Umbombo—Kodi Ukutitani?
UMBOMBO ukuwononga moyo wa anthu miyandamiyanda. Aumbombo ukuwakhalitsa okakala mtima ndipo ukudzetsa zoŵaŵa ndi chisoni kwa anthu amene amavutika nawo. M’moyo wanu mwina zotsatira zake za umbombo zikukukhudzani. Ngakhale kuba kofala m’masitolo kumakweza mitengo ya zimene mumagula. Ngati malipiro anu ngotsika ndipo mitengo ya zofunika zatsiku ndi tsiku simungaithe, ndiye kuti mwina mukuvutika ndi umbombo wa wina.
Anjala ndi Omafa
Kudzikonda kwaumbombo kwa maiko kumalepheretsa maboma kuchita khama kuti athandize osauka. Kalelo mu 1952, wasayansi ndiponso katswiri wa zakadyedwe Bwana John Boyd Orr anati: “Maboma ngokonzeka kugwirizanitsa anthu ndi chuma kaamba ka nkhondo yadziko koma Maulamuliro Aakulu ngosakonzeka kugwirizana kuti athetse njala ndi umphaŵi padziko.”—Food Poverty & Power, lolembedwa ndi Anne Buchanan.
Inde, thangato pang’ono limaperekedwa. Koma kodi moyo ngwotani kwa anthu ambiri osauka ndi onyanyalidwa padziko? Lipoti laposachedwa linanena kuti ngakhale kuti m’madera ena chakudya chachuluka, “njala ndi matenda ake ikali kuvuta unyinji wa osauka padziko . . . Mmodzi mwa anthu asanu alionse [oposa mamiliyoni chikwi] padziko amagona njala masiku onse.” Lipotilo likupitiriza kuti: “Ndiponso, anthu [2,000,000,000] akuzunzika ndi ‘njala yobisika’ chifukwa cha . . . [chakudya] chosamanga thupi chimene chingayambitse matenda owopsa.” (Developed to Death—Rethinking Third World Development) Ziŵerengero zimenezi ziyeneradi kukhala m’mitu ya nkhani!
Akapolo
Akulu a apandu amadzilemeza mwa kuvulaza munthu mmodzi ndi mmodzi ndi anthu ambiri. Anamgoneka, chiwawa, uhule, ndi kudyerera ena m’zachuma kwamanga anthu miyandamiyanda ukapolo. Ndiponso, Gordon Thomas m’buku lake lakuti Enslaved akuti: “Malinga ndi Anti-Slavery Society, padziko lonse pali akapolo ngati 200 miliyoni. Pafupifupi 100 miliyoni a iwo ndi ana.” Kodi chochititsa chake chachikulu nchiyani? Lipotilo likufotokoza kuti: “Chikhumbo cha kugwira ena ukapolo chikali mbali yoipa ya chibadwa cha munthu. . . . [Ukapolo ulipo] chifukwa cha chilakolako, umbombo ndi kukonda mphamvu.”
Amphamvu amalanda ofooka ndi osatetezereka ndi kupha ambiri. “Pa Aindiya mamiliyoni aŵiri omwe ankakhala m’Brazil pamene azungu anafika, mwina zikwi mazana aŵiri okha ndiwo alipo.” (The Naked Savage) Chifukwa ninji? Chifukwa chake chachikulu ndi umbombo.
Kusiyana Komakula kwa Olemera ndi Osauka
The New York Times inasimba kuti James Gustave Speth, woyang’anira United Nations Development Program, ananena kuti “gulu la apamwamba limene likupangika padziko . . . likukundika chuma chochuluka ndi mphamvu, pamene oposa theka la anthu atsalira mmbuyo.” Kusiyana kowopsa kumeneku kwa olemera ndi osauka kukuonetsedwa kwambiri ndi mawu ake akuti: “Tikali ndi anthu oposa theka papulaneti lino amene amalandira ndalama zosakwanira $2 patsiku—anthu oposa [3,000,000,000].” Anawonjezera kuti: “Kwa anthu osauka m’dzikoli la magulu aŵiri, mkhalidwewu umawatayitsa mtima, kuwakwiyitsa, kuwakhumudwitsa.”
Kutaya mtima kumeneku kumakula chifukwa chakuti ambiri olemera amachita ngati alibe chikumbumtima kapena chifundo mpang’ono pomwe pa vuto la amphaŵi ndi makamu anjala.
Ovutika ndi umbombo ali ponseponse. Mwachitsanzo, onani nkhope zothedwa nzeru za othaŵa kwawo opezeka m’nkhondo yolimbirana ulamuliro ku Bosnia, Rwanda, ndi Liberia. Onani kuvutika pankhope za awo amene akufa ndi njala pakati pa chakudya cha mwana alirenji cha dzikoli. Chimachititsa zonsezi nchiyani? Umbombo—wamtundu uliwonse!
Kodi mungapulumuke bwanji pozingidwa ndi anthu olusa aumbombo m’malo oipa chonchi? Nkhani ziŵiri zotsatira zidzayankha funsoli.