Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 6/8 tsamba 28-30
  • Kodi Abusa Achikristu Amafunikira Kupanga Lumbiro la Kusakwatira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Abusa Achikristu Amafunikira Kupanga Lumbiro la Kusakwatira?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukwatira Kapena Kusakwatira?
  • Chimene Chinayambitsa Umbeta Wokakamiza
  • Kodi Atumiki Achikhristu Safunika Kukwatira?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Umbeta—Khomo la Ntchito Yopanda Chocheukitsa
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Wosakwatira Koma Wokwanira Kaamba ka Utumiki wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Mulungu Amakuona Motani Kulambira kwa Dziko Lachikristu?
    Nsanja ya Olonda—1996
Galamukani!—1998
g98 6/8 tsamba 28-30

Lingaliro la Baibulo

Kodi Abusa Achikristu Amafunikira Kupanga Lumbiro la Kusakwatira?

UMBETA, kuti tinene zoona, ndiko kukhala wosakwatira. Komabe, malinga ndi The New Encyclopædia Britannica, liwulo “nthaŵi zambiri limagwiritsiridwa ntchito mogwirizana ndi udindo wa munthu yemwe ali mbetayo monga mkulu wachipembedzo, wodziŵa kwambiri zachipembedzo, kapena wodzipereka pa zachipembedzo.” Liwu lakuti “mbeta” limatanthauza “anthu amene analumbira lumbiro lopatulika kapena anthu odzimana kapena omwe amakhulupirira kuti kusakwatira nkwabwino kwa munthuyo chifukwa cha udindo wake kutchalitchi kapena kuti asonyeze kuti ngwolimbikira zachipembedzo.”

Mmbuyomu, zipembedzo zina zazikulu zinangolamula kuti abusa awo afunikira kukhala mbeta. Ndipotu, pazipembedzo zonse za m’Dziko Lachikristu, Chikatolika nchimene chapambana kudziŵika ndi umbeta. Lero, pali mkangano ndithu pankhani yaumbeta wachikatolika. Magazini yotchedwa The Wilson Quarterly inati, “m’zaka makumi angapo zapitazo, kufufuza kwa kaŵirikaŵiri kwasonyeza kuti kulamula kuti anthu azikhala mbeta, kukhala chofunikira kwa ansembe achikatolika kuyambira m’zaka za zana la 12, ndiko kwakhala muzu wa mavuto amene tchalitchicho chikukumana nawo polemba ansembe ndi kukhala nawo.” Malinga ndi katswiri wa zachikhalidwe cha anthu, Richard A. Schoenherr, “pali umboni wamphamvu wakuti kusintha kwa nthaŵi ndi chikhalidwe cha anthu kukupangitsa ena kutsutsa kuti ansembe achikatolika asamangokhala mbeta zachimuna zokha.” Kodi Baibulo limati bwanji pankhani yaumbetayi?

Kukwatira Kapena Kusakwatira?

M’mbiri yonse, amuna ndi akazi osaŵerengeka odzipereka pachipembedzo asankha kukhala mbeta. Chifukwa chiyani? Zifukwa zawo zambiri zinali zakuti ankakhulupirira kuti zinthu zakuthupi zinali “muzu wa zoipa.” Zimenezo zinayambitsa maganizo akuti munthu angakhale woyera mwauzimu kokha mwa kupeŵa kugonana. Komabe, Baibulo silimanena choncho. M’Baibulo, ukwati umaonedwa ngati mphatso yabwino, yoyera yochokera kwa Mulungu. Nkhani ya m’Genesis yonena zachilengedwe imasonyeza kuti ukwati ndi “wabwino” m’maso mwa Mulungu ndipo mwachionekere sumalepheretsa munthu kukhala paunansi wabwino wauzimu ndi Mulungu.—Genesis 1:26-28, 31; 2:18, 22-24; onaninso Miyambo 5:15-19.

Mtumwi Petro ndi atumiki ena ovomerezedwa a Mulungu omwe anali ndi maudindo mumpingo wachikristu woyambirira anali amuna okwatira. (Mateyu 8:14; Machitidwe 18:2; 21:8, 9; 1 Akorinto 9:5) Malangizo a mtumwi Paulo kwa Timoteo onena za kuika oyang’anira mpingo kapena “abishopu” akumveketsa bwino zimenezi. Analemba kuti: ‘Bishopu ayenera kukhala wopanda chitonzo, ‘mwamuna wa mkazi mmodzi.’ (1 Timoteo 3:2, Revised Standard Version, Lachikatolika) Taonanitu kuti panopa sanasonyezepo ngakhale pang’ono kuti kunali kosayenera kuti “bishopu” akwatire. Panopa Paulo anangosonyeza kuti “bishopu” asakhale ndi akazi angapo; ngati ali wokwatira, mkazi wake angokhala mmodzi yekhayo. Ndiponso, Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, yomwe analemba McClintock ndi Strong, inati: “M’Chipangano Chatsopano mulibe mawu alionse omwe angamvedwe ngati kuti ndi lamulo loletsa atsogoleri achipembedzo kukwatira chifukwa cha Uthenga Wabwino.”

Ngakhale kuti Baibulo limalemekeza ukwati kwambiri, silimatsutsa umbeta, ngati munthu wausankha mwaufulu. Baibulo limautchula kuti ndiwo njira yabwino kwa ena. (1 Akorinto 7:7, 8) Yesu Kristu anati amuna ndi akazi ena adzangosankha okha kukhala mbeta. (Mateyu 19:12) Chifukwa chiyani? Osati chifukwa choganiza kuti ukwati uli ndi kanthu kena kodetsa kamene kangawalepheretse kupita patsogolo mwauzimu iyayi. Anangosankha njira imeneyo kuti asadodometsedwe pochita chifuniro cha Mulungu poona kuti nthaŵi ikufulumira kutha.

Chimene Chinayambitsa Umbeta Wokakamiza

Komabe, zinthu zinasintha zaka mazana ambiri nthaŵi ya Kristu itapita. David Rice, wa tchalitchi cha Dominic, yemwe anasiya unsembe kuti akakwatire, anafotokoza kuti, pazaka mazana atatu oyambirira a Nyengo Yathu ino, “kunali abusa okwatira ndi osakwatira omwe.” Kenako, anthu odzitcha Akristu, anayamba kusonkhezeredwa ndi zimene wolemba wina wa zachipembedzo anafotokoza kuti “malingaliro achigiriki ophatikizidwa ndi a Baibulo,” amene anapotoza mmene anthu amaonera kugonana ndiponso ukwati.

Nzoona kuti ena anangofuna kukhala mbeta “kuti amasuke ndithu ndi kudzipereka [okha] pantchito ya Ufumu wa Mulungu.” Komabe, ena ankasonkhezeredwa ndi nzeru ya anthu akunja imene anatengera. The New Encyclopædia Britannica inati: “Chikhulupiriro chakuti kugonana kumadetsa ndipo nkosagwirizana ndi chiyero chinayambira [m’tchalitchi chotchedwa chachikristu] ngati chosonkhezera kwambiri anthu kukhala mbeta.”

Rice anati, m’zaka za zana lachinayi, tchalitchi “chinkaletsa wansembe wokwatira kugona ndi mkazi wake usiku wotsatana ndi tsiku la Ukalisitiya.” Pamene tchalitchi chinayamba kudya Ukalisitiya tsiku lililonse, zinatanthauza kuti ansembe anafunikira kulekeratu kugona ndi akazi. Patapita nthaŵi, ansembe anangowaletseratu kukwatira. Choncho, aliyense amene akanadzakhala mbusa m’tchalitchi anali kukakamizidwa kukhala mbeta.

Mtumwi Paulo anachenjeza kuti zimenezo zidzachitika. Analemba kuti: “Mzimu ukunena momvekera bwino kuti m’nthaŵi yomaliza kudzakhala ena amene adzakana chikhulupiriro ndi kusankha kumvera mizimu yosocheretsa ndi ziphunzitso zochokera ku ziŵanda . . . Azidzati ukwati ngwoletsedwa.”—1 Timoteo 4:1, 3, Jerusalem Bible.

Yesu Kristu anati: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Kukana malamulo a Mulungu kwasonyezedwa kuti ndi kwachabe ndi ntchito zake kapena mwa zotsatirapo zake. Wolemba mabuku David Rice anafunsa ansembe ambiri padziko lapansi za nkhani yaumbeta wokakamiza. Ena omwe iye analankhula nawo anati: “Umangokhalabe wansembe, nkumachita zimene ungathe, ndipo mochenjera umangogwiritsira ntchito mwayi umene akazi ena odzipereka, okusirira amapereka woti ugone nawo.”

Rice, pogwira mawu a Mateyu 7:20, anati: “Yesu anati, ‘mudzawazindikira ndi zipatso zawo.’” Ndiyeno anadzakambapo za tsoka lochitika chifukwa cha umbeta wokakamiza, kuti: “Zipatso za umbeta wokakamiza ndizo amuna achinyengo zikwizikwi, akazi zikwizikwi okhala ndi moyo wosokonekera, ana zikwizikwi okanidwa ndi atate awo omwe ali ansembe, zikakhala za ansembe ovutika mtimawo ndiye sitinena.”

Umbeta wokakamiza wafikira pakukhala wovulaza mwauzimu. Komano Umbeta wodzisankhira mwaufulu, ngakhale kuti suli chofunika choti munthu akhale woyera kapena kuti apulumuke, wakhala njira ya moyo yopindulitsa ndi yokhutiritsa mwauzimu kwa omwe ‘angathe kuulandira.’—Mateyu 19:12.

[Mawu a Chithunzi patsamba 28]

Life

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena