Lingaliro la Baibulo
Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?
KUNGOYAMBIRA pa ndege ndi mabomba a atomu mpaka kusintha majini m’maselo ndiponso kubalitsa nkhosa popanda yamphongo, zaka zathu za zana la 20 zino zangokhala nyengo yasayansi basi. Asayansi atumiza anthu ku mwezi, athetseratu nthomba, asinthiratu ulimi, ndipo akonzera anthu mamiliyoni zikwi zambiri makina olankhulirana nthaŵi yomweyo padziko lonse. Chotero, nzosadabwitsa kuti asayansi akamalankhula anthu amamvetsera. Koma asayansi amati bwanji ponena za Baibulo ngati amanenapo nkomwe kalikonse? Ndipo kodi Baibulo limatiuzanji ponena za sayansi?
Kodi Zozizwitsa si Sayansi?
“Anthu odziŵa sayansi amakhulupirira zoti ‘pamene pali chochitika pali chochititsa.’ Amakhulupirira kuti mwachibadwa chilichonse chili ndi chifukwa chimene chakhalirako,” ikutero insayikulopediya yamakono. Ophunzira Baibulo nawonso amakhulupirira mapulinsipulo a sayansi odziŵika. Komabe, amazindikira kuti kaŵirikaŵiri Baibulo limasimba zochitika zozizwitsa zimene sayansi siingafotokoze malinga ndi chidziŵitso chimene anthu ali nacho lero. Zitsanzo zina ndizo kuima kwa dzuŵa m’tsiku la Yoswa ndi kuyenda kwa Yesu pamadzi. (Yoswa 10:12, 13; Mateyu 14:23-34) Komabe, limazilongosola zozizwitsa zimenezi kuti zinachitika mwa mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito mwa njira yachilendo.
Mfundo imeneyi njaikulu. Baibulo likananena kuti anthu angayende pamadzi popanda chithandizo cha Mulungu kapena kuti dzuŵa lingaimikidwe m’mlengalenga popanda chifukwa, likanamveka ngati likutsutsa sayansi. Komabe, pamene limati zinthu zimenezo zinachitika mwa mphamvu ya Mulungu, sikuti likutsutsa sayansi koma lingofotokoza zimene sayansiyo singathe kufotokoza.
Kodi Baibulo Limatsutsa Sayansi?
Nanga bwanji za nkhani zija zimene Baibulo limasimba zochitika wamba pamoyo wa anthu kapena kutchula maluŵa, nyama, kapena zodabwitsa zachilengedwe? Muyenera kudziŵa kuti sitimapeza chitsanzo chilichonse chotsimikiza kuti Baibulo limatsutsa maumboni a sayansi odziŵika pankhani zoterozo titapenda nkhani yake yonse.
Mwachitsanzo, Baibulo limagwiritsira ntchito mawu a ndakatulo amene amasonyeza maganizo a anthu omwe anakhalako zaka zikwi zambiri zapitazo. Pamene buku la Yobu likuti Yehova akuyala kapena kusula thambo “lolimba ngati kalirole woyengeka,” likufotokoza bwino kuti miyamba ili ngati kalirole wachitsulo woŵala kwambiri. (Yobu 37:18) Simutofunikira kuliona fanizolo ngati zenizeni, monga momwedi simungaone ngati zenizeni fanizo loti dziko lapansi lili ndi “maziko” kapena “mwala wake wa pangondya.”—Yobu 38:4-7.
Zimenezo nzofunika chifukwa chakuti ochitira ndemanga ambiri awatenga mafanizo amenewo monga zenizeni. (Onani 2 Samueli 22:8; Salmo 78:23, 24.) Amati Baibulo limaphunzitsa zina zonga zotsatirazi, zogwidwa mawu mu The Anchor Bible Dictionary.
“Dziko lapansi pamene anthu akukhala lili ngati chinthu chobulungika, cholimba, kapena mbale, yomayandama pamadzi ambiri opanda mapeto. Madzi enanso ofanana ndi a munsiwo, nawonso opanda mapeto, ali kumwamba, amenewo amagwa ngati mvula kupyolera m’ziboo ndi ngalande za thanki yakumwamba. Mwezi, dzuŵa, ndi zounikira zina zili kuchinthu chopindika chophimba dziko lapansi. Chinthu chimenecho ndicho ‘thambo’ (rāqîa‛) lodziŵika lofotokozedwa ndi ansembe.”
Mwachionekere, mafotokozedwe ameneŵa sakugwirizana ndi sayansi yamakono. Koma kodi kumeneku ndi kulongosola koyenera kwa zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za miyamba? Ayi ndithu. The International Standard Bible Encyclopaedia ikuti mafotokozedwe oterowo a thambo lachihebri “ngozikidwa pa malingaliro amene anali ofala ku Europe mu Nyengo Zapakati osati pa mawu enieni a m’Chipangano Chakale.” Kodi malingaliro a m’nyengo zapakati amenewo anachokera kuti? Monga mmene David C. Lindberg akulongosolera m’buku lakuti, The Beginnings of Western Science, kwenikweni anazikidwa pa sayansi ya zakuthambo ya wafilosofi wachigirikiyo Aristotle, yemwe mabuku ake anali maziko a maphunziro a nyengo zapakati.
Mulungu akanalemba Baibulo m’chinenero chimene chikanangomvedwa ndi wasayansi wa m’zaka za zana la 20, zikanakhala zopanda tanthauzo ndi zosokoneza. M’malo mwa mawu a sayansi, Baibulo lili ndi mafanizo omveka bwino a moyo watsiku ndi tsiku wa anthu amene anawalemba—mafotokozedwe ogwira mtima kwa anthu akalewo ndi a lero omwe.—Yobu 38:8-38; Yesaya 40:12-23.
Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu
Komabe, mawu ena a m’Baibulo amakhala ngati akusonyeza chidziŵitso chimene anthu a panthaŵiyo analibe. Yobu akulongosola kuti Mulungu “ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.” (Yobu 26:7) Lingaliro loti dziko lalenjekeka “pachabe,” linali losiyana kwambiri ndi nthanthi za anthu ambiri akale, amene anali kuti lakhazikika panjovu kapena pankhasi za m’nyanja. Chilamulo cha Mose chili ndi malamulo aukhondo oposeratu zamankhwala zomwe anthu panthaŵiyo anali kudziŵa. Mwachionekere, malangizo a kubindikira anthu amene anawaganizira kuti anali ndi khate ndi kuletsanso kugwira mitembo kunatetezera moyo wa Aisrayeli ambiri. (Levitiko 13; Numeri 19:11-16) Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, mankhwala a Asuri akuti “anali kuphatikiza chipembedzo, kuwombeza maula, ndi zamizimu” ndipo mankhwala awo analinso tudzi ta galu ndi mikodzo ya anthu.
Monga buku loti ndi Mlengi analiuzira, munthu angayembekezeredi kuti Baibulo likhale ndi chidziŵitso cholondola cha sayansi chimene chinalembedwa kale sayansiyo isanabadwe, ngakhale kuti silimagwiritsira ntchito mafotokozedwe asayansi chifukwa akanakhala opanda tanthauzo kapena osokoneza kwa anthu akale. Baibulo lilibe chilichonse chimene chimatsutsa maumboni odziŵika a sayansi. Komabe, Baibulo lili ndi zambiri zimene zimatsutsa nthanthi zopanda umboni, monga nthanthi yachisinthiko.
[Mawu Otsindika patsamba 17]
Kunena kwa Yobu koti dziko ‘lalenjekeka pachabe’ kumasonyeza chidziŵitso chimene anthu a m’nthaŵi yake analibe
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
NASA