Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ypq funso 5 tsamba 15-17
  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?
  • Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kuthana ndi Khalidwe Lopezerera Ena
    Galamukani!—2003
  • Kupezerera Ena Zina mwa Zoyambitsa Zake ndi Zotsatirapo Zake
    Galamukani!—2003
  • Kupezerera Ena ndi Vuto la Padziko Lonse
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
ypq funso 5 tsamba 15-17
Mnyamata akuvutitsidwa ndi mnyamata wina, ana ena a m’kalasi ali pompo

5

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Zimene mungachite zingapangitse kuti asiye kukuvutitsani kapena azikuvutitsani kwambiri.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Taganizirani izi: Mnyamata wina dzina lake Thomas sakufunanso kupita kusukulu chifukwa chakuti anzake akhala akufalitsa nkhani zabodza zokhudza iyeyo. Izi zapangitsa kuti azimupatsa mayina achipongwe. Ena amamuphumitsa mabuku kenako n’kukhala ngati inali ngozi, kapena kumukankha n’kuthawa iyeyo potembenuka osadziwa kuti wamukankha ndani. Dzulo laliwisili ena analemba zomuopseza pa intaneti.

Kodi inuyo mukanakhala Thomas, mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Musaganize kuti palibe chimene mungachite. Ndipotu mungathe kupangitsa kuti munthu asiye kukuvutitsani popanda kumubwezera. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

  • MUSAMASONYEZE KUTI ZAKUKHUDZANI. Baibulo limati: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.” (Miyambo 29:11) Mukayesetsa kuti muoneke ngati sizinakukhudzeni, anthu amene akukuvutitsaniwo akhoza kusiya.

  • MUSAMABWEZERE. Baibulo limati: “Musabwezere choipa pa choipa.” (Aroma 12:17) Kubwezera kungachititse kuti zinthu ziipireipire.

  • MUSAMAPITE PAMALO AMENE ANTHU ANGAKUVUTITSENI. Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Choncho muziyesetsa kupewa malo amene mukudziwiratu kuti mungakumaneko ndi anthu omwe angakuvutitseni.

  • MUZICHITA ZIMENE SAKUYEMBEKEZERA. Baibulo limati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Mwina mungangoyankha mwanthabwala. Mwachitsanzo, ngati munthu wakunyozani kuti ndinu wonenepa kwambiri, mukhoza kungovomereza moseka n’kunena kuti: “Ndiyesetsa kuti ndiwondeko.”

  • MUZINGOCHOKAPO. Mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Nora, anati: “Anthu ena akamakuvutitsa, iwe n’kungochokapo, zimasonyeza kuti ndiwe wanzeru komanso wolimba mtima kuposa iwowo. Zimasonyezanso kuti ndiwe wodziletsa, khalidwe lomwe anthu ovutitsa anzawo sakhala nalo.”—2 Timoteyo 2:24.

  • MUSAMACHITE ZINTHU MODZIKAYIKIRA. Amene amavutitsa anzawo amapezerera anthu amene amadzikayikira chifukwa amadziwa kuti sangawabwezere. Koma akaona kuti simukuwapatsa mpata komanso simukuwaopa, angakusiyeni.

  • MUZIUZA ENA. Munthu wina amene anali mphunzitsi anati: “Ndikulimbikitsa aliyense amene akuvutitsidwa kuti aziuza ena. Kuuza ena n’kothandiza ndipo kungachititse kuti anthu ena asadzavutitsidwenso.”

Mnyamata wina sakuchita mantha pamene akuvutitsidwa

Kusadzikayikira kungapangitse kuti mukhale olimba mtima kuposa munthu amene akukuvutitsani

KODI MUKUDZIWA?

Kuwonjezera pa kumenyedwa, anthu amavutitsidwanso m’njira zina monga:

  • Mawu a ngati moto akutuluka m’kamwa mwa munthu wovutitsa anzake

    Mawu achipongwe. Mtsikana wina wazaka 20 dzina lake Celine, ananena kuti: “Sindidzaiwala mayina amene anzanga ankandipatsa komanso zimene ankandinena. Ndinkadziona kuti ndine munthu wachabechabe, wosafunika komanso wopanda nzeru. Bola akanangondimenya.”

  • Mnyamata wakhala yekha chifukwa choti anzake akumusala

    Kukusala. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Haley anati: “Anzanga akusukulu ankandisala. Pa nthawi ya chakudya, sankafuna kuti ndikhale patebulo yawo. Kwa chaka chathunthu, ndinkangokhalira kulira komanso kumadya pandekha.”

  • Mtsikana akuchoka pa kompyuta ataona mauthenga omunyoza amene ena amutumizira

    Kukuipitsira mbiri pa intaneti. Mnyamata wina wazaka 14 dzina lake Daniel anati: “Kungodina mabatani angapo pakompyuta, ungawonongeretu mbiri ya munthu wina, ngakhale moyo wake kumene. Ena angaganize kuti ndikungokokomeza, koma zimachitika.”

Mafunso

ZOONA KAPENA ZONAMA?

MAYANKHO

1 Anthu akhala akuvutitsa anzawo kuyambira kale kwambiri.

1 Zoona. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza za Anefili, anthu omwe dzina lawoli limatanthauza “Ogwetsa Anzawo.”—Genesis 6:4.

2 Kuvutitsa ena si koopsa, n’kucheza basi.

2 Zonama. Achinyamata ambiri amene amavutitsidwa amafika podzipha.

3 Kuti anthu asiye kukuvutitsani, muyenera kubwezera.

3 Zonama. Nthawi zambiri anthu omwe amavutitsa ena amakhala amphamvu kuposa anthu amene akuwavutitsawo, ndipo kubwezera sikungathandize.

4 Mukaona munthu wina akuvutitsidwa, ndi bwino kungonyalanyaza.

4 Zonama. N’kulakwa kungoonerera ena akuvutitsidwa. Ngati simunena chilichonse, mumasonyeza kuti mukugwirizana nazo.

5 Anthu amene amavutitsa ena amakhala odzikayikira.

5 Zoona. Ngakhale kuti anthu ena amene amavutitsa anzawo amaoneka odzidalira, ambiri amakhala odzikayikira ndipo amavutitsa ena kuti mwina azisangalalako.

6 Anthu okonda kuvutitsa anzawo akhoza kusintha.

6 Zoona. Ngati atathandizidwa, anthu omwe amavutitsa anzawo akhoza kusintha.

ZOTI NDICHITE

  • Munthu wina atayamba kundivutitsa, ndingatani?

KUTI MUDZIWE ZAMBIRI

Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?

Onerani vidiyo yakuti, Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani? pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny. (Pitani pamene alemba kuti, ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena