Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 4/8 tsamba 21-23
  • Kuchita Mfunzi—Kodi Kumavulaza Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchita Mfunzi—Kodi Kumavulaza Motani?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mfunzi Nchiyani?
  • Kukhala Wamfunzi
  • Zotsatirapo Zosatha
  • Mmene Mungasinthire
  • Kupezerera Ena Zina mwa Zoyambitsa Zake ndi Zotsatirapo Zake
    Galamukani!—2003
  • Kuthana ndi Khalidwe Lopezerera Ena
    Galamukani!—2003
  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kupezerera Ena ndi Vuto la Padziko Lonse
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 4/8 tsamba 21-23

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kuchita Mfunzi—Kodi Kumavulaza Motani?

‘Ndikungomseŵeretsa basi! Kodi pali cholakwa apa? Ndi iko komwe, Ron amafuna zomwezo.’

MWINAMWAKE ndinu wokulirapo ndi wamphamvu kuposa anzanu ambiri. Kapena mwina ndinu wochenjeretsa, wonyodola, ndi wandewu. Mulimonse mmene zingakhalire, kuopseza, kunyodola, kapena kumseka munthu wina momchititsa manyazi kumakhala kwapafupi kwa inu.

Ngakhale kuti kuchitira ena mfunzi kungaseketse mabwenzi anu, si nkhani yaing’ono imeneyo. Kunena zoona, ofufuza ena akupeza kuti kuchita mfunzi kumavulaza kwambiri ovutitsidwawo kuposa mmene anaganizira. Pofunsa achichepere ausinkhu wopita kusukulu ku United States, anapeza kuti “90 peresenti ya ochitidwa mfunziwo anali kudandaulanso ndi zotulukapo zina—kutsika magiredi awo, kukula kwa nkhaŵa, kutayikidwa mabwenzi kapena kusoŵa nthaŵi yocheza.” Ku Japan wachichepere wazaka 13 “anadzimangirira pambuyo polemba kalata yaitali yolongosola za kuchitidwa mfunzi kwake zaka zitatu.”a

Kodi nchiyani chimampangitsa munthu kukhala wamfunzi? Ndipo ngati inu muli wotero, kodi mungasinthe motani?

Kodi Mfunzi Nchiyani?

Baibulo limanena za amfunzi omwe anakhalako Chigumula cha Nowa chisanachitike. Ankatchedwa Anefili—liwu limene limatanthauza “ogwetsa ena.” M’nthaŵi ya nkhanza yawo “dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.”—Genesis 6:4, 11.

Komabe, simutofunikira kumenya kapena kuvutitsa anthu kuti mutchedwe wamfunzi. Aliyense amene amachitira anthu ena mwankhanza—makamaka ofooka kapena osalimba— angatchedwe wamfunzi. (Yerekezerani ndi Mlaliki 4:1.) Amfunzi amayesa kuopseza, kapena kulamulira. Koma ambiri amagwiritsira ntchito milomo yawo, osati nkhonya zawo. Ndithudi, kuchita mfunzi pa malingaliro ndiko mtundu wozoloŵereka wa kusautsa kumeneku. Choncho kumaphatikizapo chipongwe, mwano, kunyodola, ndi kutukwana.

Komabe, nthaŵi zina mfunzi ina siyachindunji. Mwachitsanzo, talingalirani zimene zinachitikira Lisa.b Anakula ndi gulu la atsikana anzake. Koma pamene anangofika zaka 15, zinthu zinayamba kusintha. Lisa anakongola kopambana ndipo anthu ambiri anayamba kumamcheukira. Akulongosola kuti: “Mabwenzi anga anayamba kumandinyalanyaza ndi kundinenera za mwano kumbali kapena ndikumva.” Anafalitsanso mabodza onena za iye, poyesa kuwononga mbiri yake. Inde, atasonkhezeredwa ndi nsanje, anamchita mfunzi mwanjira yankhanza ndi yopanda chifundo.

Kukhala Wamfunzi

Kaŵirikaŵiri munthu amakhala wandewu chifukwa cha mkhalidwe wa kunyumba kwawo. “Atate wanga anali wandewu,” anatero wachichepere wotchedwa Scott, “choncho ndinalinso wandewu.” Nayenso Aaron mkhalidwe wa kwawo unali wovuta. Akukumbukira kuti: “Ndinazindikira kuti anthu anadziŵa za mkhalidwe wa banja langa—kuti unali wosiyana—ndipo sindinafune kuti anthu azindimvera chisoni.” Chotero pamene Aaron anali m’maseŵero, anafuna kupambana basi. Koma kupambanako sikunamkhutiritse. Anali kuwanyodola ochita naye mpikisanowo—kuwaputa pakulephera kwawo.

Wina ndi Brent yemwe analeredwa ndi makolo oopa Mulungu. Koma akuvomereza kuti: “Ndinkaseketsa anthu, koma nthaŵi zina sindinadziŵe poimira, ndipo ndinkakhumudwitsa ena.” Kufuna kwake kuseka ndi kutinso anthu amtame kunampangitsa Brent kusasamala malingaliro a anthu ena.—Miyambo 12:18.

Achichepere ena imawasonkhezera ndi wailesi yakanema. Mafilimu a upandu amatamanda ‘majaha okanga’ ndipo amachititsa kuganiza kuti kukhala wachifundo si chamuna. Nthabwala zotchuka nzodzala ndi mawu onyodola okhaokha. Kaŵirikaŵiri malipoti a panyuzi amatchula za ndewu ndi mawu onyozana onenedwa pa zochitika za maseŵero. Mabwenzi athu amasonkhezeranso mmene timachitira ndi ena. Pamene anzathu ali amfunzi, nkwapafupi kwa ife kungoloŵerera m’gululo kuopera kuti angatembenukirenso ife.

Mumkhalidwe uliwonse, ngati mumachita machenjera a kuchita mfunzi, ndiye kuti omwe mukuchita mfunziwo sindiwo okha amene akuvulala.

Zotsatirapo Zosatha

Magazini yotchedwa Psychology Today ikuti: “Kuchita mfunzi kungayambire paubwana, koma kumapitiriza mpaka munthu atakula.” Nkhani ina ya kufufuza kofalitsidwa mu The Dallas Morning News inanena kuti “65 peresenti ya anyamata odziŵika kukhala amfunzi a m’giredi yachiŵiri, pomafika zaka 24 anali atachita kale upandu waukulu.”

Zoona, sikuti amfunzi onse amakhala apandu. Koma ngati muzoloŵera kumangotosa ena m’maso mudzagwera m’mavuto aakulu mtsogolo. Mutaloŵa nazo muukwati, zingachititse nsautso yaikulu kwa mnzanu wa muukwati ndi kwa ana anu. Popeza olemba ntchito amakonda anthu odziŵa kumvana bwino ndi ena, zingakumanitseni mwaŵi wa ntchito. Mtsogolonso mungamanidwe mathayo mumpingo wachikristu. “Tsiku lina, ndingakonde kudzayenerera kukhala mkulu,” anatero Brent, “koma atate wanga anandithandiza kuzindikira kuti anthu sangabwere kwa ine ndi zothetsa nzeru zawo ngati amaganiza kuti mwina ndingawayankhe kanthu kena kamwano.”—Tito 1:7.

Mmene Mungasinthire

Si nthaŵi zonse pamene timaona zolakwa zathu bwinobwino. Malemba akutichenjeza kuti wina “adzidyoletsa yekha m’kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.” (Salmo 36:2) Choncho mungapemphe kholo, bwenzi lodalirika, kapena Mkristu wokhwima kuti azikuyang’anirani. Inde, kuuzidwa choona kumapweteka, koma kungakuthandizeni kuona masinthidwe omwe muyenera kuchita. (Miyambo 20:30) “Ndiganiza kuti kumvetsera ndicho chinthu chachikulu chimene chinandithandiza,” akutero Aaron. “Omwe anali oona mtima anandiuza chimene ndinali kulakwa. Nthaŵi zonse sindinakonde kumva zimenezo, koma zinali zofunikira kwenikweni kwa ine.”

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kusintha modabwitsa umunthu wanu wonse? Ayi, nkotheka kuti kungakhale chabe [kungowongolera, NW ] kuganiza kwanu ndi makhalidwe anu ena. (2 Akorinto 13:11) Mwachitsanzo, mwina kufikira tsopano mumadziona ngati wopambana ena chifukwa cha usinkhu, nyonga, kapena nzeru zanu. Koma Baibulo limatilangiza kukhala ‘odzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.’ (Afilipi 2:3) Zindikirani kuti ena—mosasamala kanthu za usinkhu kapena nyonga—ali ndi mikhalidwe yokhumbirika imene inu mulibe.

Muyeneranso kuleka chizoloŵezi chakukhala wandewu kapena wolamulira. Menyerani nkhondo ‘kusapenyerera zanu za nokha, koma kupenyereranso za anzanu.’ (Afilipi 2:4) Ngati mukufuna kulankhula, teroni popanda kukhala wachipongwe, wonyodola, kapena wonyoza.—Aefeso 4:31.

Ngati mtima wanu ukufuna kuchita mfunzi, kumbukirani kuti Mulungu anawononga Anefili amfunzi aja. (Genesis 6:4-7; 7:11, 12, 22) Patapita zaka mazana ambiri, m’masiku a mneneri Ezekieli, Mulungu anaipidwa kwambiri ndi aja anali ndi liwongo la ‘kukankha’ ndi ‘kugunda’ opanda chithandizo. (Ezekieli 34:21) Kudziŵa kuti Yehova amadana ndi mfunzi kungathandize kwambiri wina kupanga masinthidwe ofunikawo!

Kusinkhasinkha mwapemphero mapulinsipulo a Baibulo kumathandizanso. Lamulo la Chikhalidwe limati: “zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Pamene mulakalaka kuopseza wina, dzifunseni kuti: ‘Kodi ineyo ndimafuna kuvutitsidwa, kuopsezedwa, kapena kunyazitsidwa? Nangano bwanji ndikuchitira ena zimenezo?’ Baibulo limatilamula ‘kukhalirana okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo.’ (Aefeso 4:32) Yesu anaika chitsanzo changwiro pankhani imeneyi. Ngakhale anali woposa anthu ena onse, anachita ndi aliyense mokoma mtima, mwachifundo, ndi mwaulemu. (Mateyu 11:28-30) Tayesani kuchita zofananazo pamene mukumana ndi wina wofookerapo kuposa inu—kapena ngakhale wina yemwe amakukwiyitsani.

Koma bwanji ngati khalidwe lanu la ndewu linayamba chifukwa chakupsa mtima ndi mmene amachitira nanu kunyumba? Nthaŵi zina mkwiyo umenewo ungalungamitsidwe. (Yerekezerani ndi Mlaliki 7:7.) Komabe, ngakhale zili choncho, Baibulo limatiuza kuti munthu wolungamayo Yobu anachenjezedwa kuti: “Muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo; . . . Chenjerani, musalunjike kumphulupulu.” (Yobu 36:18, 21) Ngakhale ngati mukuchitidwa nkhanza, simuyenera kuchita ena nkhanza. Chinthu chabwinopo chingakhale kukambitsirana ndi makolo anu. Ngati amakuchitani nkhanza kwambiri, mungafune chithandizo cha ena kuti akutetezereni.

Kusintha kungakhale kovuta, koma nkotheka. Brent akuti: “Chimenechi ndimachipempherera pafupifupi tsiku lililonse, ndipo Yehova wandithandiza kuwongokera bwino.” Pamene nanunso mukuwongolera njira zimene mumachitira ndi anthu, mosakayika mudzaona kuti anthu adzakukondani. Kumbukirani, kuti anthu angaope amfunzi, koma palibe yemwe amawakonda.

[Mawu a M’munsi]

a Ponena za nkhani ya mmene ofunzidwa angapeŵere kusautsidwa, onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . .Nchiyani Chomwe Ndingachite Ponena za Ovutitsa ku Sukulu?,” m’kope lathu la August 8, 1989.

b Maina ena asinthidwa.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

“Kuchita mfunzi kungayambire paubwana, koma kumapitiriza mpaka munthu atakula”

[Chithunzi patsamba 22]

Mawu onyoza ndi mtundu wina wa kuchita mfunzi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena