Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 1/8 tsamba 9-10
  • Dziko Lopanda Umbombo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lopanda Umbombo
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto la Maphunziro?
  • Kuloŵererapo kwa Mulungu
  • “Kuwononga Iwo Akuwononga Dziko”
  • Kodi Alipo Amene Angasinthedi Dzikoli?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Alipo Amene Amasamaladi
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Umbombo—Kodi Ukutitani?
    Galamukani!—1997
  • Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 1/8 tsamba 9-10

Dziko Lopanda Umbombo

“POPANDA kusintha maganizo a munthu padziko lonse, palibe chimene chidzasintha ndi kutikhalira bwino monga anthu, ndipo ngozi imene dziko lathu lidzakumana nayo . . . siidzapeŵeka.”—Václav Havel, pulezidenti wa Czech Republic.

Anthu ambiri amavomereza kuti dongosolo la dziko lilipoli silidzapulumuka. Ena, monga Václav Havel, amaona kuti kusintha maganizo ndi zochita za munthu padziko lonse lapansi ndiko njira yokha yochitira. Mwachitsanzo, wosinkhasinkha wina pa zimene zikuchitika padziko lapansi akuti: “Chiyembekezo chakuti anthu osauka kwambiri mamiliyoni mazanamazana adzakhala ndi chakudya ndi zofunika zina pamoyo, chidzakhala chosaphula kanthu . . . pokhapo mitundu ya m’dziko itachitapo kanthu motsimikiza mtima kusintha maganizo amene alipo.”—Food Poverty & Power.

Komabe, kodi tingazikedi chiyembekezo chathu cha kupulumuka pa kusintha kwinakwake kwakukulu kwa chibadwa cha munthu? Kodi tingadaliredi maboma kuti ‘adzachitapo kanthu motsimikiza mtima kusintha maganizo amene alipo’? Ena amaganiza choncho. ‘Mulungu anatipatsa ufulu wakudzisankhira ndipo zili kwa ife kusintha zinthu,’ iwo amatero. Koma zinthu zoipa zimene zachitika m’mbiri zikukayikitsa kwambiri chikhumbo cha munthu ndi kukhoza kwake kupanga masinthidwe ofunikira. Kuona zinthu m’njirayi sindiko kugogomezera mbali yoipa, koma m’malo mwake, ndi kunena zoona. Kodi mungaike moyo wanu m’manja mwa dokotala wa opaleshoni ngati mwadziŵa kuti odwala ake oyamba onse anafa?

Vuto la Maphunziro?

“Vuto lake likukhudza maphunziro,” akutero Ted Trainer, mu Developed to Death—Rethinking Third World Development. Akunena kuti “sitingayembekezere kusintha kuloŵa m’dongosolo ladziko lokhalika bwino” ngati anthu saphunzitsidwa kuti aone kuti kusintha kwakukulu kukufunika.” Ndithudi anthu afunikira kuwaphunzitsa za kufunika kwake kwa kusintha maganizo ndi zochita zawo kuti dziko lipulumuke. Kwenikweni, nkoyenera, ndipo Baibulo limanena za programu ya maphunziro imeneyi. Limanena kuti dziko lapansi “lidzadzala ndi odziŵa Yehova.” Ndiyeno, palibe amene ‘adzaipitsa kapena kusakaza’ kulikonse padziko lapansi.—Yesaya 11:9.

Koma palibe maphunziro alionse, ngakhale programu ya Mulungu ya maphunziro, amene mwa iwo okha adzachotsa anthu aumbombo padziko lapansi amene amaipitsa ndi kusakaza zinthu kwambiri. Maphunziro adzangosintha anthu amene akufuna kusintha, anthu amene akufuna kugwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Malinga ndi kunena kwa Yesu Kristu, iwo ndi ochepa. (Mateyu 7:13, 14) Choncho Baibulo silimazika lonjezo lake la kusintha pa chiyembekezo china chongoyerekezera chakuti tsiku lina mtundu wonse wa munthu udzazindikira ukulu wa vutoli ndi kusintha njira zake. Limanena kuti Mulungu adzachitapo kanthu mwachindunji kuchotsa anthu aumbombo padziko lapansi.

Kuloŵererapo kwa Mulungu

Ambiri amaona kuti lingaliro limeneli lakuti Mulungu adzachitapo kanthu mwachindunji ndi loto chabe kapena madzi amphutsi. “Chidziŵitso chachikulu chopezedwa m’zaka za zana la 18 chinatikakamiza kutaya lingaliro lotonthoza lonena za Mulungu woloŵerera pazinkhani amene adzakonza nyumba ya munthu,” ikutero World Hunger: Twelve Myths. Koma kodi tiyenera kukhulupirira zonena za anthu oganiza ndi mafilosofi a awo amene ataya chikhulupiriro mwa “Mulungu woloŵerera pazinkhani”? Kodi njira zawo zothetsera mavuto sindizo madzi amphutsi?

Nkwanzeru kwambiri kuzika chiyembekezo chathu cha kupulumuka pamaulosi osaphonya opezeka m’Baibulo amene amanena za kuloŵererapo kwa Mulungu. Kukhulupirira malonjezo a Mulungu si “lingaliro lotonthoza” chabe—ndiko chiyembekezo chokha chenicheni cha kupulumuka chimene tili nacho!

“Kuwononga Iwo Akuwononga Dziko”

Kodi nchiyani kwenikweni chimene Mulungu akulonjeza? Eya, chinthu chimodzi chimene akulonjeza ndicho kuchotsapo padziko lapansi awo amene amaipitsa ndi kuwononga malo okhala. Chivumbulutso 11:18 chimalengeza kuti iye ali ndi “nthaŵi” ya “kuwononga iwo akuwononga dziko.” Kodi zimenezo zidzatanthauzanji? Zidzatanthauza kutha kwa awo onse amene tsopano akutsendereza aumphaŵi ndi ofooka. Mulungu ‘adzaweruza ozunzika mwa anthu, kupulumutsa ana a aumphaŵi, ndi kuphwanya wosautsa.’ Adzachotsapo aumbombo ndi kulola osalakwa ovutika chifukwa cha iwo kutukuka. “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; . . . Adzaombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.”—Salmo 72:4, 12-14.

Zimenezo zidzabweretsa kusintha kwakukulu chotani nanga! Malinga ndi kunena kwa mtumwi Petro, kusintha kumeneku kudzakhaladi kwaponseponse kwakuti kudzapanga “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano.” (2 Petro 3:13) Mu “dziko latsopano” limeneli, aliyense adzakhala ndi gawo lokwanira la zakudya za dziko lapansi. (Mika 4:4) Ngakhale tsopano pali chakudya chochuluka chokwanira aliyense. Kugaŵa mosalingana ndiko vuto. “Kwanenedwa kuti tingalime zakudya zokwanira zochirikiza anthu ngati [38,000,000,000-48,000,000,000] panthaka yolimika ya dziko lonse lapansi,” Anne Buchanan akutero m’buku lake lakuti Food Poverty & Power.

Pulanetili lidzapulumuka. Mlengi wake “sanalilenga mwachabe [koma] analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Chochita cha Mulungu pa anthu aumbombo chidzakhala nthaŵi yaifupi ya “chisautso chachikulu.” (Mateyu 24:21, NW ) Ndiyeno opulumuka chisautso chimenecho adzasangalala ndi dziko lapansi la paradaiso, lodzala ndi anthu omasukiratu paumbombo. (Salmo 37:10, 11; 104:5) Zidzakhala monga momwe Baibulo limalonjezera kuti: “Mulungu adzapukuta misozi pankhope zonse.”—Yesaya 25:8.

Inuyo mungakhale mmodzi wa opindula achimwemwe ndi chochita cha Mulungu cha kuchotsa umbombo padziko lapansi. Ngati mukufunadi kuchita chifuniro cha Mulungu, gwiritsirani ntchito zithandizo zonse zoperekedwa kuti zikuthandizeni kupulumuka tsopano m’dziko laumbombo. Chitanipo kanthu kuti mukapulumuke “chisautso chachikulu.” Mboni za Yehova nzokonzekera kukuthandizani kuphunzira zimene muyenera kudziŵa. Khalani aufulu kuzifikira pa Nyumba ya Ufumu ya kwanuko kapena lemberani ku keyala yapafupi kwambiri yosonyezedwa patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena