unatero mutu wa nkhani m’nyuzipepala yotchuka yachibritishi. “Ndewu Panyumba Ipatsidwa Mlandu wa Kuwonjezereka kwa Upandu,” inateronso ina. Ndipo yachitatu inati: “Zomwerekeretsa ‘Zisonkhezera Maupandu Zikwi Zambiri.’” Magaziniwo Philippine Panorama anayerekezera kuti 75 peresenti ya maupandu onse achiwawa ku Manila anachitidwa ndi ogwiritsira ntchito anamgoneka.

Zinthu zinanso zingakhale zikumasonkhezera khalidwe la upandu. “Umphaŵi woyendera limodzi ndi kulemera kwambiri” ndiwo chimodzi cha zinthuzo chimene mkulu wa apolisi wa ku Nigeria anatchula. Chisonkhezero cha mabwenzi ndi kusoŵa kwa ntchito, kusoŵa kwa malamulo olimba, kunyonyotsoka kwa makhalidwe m’mabanja ambiri, kusalemekeza olamulira ndi malamulo, ndi chiwawa chopambanitsa m’mafilimu ndi mavidiyo nazonso zikutchulidwa.

Chinanso nchakuti anthu ambiri samakhulupiriranso kuti upandu sumaphula kanthu. Katswiri wa kakhalidwe ka anthu pa Bologna University ku Italy ananena kuti pazaka zambiri, “chiŵerengero cha kuba kochitidwa lipoti ndi chiŵerengero cha anthu opezedwa ndi mlanduwo zakhala zosiyana kwambiri.” Iye anati “chiŵerengero cha opezedwa ndi mlandu poyerekezera ndi chiŵerengero chonse cha kuba kochitidwa lipoti chatsika kuchoka pa 50 kufika pa 0.7 peresenti.”

Mawu a The New Encyclopædia Britannica ngomvetsa chisoni koma ali oona akuti: “Upandu womawonjezereka ukuoneka kukhala mbali ya maiko onse amakono otukuka, ndipo malamulo amene apangidwa kapena zilango sizinganenedwe kuti zathandiza kwambiri pa vutolo. . . . M’maiko amakono otsungula, mmene chitukuko cha chuma ndi chipambano cha munthu mwini zili makhalidwe aakulu, palibe chifukwa chokhulupirira kuti ziŵerengero za upandu sizidzapitiriza kuwonjezereka.”

Kodi Lingaliro Limeneli ndi Lonyanyitsa?

Kodi mkhalidwewo ulidi woipa kwambiri? Kodi madera ena samasimba za kutsika kwa upandu? Zoona, ena amatero, koma ziŵerengero zingakhale zosokeretsa. Mwachitsanzo, zinamveka kuti upandu ku Philippines unatsika ndi 20 peresenti ataletsa mfuti. Koma Asiaweek inafotokoza kuti mkulu wina wa boma akhulupirira kuti mbala za galimoto ndi mbala za m’mabanki zinali zitasiya kuba galimoto kapena m’mabanki ndipo zinali “zitayamba uchifwamba.” Kuboola mabanki angapo ndi kuba galimoto zingapo kunatsitsa chiwonkhetso cha milandu ya upandu, koma kutsika kumeneku kunakhala kopanda tanthauzo chifukwa cha kuwonjezereka kwa uchifwamba koŵirikiza kanayi!

Posimba za Hungary, magazini akuti HVG analemba kuti: “Poyerekezera ndi theka loyamba la 1993, ziŵerengero za upandu zatsika ndi 6.2 peresenti. Zimene apolisi anaiŵala kutchula nzakuti kutsikako . . . makamaka kuli chifukwa cha kusintha kwa kayendetsedwe ka zinthu.” Mtengo umene kale analembetserapo mlandu wa kuba, chinyengo, kapena kuwononga katundu unakwezedwa ndi 250 peresenti. Chotero upandu wokhudza katundu wa mtengo wosafika pamenepo sumalembedwanso. Popeza kuti upandu wokhudza katundu umapanga chigawo chimodzi mwa zinayi za upandu wonse m’dzikolo, kutsika kumeneko sikunali kwenikweni.

Inde kupeza ziŵerengero zolondola za upandu nkovuta. Chochititsa china nchakuti maupandu ambiri—mwinamwake kufika pa 90 peresenti m’magulu ena—samachitidwa lipoti. Koma kutsutsana ngati upandu wachepa kapena wawonjezereka nkosafunikira kwenikweni. Anthu amafuna kuti upandu uthetsedwe, osati kungochepetsedwa.

Maboma Akuyesa

Kufufuza kwa United Nations kwa mu 1990 kunasonyeza kuti maiko otukuka kwambiri amawonongera avareji ya 2 mpaka 3 peresenti ya mabajeti awo apachaka pa kuyesa kuthetsa upandu, pamene maiko omatukuka amawononga zochulukirapo, avareji ya 9 mpaka 14 peresenti. M’madera ena kuwonjezera apolisi ndi kuwapatsa zipangizo zabwinopo ndiko chinthu choyamba. Koma zotulukapo zake nzosiyanasiyana. Nzika zina za ku Hungary zikudandaula kuti: “Kulibe apolisi okwanira kugwira apandu koma nthaŵi zonse amakhalapo okwanira kugwira akuswa malamulo a pamsewu.”

Maboma ambiri posachedwapa apeza kuti nkofunika kupanga malamulo amphamvu kwambiri. Mwachitsanzo, popeza kuti “uchifwamba ukuwonjezereka m’Latin America yense,” akutero magazini a Time, maboma a kumeneko apanga malamulo “amphamvu kwambiri komanso osathandiza. . . . Kupanga malamulo ndi nkhani ina,” akuvomereza motero, “kuwatsatira ndi nkhaninso ina.”

Kwayerekezeredwa kuti mu 1992 ku Britain kunali maprogramu oposa 100,000 a neighborhood watch (anthu omalonderana chuma), oyang’anira nyumba zosachepera mamiliyoni anayi. Maprogramu ofananawo anapangidwa ku Australia chapakati pa ma 1980. Cholinga chake, ikutero Institute of Criminology ya ku Australia, ndicho kuchepetsa upandu “mwa kuthandiza nzika kuzindikira kuti chisungiko nchofunika, mwa kuwongolera maganizo a anthu ndi khalidwe lawo pochita lipoti upandu ndi zochitika zokayikitsa m’madera awo ndi kuchepetsa ngozi ya upandu mwa chithandizo cha kuika zizindikiro pa katundu wa munthu ndi kuika zipangizo zothandiza za chisungiko.”

Mawailesi akanema amagwiritsiridwa ntchito m’madera ena kulunzanitsa nyumba za polisi ndi malo a malonda. Makamera a vidiyo amagwiritsiridwa ntchito ndi apolisi, mabanki, ndi masitolo monga njira yoletsera upandu kapena monga chipangizo chodziŵira akuswa malamulo.

Ku Nigeria apolisi ali ndi malo pamene amafufuzira m’misewu yaikulu pofuna kugwira mbala ndi akuba galimoto. Boma lakhazikitsa gulu lolimbana ndi amalonda aukatangale kuti lithetse chinyengo. Makomiti achimvano pakati pa apolisi ndi anthu opangidwa ndi atsogoleri a anthu amauza apolisi za upandu ndi za anthu akhalidwe lokayikitsa.

Alendo ku Philippines amapeza kuti nyumba sizimasiyidwa popanda munthu ndi kuti anthu ambiri ali ndi agalu olonda. Eni mabizinesi amalemba ntchito alonda awoawo kutetezera mabizinesi awo. Malonda a zipangizo za galimoto zoletsa mbala kuba amayenda bwino. Anthu amene akhoza amasamukira ku zigawo zotetezereka kwambiri kapena m’mafulati.

Nyuzipepala ya ku London The Independent inati: “Pamene chidaliro m’zamalamulo chikuchepa, anthu ochuluka akulinganiza chitetezo cha malo awo.” Ndipo anthu omawonjezereka akukhala ndi zida. Mwachitsanzo, ku United States kwayerekezeredwa kuti theka la mabanja onse ali ndi mfuti imodzi.

Maboma nthaŵi zonse akupeza njira zatsopano zothetsera upandu. Koma V. Vsevolodov, wa pa Academy of Home Affairs ku Ukraine, akunena kuti malinga ndi maumboni a UN, anthu ambiri aluso akupeza “njira zapadera zochitira upandu” kwakuti “kuphunzitsa anthu osungitsa lamulo” kukutsala kutali. Apandu ochenjera amaika ndalama zochuluka m’malonda ndi m’mautumiki a boma, akumagwirizana ndi anthu ndi “kudzipezera malo apamwamba m’chitaganya.”

Kutaya Chidaliro

Anthu omawonjezereka m’maiko ena afika pa kuganiza kuti boma lenileni lili ndi mbali m’vutolo. Asiaweek inagwira mawu mkulu wa kagulu koletsa upandu amene anati: “Pafupifupi 90% ya anthu omwe timagwira ali apolisi kapena asilikali.” Kaya ali oona kapena abodza, malipoti onga ameneŵa anasonkhezera wopanga malamulo wina kunena kuti: “Ngati aja oikidwa kusungitsa malamulo ndiwonso akuwaswa, ndiye kuti chitaganya chathu chili m’vuto.”

Mbiri ya kusaona mtima kwa akuluakulu yagwedeza maboma kumbali zosiyanasiyana za dziko, ikumachepetsabe chidaliro cha nzika zake. Kuwonjezera pa kutaya chikhulupiriro mu kukhoza kwa maboma kuthetsa upandu, anthu tsopano akukayikira kutsimikiza kwawo kuchita zimenezo. Mphunzitsi wina anafunsa kuti: “Kodi olamulira ameneŵa angathetse motani upandu pamene iwo eniwo ali mkati mwenimweni mwa upanduwo?”

Maboma amadza ndi kupita, koma upandu umatsala. Komabe, ikudza nthaŵi pamene sikudzakhalanso upandu!

[Zithunzi patsamba 7]

Zoletsa upandu: Makamera a TV ndi poonera, zitseko zachitsulo zofunyululika, ndi mlonda ndi galu wophunzitsidwa

[Chithunzi patsamba 8]

Upandu umachititsa anthu kukhala andende m’nyumba zawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena