Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 4/8 tsamba 12-14
  • Kodi Akazi Ali ndi Tsogolo Lotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akazi Ali ndi Tsogolo Lotani?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzitsa Amuna ndi Atate
  • Mulungu Amasamalira Akazi
  • Akazi Amene Alemekezedwa
  • Njira Yothetseratu
  • Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • ‘Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Akazi Achikristu Ayenera Kuchitiridwa Ulemu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Mulungu Amaona Kuti Akazi Ndi Otsika?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 4/8 tsamba 12-14

Kodi Akazi Ali ndi Tsogolo Lotani?

“MBIRI ya mtundu wa anthu njodzaza ndi nkhani zonena za amuna kuvutitsa ndi kupondereza mkazi mobwerezabwereza.” Chinatero chikalata cha zigamulo chotchedwa Declaration of Sentiments cholembedwa mu Seneca Falls, New York ku America zaka 150 zapita polimbana ndi chisalungamo chimene akazi amakumana nacho.

Kuchokera nthaŵiyo zinthu zaongokerapo, koma malinga nkunena kwa The World’s Women 1995, kabuku kofalitsidwa ndi United Nations kanati, pali zambiri zoyenera kuchitika. “Kaŵirikaŵiri, akazi ndi amuna amasiyana, kusiyana pa mwaŵi wa maphunziro ndi ntchito, ndi pa zaumoyo, chitetezo cha munthu mwini ndi nthaŵi yakusanguluka,” kanatero kabukuko.

Chifukwa chakuti ambiri akuzindikira zimenezi, maiko akukhazikitsa malamulo otetezera ufulu wa akazi. Koma malamulo sangasinthe mitima ya anthu, mmene muli mizu ya chisalungamo ndi tsankho. Mwachitsanzo, lingalirani za vuto la mahule achitsikana. Ponena za chinthu chochititsa manyazi padziko lonsechi, Newsweek inati: “Malamulo ofuna kuthetsa kusokoneza ana powachititsa chiwerewere ndi abwino koma sathandiza.” Mofananamo, lamulo palokha sililepheretsa chiwawa. “Maumboni amasonyeza kuti kuchitira chiwawa akazi ndi vuto la padziko lonse,” linatero lipoti la Human Development Report 1995. “Malamulo ambiri ngosakwanira kuti nkuthetsa chiwawa chimenechi—pokhapokha chikhalidwe cha anthu chomwe chilipo lerochi chitasintha.”—kanyenye ngwathu.

“Chikhalidwe cha anthu” chimazika mizu pa miyambo yomwe inayambika kalekale—chinthu chovuta kwambiri kuchisintha. “Mwambo umapangitsa amuna kukhulupirira kuti akazi ayenera kuonedwa monga chida chogwiritsira ntchito osati kuwakonda, kungowagwiritsira ntchito osati kuwasamalira,” anatero mkazi wina wa ku Middle East. “Zotsatira zake mkazi saloledwa kulankhulapo, alibe mphamvu, ndipo ali ndi mpata wochepa woti nkuwongolera zinthu.”

Kuphunzitsa Amuna ndi Atate

Pamfundo zoti zitsatiridwe zoperekedwa mu Beijing, China, mu 1995, pamsonkhano wa nkhani zokhudza akazi dziko lonse kunalengezedwa kuti “patakhala kuti onse achitapo kanthu mwamsanga ndipo mogwirizana” pakhoza kukhala “dziko la mtendere, chilungamo ndi chikondi” mmene akazi akhoza kumalemekezedwa.

Ziyenera kuyambira panyumba ndi amuna ndi atate kuchitapo kanthu kuti azimayi azikhala ‘mwamtendere, mwachilungamo, ndi mwachikondi.’ Pankhani imeneyi, Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti maphunziro a m’Baibulo ndiyo njira yopangitsira zimenezi. Zaona kuti anthu ataphunzira kuti Mulungu amawayembekezera kulemekeza ndi kuŵerengera akazi awo pamodzi ndi ana awo aakazi, amayamba kuchita zimenezo mwamsanga.

Ku Central Africa, Pedro, mwamuna wokhala ndi mkazi ndi ana anayi, tsopano amamvetsera zimene mkazi wake akufuna. Amamthandiza kulera ana, amakonza ngakhale zakudya pamene banjalo lalandira alendo. Khalidwe loganizira ena chotero silichitikachitika m’dziko lake. Kodi chimampangitsa kuti aziyamikira ndi kugwirizana ndi mkazi wake nchiyani?

“Pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo, ndinaphunzira mapulinsipulo aŵiri onena za udindo wa mwamuna,” anatero Pedro. “Zimenezi zimakhudza kwambiri mmene ndimakhalira ndi mkazi wanga. Loyamba, pa 1 Petro 3:7 limalongosola kuti mwamuna ayenera kulemekeza mkazi wake “monga chotengera chochepa mphamvu.” Lachiŵiri, pa Aefeso 5:28, 29 limati mwamuna azikonda mkazi wake ‘monga ngati thupi la iye yekha.’ Popeza ndimatsatira malangizo amenewo, tsopano timagwirizana kwambiri. Motero ife amunafe tiyenera kumaona uphungu wa Mulungu monga waphindu kuposa miyambo yathu.”

Michael, wa ku West Africa, anavomereza kuti asanayambe kuphunzira Baibulo ndi Mboni, sankasamala kwenikweni mkazi wake. “Nthaŵi zina ndinkammenya ndikakwiya,” iye anavomereza motero. “Koma Baibulo linandiphunzitsa kuti ndiyenera kusintha khalidwe langa. Tsopano ndimayesetsa kugwira mtima wanga ndi kukonda mkazi wanga monga thupi langa. Motero tonse ndife osangalala kuposa kale.” (Akolose 3:9, 10, 19) Mkazi wake, Comfort anavomereza kuti: “Tsopano Michael amandilemekeza ndipo amandikonda kusiyana ndi mmene amachitira amuna ambiri kwathu kuno. Timatha kukambitsirana zovuta zathu ndi kuthandizana kuzithetsa.”

Pedro ndi Michael anaphunzira kulemekeza ndi kuyamikira akazi awo chifukwa anatsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu, amene amasonyeza bwino kuti kuchitira akazi chisalungamo kumamnyansa Mlengi wathu.

Mulungu Amasamalira Akazi

Nthaŵi zonse Mulungu wakhala akulingalira zakuti akazi azikhala bwino. Ngakhale kuti anauza makolo athu oyambirirawo kuti chifukwa cha kupanduka kwawo, kupanda ungwiro kudzapangitsa kuti akazi ‘azilamuliridwa,’ ichi sindicho chinali chifuniro cha Mulungu. (Genesis 3:16) Anamlenga Hava monga ‘wothangata’ Adamu ndiponso ngati bwenzi lake. (Genesis 2:18) M’Chilamulo cha Mose chimene anapereka kwa Aisrayeli, Yehova anatsutsa mwachindunji kuzunza akazi amasiye ndipo analangiza Aisrayeli kuti azikhala nawo mokoma mtima ndi kumawathandiza.—Eksodo 22:22; Deuteronomo 14:28, 29; 24:17-22.

Potsanzira Atate wake wakumwamba, Yesu sanatsatire miyambo yofala ya m’tsiku lake imene imaluluza akazi. Ankalankhula ndi akazi mokoma mtima—ngakhale amene anali ndi mbiri yoipa. (Luka 7:44-50) Ndiponso, Yesu ankasangalala kuthandiza akazi odwala. (Luka 8:43-48) Nthaŵi ina pamene anaona mkazi wamasiye akulira mwana wake wamwamuna mmodzi yekha amene anali atangomwalira kumene, anapita kwa onyamula malirowo ndi kudzutsa m’nyamatayo.—Luka 7:11-15.

Akazi anali ena a ophunzira oyambirira a Yesu ndipo anali oyamba kuona kuti waukitsidwa kwa akufa. Baibulo limanena kwambiri za akazi monga Lidiya, Dorika, ndi Priska monga zitsanzo za kuchereza alendo, chifundo, ndi kulimba mtima. (Machitidwe 9:36-41; 16:14, 15; Aroma 16:3, 4) Ndipo Akristu oyambirira anaphunzitsidwa kulemekeza akazi. Mtumwi Paulo anauza mmishonale mnzake Timoteo kuti aziona “akazi aakulu ngati amayi; akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.”—1 Timoteo 5:2.

Akazi Amene Alemekezedwa

Ngati ndinu Mkristu, mudzalemekeza ndi kukonda akazi mofananamo. Simudzagwiritsira ntchito mwambo monga chifukwa chozunzira akazi. Kuchitira akazi ulemu kukhozanso kupereka umboni womveka bwino wa chikhulupiriro chanu. (Mateyu 5:16) Salima, mayi wachitsikana wa ku Afirika, anasimba za mmene anapindulira mwa kuona anthu akugwiritsa ntchito mapulinsipulo achikristu.

“Ndinakulira kumalo kumene akazi ndi atsikana amawachitira nkhanza kwambiri. Amayi anga ankagwira ntchito maola 16 patsiku, komabe ngati sanachite chinachake ankangowanena. Komabe choipa koposa zonsezo, atate amati akamwa kwambiri amawamenya. Akazi ena m’dera lathu nawonso anali ndi mavuto ofananawo. Koma ndimazindikira kuti khalidwe limenelo nloipa—kuti limatipangitsa kukhala okhumudwa ndi osasangalala. Komabe, sipanali njira yoti nkuzisinthira.

“Komabe, pamene ndinali mtsikana ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinasangalala kwambiri ndi mawu a mtumwi Petro, amene ananena kuti akazi ayenera kulemekezedwa. Komabe ndinalingalira kuti, ‘Nzokayikitsa kuti anthu akhoza kutsatira uphungu umenewu, makamaka polingalira za chikhalidwe chathu.’

“Komabe, pamene ndinapita ku Nyumba ya Ufumu, kumene Mboni zimasonkhana, amuna pamodzi ndi akazi anandilandira mokoma mtima. Chodabwitsa kwambiri chinali chakuti amuna amene analipo anali kusamaliradi akazi awo. Pamene ndinayamba kuwadziŵa bwino anthu kumeneko, ndinazindikira kuti ichi ndicho chomwe Mboni zonse zimayembekezeredwa kuchita. Ngakhale kuti ena mwa amunawo anachokera komwe kunali miyambo yofanana ndi yakwathu, anali kuchitira akazi ulemu. Ndinafuna kukhala mmodzi wa banja lalikulu limeneli.”

Njira Yothetseratu

Ulemu umene Salima anauonawo sikuti unangochitika mwangozi ayi. Unali chifukwa cha maphunziro ochokera m’Mawu a Mulungu, amene amathandiza anthu kumaonana monga olemekezeka monga mmene Mulungu amachitira. Izi ndi chizindikiro cha zomwe zingachitike tsopano lino ndi zomwe zidzachitika paliponse pamene Ufumu wa Mulungu udzakhala ukulamulira padziko lonse. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Boma lakumwamba limeneli lidzachotsa chisalungamo chonse. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Pamene maweruziro anu [Yehova] ali pa dziko lapansi, okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.”—Yesaya 26:9.

Ngakhale tsopano, maphunziro achilungamo akusintha kalingaliridwe ka anthu ochuluka. Pamene anthu onse okhala ndi moyo akhala pansi pa Ufumu wa Mulungu, maphunziro ameneŵa adzapitirira padziko lonse lapansi ndipo adzathetsa kupondereza akazi konse kumene amuna amachita, zotsatira za kuchimwa kwa Adamu. Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu, sadzalola kuti kuchitira chisalungamo akazi kudzasokoneze ulamuliro wake. Polongosola za ulamuliro wa Kristu, Baibulo limati: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.”—Salmo 72:12-14.

Nkhani izi zanena kwambiri za mavuto amene akazi amakumana nawo. Komabe, nzodziŵikiratu kuti amuna ambiri nawonso akhala akuzunzidwa. M’mbiri yonse, amuna oipa olamulira achitira amuna ndiponso akazi zoipa zoopsa zambiri. Ndipo akazi ena achitanso chimodzimodzi. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za kukhetsa mwazi wosalakwa kochitidwa ndi akazi oipa monga Yezebeli, Ataliya, ndi Herodia.—1 Mafumu 18:4, 13; 2 Mbiri 22:10-12; Mateyu 14:1-11.

Motero anthu akufunikira dziko latsopano la Mulungu, pansi pa ulamuliro wa Ufumu. Posachedwa, tsiku limenelo litayambika, palibe mkazi kapena mwamuna amene adzakhala wodedwa kapena adzachitiridwa nkhanza. M’malo mwake, tsiku lililonse lidzakhala ‘lokondweretsa’ kwa aliyense.—Salmo 37:11.

[Chithunzi patsamba 13]

Amuna achikristu amatsatira malangizo a m’Baibulo ndipo amalemekeza akazi awo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena