Chida Chatsopano m’Kulimbana ndi Nthenda ya Malungo
MONGA momwe kunasimbidwira mu Awake! ya May 8, 1993, nthenda ya malungo ikuyambikanso monga mliri wa dziko. The New York Times (ya March 23, 1993) inasimba kuti “chaka chatha, Brazil anali ndi chiŵerengero cha odwala malungo 560,000.” Nzika za Brazil 8,000 zimafa ndi malungo pachaka. Tsopano wofufuza wina wa ku Colombia, Dr. Manuel Elkin Patarroyo, wadza ndi lingaliro lina—katemera wa kemikolo ya synthetic amene amagulidwa pamtengo wa 30 cents chabe pamipimo itatu. “Wotsika mtengo kuposa mtengo wa Coca-Cola [mu Colombia],” anatero Dr. Patarroyo. Patsopano lino katemerayo wakhaladi wamphamvu mwa odwala pafupifupi 67 peresenti amene anapatsidwa katemerayo. Pamene kuli kwakuti sali yankho lenileni pamalungo akuphawo, imeneyi ikuwonekera kukhala ili njira yaikulu yopita patsogolo munkhondo yolimbana ndi matenda a malungo.