Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 7/15 tsamba 14-15
  • Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?
  • Galamukani!—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1 ZIZINDIKIRO ZA MALUNGO
  • 2 KODI MALUNGO AMAFALIKIRA BWANJI?
  • 3 KODI TINGADZITETEZE BWANJI?
  • Imfa pa Mapiko Ofeŵa
    Galamukani!—1994
  • Kubwerera m’Zakale Polimbana ndi Malungo
    Galamukani!—1997
  • Chida Chatsopano m’Kulimbana ndi Nthenda ya Malungo
    Galamukani!—1993
  • Kodi Nchifukwa Ninji Nthenda “Zochiritsika” Zabukanso?
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 7/15 tsamba 14-15

Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?

Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti m’chaka cha 2013 anthu oposa 198 miliyoni anadwala malungo ndipo anthu pafupifupi 584,000 anamwalira ndi matendawa. Pa anthu 5 alionse, 4 anali ana osakwana zaka 5. Matendawa amapezeka m’mayiko pafupifupi 100 ndipo mwina anthu 3.2 biliyoni akhoza kudwala.

1 ZIZINDIKIRO ZA MALUNGO

Zizindikiro za malungo ndi izi: kutentha thupi, kuzizidwa, kupweteka kwa mutu, kuphwanya thupi, kuchita mseru ndiponso kusanza. Zizindikirozi zikhoza kuonekera pa maola 48 kapena 72 alionse malinga ndi mtundu wa malungo komanso nthawi imene munthu wakhala akudwala.

2 KODI MALUNGO AMAFALIKIRA BWANJI?

  1. Tchati chosonyeza mmene tizilombo ta malungo timafalikirira m’thupi la munthu

    Tizilombo ta malungo timalowa m’magazi a munthu akalumidwa ndi udzudzu waukazi wa anofelesi.

  2. Tizilomboti timapita kuchiwindi n’kuyamba kuswana.

  3. Maselo a chiwindi akaphulika tizilomboti timalowa m’maselo ofiira a magazi n’kuswananso mmenemo.

  4. Tizilombo ta malungo timalowa m’maselo ofiira a magazi ndipo maselowo amaphulika

    Maselo ofiirawo akaphulika tizilomboto timafalikira m’maselo ena ofiira.

  5. Izi zimachitika mobwerezabwereza. Ndiyeno munthu amamva zizindikiro nthawi iliyonse imene maselo ofiirawo aphulika..

3 KODI TINGADZITETEZE BWANJI?

Ngati mumakhala m’dziko limene kuli malungo, chitani izi:

  • Muzigona m’masikito. Masikitowo azikhala

    • onyikidwa m’mankhwala.

    • osang’ambika.

    • oyalidwa bwino kuti udzudzu usakhale ndi mpata wolowa.

  • Muzipopera mankhwala m’nyumba.

  • Ngati n’kotheka muziika sefa m’mawindo kuti udzudzu usalowe. Mukhozanso kuyatsa fani kuti udzudzu uthawe.

  • Muzivala zovala zoteteza khungu lanu kuti musalumidwe.

  • Pewani malo alionse amene udzudzu ungaswane.

  • Mukayamba kudwala malungo muzipita kuchipatala mwamsanga.

Mmene tizilombo ta malungo timayendera

Munthu angadwale matendawa ngati walumidwa ndi udzudzu umene uli ndi tizilombo tamalungo. Komanso udzudzu umene ulibe tizilomboti ungakhale nato ngati waluma munthu amene akudwala malungo. Ndiyeno udzudzuwo ukaluma munthu wina ungamupatsire matendawa.

Ngati mukufuna kupita kudziko limene kuli malungo, chitani izi:

  • Fufuzani kaye mfundo zonse zothandiza musananyamuke. Mudziwiretu mtundu wa mankhwala amene angakuthandizeni chifukwa malungo amakhala osiyanasiyana malinga ndi dera. Fufuzaninso zimene muyenera kupewa malinga ndi mmene thupi lanu lilili.

  • Mukafika m’dzikolo, muyenera kutsatira mfundo zimene talemba pamwambapa pa kamutu kakuti, “Ngati mumakhala m’dziko limene kuli malungo.”

  • Mukayamba kudwala malungo pitani kuchipatala mwamsanga. Kumbukirani kuti zizindikiro za malungo zikhoza kuyamba kuonekera patapita mlungu umodzi kapena milungu 4 kuchokera pamene munalumidwa ndi udzudzu.

ZINA ZIMENE MUNGACHITE

  1. Muzilandira chithandizo chimene boma kapena mabungwe ena amapereka.

  2. Muzipeza mankhwala ovomerezeka. (Mankhwala achinyengo angachititse kuti musachire msanga kapena kufa kumene.)

  3. Pakhomo panu pasakhale malo amene udzudzu ukhoza kuswana.

Ngati mumakhala m’dera limene kuli malungo kapena munapitako posachedwapa, musanyalanyaze zizindikiro izi:

  • Kutentha thupi

  • Kuchita thukuta

  • Kunjenjemera ndiponso kuzizidwa

  • Kupweteka mutu

  • Kuphwanya thupi

  • Kufooka

  • Mseru

  • Kusanza

  • Kutsegula m’mimba

Ngati munthu wodwala malungo sapeza msanga mankhwala, magazi angachepe kwambiri ndipo akhoza kufa. Muyenera kupita mwamsanga kuchipatala mukangoyamba kumva zizindikirozo. Ana ndi amayi oyembekezera amafunika kuthandizidwa mwamsanga kwambiri.a

a Kuti mudziwe zambiri, onani Galamukani! ya November 2011, tsamba 24 ndi 25 ndiponso ya November 2009, tsamba 26 mpaka 29.

KODI MUKUDZIWA?

Wotchi ili pa mapu a Africa

Ku Africa mwana mmodzi amafa ndi malungo pa miniti iliyonse

  • Zimakhala zoopsa kwambiri pamene ana ndi amayi oyembekezera adwala matendawa.

  • Ku Africa mwana mmodzi amafa ndi malungo pa miniti iliyonse.

  • Mwa apa ndi apo, anthu amadwala malungo chifukwa choikidwa magazi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena