Madzi ndi Thanzi Lanu
“SIKUTI ludzu ndilo lizikudziŵitsani kuchuluka kwa madzi amene thupi lanu likufuna,” inatero magazini yotchedwa Health. “Komatu kumwa madzi ambiri nkofunika kuti thupi ndi maganizo athu azikhala bwino, kuphatikizapo kaonekedwe kathu.” Matupi athu amataya madzi nthaŵi zonse mwa kutuluka thukuta, misozi, ndi mkodzo kuphatikizapo popuma. Madzi otayika ameneŵa amafunika kubwezeretsedwa. Kodi amafunika ochuluka motani? Akatswiri ambiri odziŵa za zimenezi amati koma kumwa matambula asanu ndi atatu a madzi—malita aŵiri—tsiku lililonse.
Chifukwa ninji? Madzi ndi ofunika poyendetsa chakudya m’thupi ndiponso kuchotsa zoipa. Ngofunika pothandiza kupangitsa thupi lathu kutentha moyenera ndi kufeŵetsa mokumanira mafupa. “Madzi atangochepa ngakhale pang’ono chabe m’thupi mukhoza kumva kutopa . . . kapena kudwala,” inatero Health. “Kuchepa madzi m’thupi ndiko chopangitsa kufooka kwa thupi chomwe kaŵirikaŵiri chimanyalanyazidwa.” Magaziniwo anati: “Musapusitsidwe ndi khofi ndi tiyi, zakumwa zoziziritsa kukhosi zokhala ndi caffeine, ndiponso moŵa kuti poti nzamadzi; kwenikweni zimathandizira kuchepetsa madzi m’thupi.” Caffeine ndi moŵa zimachititsa munthu kukodza kwambiri ndiye nkupangitsa thupi kutaya madzi ambiri.
Kuwonjezera apo, “thupi lanu limafunika madzi kuti lizikhala lofeŵa ndi losathetheka.” Pofuna kuthandizira zimenezi, pangafunike kudzola mafuta ofeŵetsa khungu. Koma sikuti amafeŵetsadi khungu. M’malo mwake amaika kachikuto kochepa pamwamba pa khungu kamene kamathandiza kuti madzi amene ali m’khungu asaume. Kusunga madzi ameneŵa kumakhala kofunika kwambiri pamene tikukula, popeza mphamvu za khungu lathu zosunga madzi zimanka nzichepa.
Momvetsa chisoni, mbali zambiri za dziko lapansi, pamafunikira khama kuti upeze madzi abwino, osada. Komabe nkofunika kutero. Mwanjira iliyonse, imwani madzi ambiri, ndipo gwiritsirani ntchito njira yosavutayi kuti muzioneka bwino ndi kudzimva athanzi!