Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 1/8 tsamba 6-9
  • Kupulumuka m’Dziko Laumbombo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupulumuka m’Dziko Laumbombo
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitani Zimene Mungathe m’Mikhalidweyo
  • Peŵani Kuyambukiridwa ndi Umbombo
  • Musataye Konse Chiyembekezo cha Kulanditsidwa
  • Pambanani M’kupeŵa Msampha wa Kusirira
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Tayerekezerani Dziko Lopanda Umbombo
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Nyengo Yaumbombo”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Ndalama Tingazione Motani M’njira Yoyenera?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 1/8 tsamba 6-9

Kupulumuka m’Dziko Laumbombo

“NDIDZAPULUMUKA bwanji?” James Scott anadzifunsa funso limenelo atatayikiratu mothetsa nzeru m’mapiri a Himalaya. Anali pangozi yeniyeni ya kuuma ndi kuzizira kapena kufa ndi njala. Anakumbukira kuti anaona anthu m’mipikisano ya karate “akutha mphamvu pang’onopang’ono, nkhonya iliyonse ikuwafooketsa, mpaka . . . atakhaliratu opandiratu chitetezo.” Iye anati: “Ndi mmene ndinamvera pamene ndinali kumanga zipu ya chola changa chogonamo ndi kudya chipale chofeŵa mofooka. Mzimu wanga unafooka ndipo chikhumbo chonse cha kukhala ndi moyo chinatheratu. Ndinali ndisanalefukepo motero.”—Lost in the Himalayas.

Anthu ambiri lerolino ali ngati iye m’lingaliro lina—ogwidwa m’dziko lodzala ndi umbombo. Mungamve kuti mulikutha mphamvu pang’onopang’ono ndi kugonjetsedwa. Ndi anthu ochepa amene angathaŵiretu zotsatira zake zaumbombo zapanthaŵiyo. Malinga ndi kumene mukukhala m’dziko lapansi, mavuto amene mumakumana nawo amasiyana kwambiri—umbombo umakhudza anthu m’maiko omatukuka mosiyana kwambiri ndi mmene umakhudzira a m’maiko olemera. Chikhalirechobe, kaya akhale mavuto a mtundu wanji, mwinamwake mungaphunzire mmene mungapulumukire wosavulala kwenikweni mwakuthupi, malingaliro, ndi mwaumzimu mpaka chilanditso chitadza. Motani? Mwa kutsatira uphungu wofunika wa akatswiri a kupulumuka.

Uphungu wawo uli ndi mfundo ziŵiri zazikulu. Yoyamba ndiyo kupeŵa kuipitsirako mkhalidwe wovuta kale. “Cholinga chanu,” ikutero The Urban Survival Handbook, “chikhale chopeŵa ngozi zosafunikira . . . ndi kuchepetsa kuvulaza kwa ngozi zija zimene simungapeŵe.” Yachiŵiri—ndipo mwinamwake yofunika koposa—ikukhudza maganizo. “Kupulumuka,” ikutero The SAS Survival Handbook, “ndiko mkhalidwe wa maganizo monga momwe kupirira kwakuthupi ndi chidziŵitso kulili.”

Chitani Zimene Mungathe m’Mikhalidweyo

“Ku United States munthu mmodzi amaphedwa masekondi 22 alionse, kulandidwa katundu masekondi 47 alionse ndi kuvulazidwa kwambiri masekondi 28 alionse,” ikutero Staying Alive—Your Crime Prevention Guide. Kodi mungachitenji m’mikhalidwe yonga imeneyo? Chinthu chokha chimene mungachite ndicho kuyesa kupeŵa kudzipanga munthu wosavuta kuukira. Khalani watcheru ndi wochenjera. Chitani zimene mungathe kuchepetsa ngozi.a

Mwachitsanzo, musaipitsiretu mkhalidwe wanu mwa kukhala wonyengeka msanga. The New York Times ikuti 18 peresenti ya Aamereka akuvomera kuti amanyengeka—kuberedwa madola zikwi zambiri mwachinyengo ndi anthu opanda mwambo amene amafunafuna woti anyenge mosavuta. Kaŵirikaŵiri atsoka amakhala achikulire monga mkazi wina wamasiye wazaka 68 amene anambera $40,000. Zimene zinamchitikira zinachititsa kuti mutu uwu ulembedwe: “Ngati Tsitsi Ndi Laimvi, Atsinzina Ntole Amaliona Kubiriŵira [kutanthauza ndalama zobiriŵira, kapena madola].”

Koma simuyenera kungokhala watsoka winanso wosadziŵa kanthu ndi wopanda thandizo wongoyembekezera kudyeredwa masuku pamutu. Staying Alive ikutichenjeza kuti: “Chenjerani ndi mmbulu m’zovala za nkhosa.” Gogo wina wamkazi wazaka 70 anamvetsera uphunguwu. Anamuuza kuti adzampatsa inshuwalansi ya malipiro onse a mankhwala, pamtengo wa $10 chabe pamwezi. “Chinthu chokha chimene Gogoyo akanachita,” lipotilo likutero, “chinali kupatsiratu wosatsa malondayo $2,500 basi.” Sanatero. Mwa kuimbira foni kampani ya inshuwalansiyo, anapeza kuti mwamunayo anali wakuba. “Pomthirira wamalondayo kapu yachiŵiri ya tiyi, apolisi anafika namgwira.”

Kuchita zimene mungathe kuti mudzitetezere kukutchulidwa mu uphungu wa m’Baibulo. “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15; 27:12) Ambiri amati Baibulo nlachikale ndipo silimagwira ntchito. Koma uphungu wake wabwino ungakuthandizeni kupulumuka. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Nzeru [yonga ija yopezeka m’Baibulo] ichinjiriza monga ndalama zichinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.”—Mlaliki 7:12.

Oŵerenga Galamukani! ambiri apeza zimenezi kukhala zoona. Mwachitsanzo, ena apeza chitetezo chakutichakuti mwa kufuula kwambiri atawopsezedwa ndi chigololo chokakamiza kapena chiwawa china chilichonse, mogwirizana ndi zotchulidwa pa Deuteronomo 22:23, 24. Ena atsatira uphungu wa Baibulo wa kupeŵa chilichonse “choipitsa thupi kapena mzimu.” (2 Akorinto 7:1, The Twentieth Century New Testament) Choncho iwo adzitetezera kwa amalonda a fodya ndi anamgoneka, amene amadzilemeza mwa kuwononga thanzi la anthu. Oŵerenga ambiri apeŵanso misampha ya alaliki a pa TV ofunafuna ndalama ndi andale ofunitsitsa ulamuliro. (Onani bokosi, tsamba 7.) Ŵerengani Baibulo. Mwinamwake mudzadabwa kuona kuchuluka kwa uphungu wothandiza umene limapereka.

Peŵani Kuyambukiridwa ndi Umbombo

Eya, umbombo ulinso ndi ngozi ina—inuyo mungakhale waumbombo. Zimenezi zidzakulandani mikhalidwe yabwino kwambiri imene imakusiyanitsani ndi zinyama. Pofotokoza malonda opanda zitsogozo omwe amalonda anali kukhwathulamo zilizonse zimene anatha kutenga, wopenyerera wina anagwidwa mawu akuti: “Koma nkhumbazo zinali kudya. Umbombo wake . . . unangokhala wosalamulirika.” Ngakhale nkhumba sizili ndi umbombo wonga wa amalonda adyera amenewo! Ndithudi iwo anaoneka kuti ananyalanyaza uphungu wabwino wa Yesu Kristu wakuti: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse.”—Luka 12:15.

Yesu Kristu anapereka uphunguwo chifukwa anadziŵa mmene mungadziwonongere kwambiri ngati mwakhala aumbombo. Kukhumba kwambiri chuma—ndiponso kukhumba kwambiri ulamuliro kapena kugonana—kungakhale chikhumbo chachikulu koposa m’moyo wanu, ndi kukulandani nthaŵi iliyonse kapena malingaliro amene mungakhale nawo osamalira anthu kapena zofunika zauzimu. “Ndalama,” akutero Anthony Sampson m’buku lake lakuti The Midas Touch, “zalanda mikhalidwe yambiri ya chipembedzo.” Motani? Ndalama zimakhala mulungu. Zinthu zonse amazichita chifukwa cha umbombo ndi phindu. Chochititsa chachikulu ndicho phindu. Lochuluka kwambiri ndilo labwino kwambiri. Komabe, kunenadi zoona, kaya nthaŵi imene mumatayirapo ikhale yaikulu chotani, umbombo wa chuma sudzakhutiritsidwa konse mokwanira. Mlaliki 5:10 amati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.” Momwemonso, “wokonda” ulamuliro, chuma, kapena kugonana sadzakhutira konse, kaya angapeze zochuluka chotani.

Musataye Konse Chiyembekezo cha Kulanditsidwa

Mfungulo ina yofunika pa kupulumuka ndiyo kukhalabe ndi chiyembekezo ndi kaonedwe kabwino ka zinthu. Nthaŵi zina pamakhala palibe zimene mungachite kuti muthaŵe zotsatirapo za anthu aumbombo. Mwachitsanzo, anthu anjala sangachite chilichonse kuti athaŵe mkhalidwe wawo wapanthaŵiyo. Komabe, musaleme; musagonje. “Nkwapafupi kugonja, kulephera ndi kungodzichitira chisoni” mutakhala pamalo oipa kapena angozi, ikutero The SAS Survival Handbook. Musagonjere kaonedwe ndi maganizo oipa. Mungadabwe kuona kuchuluka kwa zimene mungapirire. “Amuna ndi akazi asonyeza kuti angapulumuke m’mikhalidwe yoipitsitsa koposa,” likutero buku lamalangizo limodzimodzilo. Kodi anachita motani zimenezo? Iwo anapulumuka, likutero, “chifukwa cha kulimbikira kwawo kuchita zimenezo.” Limbikirani kuti dongosolo lino laumbombo lisakugonjetseni.

James Scott, wotchulidwa poyambayo, anamlanditsa m’kupita kwa nthaŵi ku amene akanakhala manda ake a ku Himalaya. Iye anati nkhondo yake yakuti apulumuke inamphunzitsa kwenikweni phunziro limodzi lofunika. Kodi linali lotani? “Palibe chothetsa nzeru m’moyo chimene chili cholimba kwambiri moti nkusalimbana nacho,” iye anatero. Tim Macartney-Snape, wokwera mapiri wachidziŵitso amene anadabwa kwambiri kuti James Scott anatha kupulumuka nthaŵi yaitali kwakuti anampeza wamoyo, anatengaponso phunziro lina. Iye anati: “Malinga uli ndi chiyembekezo ngakhale chaching’ono kwambiri, usachitaye.” Choncho, kaya zinthu zikhale zokayikitsa motani, mumangoipitsiratu zinthu ngati mwataya chiyembekezo. Musataye chiyembekezo chakulanditsidwa.

Koma kodi pali “chiyembekezo ngakhale chaching’ono kwambiri” chilichonse, mwaŵi uliwonse wa chilanditso ku dziko lodzala ndi umbombo? Kodi anthu aumbombo amene akuwononga pulaneti lino ndi kuipitsa moyo wa anthu miyandamiyanda adzachotsedwapo? Kwenikweni, chitsimikizo chilipo chakuti mtsogolo muli chilanditso. Onani yankho la Baibulo m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Chiwawa—Mungadzichinjirize Inumwini,” m’kope la Galamukani! la May 8, 1989, masamba 28-32.

[Bokosi patsamba 7]

Machenjezo a Baibulo a Panthaŵi Yake

Miyambo 20:23 “Miyeso yosiyana inyansa Yehova, ndi mulingo wonyenga suli wabwino.”

Yeremiya 5:26, 28 “Mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu. Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wawo, kuti apindule; mlandu wa aumphaŵi saweruza.”

Aefeso 4:17-19 “Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.”

Akolose 3:5 “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.”

2 Timoteo 3:1-5 “Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.”

2 Petro 2:3 “M’chisiriro adzakuyesani malonda ndi mawu onyenga; amene chiweruzo chawo sichinachedwa ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chawo sichiodzera.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena