Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 4/8 tsamba 3
  • Kukonda Kwathu Munda wa Maluŵa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukonda Kwathu Munda wa Maluŵa
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Minda Ingawongole Thanzi la Munthu
  • Kupenda Minda Ina Yotchuka ya Maluŵa
    Galamukani!—1997
  • Chakudya Chochokera M’dimba Lanu
    Galamukani!—2003
  • Munda Wokongola
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Munda Wokongola Mogometsa
    Galamukani!—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 4/8 tsamba 3

Kukonda Kwathu Munda wa Maluŵa

KODI mumasangalala ndi bata la munda wokongola monga pobisalira phokoso ndi moyo wotanganitsa? Ngati mukufuna kuchita pikiniki ndi banja lanu kapena kuwongola miyendo ndi bwenzi lanu, kodi mumakonda kupita ku mapaki abata okhala ndi kapinga, maluŵa, mitengo ya mthunzi, ndi maiŵe? Inde, munda umakhaladi wotonthoza, wopumulitsa, wamtendere, ndipo ngakhale wochiritsa!

Ngakhale ena sangafunitsitse kukhala ndi munda wa maluŵa, mwina chifukwa cha kusoŵa nthaŵi, tonsefe timakondwera ndi maonekedwe a maluŵa, mafungo abwino, mawu, ndi zipatso za m’munda. Thomas Jefferson—wolemba mapulani a nyumba, wasayansi, loya, woyambitsa kupanga zinthu, ndi pulezidenti wa United States—anali kukonda minda ya maluŵa. Iye analemba kuti: “Palibe ntchito imene imandisangalatsa kwambiri monga kulima maluŵa. . . . Ndimakondabe maluŵa kwambiri. Koma ngakhale ndine wokalamba, ndine mlimi wamng’ono.”

Ambiri amaganiza monga iye. Chaka chilichonse alendo mamiliyoni ambiri amapita ku minda yotchuka ya padziko lonse—Kew Gardens (Royal Botanic Gardens), ku England; minda ya ku Kyoto, Japan; minda ya ku Palace of Versailles, ku France; Longwood Gardens, ku Pennsylvania, U.S.A., kungotchula ingapo. Maiko ambiri alinso ndi malo ena m’mizinda amene nyumba zake, zomangidwa m’mbali mwa misewu yaikulu yokhala ndi mitengo m’mbali mwake, zili ndi zitsamba, mitengo, ndi zomera za maonekedwe owala pozungulira pake—monga paradaiso wamng’ono.

Minda Ingawongole Thanzi la Munthu

Zapezeka kuti pamene anthu aona maluŵa, thanzi lawo limakhalapo bwino, ngakhale amangoona maluŵa, mitengo, zitsamba, ndi mbalame padzenera. Zimenezi zinachititsa chipatala china cha ku New York City kubzala munda wa maluŵa patsindwi pake. “Ambiri anakondwera,” anatero mkulu wina wa chipatala. “Walimbikitsa odwala ndi antchito omwe. . . . Tikuona kuti ungachiritsedi m’njira zambiri.” Zoonadi, kufufuza kukusonyeza kuti anthu angathandizidwe kuthupi, m’maganizo, ndi mumtima mwa kuona zinthu za m’chilengedwe.

Ndiponso, munthu wokonda zauzimu amamva kukhala pafupi kwambiri ndi Mulungu pamene ali pakatikati pa ntchito za manja Ake. Mbali imeneyi ya munda inayambira m’munda woyambawo wa padziko lapansi, Munda wa Edene, mmene Mulungu nthaŵi yoyamba analankhula ndi munthu.—Genesis 2:15-17; 3:8.

Kukonda munda wa maluŵa kuli kulikonse. Ndipo chimenechi chili ndi tanthauzo lake, monga tidzaonera. Komabe, tisanakambitsirane mbali imeneyo, tikukupemphani “kuyenda” m’minda ya maluŵa ingapo ya m’mbiri ndi kuona mmenedi anthu onse amalakalakira Paradaiso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena