‘Ilandireni’
1 Nthaŵi ina, polankhula ndi ophunzira ake za ukwati, Yesu ananena za kusakwatira kapena kusakwatiwa monga ‘chopatsidwa’ kapena kuti mphatso. Ndiyeno iye anati: “Amene angathe kulandira ichi achilandire.” (Mat. 19:10-12) Patapita zaka zingapo, mtumwi Paulo analemba za ubwino wokhala wosakwatira kapena wosakwatiwa ndipo analimbikitsa ena kutsatira chitsanzo chake chokhala wosakwatira. (1 Akor. 7:7, 38) Anthu ambiri masiku ano ‘alandira’ mphatso yosakwatira kapena yosakwatiwa ndipo akusangalala ndi ubwino wake. Kodi ubwino wake wina ndi uti?
2 Kutumikira ‘Popanda Chocheukitsa’: Paulo anadziŵa kuti kukhala wosakwatira kunam’patsa mpata wotumikira Yehova ‘popanda chocheukitsa.’ Mofananamo masiku ano, mbale wosakwatira angafunsire kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, ndipo nthaŵi zambiri munthu wosakwatira kapena wosakwatiwa amakhala womasuka kuyamba ntchito ya upainiya, kukatumikira kumene olalikira ali ochepa, kutumikira pa Beteli kapena kudzipereka kuti achite mautumiki ena apadera. Iye angakhale ndi nthaŵi ndiponso mipata yambiri yochita phunziro laumwini lozama ndiponso kusinkhasinkha mwakuya ndi kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Munthu wosakwatira kapena wosakwatiwa nthaŵi zambiri amakhala ndi nthaŵi yochuluka yodzipereka pothandiza anthu ena. Ntchito zonsezi ‘zimapindulitsa’ mwiniyo.—1 Akor. 7:32-35; Mac. 20:35.
3 Kutumikira Mulungu popanda chocheukitsa kotero kuli ndi mphoto yaikulu. Atakhala ku Kenya zaka 27, mlongo wosakwatiwa analemba kuti: “Ndinali ndi mabwenzi ambiri ndiponso ntchito yochuluka. Tinali kuchitira zinthu pamodzi [ndipo] tinali kuchezerana. . . . Ndinatha kugwiritsa ntchito ufulu wowonjezeka wotha kupita malo alionse umene ndinali nawo chifukwa chosakwatiwa kuti ndidzitangwanitse m’utumiki, ndipo zimenezi zandipatsa chimwemwe chachikulu.” Iye anawonjezera kuti: “M’zaka zonsezi ubwenzi wanga ndi Yehova wakula kwambiri.”
4 Kugwiritsira Bwino Ntchito Mphatso Yokhala Wosakwatira Kapena Wosakwatiwa: Yesu anati cholinga chokhalira ndi mphatso yosakwatira kapena yosakwatiwa chiyenera kukhala “chifukwa cha Ufumu wa kumwamba.” (Mat. 19:12) Monga mmene zimakhalira ndi mphatso iliyonse, kusakwatira kapena kusakwatiwa kuyenera kugwiritsidwa ntchito bwino kuti kukhale kosangalatsa ndi kopindulitsa. Mwa kugwiritsira ntchito mipata imene kusakwatira kapena kusakwatiwa kumakhala nayo ndiponso mwa kudalira Yehova kuti awapatse nzeru ndi nyonga, anthu ambiri osakwatira kapena osakwatiwa atha kudziŵa phindu lolandira mphatsoyi.