Mawu Aukali Amaswa Mzimu wa Munthu
“Wopusa wamazizi iwe!”a Mkazi wina ku Japan amakumbukira bwino mawu ameneŵa—ankanyozedwa choncho kaŵirikaŵiri pamene anali mwana wamng’ono. Ndani amateroyo? Ana asukulu? Abale ake? Ayi. Koma makolo ake. Iye akukumbukira kuti: “Ndinkapsinjika maganizo chifukwa maina onyoza ameneŵa ankandikhumudwitsa kwambiri.”
Mwamuna wina ku United States akukumbukira kuti ali mwana amachita mantha ndipo amakhala ndi nkhaŵa akangobwera bambo ake panyumba. “Mpaka lero ndimakumbukira bwino mawiro a galimoto ikubwera kunyumba,” akukumbukira choncho, “ndipo ndimakumbukirabe mantha omwe ndinali nawo. Mlongo wanga wamng’ono ankabisala. Abambo anga sankafuna kuti kanthu kalakwikepo mpang’ono pomwe ndipo nthaŵi zonse ankatinyoza chifukwa chochita zinthu zonse mosafikitsa pomwe iwo amafuna.”
Mlongo wa munthu ameneyu akuwonjezera kuti: “Sindikumbukirapo kuti kholo langa lililonse linatikumbatirapo, kutipsompsona, kapena kunenapo kuti ‘Ndimakukondani’ kapena ‘ndimakunyadirani’ Ndipo kwa mwana, ngati sauzidwapo kuti ‘ndimakukonda’ amangomva kuti nchimodzimodzi ndi kuuzidwa kuti ‘ndimakuda’—nthaŵi yonse yamoyo wake.”
ENA akhoza kunena kuti mavuto amene anthu ameneŵa anakumana nawo akali ana ndi ochepa. Kunena zoona si zachilendo kwa ana kunyozedwa, kunenedwa mopanda chikondi ndiponso kuvutitsidwa. Zimenezi sizilembedwa m’nyuzipepala kapena kusonyezedwa pa TV. Kusakaza kwake sikuoneka. Koma ngati makolo azunza ana awo mwanjira imeneyi tsiku ndi tsiku, zotsatira zake zikhoza kukhala zowononga kwambiri ndithu—ndipo zosatha kwa moyo wonse.
Lingalirani za kupenda kochitidwa mu 1990 pa zotsatira za kufufuza kochitidwa mu 1951 pomwe anafufuza kaleredwe ka makolo pa kagulu ka ana a zaka zisanu. Ofufuza anatha kupezanso ambiri mwa ana ameneŵa, amene tsopano ali m’zaka zawo zapakati pa 40 ndi 60, kuti aone momwe kuleredwa kwawo kunakhudzira moyo wawo. Kufufuza kwachiŵiriku kunasonyeza kuti ana omwe amavutika kwambiri m’moyo wawo, amene malingaliro awo ndi osakhwima, ndipo amene amapeza mavuto m’banja, ndiponso kusagwirizana ndi mabwenzi, ngakhalenso kuntchito, sanali ana amene makolo awo anali amphaŵi kapena olemera kapenanso ngakhale ana omwe makolo awo mwachionekere ali ndi mavuto. Anali ana omwe makolo awo samakhalirana nawo pafupi, samawasonyeza nsangala ndipo amawasonyeza chikondi pang’ono kapena samasonyeza nkomwe.
Zimene anapezazi zikusonyeza choonadi chomwe chinalembedwa kale pafupifupi zaka 2000 zapitazo: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21) Kunyoza ana kochitidwa ndi makolo ndithudi kumawaputa ndipo zotsatira zake zimakhala kutaya mtima.
Malinga ndi buku lotchedwa Growing Up Sad, sikale kwambiri pamene madokotala ankaganiza kuti ana sangapsinjike maganizo. Koma nthaŵi ndi zochitika zasonyeza kuti zimenezi zimachitika. Lero, alembi a bukulo amati, kupsinjika maganizo kwa ana nkodziŵika ndiponso sikwachilendo. Chochititsa china ndicho kukanidwa ndiponso kuzunzidwa ndi makolo. Alembiwo akunena kuti: “Nthaŵi zina makolo avutitsa ana awo mwakuwadzudzula ndi kuwanyoza mosalekeza. Nthaŵi zina sipakhala nkomwe mgwirizano wapakati pa makolo ndi ana: makolo sasonyeza chikondi kwa mwana. . . . Zotsatira zake zimakhala zoipa kwa ana okhala ndi makolo oterowo chifukwa kwa mwana—kaya wamkulu, pa zoterezi—chikondi chimakhala ngati dzuŵa ndi madzi ku mbewu.”
Kupyolera mwa chikondi cha makolo, ngati chisonyezedwa bwino ndipo poyera, ana amazindikira choonadi chakuti: Amakondedwa; ngofunika. Ambiri amasokoneza mfundo imeneyi ya kukhala okondedwa ndi ofunika naganiza kuti kufuna kukondedwa ndi kukhala wofunika ndiko kudzikuza ndi kudzikonda. Koma pankhani ino, zimenezo sindizo zomwe tikutanthauza. Mlembi wina akunena zotere m’buku lake: “Momwe mwana wanu amadzionera iye yekha zimayambukira mtundu wa mabwenzi amene amasankha, momwe amagwirizanirana ndi ena, munthu amene amasankha kukwatirana naye, ndiponso zimene adzachita m’moyo wake.” Baibulo limanena mmene kulili kofunika kukhala achikatikati, kusadzikweza mopambanitsa pamene limaika lamulo ili monga lachiŵiri pa malamulo: ‘Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.’—Mateyu 22:38, 39.
Nzovuta kuganiza kuti pali kholo limene lingafune kuwononga kudzidalira kwa mwana, chinthu chomwe nchofunika koposa koma chosachedwa kuwonongeka. Koma, nanga nchifukwa ninji zotere zimachitika kaŵirikaŵiri? Ndipo tingapewe bwanji kuchita zimenezo?
[Mawu a M’munsi]
a Mu Chijapani, noroma baka!