Umbeta—Njira Yopatsa Mphoto ya Moyo
“Ali womasuka kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali.”—1 AKORINTO 7:39, 40.
1. Kaya ndife osakwatira kapena okwatira, nchiyani chimene tiri ndi mangawa kwa Yehova?
YEHOVA amafunikira kulambira kwa mtima wonse kwa awo omwe adzipereka kwa iye. Kaya ndife okwatira kapena ndife osakwatira, tiyenera kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo, ndi mphamvu. (Marko 12:30) Zowona, Mkristu wosakwatira ali ndi zocheutsa zochepa kuposa awo ogwirizana mu ukwati. Koma kodi mtumiki wosakwatira wa Yehova angakhaledi wachimwemwe?
2, 3. (a) M’chenicheni, nchiyani chimene Paulo ananena pa 1 Akorinto 7:39, 40? (b) Ndi mafunso otani amene timafunikira kuwalingalira?
2 Mtumwi Paulo akuyankha kuti inde. Ponena za awo amene anali okwatira koma amene mikhalidwe yawo inasintha, iye akulemba kuti: “Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali moyo, koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga, ndipo ndiganiza kuti inenso ndiri nawo mzimu wa Mulungu.—1 Akorinto 7:39, 40.
3 Popeza Paulo akusonyeza kuti anthu osakwatira angakhale achimwemwe, ndani amene molinganizika angalingalire kukhala wosakwatira, chifupifupi kwa nthaŵi ina? Nchiyani chimene chimathandizira ku chimwemwe cha Akristu osakwatira? Ndithudi, ndimotani mmene umbeta ungakhalire njira yopatsa mphoto ya moyo?
Zaka Zopatsa Mphoto za Umbeta
4. Nchiyani chimene chiri chowona ponena za zaka za unamwali?
4 Mfumu yanzeru Solomo inafulumiza kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, [aukalamba], ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, ‘Sindikondwera nazo.’” (Mlaliki 12:1) Zaka za unyamata ndi unamwali mwachisawawa ziri nthaŵi za chifupifupi kuyerekezera kwa zenizeni ndi umoyo wabwino. Ndi choyenerera chotani nanga, kuti zinthu zimenezi zigwiritsiridwe ntchito mu utumiki wa Yehova popanda zocheutsa! M’kuwonjezerapo, zaka zoyambirira zimenezi ziri nthaŵi ya kupeza chidziŵitso m’moyo, kukulitsa kukhazikika. Koma iyi irinso nthaŵi pamene anthu achichepere akudziko amakumana ndi chikondi chonyenga. Mwachitsanzo, lingalirani zotulukapo za kufufuza kokhudza anthu 1,079 a misinkhu ya 18 ndi 24. Iwo anali ndi avereji ya “zokumana nazo za chikondi” zisanu ndi ziŵiri aliyense ndipo mosasiyana iwo ananena kuti zokumana nazo zawo zaposachedwapa zinali chikondi chowona, osati chikondi chonyenga.
5. Ponena za ukwati, ndi mafunso aumwini otani amene ali oyenerera kaamba ka anthu achichepere kuwalingalira?
5 Ziŵerengero za kulekana, kutha kwa ukwati ndi mabanja osweka zimasonyeza kusayenerera kwa uphungu waukwati wa mwamsanga. M’malo mothamangira m’kucheza, ubwenzi, ndi ukwati, Akristu achichepere amakhala anzeru kulingalira ndi chonulirapo chabwino ponena za mmene angagwiritsire ntchito zaka zawo zoyambirira mu utumiki wosacheutsidwa kwa Yehova. M’kuŵerengera mikhalidwe yanu monga munthu wachichepere, mungachite bwino kudzifunsa inu mwini mafunso awa: Kodi tsopano ndiri wachikulire mwamaganizo ndi wokonzekera kuganizira mosamalitsa za ukwati? Kodi ndiri ndi chidziŵitso chokwanira m’moyo kukhala mnzake wa mu ukwati wabwino? Kodi moyenerera ndinganyamule mathayo a ukwati ndipo mothekera abanja ndi ana? M’chiyang’aniro cha kudzipereka kwanga kwa Yehova, kodi sindiyenera kumupatsa iye nyonga ndi mphamvu ya uchichepere popanda zocheutsa zogwirizana ndi ukwati?
Mphoto za Umbeta Woyera
6, 7. (a) Ndi mwaŵi wina uti umene mwachisawawa umasangalalidwa ndi Akristu osakwatira? (b) M’chigwirizano ndi ichi, nchiyani chimene m’mishonale wosakwatira mu Africa ananena?
6 Akristu osakwatira amasangalala ndi ufulu kuchokera ku zocheutsa ndipo angapeze “zambiri zochita mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akorinto 7:32-34; 15:58) M’malo molunjikitsa chidwi pa munthu mmodzi wa chiwalo chosiyana, munthu wosakwatira ali ndi mwaŵi wambiri wa kufutukula mu chikondi cha Chikristu kaamba ka ambiri mu mpingo, kuphatikizapo achikulire ndi ena omwe ali ofunikira thandizo lachikondi. (Masalmo 41:1) Mwachisawawa, anthu osakwatira ali ndi nthaŵi yambiri kaamba ka kuphunzira ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu. (Miyambo 15:28) Iwo ali ndi mwaŵi wochuluka wa kukulitsira unansi wathithithi ndi Yehova, kuphunzira kudalira mokulira pa iye ndi kufuna chitsogozo chake. (Masalmo 37:5; Afilipi 4:6, 7; Yakobo 4:8) Mwamuna wosakwatira yemwe wakhala akutumikira Yehova kwa zaka zingapo monga m’mishonale mu Africa ananena kuti:
7 “Moyo m’midzi ya ku Africa wakhala wopepuka mkati mwa zaka zimenezi, popanda zocheutsa zambiri za kutsungula kwa makono. Popanda zocheutsa zimenezi, ndakhala ndi mwaŵi wabwino wa kuphunzira ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu. Ichi chandipangitsa ine kukhala wamphamvu. Inde, moyo wa umishonale wakhaladi dalitso lenileni ndi chinjirizo molimbana ndi kukondetsa zinthu za kuthupi. Mkati mwa madzulo osangalatsa kumalo otentha pakhala nthaŵi yokwanira ya kusinkhasinkha ndi kuwunikira pa chilengedwe cha Yehova ndi kusendera kufupi ndi iye. Chimwemwe changa chachikulu kwambiri chimabwera madzulo aliwonse pamene maganizo anga adakali ogalamuka, ndipo pamene ndiri ndekha ndingathere nthaŵi ina pansi pa miyamba ya nyenyezi kuyenda ndi kulankhula ndi Yehova. Ichi chandikokera ine kufupi ndi Yehova.”
8. Ponena za umbeta, nchiyani chimene chinanenedwa ndi mlongo wosakwatiwa wokhala ndi zaka zambiri za utumiki pa malikulu a Sosaite?
8 Chodziŵika, kachiŵirinso, iri ndemanga ya mlongo wosakwatiwa wokhala ndi zaka zambiri za utumiki pa malikulu a Watch Tower Society: “Ndasankha kutsogoza moyo wa umbeta mu utumiki wanga kwa Yehova. Kodi ndimadzimva wosungulumwa? Kutalitali. Ndithudi, mphindi zanga zokhala ndekha ziri pakati pa zabwino koposa. Ndingalankhule ndi Yehova m’pemphero. Ndingasangalale ndi kusinkhasinkha ndi phunziro laumwini popanda zocheutsa. . . . Umbeta wagawirako osati zochepa ku chimwemwe changa.”
9. Ndi mwaŵi wina uti wa utumiki umene Mkristu wosakwatira angakhale wokhoza kusangalala nawo?
9 Munthu wosakwatira angalandirenso mwaŵi wautumiki umene sungakhale wotseguka kwa anthu okwatira okhala ndi mathayo abanja. Mwachitsanzo, pangakhale mwaŵi wa kudzilowetsa mu utumiki wa nthaŵi zonse monga mpainiya mu gawo limene chifuno kaamba ka olengeza a Ufumu chiri chokulira. Kapena mwamuna wosakwatira wachichepere angapatsidwe mwaŵi wa kutumikira monga chiwalo cha banja la Beteli pa malikulu a Watch Tower Society kapena ofesi ya nthambi. Mkazi wachichepere wosakwatiwa angakhale wokhoza kugwirizana ndi mlongo wosakwatiwa wachikulirepo mu utumiki wa upainiya mu mpingo wawo wa kumaloko kapena mpingo wina wokhala ndi gawo lomwe likufunika kukwaniritsidwa. Bwanji osakambitsirana kuthekera koteroko ndi woyang’anira wa dera? Monga Mkristu wosakwatiwa, dzipangeni inu mwini kukhalapo kaamba ka utumiki wowonjezereka ku chilemekezo cha Yehova, ndipo iye adzakudalitsani inu mochuluka.—Malaki 3:10.
Zitsanzo za Kale
10. Ndi ndani amene anapereka chitsanzo choyambirira cha mtumiki wosakwatira wa Yehova, ndipo nchiyani chimene mukulingalira kuti umbeta wake unali ndi mwaŵi?
10 Chitsanzo choyambirira cha mtumiki wosakwatira wa Yehova chinali Yesu Kristu. Iye anali womwerekera kotheratu m’kuchita chifuno cha Mulungu. “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake,” anatero Yesu. (Yohane 4:34) Iye anali wotanganitsidwa chotani nanga—kulalikira, kuchiritsa odwala, ndi zina zowonjezereka! (Mateyu 14:14) Yesu anali ndi chikondwerero chenicheni mwa anthu ndipo anali wokhazikika pamaso pa amuna, akazi, ndi ana. Ndithudi, iye anayendayenda mu utumiki wake, ndi ena akutsagana naye pa nthaŵi zina. (Luka 8:1-3) Koma ikanakhala yovuta chotani nanga ntchito imeneyo ngati iye akanayenera kutsagana ndi mkazi ndi ana a ang’ono! Mosakaikirika, umbeta unali mwaŵi mu nkhani ya Yesu. Lerolino, Mkristu wosakwatira angasangalale ndi mwaŵi wofananawo, makamaka ngati iye aitanidwa kukalalikira uthenga wa Ufumu ku malo a ku midzi kapena ku malo owopsya.
11, 12. Ndi zitsanzo zabwino zotani zimene zingagwidwe mawu kaamba ka alongo osakwatiwa amene akutumikira Yehova lerolino?
11 Koma ena amapeza umbeta kukhala wogwira ntchito ndi wopatsa mphoto. Mwana wa mkazi wa Yefita modzipereka anakwaniritsa lumbiro la atate wake mwakukhala wosakwatira mu chitaganya chomwe chinapereka chigogomezero chachikulu pa ukwati ndi ana. Iye anapeza chimwemwe mu utumiki wake kwa Yehova, ndipo chinali chodziŵika kuti ena anamulimbikitsa iye mokhazikika. Nkulekelanji, popeza kuti “ana akazi a Israyeli akamuka chaka ndi chaka kumlirira mwana wa Yefita wa ku Gileadi, masiku anayi pa chaka”! (Oweruza 11:34-40) Mofananamo, Akristu okwatira ndi ena ayenera kuyamikira ndi kulimbikitsa akazi osakwatiwa amene mwamphamvu akutumikira Yehova lerolino.
12 Ana a akazi anamwali anayi a Filipo “ananenera.” (Machitidwe 21:8, 9) Akazi osakwatiwa amenewa angakhale anapeza chikwaniritso chochuluka kuchokera ku utumiki wawo wokangalika kuchilemekezo cha Yehova. Mofananamo, akazi ambiri achichepere osakwatiwa lerolino apeza mphoto ya mwaŵi wa kutumikira monga apainiya, kapena olengeza a nthaŵi zonse a Ufumu. Ndithudi, iwo amafunikira chiyamikiro monga mbali ya ‘khamu lalikulu la akazi akulalikira uthenga.’—Masalmo 68:11.
13. Kodi ndimotani mmene nkhani ya Paulo ikuchitira chitsanzo kuti umbeta ungakhale njira yopatsa mphoto ya moyo?
13 Mtumwi Paulo anapeza umbeta kukhala wopatsa mwaŵi. Iye anayenda zikwi za mamailosi mu utumiki wake ndi kukumanizana ndi mavuto a akulu, zowopsya zochuluka, kusala tulo, njala yowawa. (2 Akorinto 11:23-27) Mosakaikira, zonsezi zikanakhala zovuta kwambiri ndi zotsendereza ngati Paulo anali wokwatira. M’kuwonjezerapo, sichiri chothekera nkomwe kuti iye akanakhala ndi mwaŵi wake monga “mtumwi kwa amitundu” ngati iye anali kulera banja. (Aroma 11:13) Mosasamala kanthu za ziyeso zomwe anakumanizana nazo, Paulo anali ndi chitsimikiziro choyamba chakuti umbeta ungakhale njira yopatsa mphoto ya moyo.
Zitsanzo Zamakono
14. Ndi zokumana nazo zotani zimene zinasangalalidwa ndi makoputala, ambiri a amene anali osakwatira?
14 Mofanana ndi Paulo ndi Akristu ena oyambirira osakwatira, unyinji wa anthu a Mulungu amene anagawanamo mu ntchito ya ukoputala (kuyambira 1881 kunka mtsogolo) anali anthu osakwatira opanda mabanja owadalira. Iwo modzipereka anapita ku mizinda ya chilendo, matauni, ndi malo a kumidzi, kufunafuna awo a mitima yabwino ndi kugawira mabukhu a Baibulo kwa iwo. Kuyenda kungakhale kwa pa sitima, pa njinga yopalatsa, pa ngolo yokokedwa ndi ng’ombe, kapena pa galimoto. Mokulira, iwo mwachimwemwe anayenda kuchokera kunyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20, 21) “Nthaŵi zina anali kusinthanitsana [mabukhu a Baibulo] ndi zotulutsidwa m’munda, nkhuku, sopo ndi chirichonse chomwe analibe, chomwe akanagwiritsira ntchito kapena kugulitsa kwa ena,” inakumbukira tero mboni imodzi ya Yehova, ikumawonjezera kuti: “Nthaŵi zina, m’malo okhala omwazikanamwazikana, iwo anakhala ndi alimi ndi osunga ng’ombe usiku, ndipo panthaŵi zina anali kugona mosungira zakudya za zoweta . . . Okhulupirika amenewa [ambiri amene anali osakwatira] anapitiriza kwa zaka ndi zaka kufikira ukalamba unawapitirira iwo.” Ndithudi, mmodzi wa iwo analankhula kaamba ka makoputala anthaŵi yakale amenewo mwachisawawa pamene analemba kuti: “Tinali achichepere ndi achimwemwe mu utumiki, osangalatsidwa kuthera mphamvu yathu mu utumiki wa Ya.”
15. Kwa apainiya ambiri osakwatira, ndi khomo lotani lotsogolera ku utumiki wowonjezereka limene linatseguka zaka 45 zapita?
15 Apainiya ambiri, kapena olengeza Ufumu a nthaŵi zonse, a pambuyo pake analinso osakwatira. Iwo kaŵirikaŵiri anachitira umboni ku malo otalikirana, anathandiza kuyambitsa mipingo yatsopano, ndipo anasangalala ndi madalitso ena mu utumiki wa Yehova. Kwa ena a iwo, khomo losangalatsa lotsogolera ku ntchito yowonjezereka linatseguka pamene Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower inayamba kugwira ntchito mu 1943 pamene Nkhondo ya Dziko ya II inali mkati. (1 Akorinto 16:9) Inde, ambiri a apainiya osakwatira amenewo analandira maphunziro a umishonale pa Sukulu ya Gileadi ndipo mwamsanga anali kufalitsa uthenga wa Ufumu m’magawo atsopano. Osatsenderezedwa ndi mathayo a m’banja, iwo anadzipanga iwo eni kukhalapo kaamba ka utumiki wa Yehova, ndipo ena a omaliza maphunziro oyambirira amenewo adakali osakwatira ndipo okangalika m’munda wa umishonale kapena mbali ina ya utumiki wa nthaŵi zonse.
16. Ndi chitsimikiziro chotani chimene chiripo chakuti ziwalo zosakwatira za banja la Beteli zapeza umbeta kukhala njira yopatsa mphoto ya moyo?
16 Akristu ambiri osakwatira akhala akutumikira kwa zaka zambiri monga ziwalo za banja la Beteli pa malikulu a Watch Tower Society kapena pa nthambi zake kwina kulikonse m’dziko lapansi. Kodi iwo apeza umbeta kukhala njira yopatsa mphoto ya mwaŵi? Inde, ndithudi. Mwachitsanzo, mbale wosakwatira yemwe wakhala akutumikira pa Beteli ya Brooklyn kwa zaka zochuluka anachitira ndemanga kuti: “Chimwemwe cha kuwona mamiliyoni a magazini ndi zofalitsidwa zina zokhala ndi uthenga wa Mawu a Mulungu zikufalikira ku malekezero a dziko lapansi chakhala mphoto yozizwitsa mwa iyo yokha.” Pambuyo pa zaka 45 za utumiki wa pa Beteli, mbale wina wosakwatira ananena kuti: “Tsiku lirilonse ndimapempha Atate wa kumwamba wachikondi m’pemphero kaamba ka thandizo ndi nzeru kudzisunga inemwini waumoyo wabwino mwauzimu ndiponso mwa kuthupi ndiponso wamphamvu kotero kuti ndipitirize kuchita chifuniro chake chofutukulika. . . . Ndasangalaladi ndi njira ya moyo yachimwemwe, yopatsa mphoto ndi yodalitsidwa.”
Kusunga Umbeta Woyera
17. Kodi ndi zithandizo ziŵiri ziti zimene ziripo m’kusunga chiyero mu umbeta?
17 Kunena kuti moyo wa umbeta ungakhale wopatsa mphoto chiri chotsimikizirika kuchokera ku zitsanzo za Baibulo ndi zamakono. Ndithudi, mkati mwa nthaŵi iriyonse ya moyo wanu imene mungathere m’mkhalidwe wa umbeta, mukafunikira ‘kuima wokhazikika mu mtima mwanu.’ (1 Akorinto 7:37) Koma nchiyani chimene chingathandize kusunga chiyero pamene muli wosakwatira? Magwero a akulu kwambiri athandizo ali Yehova, “Wakumva pemphero.” (Masalmo 65:2) Chotero chipangeni icho chizoloŵezi kupembedzera iye mobwerezabwereza. “Limbikani m’kupemphera,” kupempha kaamba ka mzimu wa Mulungu ndi thandizo lake m’kusonyeza zipatso zake, zomwe zimaphatikizapo mtendere ndi chidziletso. (Aroma 12:12; Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Kenaka, kachiŵirinso, ndi mkhalidwe wa pemphero, sinkhasinkhani mokhazikika ndipo nthaŵi zonse gwiritsirani ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu.
18. Kodi ndimotani mmene 1 Akorinto 14:20 akugwirizanira m’kukhala woyera monga munthu wosakwatira?
18 Thandizo lina m’kusunga umbeta woyera liri kupewa chirichonse chimene chimadzutsa chilakolako cha chisembwere. Mwachiwonekere, ichi chimaphatikizapo zithunzithunzi za maliseche ndi zosangulutsa za makhalidwe oipa. Paulo ananena kuti: “M’choipa khalani makanda, koma m’chidziŵitso akulu misinkhu.” (1 Akorinto 14:20) Musafunefune chidziŵitso kapena luso ponena za choipa, koma ndi thandizo la Mulungu mwanzeru khalani opanda chidziŵitso ndi opanda liwongo monga ana m’nkhaniyi. Panthaŵi imodzimodziyo, kumbukirani kuti mkhalidwe woipa wa chisembwere ndi kuchita cholakwa ziri zosayenera m’maso mwa Yehova.
19. Ndi malemba otani amene aloza ku njira zina za kukhala woyera monga munthu wosakwatira?
19 Mudzathandizidwanso kukhalabe woyera monga Mkristu wosakwatira mwa kuchinjiriza mayanjano anu. (1 Akorinto 15:33) Pewani kuyanjana ndi awo amene amapanga kugonana ndi ukwati mbali zazikulu m’miyoyo yawo ndi kukambitsirana. Mwanjira iriyonse pewani kulankhula zopanda pake! Paulo anapereka uphungu kuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.”—Aefeso 5:3, 4.
Mtsogolo Mopatsa Mphoto
20. Kuika zaka za wina za umbeta kukugwiritsiridwa ntchito kwabwino koposa mu utumiki wa Yehova kumatulukapo mu chiyani?
20 Kuika zaka zanu monga Mkristu wosakwatira ku kuthekera kwa kugwiritsiridwa ntchito kwabwino koposa mu utumiki wa Yehova kudzabweretsa chikwaniritso cha panthaŵi ino ndi mtendere wa maganizo. Kuchita tero kudzathandizira ku kukula kwanu kwauzimu ndi kukhazikika. Ngati mukhalabe wosakwatira kaamba ka Ufumu kufikira mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu, Yehova sadzaiwala zoyesayesa zanu zodzipereka mu utumiki wake wopatulika.
21. Ngati mudzayenera kukwatiwa mtsogolo pambuyo pa nyengo ya chiyero ndi umbeta wopatsa mphoto, kodi inu mudzalowa mu ukwati ndi chiyani?
21 Ngati inu mwakhama mulondola zikondwerero za Ufumu monga mwamuna kapena mkazi wosakwatira, mudzasangalala ndi madalitso ambiri. (Miyambo 10:22) Kenaka ngati mudzakwatira nthaŵi ina kutsogolo, mudzalowa mu ukwati ndi chidziŵitso chokulira ndi chiyambi cholemera chauzimu. Kuwonjezerapo, mwakutsatira uphungu wa m’Malemba, mudzasankha mnzanu wodzipereka wosunga umphumphu yemwe adzakuthandizani inu kutumikira Mulungu mokhulupirika. Panthaŵi ino, mungapeze umbeta kukhala njira yopatsa mphoto mu utumiki wa Mulungu wathu wa chikondi, Yehova.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Pakati pa atumiki a Yehova, ndi ziti zomwe ziri mphoto zina za umbeta woyera?
◻ Ndi zitsanzo za m’Malemba zotani zimene ziripo za kusonyeza kuti umbeta ungakhale wopatsa mphoto?
◻ M’nthaŵi zamakono, ndi zitsanzo zotani za umbeta wopatsa mphoto zimene tiri nazo?
◻ Nchiyani chimene chingathandize Mkristu kukhalabe woyera pamene ali wosakwatira?
[Bokosi patsamba 19]
Zothandiza m’Kusunga Umbeta Woyera
◆ Pempherani mokhazikika kaamba ka mzimu wa Mulungu ndi thandizo lake m’kusonyeza zipatso zake
◆ Sinkhasinkhani ndipo mokhazikika gwiritsirani ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu
◆ Pewani zithunzithunzi za maliseche ndi zosangulutsa zoipa
◆ Chinjirizani mayanjano anu
◆ Pewani kulankhula konyansa ndi zolankhula zopanda pake
[Zithunzi patsamba 19]
Mwana wamkazi wa Yefita, mtumwi Paulo, ndi atumiki ena a Yehova anapeza umbeta kukhala njira yopatsa mphoto ya moyo. Kodi mungatero?