Madzi Moyo wa Pulanetili
MADZI ngofunika kwa chamoyo chilichonse padziko lapansi, alibe mtundu, alibe fungo, nga zii utawalaŵa, ndipo alibe mphamvu ya chakudya. Munthu, nyama, kapena chomera sichingakhale ndi moyo popanda iwo. Madzi ngofunika kwa chamoyo chonga njovu mpaka kachirombo kosaoneka ndi maso; palibe chimene chingaloŵe m’malo mwake. Aliyense wa anthu opitirira mamiliyoni zikwi zisanu padziko lapansi amafunikira kumwa, kupyolera m’zakumwa ndi zakudya, madzi okwanira pafupifupi malita aŵiri ndi theka tsiku lililonse kuti akhale wathanzi. Ngati palibe madzi, palibenso moyo.
Popanda madzi, mbewu sizingalimidwe, sikungakhalenso kuŵeta ziŵeto. Ngati palibe madzi, palibe chakudya—ngati palibe chakudya, palibenso moyo.
Mwamwaŵi, madzi ngambiri zedi. Chithunzi chake chitatengedwa kuchokera mumlengalenga, pulaneti lathu labuluu lokongolali limangooneka ngati kuti lingatchedwe Madzi, osatinso Dziko Lapansi. Zoonadi, madzi onse a padziko lapansi atamiza bwinobwino mtunda wonse wa pulanetili, mbulunga yonse ingakhale nyanja yamchere yozama makilomita aŵiri ndi theka. Mtunda wonse wa dziko lapansi ungathe kukwanira m’nyanja yamchere ya Pacific Ocean, mpaka mbali ina ya nyanjayo kukhalako.
Ndithudi, madzi ambiri a padziko lapansi ali m’nyanja, ndipo madzi a m’nyanja ngamchere. Munthu atati azimwa madzi a m’nyanja okhaokha, iye angathe kufa ndi ludzu mofulumira ndi kutha madzi m’thupi pamene thupi lake likumalimbana ndi kuchotsa mchere wosafunikira. Madzi a m’nyanja sali bwinonso paulimi kapena pamaindasitale—amapha mbewu zambiri ndipo amachititsa dzimbiri mosavuta makina ambiri. Choncho, kwakukulukulu, anthu angagwiritsire ntchito madzi a m’nyanja pokhapokha atachotsa mcherewo, ndipo imeneyo ndi ntchito yolira ndalama zambiri.
Mwa madzi onse a padziko lapansi ndi 3 peresenti yokha amene ali abwino, opanda mchere. Pafupifupi madzi onse abwinowo—cha m’ma 99 peresenti—anakanirira m’madzi oundana ndi m’miyala ya ayezi kapena ali pansi penipeni pa nthaka. Okwanira 1 peresenti yokha ndiwo amapezeka mosavuta.
Peresenti imodzi yokha ikumveka ngati kuti njochepa kwambiri. Kodi tingati madzi abwino adzatha? Mwinamwake sizidzatero. Magazini yotchedwa People & the Planet ikuti: “Ngakhale madzi ameneŵa [1 peresenti], atagaŵidwa bwinobwino kuzungulira dziko lonse lapansi ndi kugwiritsiridwa ntchito moyenerera, angachirikize chiŵerengero cha anthu omwe alipo padziko lonse lapansi lerolino kuŵirikiza kaŵiri kapena katatu.”
Zoonadi, madzi onse a padziko lapansi sawonjezeka kapena kuchepa. Magazini ya Science World ikuti: “Madzi amene mukugwiritsira ntchito lero mwinamwake nyama yotchedwa dinosaur inawamwako kupha ludzu lake. Izi zili choncho chifukwa chakuti madzi amene ali pa Dziko Lapansi lerolino ndi okhawo amene takhala nawo kuyambira kale—kapena amene tidzakhala nawo kosatha.”
Izi zili choncho chifukwa chakuti madzi a pansi penipeni ndi pamwamba pa dziko lapansi amazungulirazungulira mosalekeza—kuchokera m’nyanja zamchere amapita mumlengalenga, kenaka panthaka, m’mitsinje, ndipo amabwereranso ku nyanja zamchere. Nzogwirizana ndi mmene munthu wanzeru analembera kalekale kuti: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja simasefukira ayi; kumalo omwe mitsinjeyo imachokera nkumenenso imabwerera.”—Mlaliki 1:7, New English Bible.
Komabe, ngakhale kuti pali madzi abwino ochuluka padziko lapansi, kumadera ambiri kuli vuto la madzi. Nkhani zotsatira zikufotokoza za mavuto ake ndi mmene angathetsedwere.
[Chithunzi patsamba 23]
Chithunzi cha NASA