Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 3/8 tsamba 9-10
  • Dziko Lopanda Upandu—Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lopanda Upandu—Motani?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutuluka m’Magulu a Apandu
  • Masukani Pamzimu wa Dziko
  • Kodi Nchifukwa Ninji Upandu Wolinganiza Ukuwonjezeka?
    Galamukani!—1997
  • Mmene Upandu Wolinganiza Umakukhudzirani
    Galamukani!—1997
  • Kumasuka ku Upandu Wolinganiza—“Ndinali wa Yakuza”
    Galamukani!—1997
  • Nchifukwa Ninji Pali Upandu Wochulukira Chotero?
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 3/8 tsamba 9-10

Dziko Lopanda Upandu—Motani?

NKHONDO yolimbana ndi upandu wolinganiza ikumenyedwa padziko lonse. “Pakhala chipambano chachikulu pakulimbana ndi Mafia panthaŵi yaifupi kwambiri,” inatero U.S.News & World Report, “kwenikweni chifukwa cha lamulo limodzi, lija la Racketeer Influenced and Corrupt Organizations Act (Lamulo la Mabungwe Olamuliridwa ndi Chinyengo ndi Aukatangale), kapena kuti RICO.” Limalola kuzenga mlandu magulu a apandu pachifukwa cha zochita zakutizakuti zachinyengo, osati chabe pazochita za munthu mmodzi. Zimenezi limodzi ndi mauthenga opezedwa mwa kutcha zogwira uthenga m’mawaya a telefoni ndi kwa mamembala aukazitape m’maguluwo ofuna kuti awachitire chifundo zathandiza kwambiri pankhondo yolimbana ndi Mafia ku United States.

Nakonso ku Italy, boma likulimbana mwamphamvu ndi magulu a apandu. Kumadera monga Sicily, Sardinia, ndi Calabria, kumene upandu wolinganiza wavutitsa kwambiri, magulu a asilikali aikidwa kuti aziyendera nyumba zoloŵamo onse ndi magawo ofunika kuti aletse kuukira kwa apandu. Boma limaona zimenezi ngati nkhondo yachiweniweni. Pokhala kuti atsogoleri a mbiri yoipa a magulu a apandu ali m’ndende ndipo yemwe kale anali nduna yaikulu ya boma akumzenga mlandu wakuti anali wogwirizana ndi Mafia, Italy tsopano akuona zotulukapo zabwino.

Ku Japan, boma linaika ziletso pa yakuza pamene linaika Anti-Organized Crime Law (Lamulo Loletsa Upandu Wolinganiza) pa March 1, 1992. Mwa lamuloli, pamene gulu alitcha kuti ndi la upandu wolinganiza, amaliletsa kuchita zinthu zokakamiza mwachiwawa 11, kuphatikizapo kufuna ndalama zachitseka pakamwa, kukhala ndi phande pakunyengezera kupereka chitetezo, ndi kuloŵerera pakuthetsa mikangano kuti awalipire. Mwa kuona kuti lamulo limeneli likutsatiridwa, boma likufuna kuchotsapo magwero onse a ndalama za maguluwa. Lamulolo ladzetsa mavuto aakulu pa magulu a apandu. Magulu ena asweka, ndipo mtsogoleri wina wa apandu anadzipha—mwachionekere chifukwa cha kuumitsa lamulo limeneli.

Ndithudi, maboma ndi mabungwe oona kuti malamulo akutsatiridwa akulimbikira kulimbana ndi upandu wolinganiza. Ngakhale zili choncho, Mainichi Daily News, ponena za msonkhano wa oweruza ndi akuluakulu a polisi a padziko lonse umene unaliko mu 1994, inati: “Upandu wolinganiza ukulimbabe ndi kulemerabe pafupifupi kumbali iliyonse ya dziko lapansi, kukundika ndalama zokwana madola 1,000,000,000,000 zonse pamodzi pachaka.” Mwachisoni, kuyesayesa kwa anthu kuchotsapo magulu a apandu padziko lapansi nkopereŵera. Chifukwa china chimene zimenezi zakhalira choncho nchakuti chiweruzo samachipereka msanga ndipo chimakhala chosatsimikizika. Anthu ambiri amaona malamulo kaŵirikaŵiri kukhala okomera mpandu, osati wochitiridwa upandu. Zaka zoposa 3,000 kalelo Baibulo linati: “Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.”—Mlaliki 8:11.

Kutuluka m’Magulu a Apandu

Kuwonjezera pa kulimbana ndi upandu wolinganiza kuchokera kunja, maboma ayesa kuthandiza a mkati mwake kutuluka m’magulu a upanduwo. Kachitidwe kameneka sikapafupi. Malinga ndi mwambi wakale, “njira yokha yosiyira Umafia ndiyo m’bokosi lamaliro.” Kuti membala alekane ndi gulu la yakuza, ayenera kulipira ndalama zambiri kapena ayenera kumdula chala cha kaninse kapena mbali ya chalacho. Kuwonjezera pa mantha a kulekana ndi magulu achizemberawo, amene kale anali membala wa gulu laupandu ayenera kudziŵa kuti zidzamuvuta kukhala ndi moyo woonekera. Akafunsira ntchito, adzamkanira nthaŵi zambiri. Komabe, m’maiko ena, apolisi amakambitsirana mwachinsinsi ndi mamembala a maguluwa amene akuyesa kutulukamo koma akuvutika kwambiri kupeza ntchito yabwino.

Polimbana ndi chitsutso cha banja laupandulo ndi tsankhu la anthu, membala wa gulu afunikira chisonkhezero chachikulu kuti asabwerere m’mbuyo. Kodi nchiyani chingamsonkhezere? Chingakhale chikondi cha pa banja lake, kufunitsitsa moyo wamtendere, kapena chikhumbo cha kuchita chabwino. Komabe, chisonkhezero chachikulu kopambana chikusonyezedwa bwino ndi nkhani ya Yasuo Kataoka m’nkhani yotsatira.

Yasuo Kataoka ndi mmodzi wa mazana amene asinthiratu moyo wawo. Achotsa mikhalidwe yaunyama yomwe anali nayo ndipo m’malo mwake aikamo umunthu watsopano ‘wolengedwa monga mwa chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.’ (Aefeso 4:24, NW) Tsopano, anthu omwe kale anali ngati mimbulu akukhala mwamtendere pakati pa nzika zoleza mtima zonga ana a nkhosa, ndipo akuthandizanso ndi ena!—Yesaya 11:6.

Masukani Pamzimu wa Dziko

Monga tachulira m’nkhani yathayo, magulu onse a apandu sindiwo okha akulamulidwa ndi ulamuliro umodzi wosaoneka wa Satana Mdyerekezi komanso dziko lonse. Anthu sakuzidziŵa nkomwe zimenezi, koma Satana walinganiza dziko kuti likwaniritse zonulirapo zake zaupandu. Monga momwe magulu aupandu amaperekera chuma ndi kukhala ndi mabanja ongopeka, iye akudzisonyeza ngati mbuye wochitira ena zabwino mwa kupatsa anthu chuma, zosangalatsa, ndi mkhalidwe wa umodzi. Ngakhale simukudziŵa kalikonse, mwina mungakhale mutanyengedwa ndi machenjera ake oipa. (Aroma 1:28-32) Baibulo limatiuza kuti “ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu.” (Yakobo 4:4) Nkwangozi kupanga chibale ndi dzikoli, limene Satana akulilamulira. Mlengi wa chilengedwe chonse wakonzekeretsa makamu a angelo olamulidwa ndi Yesu Kristu kugwira Satana ndi ziŵanda zake kuti ayeretse dziko mwa kuchotsapo chisonkhezero chawo choipa.—Chivumbulutso 11:18; 16:14, 16; 20:1-3.

Choncho kodi mungamasuke motani pachisonkhezero cha dziko la Satana? Osati mwa kukhala ndi moyo wodzipatula kwa ena koma mwa kumasuka pamaganizo ndi malingaliro omwe adzaza dziko lerolino. Kuti muchite zimenezo, mudzafunikira kulimbana ndi machenjera a Satana owopsera ndi kukana zonyengerera zimene amapereka kuti anthu asamthaŵe. (Aefeso 6:11, 12) Zimenezi zidzafuna kudzimana, koma mungamasuke monga achitira ena ngati ndinu wotsimikiza mtima ndipo ngati mugwiritsira ntchito thandizo limene Mboni za Yehova zikupereka.

Kodi nchiyani chidzatsatirapo Mulungu atayeretsa dziko lachipwirikitili? “Adzadula mbumba za oipa,” likutero Baibulo, ndipo likupitiriza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:28, 29) Ndiyeno, sipadzakhala chifukwa choopera awo omwe anali ndi mikhalidwe yaunyama, popeza adzakhala atasandulizidwa ndi ‘kudziŵa Yehova,’ kumene kudzadzaza dziko lapansi.—Yesaya 11:9; Ezekieli 34:28.

Lerolino kusandulika kumeneku kukuchitikadi, monga momwe ikusonyezera nkhani yotsatira yosimba za moyo wa yemwe kale anali wa yakuza ku Japan.

[Chithunzi patsamba 10]

M’dziko latsopano la Mulungu, onse adzasangalala ndi ntchito ya manja awo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena