Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 3/8 tsamba 14-16
  • Likodzo Kodi Lili Pafupi Kutha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Likodzo Kodi Lili Pafupi Kutha?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Umoyo wa Kachilomboko
  • Njira Zothetsera ndi Mavuto Ake
  • Kodi Mtsogolo Muli Chiyembekezo Chotani?
  • Chigoba cha Nkhono Yam’madzi
    Galamukani!—2011
  • Chigoba cha Nkhono ya M’madzi
    Galamukani!—2012
  • Mwana Wanu Akatentha Thupi
    Galamukani!—2003
  • Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 3/8 tsamba 14-16

Likodzo Kodi Lili Pafupi Kutha?

NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU NIGERIA

MOSASAMALA kanthu za chitukuko chodabwitsa m’ntchito zamankhwala ndi sayansi, anthu akulephera kuthetsa mavuto awo akalekale. Zili chonchonso ponena za kuyesayesa kugonjetsa likodzo.

Kukuoneka kuti zofunika zonse zothetsera nthendayo zilipo. Madokotala amadziŵa za umoyo wa kachilombo konyamula nthendayo. Nthendayo amaizindikira msanga. Mankhwala amphamvu alipo ochiritsa. Atsogoleri a maboma ngofunitsitsa kuchirikiza zoyesayesa za kuithetsa. Komabe, kukukaikitsa kutha kwa nthenda imeneyi yomwe ikukantha anthu mu Afirika, mu Asia, mu Caribbean, mu Middle East, ndi mu South America.

Likodzo (lotchedwanso bilharziasis kapena schistosomiasis) lavutitsa anthu kwa zaka zikwi zambiri. Mazira ouma opezeka pa mitembo youmikidwa ya Aigupto amapereka umboni wakuti nthenda imeneyi inkawagwira Aigupto m’masiku a afarao. Zaka mazana makumi atatu pambuyo pake, nthenda imodzimodziyo ikuwagwirabe Aigupto, kufooketsa thanzi la anthu mamiliyoni ambiri a m’dzikomo. M’midzi ina ya ku Nile Delta, 9 pa anthu 10 alionse anagwidwa nayo.

Igupto wangokhala limodzi la maiko 74 kapena oposerapo kumene likodzo lili lofala. Padziko lonse, malinga ndi ziŵerengero za World Health Organization (WHO), anthu okwana 200 miliyoni amagwidwa nayo nthendayo. Mwa anthu 20 miliyoni odwala mobwerezabwereza, pafupifupi 200,000 amafa chaka chilichonse. M’madera otentha, pa matenda onse oyambitsidwa ndi tizilombo, likodzo laikidwa lachiŵiri kwa malungo malinga ndi unyinji wa anthu amene limagwira ndi kuwononga kwake anthu ndi chuma.

Umoyo wa Kachilomboko

Kulizindikira likodzo, ndiponso kudziŵa kutetezera ndi kulichiza, kumatanthauza kuzindikira kachilombo kamene kamaliyambitsa. Mfundo yaikulu nayi: kuti kakhalepobe kwa mibadwomibadwo, kachilombo kameneka kamafunikira kukhala m’thupi mwa zolengedwa zamoyo ziŵiri, mmene kati kazidya ndi kukula. Chimodzi nchoyamwitsa, monga munthu; china ndi nkhono ya m’madzi.

Nazi zimene zimachitika. Pamene munthu wokhala ndi kachilomboko akodzera kapena kuchitira chimbudzi m’madzi a padziŵe, m’nyanja, m’kamfuleni, kapena m’mtsinje, amasiyamo mazira akachilomboko—mwina mazira okwanira miliyoni imodzi patsiku. Mazira amaneŵa ngaang’ono kwambiri moti sangaonedwe popanda maikulosikopo. Pamene maziraŵa aloŵa m’madzi, amasweka, tizilomboto nkutuluka. Tizilomboto timagwiritsira ntchito ubweya waung’ono wa pathupi lawo kusambira kukapeza nkhono ya m’madzi, nkuiloŵa. Kwa milungu inayi kapena isanu ndi iŵiri timaswana tili m’nkhono momwemo.

Pamene tikutuluka m’nkhonoyo, timafunikira kukaloŵa mwa munthu kapena nyama ina yoyamwitsa asanathe maola 48. Tikapanda kutero, timafa. Kachilomboko kakangopeza munthu yemwe waloŵa m’madzi, kamaboola khungu ndi kuloŵa m’mwazi. Munthuyo angangomva kuyabwa, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri samazindikira kuti kena kake kamuloŵa. M’mwazimo, kachilomboko kamaloŵa m’mitsempha ya chikhodzodzo kapena ya matumbo, zikumadalira pa mtundu wa kachilomboko. M’milungu yoŵerengeka chabe, tizilomboto timakhala nyongolotsi zazikulu zazimuna ndi zazikazi mpaka kutalika mamilimita 25. Titakwerana, yaikaziyo imayamba kuika mazira m’mwazi wa munthuyo, choncho nkutsiriza utali wa umoyo wake.

Pafupifupi theka la mazirawo amatuluka m’thupi mwa munthuyo kudzera m’tudzi (kamwazi) kapena m’mkodzo (likodzo). Mazira ena onse amatsala m’thupi mommo ndi kumawononga ziŵalo zofunika. Pamene nthendayo ikukula, wodwalayo amayamba kutentha thupi, kutupa mimba, ndi kukhera mwazi mkati mwathupi. Potsirizira pake nthendayo imabala kansa ya kuchikhodzodzo kapena chiŵindi ndi impso zimalephera kugwira bwino ntchito. Odwala ena amaleka kubala amapuŵala ziŵalo. Ena amafa.

Njira Zothetsera ndi Mavuto Ake

Kuti kufalikira kwa nthendayi kuthetsedwe, pafunikira zinthu zinayi. Ngati iliyonse ya njirazi inati igwiritsiridwe ntchito padziko lonse, nthenda imeneyi ikanagonjetsedwa.

Njira yoyamba ndiyo kuchotsa nkhono zonse m’madzi. Nkhono ndiyo malo okuliramo kachilomboko. Popanda nkhono, sipakhala likodzo.

Anthu ayesayesa kupanga mankhwala amphamvudi owonongera nkhono koma amene sadzaipitsa madzi. M’ma 1960 ndi m’ma 1970, anapambana pakuyesayesa kuthetsa nkhono mwa kupha zamoyo zonse m’madzi. A ku Egypt’s Theodor Bilharz Research Institute anayesanso kupeza molluscicide (mankhwala ophera nkhono) amene samawononga mitundu ina ya zamoyo. Dr. Aly Zein El Abdeen, pulezidenti wa bungwelo ponena za mankhwalawo anati: “Adzatsanuliridwa m’madzi, omwe timathiririra mbewu, omwe anthu ndi nyama zimamwa, momwe nsomba zimakhalamo, chotero tiyenera kutsimikizira ndithu kuti palibe nchimodzi chomwe cha zimenezi chimene chidzakhudzidwa.”

Njira yachiŵiri ndiyo kupha tizilomboto tili mwa anthu. Mpaka m’ma 1970, mankhwala ake analinso ndi zotulukapo zovulaza, zowonjezera matenda. Kaŵirikaŵiri, kunafunikira kuti tsiku ndi tsiku munthu alandire jekiseni yopweteka. Ena anadandaula kuti mankhwalawo anali oŵaŵa kuposa nthendayo! Kuyambira pamenepo, mankhwala atsopano, onga praziquantel, atulukiridwa omwe ngamphamvudi pakulimbana ndi likodzo, ndipo ameneŵa ngakumwa.

Ngakhale kuti mankhwala ameneŵa apambana pa ntchito zoyesera mankhwala mu Afirika, ndi mu South America, vuto lalikulu la maiko ena ndilo mtengo wake. Mu 1991, a WHO anadandaula kuti: “Maiko okanthidwa ndi nthenda imeneyi sakutha kulipirira ntchito yaikulu yolimbana ndi [likodzo] chifukwa cha kukwera mtengo kwa mankhwala; mtengo wa mankhwala enieniwo kaŵirikaŵiri umaposa ndalama za bajeti ya zaumoyo m’maiko ambiri mu Afirika.”

Ngakhale kumene odwala amapatsidwa mankhwala kwaulere, anthu ambiri samapitako kukalandira mankhwala. Chifukwa nchiyani? Chifukwa chimodzi nchakuti chiŵerengero cha akufa ndi nthendayo nchaching’ono, choncho anthu ambiri samailingalira kukhala vuto lalikulu. Chifukwa china nchakuti nthaŵi zambiri anthu samazidziŵa zizindikiro za nthendayo. M’mbali zina za Afirika, mwazi m’mkodzo (chizindikiro choyamba cha nthendayo) ndi chinthu chofala kwambiri kwakuti amangoti ndiko kukula kwa munthu.

Njira yachitatu ndiyo kusamala kuti mazirawo asaloŵe m’madzi. Ngati anthu akanamanga zimbudzi kuti asaipitse mifuleni ndi maiŵe a kumaloko ndipo ngati aliyense akanazigwiritsira ntchito, kudwala likodzo kukanachepa.

Kufufuza kwa padziko lonse kumasonyeza kucheperachepera kwa nthendayi kumene amaika zimbudzi za madzi, koma ziŵiya zimenezi sizingaithetseretu nthendayo. “Munthu mmodzi yekha basi kungochitira chimbudzi m’ngalande kuswanako kupitiriza,” anatero Alan Fenwick, yemwe anaphunzira za likodzo kwa zaka zoposa 20. Palinso ngozi ya mipope yosweka ya madzi a m’chimbudzi imene ingaloŵetse zonyansazo m’madzi akumwa.

Njira yachinayi ndiyo kuletsa anthu kuti asaloŵe m’madzi oipitsidwa ndi kachilomboko. Zimenezinso zingooneka ngati nzapafupi koma nzovuta. M’maiko ambiri nyanja, mifuleni, ndi mitsinje mmene anthu amamwa, amasambamo, kuthirira mbewu, ndi kuchapiramonso zovala. Asodzi amakhala ku madzi tsiku ndi tsiku. Ndipo m’chitungu cha m’madera otentha, kwa ana madzi angakhale dziŵe lochititsa chidwi losambiramo.

Kodi Mtsogolo Muli Chiyembekezo Chotani?

Palibe kukayikira kuti anthu ndi mabungwe oona mtima akugwira ntchito mwakhama polimbana ndi likodzo ndi kuti kuwongokera kwakukulu kwakhalapo. Ofufuza akumenyera nkhondo kuti pakhale ngakhale katemera wake.

Komabe, ziyembekezo za kuithetsa nthendayi nzochepa. Mu magazini ya zamankhwala ya ku France La Revue du Praticien, Dr. M. Larivière anati: “Ngakhale kuti pakhala zipambano . .  . , nthendayo sikutha iyayi.” Ngakhale kuti ena angadzitetezeredi ndi kuichiza, vuto la likodzo konsekonse yankho lake silipezeka mpaka dziko latsopano la Mulungu litafika. Baibulo limalonjeza kuti mmenemo “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

[Chithunzi patsamba 15]

Pamene anthu aloŵa m’madzi oipitsidwa, tizilombo topatsa likodzo tingathe kuwaloŵa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena