Umbeta—Khomo la Ntchito Yopanda Chocheukitsa
“Ndi kutsata chitsatire Ambuye, [p]opanda chocheukitsa.” —1 AKORINTO 7:35.
1. Kodi ndi mbiri yosautsa yotani imene inamfika Paulo ponena za Akristu ku Korinto?
MTUMWI Paulo anali ndi nkhaŵa ya abale ake achikristu m’Korinto, Greece. Pafupifupi zaka zisanu kumbuyoko, anali atakhazikitsa mpingo mumzinda wolemera umenewo wotchuka chifukwa cha chisembwere chake. Tsopano, pafupifupi 55 C.E., pamene anali ku Efeso, m’Asia Minor, analandira mauthenga osautsa kuchokera ku Korinto onena za magaŵano ndi kulekerera mlandu woipitsitsa wa chisembwere. Ndiponso, Paulo anali atalandira kalata kuchokera kwa Akristu a ku Korinto yopempha chitsogozo ponena za kugonana, kusakwatira, ukwati, kupatukana, ndi kukwatiranso.
2. Kodi chisembwere chofala m’Korinto chingakhale chinali kuwayambukira motani Akristu mumzindawo?
2 Chisembwere chonyansitsa chofala m’Korinto chinaoneka ngati kuti chinali kuyambukira mpingo wakumeneko m’njira ziŵiri. Akristu ena anali kulola mzimu wa kusadziletsa ndipo anali kulekerera chisembwere. (1 Akorinto 5:1; 6:15-17) Zikuchita ngati kuti ena, poipidwa ndi zokondweretsa zakugonana zokhala ponseponse mumzindawo, anachita mopambanitsa kufikira pa kuletseratu kugonana, ngakhale kwa okwatirana.—1 Akorinto 7:5.
3. Kodi ndi nkhani ziti zimene Paulo poyamba anasamalira m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto?
3 M’kalata yaitali imene Paulo analembera Akorinto, choyamba anasamalira vuto la kusagwirizana. (1 Akorinto, machaputala 1-4) Anawalangiza kuti apeŵe kutsatira anthu, kumene kungangochititsa magaŵano oipa. Anayenera kugwirizana monga “antchito anzake” a Mulungu. Ndiyeno anawapatsa malangizo olunjika osungira mpingo kukhala woyera m’makhalidwe. (Machaputala 5, 6) Ndiyeno mtumwiyo anasamalira kalata yawo.
Alimbikitsa Umbeta
4. Kodi Paulo anatanthauzanji pamene anati “kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi”?
4 Anayamba kuti: “Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.” (1 Akorinto 7:1) Mawuwo “kusakhudza mkazi” panopa akutanthauza kupeŵa kukhudzana matupi ndi mkazi pofuna kukhutiritsa chilakolako cha kugonana. Popeza Paulo anali atatsutsa kale dama, tsopano anali kunena za kugonana m’kakonzedwe ka ukwati. Chotero, Paulo tsopano anali kulimbikitsa umbeta. (1 Akorinto 6:9, 16, 18; yerekezerani ndi Genesis 20:6; Miyambo 6:29.) Kupitiriza pang’ono, analemba kuti: “Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.” (1 Akorinto 7:8) Paulo anali wosakwatira, mwinamwake wofedwa.—1 Akorinto 9:5.
5, 6. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli koonekeratu kuti Paulo sanali kulimbikitsa moyo wa amonke? (b) Kodi nchifukwa ninji Paulo analimbikitsa umbeta?
5 Kungakhale kuti Akristu m’Korinto anakhudzidŵa ndi filosofi yachigiriki, mwa imene magulu ena anathokoza kudzikana konkitsa. Kodi chimenecho chingakhale chifukwa chimene Akorinto anafunsira Paulo ngati kukanakhala “bwino” kwa Akristu kupeŵeratu kugonana? Yankho la Paulo silinasonyeze filosofi yachigiriki. (Akolose 2:8) Mosiyana ndi akatswiri a zaumulungu achikatolika, kulibe kumene analimbikitsa moyo wodzikana wa umbeta m’nyumba ya amonke kapena ya avirigo, monga ngati anthu osakwatira anali oyera kwambiri ndipo monga ngati akanathandizira chipulumutso chawo mwa moyo wawo ndi mapemphero awo.
6 Paulo analimbikitsa umbeta “chifukwa cha chivuto cha nyengo ino.” (1 Akorinto 7:26) Mwinamwake anali kunena za nthaŵi zovuta zimene Akristu analimo, zimene ukwati ukanakulitsirako mavuto ake. (1 Akorinto 7:28) Uphungu wake kwa Akristu osakwatira unali wakuti: “Kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.” Kwa amuna ofedwa, anati: “Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.” Kwa mkazi wamasiye wachikristu, analemba kuti: “Akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndiganiza kuti inenso ndili naye mzimu wa Mulungu.”—1 Akorinto 7:8, 27, 40.
Sakakamiza Kukhala Mbeta
7, 8. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti Paulo sanali kukakamiza Mkristu aliyense kukhala mbeta?
7 Mosakayikira mzimu woyera wa Yehova unali kutsogoza Paulo popereka uphungu umenewu. Nkhani yake yonse ya umbeta ndi ukwati ikusonyeza kulinganiza ndi kudziletsa. Sakuipanga kukhala nkhani ya kukhulupirika kapena kusakhulupirika. M’malo mwake, ili nkhani ya kudzisankhira, yolemerera kwambiri ku umbeta kwa aja okhoza kukhalabe oyera mumkhalidwewo.
8 Atangotchula kuti “kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi,” Paulo anawonjezera kuti: “Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.” (1 Akorinto 7:1, 2) Atalangiza anthu osakwatira ndi akazi amasiye kuti ‘akhale monganso ine,’ anafulumira kuwonjezera kuti: “Koma ngati sadziŵa kudziletsa, [asiyeni akwatire, NW]; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.” (1 Akorinto 7:8, 9) Kachiŵirinso, uphungu wake kwa amuna ofedwa unali wakuti: “Usafune mkazi. Koma ungakhale ukwatira, sunachimwa.” (1 Akorinto 7:27, 28) Uphungu wolinganiza umenewu umasonyeza ufulu wa kusankha.
9. Malinga ndi kunena kwa Yesu ndi Paulo, kodi zonse ziŵiri ukwati ndi umbeta zili motani mphatso zochokera kwa Mulungu?
9 Paulo anasonyeza kuti zonse ziŵiri ukwati ndi umbeta zili mphatso zochokera kwa Mulungu. “Mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndili ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti.” (1 Akorinto 7:7) Mosakayikira anali kukumbukira zimene Yesu ananena. Atafotokoza kuti ukwati unachokera kwa Mulungu, Yesu anasonyeza kuti umbeta wodzifunira chifukwa cha kutumikira zinthu za Ufumu uli mphatso yapadera: “Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa. Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m’mimba mwa amawo: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha ufumu wakumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.”—Mateyu 19:4-6, 11, 12.
Kulandira Mphatso ya Umbeta
10. Kodi munthu ‘angailandire’ motani mphatso ya umbeta?
10 Pamene kuli kwakuti onse aŵiri Yesu ndi Paulo analankhula za umbeta kukhala “mphatso,” sananene kuti uli mphatso yozizwitsa imene ena chabe ali nayo. Yesu anati “onse sangathe kulandira” mphatsoyo, ndipo analimbikitsa amene angathe kutero ‘kuilandira,’ zimene Yesu ndi Paulo anachita. Zoona, Paulo analemba kuti: “Nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima,” koma anali kulankhula za aja amene “sadziŵa kudziletsa.” (1 Akorinto 7:9) M’zolemba zoyambirira, Paulo anasonyeza kuti Akristu angapeŵe kutentha mtima. (Agalatiya 5:16, 22-24) Kuyenda mwa mzimu kumatanthauza kulola mzimu wa Yehova kutsogolera mapazi athu onse. Kodi Akristu achichepere angachite zimenezi? Inde, ngati atsatira kwambiri Mawu a Yehova. Wamasalmo analemba kuti: “Mnyamata [kapena mtsikana] adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mawu anu.”—Salmo 119:9.
11. Kodi kumatanthauzanji ‘kuyendayenda monga mwa mzimu’?
11 Zimenezi zimaphatikizapo kupeŵa malingaliro olekerera zinthu owanditsidwa ndi maprogramu ambiri a pa TV, akanema, nkhani za m’magazini, mabuku, ndi mawu a m’nyimbo. Malingaliro otero ngathupi. Mkristu wachichepere mwamuna kapena mkazi amene akufuna kulandira umbeta ayenera ‘kusayendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu.’ (Aroma 8:4, 5) Zinthu za mzimu zili zolungama, zoyera, zokongola, zokoma. Akristu, achichepere ndi achikulire, ayenera ‘kulingirira izi.’—Afilipi 4:8, 9.
12. Kodi nchiyani makamaka chimene chimafunika polandira mphatso ya umbeta?
12 Kulandira mphatso ya umbeta makamaka kumafuna munthu kuti asumike mtima wake pa chonulirapo chimenecho ndi kupemphera kwa Yehova kuti amthandize kuchilondola. (Afilipi 4:6, 7) Paulo analemba kuti: “Iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nawo ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga [unamwali wake, NW], adzachita bwino. [Chotero amenenso apereka unamwali wake mu ukwati achita bwino, koma amene saupereka mu ukwati adzachita bwino koposa, NW].”—1 Akorinto 7:37, 38.
Umbeta Wokhala ndi Chifuno
13, 14. (a) Kodi mtumwi Paulo anawayerekezera motani Akristu osakwatira ndi okwatira? (b) Kodi ndi m’njira yotani yokha imene Mkristu mbeta ‘angachitire bwino koposa’ aja okwatira?
13 Umbeta mwa uwo wokha suli wotamandika. Nanga, ungakhale “bwino koposa” m’lingaliro lotani? Kwenikweni zimadalira ndi mmene munthu agwiritsirira ntchito ufulu umene uwo umadzetsa. Paulo analemba kuti: “Ndithudi, ndikufuna kuti mukhale omasuka ku nkhaŵa. Mwamuna wosakwatira amadera nkhaŵa zinthu za Ambuye, mmene angapezere chiyanjo cha Ambuye. Koma mwamuna wokwatira amadera nkhaŵa zinthu za dziko, mmene angapezere chiyanjo cha mkazi wake, ndipo ali wogaŵanika. Ndiponso, mkazi wosakwatiwa, ndi namwali, amadera nkhaŵa zinthu za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi lake ndi mumzimu wake womwe. Komabe, mkazi wokwatiwa amadera nkhaŵa zinthu za dziko, mmene angapezere chiyanjo cha mwamuna wake. Koma ndikunena izi kuti inu eni mupindule, osati kuti ndikutchereni msampha, koma kukusonkhezerani kuchita choyenera ndiponso chimene chimatanthauza kutumikira Ambuye kosaleka popanda chocheukitsa.”—1 Akorinto 7:32-35, NW.
14 Mkristu mbeta amene amagwiritsira ntchito umbeta wake kulondola zonulirapo zadyera sachita “bwino koposa” Akristu okwatira. Iye apitiriza ndi umbeta, osati “chifukwa cha ufumu,” koma pa zifukwa zaumwini. (Mateyu 19:12) Mwamuna kapena mkazi wosakwatira ayenera ‘kudera nkhaŵa zinthu za Ambuye,’ kukhala wofunitsitsa ‘kupeza chiyanjo cha Ambuye,’ ndi “kutumikira Ambuye kosaleka popanda chocheukitsa.” Zimenezi zikutanthauza kupereka chisamaliro chosagaŵanika pa kutumikira Yehova ndi Kristu Yesu. Ndi kokha mwa kuchita zimenezo pamene amuna ndi akazi achikristu osakwatira amachita “bwino koposa” Akristu okwatira.
Ntchito Yopanda Chocheukitsa
15. Kodi mfundo yaikulu ya nkhani ya Paulo mu 1 Akorinto chaputala 7 njotani?
15 Mfundo yonse ya Paulo m’chaputala chimenechi njakuti: Pamene kuli kwakuti ukwati ngwololedwa ndipo, m’mikhalidwe ina, ngwoyenera kwa ena, umbeta ulidi wabwino kwa mwamuna kapena mkazi wachikristu amene akufuna kutumikira Yehova ndi zocheukitsa zochepa. Pamene kuli kwakuti munthu wokwatira ali “wogaŵanika,” Mkristu wosakwatira ali ndi ufulu wa kusumika maganizo pa “zinthu za Ambuye.”
16, 17. Kodi Mkristu wosakwatira angasumike bwino motani maganizo pa “zinthu za Ambuye”?
16 Kodi zinthu za Ambuye zimene Mkristu wosakwatira angasumikepo maganizo mwaufulu kwambiri kuposa anthu okwatira nchiyani? M’nkhani ina, Yesu analankhula za “zake za Mulungu”—zinthu zimene Mkristu sangapatse Kaisara. (Mateyu 22:21) Zinthu zimenezi kwenikweni zimakhudza moyo wa Mkristu, kulambira, ndi utumiki.—Mateyu 4:10; Aroma 14:8; 2 Akorinto 2:17; 3:5, 6; 4:1.
17 Kaŵirikaŵiri anthu osakwatira amakhala aufulu kwambiri kupereka nthaŵi pa utumiki wa Yehova, zimene zingathandizire mkhalidwe wawo wauzimu ndi ukulu wa utumiki wawo. Angathere nthaŵi yaikulu pa phunziro laumwini ndi kusinkhasinkha. Akristu amene ali mbeta nthaŵi zambiri angawonjezere mosavuta kwambiri kuŵerenga Baibulo kwawo pa ndandanda yawo kuposa aja okwatira. Angakonzekere bwino misonkhano ndi utumiki wakumunda. Zonsezi zili kaamba ka ‘kupindula kwawo.’—1 Akorinto 7:35.
18. Kodi abale ambiri osakwatira angasonyeze motani kuti akufuna kutumikira Yehova “[p]opanda chocheukitsa”?
18 Abale ambiri osakwatira amene akutumikira monga atumiki otumikira ali ndi ufulu wa kuuza Yehova kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Angafunsire kuloŵa Sukulu Yophunzitsa Utumiki, imene ili ya atumiki otumikira ndi akulu omwe ali mbeta amenenso ali ndi ufulu wa kukatumikira kumene kuli kusoŵa kwakukulu. Ngakhale abale amene saali omasuka kuchoka pampingo wawo angadzipereke kuti atumikire abale awo monga atumiki otumikira kapena akulu.—Afilipi 2:20-23.
19. Kodi alongo ambiri osakwatiwa ali odala motani, ndipo njira ina imene angakhalire dalitso ku mipingo njotani?
19 Alongo osakwatira, pokhala opanda mutu waumunthu wofunsirako ndi woikapo chidaliro, angakonde kwambiri ‘kusenza Yehova nkhaŵa zawo.’ (Salmo 55:22; 1 Akorinto 11:3) Zimenezi nzofunika makamaka kwa alongo amene ali mbeta chifukwa cha kukonda kwawo Yehova. Ngati akwatiwa m’kupita kwa nthaŵi, kudzakhala “mwa Ambuye,” kutanthauza kuti, kokha kwa munthu wodzipatulira kwa Yehova. (1 Akorinto 7:39) Akulu amayamikira kuti ali ndi alongo osakwatiwa m’mipingo mwawo; nthaŵi zambiri ameneŵa amachezera odwala ndi okalamba ndi kuwathandiza. Zimenezi zimadzetsa chimwemwe kwa onse okhudzidwa.—Machitidwe 20:35.
20. Kodi Akristu ambiri akusonyeza motani kuti ‘akutsata chitsatire Ambuye popanda chocheukitsa’?
20 Akristu achichepere ambiri alinganiza mikhalidwe yawo kuti ‘atsate chitsatire Ambuye, [p]opanda chocheukitsa.’ (1 Akorinto 7:35) Iwo akutumikira Yehova monga atumiki aupainiya a nthaŵi zonse, amishonale, kapena akutumikira pa imodzi ya maofesi anthambi a Watch Tower Society. Ndipo alidi gulu lachimwemwe chotani nanga! Kukhalapo kwawo nkotsitsimula chotani nanga! Eya, kwa Yehova ndi Yesu, iwo ali “ngati mame.”—Salmo 110:3, NW.
Palibe Lumbiro la Umbeta Wosatha
21. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli koonekeratu kuti Paulo sanalimbikitse kuchita lumbiro la umbeta? (b) Kodi anatanthauzanji pamene analankhula za kukhala ‘wopitirira pa chimake cha unyamata’?
21 Mfundo yaikulu pa uphungu wa Paulo njakuti Akristu angachite “bwino” kulandira umbeta m’moyo wawo. (1 Akorinto 7:1, 8, 26, 37) Komabe, sakuwapempha kuchita lumbiro la umbeta ayi. M’malo mwake, analemba kuti: “Ngati wina aganiza kuti akuchitira unamwali wake chosayenera, ngati anapitirira pa chimake cha unyamata, ndipo zichitika motero, achite zimene afuna; sachimwa. Asiyeni akwatire.” (1 Akorinto 7:36, NW) Liwu limodzilo lachigiriki (hy·peʹra·kmos) lotembenuzidwa “[ku]pitirira pa chimake cha unyamata” kwenikweni limatanthauza “kupyola pa kaindeinde” ndipo limanena za kupitirira pamene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu kwambiri. Chotero aja amene akhala zaka zambiri pa umbeta ndipo m’kupita kwa nthaŵi aganiza kuti ayenera kukwatira ali ndi ufulu wonse wa kukwatira wokhulupirira mnzawo.—2 Akorinto 6:14.
22. Kodi nchifukwa ninji munthu aliyense ayenera kukuona kukhala kwabwino kwa Mkristu kusakwatira akali wachichepere?
22 Zaka zimene Mkristu wachichepere amawonongera pa kutumikira Yehova popanda chocheukitsa ndizo kukundika chuma mwanzeru. Zimamlola kupeza nzeru yeniyeni, chidziŵitso, ndi luntha. (Miyambo 1:3, 4) Munthu amene wakhala mbeta chifukwa cha Ufumu, pambuyo pake ngati afuna, amakhala m’malo abwino kwambiri akusenza mathayo a muukwati ndipo mwinamwake a ukholo.
23. Kodi ena amene akulingalira zokwatira angakhale ndi cholinga chotani, koma kodi ndi funso liti limene tidzapenda m’nkhani zotsatira?
23 Akristu ena amene atha zaka zambiri akutumikira Yehova nthaŵi zonse monga mbeta amasankha mosamala mnzawo wamtsogolo ndi cholinga cha kupitiriza mu utumiki wa nthaŵi zonse wakutiwakuti. Zimenezitu nzoyamikirika koposa. Enanso angakhale akuganiza za kukwatira ndi lingaliro la kusalola ukwati wawo kupinga utumiki wawo mwanjira iliyonse. Koma kodi Mkristu wokwatira ayenera kuganiza kuti ali waufulu kusumika maganizo pa utumiki wake kwa Yehova monga momwe analili pamene anali mbeta? Funso limeneli tidzalipenda m’nkhani zotsatira.
Mwa Kubwereramo
◻ Kodi nchifukwa ninji mtumwi Paulo anaona kufunika kwa kulembera mpingo wa ku Korinto?
◻ Kodi tidziŵa bwanji kuti Paulo sanali kulimbikitsa moyo wa amonke?
◻ Kodi munthu ‘angaulandire’ motani umbeta?
◻ Kodi alongo osakwatiwa angapindule motani ndi umbeta wawo?
◻ Kodi abale osakwatira angaugwiritsire ntchito bwino motani ufulu wawo wa kutumikira Yehova ‘popanda chocheukitsa’?