Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 12
  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi anthu amavutitsa anzawo m’njira ziti?
  • N’chifukwa chiyani anthu ena amavutitsa anzawo?
  • Kodi ndi anthu otani amene amakonda kuvutitsidwa?
  • Kodi muyenera kuchita chiyani mukamavutitsidwa?
  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?
    Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
  • Kuthana ndi Khalidwe Lopezerera Ena
    Galamukani!—2003
  • Kupezerera Ena Zina mwa Zoyambitsa Zake ndi Zotsatirapo Zake
    Galamukani!—2003
  • Kupezerera Ena ndi Vuto la Padziko Lonse
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 12

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

  • Kodi anthu amavutitsa anzawo m’njira ziti?

  • N’chifukwa chiyani anthu ena amavutitsa anzawo?

  • Kodi ndi anthu otani amene amakonda kuvutitsidwa?

  • Kodi muyenera kuchita chiyani mukamavutitsidwa?

Muwerengenso zimene anzanu ena ananena pa nkhaniyi komanso zimene mphunzitsi wina ananena. Pomaliza, muyankhe mafunsowo.

Kuvutitsidwa ndi ena si nkhani yaing’ono. Pakafukufuku wina amene anachitika ku Britain anapeza kuti achinyamata 40 pa 100 alionse amene anadzipha ankavutitsidwa ndi anzawo.

Kodi anthu amavutitsa anzawo m’njira ziti?

Kuwonjezera pa kumenyedwa, anthu amavutitsidwanso m’njira zosiyanasiyana monga zotsatirazi.

  • Mawu achipongwe. Mtsikana wina yemwe ali ndi zaka 20, dzina lake Celine, ananena kuti: “Sindidzaiwala mayina amene anzanga ankandipatsa komanso mawu amwano omwe ankandinena. Zomwe ankandinenazo zinkandipangitsa kudziona kuti ndine munthu wachabechabe, wosafunika komanso wopanda nzeru. Ndimaona kuti zikanakhala bwino akanamandimenya kusiyana n’kundinena mawu achipongwewo.”

  • Kukusala. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Haley anati: “Anzanga akusukulu anayamba kundisala. Masana pa nthawi ya chakudya, ankayesetsa kuti ndisapeze malo patebulo limene iwowo akhala. Kwa chaka chathunthu, ndinkangokhalira kulira komanso kumadya pandekha.”

  • Kukuipitsira mbiri pogwiritsa ntchito foni kapena kompyuta. Mnyamata wina wazaka 14 dzina lake Daniel anati: “Kungodina mabatani angapo pakompyuta, ungawonongeretu mbiri ya munthu wina, ngakhale moyo wake kumene. Ena angaganize kuti ndikungokokomeza, koma zimachitika.” Anthu ena amavutitsanso anzawo pafoni kapena pakompyuta potumiza zithunzi kapena mauthenga oipa kambiri.

N’chifukwa chiyani anthu ena amavutitsa anzawo?

Taonani zina mwa zifukwa zimene zimachititsa kuti anthu ena azivutitsa anzawo.

  • Nawonso ankavutitsidwa. Mnyamata wina dzina lake Antonio ananena moona mtima kuti: “Ndinatopa kwambiri ndi kuvutitsidwa ndi anzanga, choncho nanenso ndinayamba kuvutitsa ena n’cholinga choti anthu amene ankandivutitsa aja azindiona kuti ndine mnzawo. Patapita nthawi ndinazindikira kuti zomwe ndinkachitazo n’zolakwika kwambiri.”

  • Amatsanzira anthu olakwika. Munthu wina wolemba mabuku dzina lake Jay McGraw analemba m’buku lake lina kuti: “Nthawi zambiri achinyamata amavutitsa anzawo . . . potsanzira zimene makolo awo kapena abale awo amachita.”​—Life Strategies for Dealing With Bullies.

  • Amafuna azioneka ngati madolo koma amakhala odzikayikira. Katswiri wina wolemba mabuku dzina lake Barbara Coloroso, analemba m’buku lake lina kuti: “Ana ambiri amene amadzikayikira ndiponso amene alibe mtendere wam’maganizo amayamba kuvutitsa anzawo kuti aiwaleko mavuto awo komanso pofuna kuti azioneka ngati madolo.”​—The Bully, the Bullied, and the Bystander.

Kodi ndi anthu otani amene amakonda kuvutitsidwa?

  • Anthu amene amangokhala okhaokha. Achinyamata ena omwe ndi amanyazi kwambiri ndipo satha kucheza ndi ena amangokhala okhaokha. Zimenezi zimachititsa kuti azipezereredwa ndi anthu ovutitsa anzawo.

  • Achinyamata amene akuoneka mosiyana ndi anzawo. Achinyamata ena amavutitsidwa ndi anzawo chifukwa choti ali ndi maonekedwe osiyana ndi anzawowo. Iwo angavutitsidwe chifukwa chosiyana nawo mtundu, chipembedzo ngakhalenso ngati ali olumala.

  • Achinyamata odzikayikira. Anthu okonda kuvutitsa ena angazindikire anthu odzikayikira. Nthawi zambiri munthu wodzikayikira amapezereredwa chifukwa sangabwezere.

Kodi muyenera kuchita chiyani mukamavutitsidwa?

  • Musasonyeze kuti zakukhudzani. Mtsikana wina dzina lake Kylie anati: “Anthu amene amakonda kuvutitsa ena amafuna kudziwa ngati zimene akuchitazo zakukhudzani. Mukangokhala osasonyeza kuti zakukhudzani, amaona kuti sanapindule chilichonse ndipo amakusiyani.” Baibulo limati: “Wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.”​—Miyambo 29:11.

  • Musabwezere. Kubwezera sikuthandiza chilichonse koma kumangowonjezera mavuto. Baibulo limati: “Musabwezere choipa pa choipa.”​—Aroma 12:17; Miyambo 24:19.

  • Musamapite dala kumalo amene anthu ena angakuvutitseni. Muziyesetsa kupewa malo aliwonse amene mukudziwiratu kuti mungakumaneko ndi anthu omwe angakuvutitseni.​—Miyambo 22:3.

  • Chitani zosiyana ndi zimene munthu amene akukuvutitsaniyo akuyembekezera. Baibulo limati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo.”​—Miyambo 15:1.

  • Muzichita tinthabwala. Mwachitsanzo, munthu yemwe akukuvutitsani akakunyozani kuti ndinu wonenepa kwambiri, mukhoza kungovomereza moseka kenako n’kunena kuti: “Ndiyesetsa kuti ndiwondeko pang’ono.”

  • Chokanipo. Mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Nora, anati: “Anthu ena akamakuvutitsa koma iwe n’kungochokapo osayankha chilichonse, zimasonyeza kuti ndiwe wanzeru komanso wolimba mtima kuposa anthu amene akukuvutitsawo. Zimasonyezanso kuti ndiwe wodziletsa, khalidwe lomwe anthu ovutitsa anzawo sakhala nalo.”

  • Musamachite zinthu modzikayikira. “Mukamachita zinthu modzikayikira kapena mwamantha, anthu okonda kuvutitsa anzawo angadziwe ndipo angakuonerereni n’kumakuvutitsani.”​—Anatero mtsikana wina dzina lake Rita.

  • Muziuza ena. Kafukufuku wina anapeza kuti anthu oposa hafu ya anthu onse amene amavutitsidwa pa Intaneti sauza ena poopa kuti achita manyazi (makamaka anyamata) komanso poopa kuti munthu yemwe amunenerayo akadziwa, akhoza kuwakhaulitsa kwambiri. Koma kumbukirani kuti anthu ovutitsa anzawo angakuvutitseni kwambiri akadziwa kuti palibe amene mungamuuze. Choncho kuuza ena kungathandize kuti asiye kukuvutitsani.

Zimene anzanu ena ananena

“Muzipewa malo amene angachititse kuti anthu ena akupezerereni n’kuyamba kukuvutitsani. Muzikumbukiranso kuti anthu amene amakonda kuvutitsa anzawo amakhala akuvutika ndi mavuto awo. Mukadziwa zimenezi, simungadandaule kwambiri ndi zimene angakuneneni.”​—Antonio.

“Musamachite zinthu modzikayikira. Musamaopenso kunena zimene mumakhulupirira. Anthu ambiri amene amakonda kuvutitsa anzawo angakusiyeni akaona kuti simukuwapatsa mpata komanso simukuwaopa.​​—Jessica.

Zimene mphunzitsi wina ananena

“Kuvutitsa ena si nkhani yaing’ono. Pasukulu imene ndimaphunzitsa, nthawi zambiri ana amakangana komanso kumenyana m’kalasi, ngakhale ana akuluakulu. Ana ena amasangalala akamavutitsa anzawo chifukwa amaona kuti zimenezi zikuwachititsa kuti akhale otchuka komanso kuti aziopedwa.

“Nthawi zambiri ana omwe amavutitsidwa ndi anzawo sauza ena chifukwa amaopa kuti munthu yemwe akuwavutitsayo awakhaulitsa kwambiri akadziwa zimenezi ndiponso kuti anzawo a m’kalasi aziwanyoza. Chifukwa chinanso n’chakuti amaona kuti palibe chimene chingachitike kwa munthu yemwe akuwavutitsayo. Ngakhale zili choncho, ndikulimbikitsa aliyense amene akuvutitsidwa kuti aziuza ena. Kuuza ena n’kothandiza ndipo kungachititse kuti anthu ena asadzavutitsidwenso.”​—Anatero Jenilee, yemwe anali mphunzitsi ku United States.

Mafunso

Zoona kapena Zonama?

  1. Anthu akhala akuvutitsa anzawo kuyambira kale kwambiri, zaka masauzande zapitazo.

  2. Kuvutitsa ena si koopsa, n’kucheza basi.

  3. Chinthu chabwino kwambiri chimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani, n’kubwezera.

  4. Ngati anthu ena akukuvutitsani, ndiye kuti muli ndi vuto.

  5. Anthu ena amene amavutitsidwa amayambanso kuvutitsa ena.

  6. Mukaona munthu wina akuvutitsidwa, ndi bwino kungonyalanyaza.

  7. Anthu amene amavutitsa ena amakhala ndi mavuto awo komanso amakhala odzikayikira.

  8. Anthu okonda kuvutitsa anzawo akhoza kusiya khalidwe loipali.

MAYANKHO

  1. Zoona. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza za Anefili, anthu omwe dzina lawoli limatanthauza “Ogwetsa Anzawo.”​​—Genesis 6:4.

  2. Zonama. Munthu angathe kufa chifukwa chovutitsidwa. Ndipo n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amene amavutitsidwa mosowetsa mtendere amafika podzipha.

  3. Zonama. Nthawi zambiri anthu omwe amavutitsa ena amakhala amphamvu kuposa anthu amene akuwavutitsawo, ndipo kubwezera sikungathandize.

  4. Zonama. Palibe munthu amene ali woyenerera kuti azivutitsidwa. Vuto limakhala ndi munthu amene akuvutitsa anzakeyo.

  5. Zoona. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena akakhala ndi mavuto awo amaphwetsera pa ena n’kumawavutitsa. Ndipo ngati anavutitsidwapo amafuna abwerezere pa ena.

  6. Zonama. Munthu amene akungoonerera ena akuvutitsidwa sangakhale wosalakwa. Choncho mukaona ena akuvutitsidwa koma inu osanena chilichonse, mumasonyeza kuti mukugwirizana nazo.

  7. Zoona. Ngakhale kuti anthu ena amene amavutitsa anzawo amakhala odzidalira, ambiri amakhala akuvutika ndi mavuto awo ndipo amavutitsa ena kuti azisangalalako.

  8. Zoona. Ngati atathandizidwa, anthu omwe amavutitsa anzawo akhoza kusintha maganizo komanso khalidwe lawo.​​—Aefeso 4:​23, 24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena