Singapore—Ngale Yowonongeka ya Asia
GOJO! Mochititsa mantha zitseko zolema zachitsulo za ndende ya akazi ya Singapore ya Changi Women’s Prison zinatsekera mkazi wina wofooka wamasiye wazaka 71, Mkristu. Pokhala mmodzi wa Mboni za Yehova, anayesa kufotokoza mkhalidwe wake kwa woweruza kuti: “Sindikufuna kuliukira bomali.”
Gojo! Anatsatiridwa ndi gogo wina wamkazi wazaka 72, Mkristu winanso. Mlandu wake? Kukhala ndi zofalitsa zinayi za Baibulo za Watch Tower Society, kuphatikizapo kope lake la Baibulo Loyera.
Zonse pamodzi, nzika za Singapore 64, za zaka 16 mpaka 72, zinamangidwa ndi kupatsidwa mlandu. Okwanira 47 anakana kupereka malipo malinga ndi chikhulupiriro chawo ndipo anawamanga nthaŵi zosiyanasiyana kuyambira pa mlungu umodzi mpaka milungu inayi. Kodi zimenezi zinachitika motani m’dziko lamzinda limene ena amati ndiwo malo okhalamo abwino koposa padziko lonse lapansi? Zinachitika motani zimenezi m’dziko lamzinda lodziŵika dziko lonse chifukwa cha chuma chake choyenda bwino, chitukuko chadzaoneni, ndi nyumba zake zamakono limodzinso ndi umene amati ufulu wake wachipembedzo?
Dziko Lamzinda Lamakono
Choyamba, mbiri yake yachidule. Mbiri yamakono ya Singapore inayamba mu 1819 pamene Sir Thomas Stamford Raffles wa ku Britain anafika. Raffles, woimira East India Company, anali kufunafuna malo ochitirapo malonda ku maiko a Kummaŵa. Anasankha kuyesa Singapore. Ndimo mmene malo ochitirapo malonda anayambira amene athandiza kwambiri chitukuko cha ku East Asia mpaka lero.
Asanatenge ufulu, akuti Singapore unali mzinda wanyankhalala. Lero, palibe amene anganene kuti Singapore ndi wanyankhalala. Sizilinso choncho. Pazaka zoposa 30 zapitazi, mzindawo pafupifupi wonse wamangidwanso chatsopano, pamene kuli kotheka aumanga monga momwe unalili kale mwa kusunga maonekedwe akale a nyumba zakale kapena kupanga nyumba zonse zakale kukhala zatsopano. Singapore wakhala podutsa zombo zambirimbiri ku Mmaŵa, ndipo nthaŵi zambiri amakhala ndi zombo zokwanira 800 pa doko lake nthaŵi imodzi. Makina a tekinoloji yapamwamba amatha kuchotsa ndi kulonga katundu m’chombo chachikulu chakatundu pamaola ochepa. Pachimake chazamalonda cha mzindawo, malo a mita imodzi mbali zonse zinayi amafuna ndiponso amalandira ngati $60,000 kapena kuposapo.
Anthu ake ngati 3,400,000 ngosiyanasiyana kwambiri. Kuli Atchaina, Amalaya, Aindiya, Azungu, ndi ena. Zina mwa zinenero zimene amalankhula ndi Chimandarini, Chimalaya, Chitamilu, ndi Chingelezi.
Makilomita 83 a njanji zapamtunda ndi pansi pa nthaka zamasitima othamanga zimapatsa Singapore limodzi la madongosolo abwino koposa a mayendedwe padziko lonse lapansi. Mapaki obiriŵira ali tayale mumzindawo, pakati pa nyumba zazitali zakamangidwe kamakono. Wodzaona malo nthaŵi yoyamba amakopeka ndi Raffles Hotel imene anaikonza yonseyo, imene tsopano yakhala chikumbutso cha dzikolo chifukwa cha chiyambi chake cha mu 1889. Chokopa chachiŵiri ndi munda wa mahekitala 52 wazomera zosiyanasiyana ndi wa mitengo yazipatso, ndiwo zamasamba, ndi maluŵa, umene mahekitala ake 4 asungidwa monga nkhalango, mmene kale munali minjuzi.
Ufulu wa Chipembedzo Ulonjezedwa
Monga mbali yochirikiza chitukuko chake chosayerekezeka, Singapore amalonjeza ufulu wachipembedzo kwa okhalamo onse. Mwachisoni, Singapore sanakwaniritse lonjezo lake. Amene atsimikiza zimenezi makamaka ndi awo amene amagwirizana ndi mpingo wa Mboni za Yehova.
Konsichushoni ya Republic of Singapore, pa Mfundo 15(1), imapereka chitsimikizo chachikulu cha ufulu wa kulambira kuti: “Munthu aliyense ali ndi choyenera chokhulupirira ndi kutsatira chipembedzo chake ndi kuchifalitsa.”
Mfundo 15(3) ya Konsichushoniyo imatsimikiza kuti: “Gulu lililonse lachipembedzo lili ndi choyenera—
(a) cha kusamalira nkhani zake zachipembedzo;
(b) cha kukhazikitsa ndi kukhala ndi zinthu zachipembedzo kapena zothandiza ena; ndi
(c) kupeza ndi kukhala ndi katundu ndi kuusunga ndi kuugwiritsira ntchito monga mwa lamulo.”
Kuyambira kalelo mu 1936, Mboni za Yehova zakhala mbali ya anthu a m’Singapore. Kwa zaka zambiri anachita misonkhano yanthaŵi zonse m’Nyumba yawo ya Ufumu imene ili pa 8 Exeter Road, kuyang’anizana ndi msika waukulu. Mpingowo unakula, nthaŵi imodzimodziyo nuthandizira m’njira yakeyake kuchititsa moyo wa anthu kukhala wabwino.
Mboni za Yehova Ziletsedwa
Zonsezi zinasintha pa January 12, 1972. Lamulo lothamangitsa munthu m’dziko linaperekedwa mogwirizana ndi lamulo lotchedwa Government Banishment Act, chaputala 109, kulamula mmishonale wachikristu Norman David Bellotti ndi mkazi wake, Gladys, amene anakhala m’Singapore zaka 23, kutuluka m’dzikomo. Mwamsanga pambuyo pake lamulo linaperekedwa lakuti Mpingo wa Singapore wa Mboni za Yehova ufafanizidwe m’kaundula. Pamaola ochepa Nyumba ya Ufumu inalandidwa ndi apolisi amene anangobwanyula chitseko chakutsogolo ndi kuloŵa. Zimenezi zitangochitika mabuku onse a Watch Tower Society analetsedwa mwa lamulo. Ndi mmene nyengo yopondereza Mboni za Yehova inayambira.
M’kupita kwa nthaŵi boma linagulitsa Nyumba ya Ufumu monga mbali ya chiweruzo chawochawo, zonsezi popanda kuwadziŵitsa—popanda kumva madandaulo, popanda kukamba mlandu, popanda mpata wochitapo kanthu.
Mobwerezabwereza boma la Singapore latchula kusatenga mbali kwa Mboni za Yehova m’zausilikali kuti ndicho chifukwa chabwino choziletseratu. Chaposachedwapa pa December 29, 1995, A K. Kesavapany, woimira Singapore wokhazikika ku United Nations ku Geneva, m’kalata yopita kwa H. E. Ibrahim Fall, Wothandiza Nduna Yaikulu ya Human Rights, wa United Nations ku Geneva, ananena zotsatirazi:
“Kuletsa gulu la Mboni za Yehova kwa Boma langa kuli chifukwa cha kuganizira chisungiko cha dziko. Kulekerera gululo kukanaika ubwino wa anthu onse ndi bata pangozi m’Singapore. Chotsatirapo chofunika cha kufafaniza dzina la Mboni za Yehova m’kaundula chinali kuti zofalitsa zawo zonse zikhale zoletsedwa potsimikiza kuti gululo latsekedwa ndi kutsekereza kufalitsa ndi kuwanditsa zikhulupiriro zawo.”
Ponena za dandaulo la kuika chisungiko cha dziko la Singapore pangozi, dziŵani kuti chiŵerengero cha anyamata okana kuloŵa usilikali chili ngati anthu asanu pachaka. Singapore ali ndi asilikali ngati 300,000. Boma la Singapore lakana nkukambitsirana komwe zakuti anthu ochepawo okana usilikali, m’malo mwake azichita ntchito zina za boma zothandiza anthu.
Kupondereza Koonekeratu
Patapita zaka zingapo za ufulu wosatsimikizika, nyengo ina ya kupondereza zoyenera za anthu moonekeratu inayambika mu 1992 pamene anthu angapo anamangidwa—pa mlandu wa kukhala ndi mabuku oletsedwa ndi lamulo lotchedwa Undesirable Publications Act. Mu 1994 Watch Tower Society inatumiza ku Singapore W. Glen How, Q.C. wazaka 75, loya ndipo mmodzi wa Mboni za Yehova moyo wake wonse. Iye pokhala Phungu wa Mfumu anamlola kuonekera m’makhoti a Singapore. Ponena za chitsimikizo chimene Konsichushoni imapatsa zipembedzo, apilo inaperekedwa ku Bwalo Lalikulu la Singapore, kuphatikizapo kalata yotsutsa kuti kumanga anthuko ndi chiletso cha mu 1972 sizinachitidwe mwa lamulo. Pa August 8, 1994, Woweruza Wamkulu Yong Pung How, wa Bwalo Lalikulu la Singapore anaikana apiloyo. Kuyesayesa kwinanso kuti achite apilo kunalephera.
Podzafika kuchiyambi cha 1995 zinaoneka kuti kutsutsa Konsichushoni ya Singapore mwa lamulo kunangokuzirako kuponderezako. Mwa njira yausilikali yotchedwa Operation Hope, apolisi achinsinsi a Secret Societies Branch ya Criminal Investigation Department mwadzidzidzi anaukira magulu aang’ono angapo a Akristu amene anali kuchita misonkhano m’nyumba zawo. Apolisi ngati 70 ndi owathandiza anaukira maguluwa mwausilikali, ndipo anamanga anthu 69. Onse anawapereka kumalo ofunsirako, ena anawafunsa usiku wonse, ndipo onse anawapatsa mlandu wa kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova ndi kukhala ndi zofalitsa za Baibulo. Ena anawabindikiritsa kwaokha kwa maola mpaka 18, osatha ngakhale kuimbira foni mabanja awo.
Alendo a ku maiko ena anawachotsera mlanduwo. Koma 64 omwe ali nzika za Singapore anawazenga mlandu m’khoti kumapeto kwa 1995 ndi kuchiyambi cha 1996. Onse 64 anawapeza ndi mlandu. Okwanira 47, a zaka zapakati pa 16 ndi 72, sanapereke malipo a madola zikwi zambiri ndipo anawaponya m’ndende kuyambira pa mlungu umodzi mpaka milungu inayi.
Asanawatumize kuzipinda zawo zandende, amuna ndi akazi anawavula maliseche ndi kuwafufuza pamaso pa anthu ena angapo. Akazi ena anawauza kutambasula manja awo, kunyonyomala kasanu, ndi kutsegula kamwa lawo ndi kunyamula lilime lawo. Mkazi mmodzi anamuuza kutsegula mtumbo wake ndi zala zake. M’ndende, amuna ena anamwa madzi a m’chimbudzi. Asungwana ena anawasunga monga apandu oopsa, kuwabindikiritsa payekhapayekha nthaŵi yonse imene anakhala m’ndende, ndi kuwapatsa zakudya zosakwanira. Alonda ena a ndende anakana ngakhale kupatsa Mbonizo ma Baibulo awo.
Koma tiyeni timve ndemanga zochepa za akazi ena amene anaponyedwa m’ndende. Zimene zonena za iwo okha zinavumbula zinali zosiyana kotheratu ndi maonekedwe audongo a mzinda wamakono umenewu.
“Chipindacho chinali chauve. Mosukusulira ndi chimbudzi zinali zowonongeka. Zinali zoterera ndi zauve. Kunsi kwa benchi imene ndinali kukhalapo kunali kangaude ndi dothi.”
“Anandiuza kuti ndivule, ndipo anandipatsa zovala za m’ndende, mbale ya sopo (yopanda sopo), ndi mswachi. Akaidi ena a m’chipinda changa anandiuza kuti akaidi osakhalitsa samawapatsa mankhwala otsukira mano kapena pepala la m’chimbudzi.”
“M’chipinda chimodzi tinalimo 20. Chimbudzi ndi chija chonyonyomala chokhala ndi khoma lofika m’chiuno. Mosambira munali mpope umodzi wokha ndi posukusulira pamodzi pokhala ndi mpope umodzi. Tinali kusamba asanu ndi mmodzi nthaŵi imodzi—tonsefe m’chipindacho tinkayenera kusamba pa theka la ola m’maŵa.”
Mosasamala kanthu za kupsinjika ndi kuponyedwa m’ndende, onse anaona kuti kutumikira Mulungu ndi mwaŵi—nthaŵi iliyonse, kulikonse, ndi mumkhalidwe uliwonse. Mverani zimene mtsikana wina ananena:
“Nditangoloŵa m’ndende, ndinayamba kudzikumbutsa nthaŵi zonse za chifuno chimene ndinalili mmenemo. Masiku onse ndinapemphera kwa Yehova kuti amve pemphero langa ndi kusandisiya. Ndinaona kuti anayankha pemphero langa chifukwa chakuti ndi mzimu wake woyera umene unandithandiza kupirira. Ndi pamene ndinazindikira kuti ndinali woyandikana naye kwambiri, ndipo zandilimbitsa kwambiri, podziŵa kuti akutiyang’anira. Ndikuona kuti unali mwaŵi kupyola m’mayesero ameneŵa chifukwa cha dzina lake.”
Manyuzipepala padziko lonse lapansi mwamsanga anaimva nkhaniyo. Oulutsa nkhani ku Australia, Canada, Hong Kong, Malaysia, Ulaya, United States, ndi ku malo ena anaulutsa zochitikazo mobwerezabwereza. The Toronto Star, ya ku Canada, inafotokoza mwachidule nkhani yokwiyitsa ya panthaŵiyo ndi mutu wake wakuti “Gogo Apatsidwa Mlandu Wokhala ndi Baibulo.” Nzoona kuti dziko lili ndi mavuto ambiri aakulu okhudza anthu ambirimbiri, koma panopo funso limene anthu odabwa akufunsa kulikonse ndi limodzimodzi. “Ku Singapore?”
Nkovuta kumvetsa chifukwa chake chipembedzo chimene chimachita zinthu poyera ndipo motetezeredwa bwino ndi lamulo m’maiko oposa 200 padziko lonse chikuzunzidwa ku Singapore. Nkovutanso kwambiri kumvetsa titaona kuti kulibe chipembedzo chinanso ku Singapore chimene achitira nkhanza choncho ndi kuchipondereza.
Ndithudi, wachiŵiri kwa mkulu wa polisi amene anatsogolera gulu logwira Mboni za Yehova anavomera pamaso pa khoti kuti imeneyo ndiyo nthaŵi yokha imene iye ndi apolisi ake analamulidwa kuthetsa msonkhano wachipembedzo. Mawu otsatirawa agwidwa kuchokera m’lipoti laumboni:
Funso: (Kwa mboni) Malinga ndi zimene mukudziŵa kodi Secret Societies Branch inafufuzapo ndi kuimba mlandu magulu alionse osalembetsa, kusiyapo Mboni za Yehova?
Yankho: Osati amene ndikudziŵa.
Ndiyeno kufunsako kunapitiriza.
Funso: (Kwa mboni) Kodi inuyo panokha panthaŵi ina iliyonse munaukirapo gulu laling’ono lachipembedzo, limene lakumana m’nyumba ndipo losalembetsa malinga ndi Societies Act?
Yankho: Ayi sindinachitepo zimenezo.
Pempho la Kuchitapo Kanthu
Amnesty International ndi International Bar Association onse anatumiza wopenyerera wawo wapadera kukaona ngati kuzenga mlanduko kukuchitika molongosoka. Wopenyerera wosakondera wa Amnesty International, Andrew Raffell, iyeyo loya wa ku Hong Kong, ananena zotsatirazi: “Ndikulemba lipoti langa kuti kuzenga mlanduko kunali ngati kwachiphamaso.” Anapitiriza kufotokoza kuti akuluakulu a boma amene anaitanidwa kudzakhala mboni analephera kufotokozera khoti chifukwa chimene akunenera kuti mabuku a Mboni za Yehova ngoipa. Raffell anandandalika ena mwa mabuku a Baibulo oletsedwa kuphatikizapo Happiness—How to Find It ndi Your Youth—Getting the Best Out Of It. Anawonjezera kuti sitinganene kuti ngoipa m’njira ina iliyonse.
Wopenyerera wa International Bar Association, Cecil Rajendra, ananena zotsatirazi:
“Kuyambira pachiyambi, wopenyererayu anaona kuti kuzenga mlandu konse kunali chabe . . . kwachiphamaso kochitidwa poyera kuti dziko lonse lione kuti demokrase ikalimo m’Singapore.
“Zotsatirapo zake zinali zodziŵikiratu ndipo panalibe kukayikira kulikonse panthaŵi ina iliyonse mapeto ake asanafike, pozenga mlandu kapena pamapeto ake kuti onse opatsidwa mlandu adzapezedwadi ndi mlandu monga ananenera poyamba.
“Ngakhale kuti mlanduwo unali m’khoti yaing’ono ndipo kwenikweni milandu imene anawapatsa inali kuswa pang’ono lamulo la Societies Act, mkhalidwe wapakhotipo unali uja wa mantha ndi chinthenthe.
“Zimenezi zinali choncho makamaka chifukwa chakuti kunali apolisi ovala yunifomu oposa 10 (6 mkati m’khoti ndi 4 kunja) ndi ena a ku Special Branch ovala zovala wamba atakhala pamipando ina yapamwamba.”
Kunena za mmene anazengera mlanduwo, Rajendra anapitiriza kuti:
“Khalidwe la Woweruzayo panthaŵi ya kupenyereraku (ndi mkati monse mwa mlanduwo, monga momwe malipoti akuchitira umboni) linali losayenera. . . . Mosemphana ndi njira zonse za kuzenga bwino mlandu, Woweruza nthaŵi ndi nthaŵi analoŵererapo kuchirikiza osumira anzawo mlandu ndi kutsutsa eni mlandu pofunsa mboni za osumira mlandu ponena za maumboni awo, mwachitsanzo Baibulo la King James, limene osumira mlandu anabweretsa kuti asonyeze kuti oimbidwa mlanduwo anali ndi mabuku oletsedwa!”
Anthu a kumaiko ena ada nkhaŵa kwambiri ndi kupondereza zoyenera za anthu kwa Singapore kwakuti magazini ina ya ku Belgium yotchedwa Human Rights Without Frontiers inafalitsa lipoti lamasamba 18 pankhani chabe ya kuukira Mboni za Yehova kwa boma la Singapore. Polemba monga wofalitsa wake, Willy Fautré, mkonzi wamkulu wa magaziniyo, anafotokoza bwino kwambiri tanthauzo la ukulu weniweni wa ufulu wa anthu m’ndale zonse:
“Ngakhale kuti ufulu wachipembedzo ndiwo chimodzi mwa zizindikiro zabwino kwambiri za mkhalidwe wa ufulu wa anthu wachisawawa pakati pa anthu alionse, ndi mabungwe a kudziko oyang’anira zoyenera za anthu ochepa kwambiri amene athandizira kuchotsapo mitundu imeneyo ya tsankhu ndi kusalekerera zinthu chifukwa cha chipembedzo kapena chikhulupiriro, kapena kupanga njira zotetezera ndi kuchirikiza ufulu wachipembedzo.”
Human Rights Without Frontiers inafalitsa mpambo wake wa zimene inayamikira m’malemba ochindikala kuchikuto chakumbuyo cha lipoti lawo.
Mboni za Yehova nzaphindu kwa Singapore. Zimalemekeza zoyenera za anansi awo ndipo sizimawachitira upandu uliwonse. Palibe nzika ya Singapore imene iyenera kudera nkhaŵa kuti wina wa Mboni za Yehova adzamloŵerera m’nyumba mwake ndi kumbera kapena kuti adzamfwamba, kummenya, kapena kumgwira ndi kuchita naye chigololo.
Utumiki wawo wodzifunira wapoyera umalimbitsa ndi kuwongolera moyo wa banja ndi kuchirikiza unzika wabwino. Zimachititsa maphunziro a Baibulo aulere kwa aliyense amene akufuna kuphunzira mapulinsipulo omangirira a Baibulo ndi mmene angawagwiritsirire ntchito m’moyo wake. Misonkhano yawo ya phunziro la Baibulo ndi pemphero ili mbali ya maphunziro awo achikristu. Zimenezi zawachititsa kukhala nzika zabwino.
Nzika za Singapore zimene zimalemekeza dziko lawo ndipo zikulifunira zabwino zonse mtsogolo ziyenera kulimbikitsa boma kuti lilingalirenso za malo oyenera a Mboni za Yehova pakati pa anthu a m’Singapore. Ino ndiyo nthaŵi yozichotsera ziletso ndi kuzibwezera chimene nzika iliyonse iyenera kukhala nacho—ufulu wa kulambira.
[Bokosi patsamba 30]
Dziko Likupenyerera
1. “Apolisi a Singapore ataloŵerera mwadzidzidzi nyumba zisanu mwausilikali February wapitayu, amuna, akazi ndi achinyamata 69 anamangidwa ndi kuperekedwa kulikulu la polisi kukafunsidwa. Misonkhano yaphunziro la baibulo sinayenere kutha choncho.”—The Ottawa Citizen, Canada, December 28, 1995, tsamba A10.
2. “Zingakhale zokondweretsa kwambiri kwa onse amene amasamala za ufulu wachipembedzo ndi zoyenera za chikumbumtima ngati Boma la Singapore lingawongolere kaonedwe kake ka anthu opanda mlanduwa ndi amtendere ndi kuwalola kutsatira chikhulupiriro chawo ndi kuchifalitsa mosaopa kapena kuletsedwa.”—Profesa Bryan R. Wilson, University of Oxford, England.
3. “Pozenga milandu motsatizana imene inachititsa mabungwe a dziko lonse a ufulu wa anthu wamba kudandaula, makhoti a ku Singapore apeza Mboni za Yehova 63 ndi mlandu kuyambira November wapitayu.”—Asahi Evening News, Japan, January 19, 1996, tsamba 3.
4. “Mboni za Yehova ziyenera kuloledwa kusonkhana ndi kutsatira chipembedzo chawo mwa mtendere mosaopa kumangidwa kapena kuponyedwa m’ndende. Ufulu wachipembedzo ndi choyenera chachikulu chimene Konsichushoni ya Singapore imalonjeza.”—Amnesty International, November 22, 1995.
5. Chan Siu-ching, wakumpando wa Bungwe Loyang’anira Chilungamo ndi Mtendere la Hong Kong Catholic Diocese, m’kalata ya pa June 1, 1995 yopita kwa Lee Kuan Yew, Minisitala Wamkulu, Ofesi ya Nduna Yaikulu, anati: “Nkhani yaikulu ndi yakuti ngakhale kuti boma la Singapore liganiza kuti awo amene akana kuloŵa usilikali akuswa lamulo ndipo ayenera kuimbidwa mlandu, mamembala ena amene amachita nawo misonkhano yachipembedzo kaamba ka kulambira sayenera kukhudzidwa. . . .
“Motero tikulemba kuti tipemphe Boma lanu:
1. kuti lisaletse Mboni za Yehova kuti zikhale ndi ufulu wa kulambira ndi wa chikumbutima;
2. kuti lisiye kupatsa mlandu mamembala a Mboni za Yehova amene amangopezeka pamisonkhano yachipembedzo.
3. kuti limasule mamembala a Mboni za Yehova amene amangidwa posachedwapa chifukwa cha kungopezeka pazochitika zachipembedzo.”
[Chithunzi patsamba 27]
Mboni za Yehova pakhoti atazipatsa mlandu
[Chithunzi patsamba 27]
Mboni ya zaka 71 imeneyi inauza woweruza kuti: “Sindikufuna kuliukira bomali.” Koma anaiponyabe m’ndende