Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 4/8 tsamba 4-7
  • Kupenda Minda Ina Yotchuka ya Maluŵa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Minda Ina Yotchuka ya Maluŵa
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Minda ya Maluŵa Yoyambirira
  • Minda ya Maluŵa ya Aluya ndi Minda ya Maluŵa ya Angelezi
  • Minda ya ku Mmaŵa
  • Chikondi Chimene Chili Kulikonse
  • Kukonda Kwathu Munda wa Maluŵa
    Galamukani!—1997
  • Chakudya Chochokera M’dimba Lanu
    Galamukani!—2003
  • Kodi Dzikoli Lidzakhaladi Paradaiso Kapena ndi Maloto Chabe?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Kodi Paradaiso Amene Baibulo Limatchula ali Kuti?
    Nsanja ya Olonda—2010
Galamukani!—1997
g97 4/8 tsamba 4-7

Kupenda Minda Ina Yotchuka ya Maluŵa

MUNTHU anayamba kuona Paradaiso m’munda wina pamalo otchedwa Edene, mwina chapafupi ndi Nyanja ya Van, ku Turkey wamakono. Mtsinje womwe unagaŵika kukhala mitsinje inayi unathirira munda umenewo wa Adamu ndi Hava, amene anayenera ‘kuulima ndi kuuyang’anira.’ Mmene kukanakhalira kosangalatsa kuyang’anira munda umene “mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya” inali paliponse mmenemo!—Genesis 2:8-15.

Edene unali mudzi wangwiro. Adamu ndi Hava ndi mbadwa zawo anayenera kuufutukula, mosakayikira akumatsanzira njira yabwino koposa imene Mulungu anapangira mudzi wawo woyamba. M’kupita kwa nthaŵi, dziko lonse lapansi linayenera kukhala paradaiso wodzala bwino ndi anthu. Koma kusamva dala kwa makolo athu oyamba kunachititsa kuti awapitikitse pamalo achisungiko ameneŵa. Mwachisoni, ena onse a m’banja la anthu anabadwira kunja kwa mudzi umenewu wa Edene.

Ngakhale zili choncho, mtundu wa munthu unapangidwa ndi Mlengi kuti uzikhala m’Paradaiso. Choncho zinali zachibadwa kuti mibadwo yakutsogolo izikapanga pokhala pawo ngati Paradaiso ameneyo.

Minda ya Maluŵa Yoyambirira

Minda ya maluŵa yotchedwa Hanging Gardens ya ku Babulo akuti inali chimodzi cha zochititsa chidwi za dziko lakale. Mfumu Nebukadinezara anaipangira mkazi wake Mmedi amene anali kufuna kwambiri nkhalango ndi zitunda zakwawo zaka zoposa 2,500 kalelo. Malo ameneŵa omangidwa mwaluso ndi njerwa okhala ndi masitepe okwera mamita 22, onse okhala ndi zomera zochuluka anali ndi nthaka yokwanira moti nkukulitsa mitengo yaikulu. Mfumukazi yofunitsitsa kwawo imeneyo iyenera kuti inamva bwino powongola miyendo pamalo okwera ameneŵa onga Edene.

Kulima minda ya maluŵa kunali kofala M’chigwa cha Nile chachonde ku Egypt. “Ku Egypt,” ikutero The Oxford Companion to Gardens, “ndiko kwachokera zithunzi za minda zakale koposa padziko lonse ndi kumene zamalimidwe . . . zinayamba kale kwambiri.” Pulani ya munda wa maluŵa wa mkulu wina wa Egypt ku Thebes, ya m’ma 1400 B.C.E., imasonyeza matamanda a madzi, misewu yaikulu ya mitengo m’mbali mwake, ndi nyumba za zosangulutsa. Kuchoka pa minda ya mfumu, minda ya pakachisi inali yachiŵiri kukongola kwake, yokhala ndi mitengo yake, maluŵa, ndi zitsamba zothiriridwa ndi mifuleni yokumba yochokera ku matamanda ndi nyanja zodzaza ndi mbalame za pamadzi, nsomba, ndi maluŵa a mtundu wa akakombo.—Yerekezerani ndi Eksodo 7:19.

Nawonso Aperisi anayamba nkale zolimalima maluŵa. Minda ya maluŵa ya ku Persia ndi Egypt inali yokongola kwambiri kwakuti pamene magulu ankhondo ogonjetsa a Alexander Wamkulu anabwerera ku Greece m’zaka za zana lachinayi B.C.E., anabwerako ndi mbewu, mitengo, ndi malingaliro ambirimbiri a zamalimidwe. Ku Athens, Aristotle ndi wophunzira wake Theophrastus anasonkhanitsa zomera zomachulukazo nayamba munda wa maluŵa, kuti aphunzire ndi kusiyanitsa zomera. Agiriki ambiri olemera anali ndi minda ya maluŵa yokongola monga Aigupto ndi Aperisi oyambirirawo.

Aroma okhala m’mizinda ankalima minda ya maluŵa pamakomo awo ochepawo a mumzinda. Olemera anapanga mapaki okongola osangulutsa panyumba zawo za kunja kwa mzinda. Ngakhale wolamulira wopondereza Nero anafuna kukhala ndi Edene wake, choncho mopanda chifundo anachotsa mabanja mazana ambiri, kugwetsa nyumba zawo, ndi kupanga paki yake ya mahekitala oposa 50 kuzungulira nyumba yake. Pambuyo pake, cha mu 138 C.E., panyumba ya Mfumu Hadrian ku Tivoli, kulima minda ya maluŵa kwa Aroma kunafika pachimake. Nyumbayo inali ndi mahekitala 243 a mapaki, matamanda a madzi, ndi akasupe.

Aisrayeli akale nawonso anali ndi minda ya maluŵa ndi mapaki. Wolemba mbiri wachiyuda Josephus analemba za mapaki osangalatsa okhala ndi mitsinje yambiri kumalo otchedwa Etamu, makilomita ngati 13 mpaka 16 kuchokera ku Yerusalemu. Mapaki a ku Etamu mwina angakhale pakati pa ‘mphanje, minda, matamanda a madzi, ndi nkhalango’ zimene Baibulo limati Solomo ‘anadzikonzera.’ (Mlaliki 2:5, 6) Kungotuluka kunja kwa Yerusalemu pa Phiri la Azitona panali Munda wa Getsemane, wodziŵika kwambiri chifukwa cha Yesu Kristu. Kunoko, Yesu anapeza malo obisala kumene anaphunzitsa ophunzira ake mwakachetechete.—Mateyu 26:36; Yohane 18:1, 2.

Minda ya Maluŵa ya Aluya ndi Minda ya Maluŵa ya Angelezi

Pamene magulu a nkhondo achiluya anafika kummaŵa ndi kumadzulo m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri C.E., iwo, monga Alexander, anapeza minda ya maluŵa ya ku Persia. (Yerekezerani ndi Estere 1:5.) “Aluya,” akulemba motero Howard Loxton “anapeza kuti minda ya maluŵa ya Aperisi inali yofanana kwambiri ndi paradaiso wolonjezedwa kwa okhulupirika m’Korani.” Monga kumene inachokera ku Persia, munda wa maluŵa wachiluya weniweni, kuchokera ku Moorish Spain mpaka ku Kashmir, unali kugaŵidwa panayi ndi mitsinje inayi yokumana pakati padziŵe kapena pakasupe, monga mitsinje inayi ya mu Edene.

Kumpoto kwa India, pafupi ndi Nyanja ya Dal m’Chigwa cha Kashmir chokongolacho, a Mogul olamulira m’zaka za zana la 17 anabzala minda yonga paradaiso yoposa 700. Imeneyi inapanga maonekedwe osiyanasiyana ochititsa kaso okhalanso ndi akasupe, zitunda, ndi mathithi aang’ono mazana ambiri. Nyumba yosangulutsa ya mwala wonyezimira wakuda yomangidwa pagombe la Nyanja ya Dal ndi Shah Jahan (yemwe anamanga Taj Mahal) idakali ndi mawu ozokota akuti: “Ngati padziko lapansi pali paradaiso, ali kuno, ali kuno, ali kuno.”

Zaka mazana angapo isanafike nthaŵiyo, Ulaya analoŵa m’nyengo ya Renaissance ya m’zaka za zana la 14 kuchoka m’Nyengo Zapakati. Malimidwe achiroma a minda ya maluŵa, omwe anazimiririka Nyengo Zapakati zitayamba m’zaka za zana lachisanu C.E., anayambanso kufala—nthaŵi ino tchalitchi chinali patsogolo. Dziko Lachikristu linali kuona munda wa maluŵa monga ‘paradaiso wogwirizira.’ Pulani ya m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi ya nyumba ya amonke ikusonyeza minda iŵiri yolembedwa kuti “Paradaiso.” Minda ya Dziko Lachikristu posapita nthaŵi inakhala yaikulu ndi yokongola kwambiri, koma m’malo mosonyeza zolinga zauzimu, yambiri inakhala zizindikiro za mphamvu ndi chuma.

Charles VIII wa France atagonjetsa Naples, Italy, mu 1495, analembera kwawo nati: “Simungakhulupirire minda yokongola imene ndili nayo mumzindawu . . . Ikuoneka monga kuti mwangosoŵa Adamu ndi Hava kuti ikhale paradaiso wa padziko lapansi.” Koma Charles akanakhala ndi moyo mpaka m’zaka za zana la 17, akanaona minda yaikulu ya Mfumu Louis XIV panthaka ya France. Buku lakuti The Garden likunenetsa kuti minda ya ku Palace of Versailles “tingainenebe kuti ndiyo yaikulu koposa ndi yokongola koposa padziko lonse.”

Komabe, nyengo ya Renaissance inapereka tanthauzo latsopano la paradaiso: chilengedwe chiyenera kukhala ndi cholinga kwa munthu wotseguka mutu amene ayenera kusintha munda wa maluŵa mwa kuchotsamo thengo lonse. Zonse mitengo ndi maluŵa anazilinganiza bwinobwino. Choncho, luso loyamba lachiroma—la kukulitsa mitengo ndi zitsamba mwa kuzimangirira ndi kuzidulira—linayambidwanso pamlingo waukulu kwambiri.

Ndiyeno, m’zaka za zana la 18 ndi 19, maulendo apanyanja ndi malonda anavumbulira maiko akumadzulo mitengo yatsopano ndi malimidwe ake. Kupanga minda ya maluŵa kunakhala ntchito yaikulu ku England. “Mu England wa m’zaka za zana la 18,” ikutero The New Encyclopædia Britannica, “munthu anatseguka maso kwambiri ndi kuona chilengedwe cha dziko limene ankakhalamo. M’malo mosintha chilengedwe cha dziko kuti chimyenere, iye anayamba kuganiza zosintha moyo wake kuti achiyenere.” Amuna monga William Kent ndi Lancelot Brown anapita patsogolo pa kukongoletsa malo ndi maluŵa. Brown anakonza malo oposa mazana aŵiri ku England. Amuna aŵiri amene anadzakhala mapulezidenti a United States, Thomas Jefferson ndi John Adams, anapita kukacheza ku England mu 1786 kuti aphunzire za minda ya maluŵa ya Angelezi.

Minda ya ku Mmaŵa

Malimidwe a ku China ayambukira kwambiri maiko a Kummaŵa monga momwe malimidwe a ku Egypt, Greece, ndi Rome ayambukirira maiko a Kumadzulo. Kwenikweni, Atchaina anali a chipembedzo cholambira zinthu zachilengedwe, ndipo anali kuona mitsinje, miyala, ndi mapiri monga mizimu yovala thupi ndipo anaziyesa zoyenera kulemekezedwa. Kenako, Chitao, Chikomfyushani, ndi Chibuda zinafala m’dzikomo ndi kupanga mitundu yawoyawo ya minda.

Kutsidya lina la Sea of Japan, minda yachijapani inali yamtundu wina, umene mpangidwe ndiwo wofunika kuposa maonekedwe ndipo kanthu kalikonse kali ndi malo akeake. Pofuna kuyerekezera mpangidwe ndi kusiyanasiyana kwa zinthu zachilengedwe pamalo ochepa, wolima munda wa maluŵa amaika miyala yake mosamala nabzala ndi kusamalira munda wake mwakhama. Zimenezi zimaoneka pa bonsai (kutanthauza “mtengo wamumtsuko”), luso la kukulitsa mtengo waung’ono kapena mwinamwake mitengo ingapo kuti ifike pamlingo wake woyenerera.

Ngakhale malimidwe ake akusiyana ndi a Kumadzulo, munda wa maluŵa wa Kummaŵa umasonyeza chikhumbo cha Paradaiso. Mwachitsanzo, m’nyengo ya Heian ku Japan (794-1185), akulemba motero wolemba mbiri ya minda ya maluŵa yachijapani Wybe Kuitert, olimawo anali kuyesa kupanga mkhalidwe wa “paradaiso wa padziko lapansi.”

Chikondi Chimene Chili Kulikonse

Kuphatikizapo ngakhale mitundu yokhalira uzimba ndi kutchera zipatso za m’thengo, imene inali kukhala m’minda “yachilengedwe”—nkhalango ndi madambo—onsewo amakonda minda ya maluŵa. Ponena za “Aaziteki a ku Mexico ndi Ainka a ku Peru,” likutero buku la Britannica, “atsogoleri a magulu a nkhondo amene anagonjetsa maikowa anasimba za minda ya maluŵa yokongola yazitunda zamasitepe, nkhalango, akasupe, ndi maiŵe okongola . . . yosasiyana ndi minda ya Kumadzulo.”

Inde, nkhalango zakale za m’mbali mwa Nile, minda ya maluŵa ya Kummaŵa, mapaki atsopano a m’mizinda, ndi minda ina yosiyanasiyana—kodi imeneyi ikuvumbulanji? Kuti munthu amalakalaka Paradaiso. Ponena za “kulakalaka Paradaiso” kwakalekale kumeneku, wolemba Terry Comito anati: “Minda ya maluŵa ndiyo malo amene anthu amamva kuti ali pamudzi.” Ndipo ndi munthu wotani amene sangakondwere kunena kuti ‘Kwathu kuli ngati Munda wa Edene’? Koma kodi Edene wapadziko lonse—ndipo osati wa olemera okha—ndi maloto okhaokha? Kapena kodi adzakhalakodi mtsogolo?

[Chithunzi patsamba 7]

Chithunzi cha minda ya maluŵa ya Hanging Gardens ya ku Babulo chojambulidwa ndi katswiri

[Chithunzi patsamba 7]

Munda wa malimidwe a ku Japan

[Chithunzi patsamba 7]

Versailles, France

M’mbiri yonse, anthu alakalaka Paradaiso

[Mawu a Chithunzi]

Ofesi ya Odzaona Malo ya Boma la France/Rosine Mazin

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena