Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 6/8 tsamba 30-32
  • Kusankhapo Pakati pa Atate Aŵiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusankhapo Pakati pa Atate Aŵiri
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukulira m’Dziko Lodzala ndi Udani
  • Kusintha Malingaliro
  • Chosankha Chovuta kwa Mnyamata Wazaka 17
  • Kuchirimika
  • Kulipsira
  • Kuthaŵira ku Greece
  • Kuyanjananso Patapita Zaka Zisanu ndi Chimodzi
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Ndinagwirizana ndi Bambo Anga Patatha Zaka Zambiri
    Baibulo Limasintha Anthu
  • Mulungu Anandithandiza Kugonjetsa Mayesero
    Galamukani!—2008
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 6/8 tsamba 30-32

Kusankhapo Pakati pa Atate Aŵiri

“Sindiwenso mwana wanga! Choka msanga m’nyumba muno ndipo udzabwerenso ukadzasiya chipembedzo chimenecho!”

NDINASAMUKADI ndi zovala zokhazo zimene ndinavala. Mfuti zinali kuphulika m’derali usikuwo, ndipo ndinasoŵa kopita. Panapita zaka zoposa zisanu ndi chimodzi ndisanabwerere kunyumba.

Kodi nchiyani chimene chinakwiyitsa atatewo mpaka kupitikitsa mwana wawo chotere? Chabwino, ndikufotokozereni mmene zinayambira.

Kukulira m’Dziko Lodzala ndi Udani

Makolo anga amakhala ku Beirut, Lebanon, dziko limene kale linali kutchuka chifukwa chokopa alendo. Komabe, kuyambira mu 1975 mpaka mu 1990, mzindawo unali pachimake pa nkhondo yosakaza. Ndinabadwa mu 1969, mwana wachisamba m’banja lachiarmeniya la ana atatu. Choncho, nthaŵi imene ndinali wochepa kunali mtendere.

Makolo anga anali a m’chipembedzo cha Armenian Apostolic Church, koma Amayi ankakonda kupita nafe kutchalitchi kaŵiri kokha pachaka—pa Isitala ndi pa Krisimasi. Choncho, banja lathu linali losapembedza kwenikweni. Komabe, ananditumiza kusekondale ya Evangelical, kumene ndinakaphunzira zachipembedzo. Komabe, panthaŵiyo, ndinalibe chidwi ndi zinthu zachipembedzo.

Chinthu china chimene Aarmeniya anaphunzira akali ana nchakuti iwo anayenera kuda Aturki. Panthaŵi ya Nkhondo Yadziko I, Aturki anapha Aarmeniya zikwi mazana ambiri ndipo analanda dera lalikulu la dziko la Armenia. Mu 1920, dera lakummaŵa limene sanalilande linakhala boma la Soviet Union. Monga mnyamata, ndinatsimikiza mtima kumenya nkhondo mpaka chilungamo chitadza.

Kusintha Malingaliro

Komabe, m’ma 1980, pamene ndinali m’zaka zaunyamata, zinthu zimene amalume anandiuza zinandisonkhezera kusintha malingaliro anga. Iwo ananena kuti Mulungu Wamphamvuyonse posachedwapa adzathetsa kupanda chilungamo konse. Iwo anafotokoza kuti mwa Ufumu umene Yesu Kristu anauza otsatira ake kuupempherera, ngakhale anthu amene anaphedwa pachipululutso adzaukitsidwa nakhala ndi moyo padziko lapansi.—Mateyu 6:9, 10; Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 21:3, 4.

Ndinachita chidwi kwambiri. Pofuna kudziŵa zambiri, ndinapitiriza kuwafunsa mafunso. Zimenezi zinayambitsa phunziro la Baibulo, limene tinali kuchitira m’nyumba ya wa Mboni wina.

Pamene ndinaphunzira za Atate wanga wakumwamba, Yehova, ndikuyamba kumkonda kwambiri, ndinayamba kulingalira kuti tsiku lina ndidzavutika kusankha—pakati pa banja langa ndi Yehova Mulungu.—Salmo 83:18.

Chosankha Chovuta kwa Mnyamata Wazaka 17

M’kupita kwa nthaŵi, Amayi anamva kuti ndikuyanjana ndi Mboni za Yehova. Iwo anakhumudwa kwambiri ndipo anandiuza kuti ndisiye kuchita phunziro langa la Baibulo. Pamene anadziŵa kuti ndinatsimikiza mtima kutsatira chikhulupiriro changa, iwo anandiopseza kuti adzauza Atate za nkhaniyo. Panthaŵiyo, sindinade nkhaŵa chifukwa chakuti ndinalingalira kuti ndidzatha kukambirana nawo Atatewo ndi kuchirimika. Koma ndinalingalira molakwa.

Pamene Atate anadziŵa kuti ndinali kuyanjana ndi Mboni za Yehova, iwo anakwiya kwambiri. Anandiopseza kuti adzandipitikitsa panyumba ngati sindisiya kuchita phunziro langa la Baibulo. Ndinawauza kuti sindidzasiya chifukwa chakuti chimene ndinali kuphunziracho chinali choonadi. Atafuula, kubangula, ndi kulumbira, iwo anayamba kulira monga mwana. Anandichonderera kuti ndisiye kuyanjana ndi Mboni.

Ndinavutika maganizo, kusoŵa wosankha pakati pa atate aŵiri—Yehova ndi iwo. Ndinadziŵa kuti onse amandikonda kwambiri, ndipo ndinafuna kusangalatsa onse aŵiriwo; koma zinaoneka kuti nzosatheka. Ndinasweka mtima kwambiri. Ndinauza Atate kuti ndidzachita zonse zimene iwo anafuna, polingalira kuti ndidzapitiriza maphunziro anga ndi kukhala wa Mboni nditakula. Panthaŵiyo ndinali ndi zaka 17 zokha zakubadwa.

Pamasiku amene anatsatirapo, ndinachita manyazi chifukwa cha zimene ndinachita. Ndinalingalira kuti Yehova sanakondwe ndiponso kuti sindinakhulupirire ndi mtima wanga wonse mawu a Davide wamasalmo, amene anati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Koma panthaŵiyo ndinali pasukulu ya sekondale, ndipo makolo anga ndiwo ankandilipirira sukuluyo.

Kuchirimika

Kwa zaka zoposa ziŵiri, sindinakachezere amalume anga kapena kuyanjananso ndi Mboni, popeza kuti ndinadziŵa kuti makolo anga anali kundilondalonda. Tsiku lina mu 1989, pamene ndinali ndi zaka 20, ndinakumana ndi wa Mboni amene ndinali kumdziŵa. Iye anandifunsa mwachikondi kuti ndimuuze ngati ndingathe kukamchezera. Popeza kuti sananene chilichonse chokhudza kuphunzira Baibulo, nthaŵi ina ndinapita kukamchezera.

M’kupita kwa nthaŵi, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndiponso kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova pa Nyumba ya Ufumu. Ndinali kuphunzirira kuntchito kwanga, kumene kunalibe munthu woti angandisokoneze. Chotsatirapo chake, ndinazindikira bwino za mkhalidwe wachikondi wa Yehova ndipo ndinadziŵanso bwino phindu la kukhala paunansi wathithithi ndi iye zivute zitani. Mu August chaka chomwecho, ndinayamba kugaŵana ndi ena zimene ndinaphunzira.

Mpaka panthaŵiyo, a m’banja langa sanali kudziŵa chilichonse. Komabe, patapita masiku angapo, ine ndi atate anga tinayambanso kukangana, koma panthaŵiyi ndinakonzekera kulimbana nawo. Anayesa kundifunsa moleza mtima kuti: “Mwanawe, kodi nzoona kuti ukuyanjanabe ndi Mboni za Yehova?” Misozi inalengeza m’maso mwawo pamene anali kuyembekezera yankho langa. Amayi anga ndi mlongo wanga anali kulira mosisima.

Ndinafotokoza kuti panali pasanapite nthaŵi yaitali kuchokera pamene ndinali kuyanjana ndi Mboni ndipo ndinatsimikiza mtima kukhala mmodzi wa iwo. Nditanena zimenezo, zinthu zinasintha nthaŵi yomweyo. Atate anafuula nanena mawu amene alembedwa pachiyambi pa nkhani ino. Kenaka anandigwira ndi kunena mofuula kuti sadzandilola kutuluka m’nyumbamo wamoyo. Ndinapulumuka m’manjamo, ndipo pamene ndinali kuthaŵa ndikutsika pamasitepe, ndinamva mbale wanga wamng’ono akuyesa kutonthoza Atatewo. “Kuyambira lero ndinu Atate wanga,” ndinapemphera motero kwa Yehova. “Ndakusankhani, chonde ndikukupemphani kuti mundisamalire.”

Kulipsira

Patapita masiku angapo, Atate anapita kunyumba kwa amalume anga, akumalingalira kuti ndinali kumeneko. Anagwira amalumewo nafuna kuwapha, koma Mboni zina zimene zinali kukachezera amalumewo zinaloŵererapo. Atatewo anachoka, nalonjeza kuti adzabweranso. Patapita nthaŵi yochepa anabwererakodi, ndipo panthaŵiyi anatsagana ndi asilikali a mfuti. Anatenga Mbonizo pamodzi ndi amalume anga, amene anali kudwala kwambiri, napita nawo kulikulu lawo la asilikali.

Kenaka anayamba kusakasaka Mboni zina m’deralo. Anakagubidizanso m’nyumba ya wa Mboni wina. Mabuku, kuphatikizapo mabaibulo amene analanda anawaunjika mumsewu nawatentha. Komatu sanachite zokhazo. Mboni zisanu ndi imodzi zinamangidwa pamodzi ndi anthu amene anali kungophunzira nawo. Onsewo anawaika m’kachipinda kakang’ono, anawafunsa, ndipo kenaka anawamenya. Ena anawatentha ndi ndudu. Nkhani imeneyi inafalikira mofulumira m’dera lonselo. Asilikali anali kundisakasaka uku ndi uku. Atate anga anauza asilikaliwo kuti ngati andipeze andikakamize kuti ndisinthe malingaliro anga, mosasamala kanthu za njira imene angagwiritsire ntchito.

Patapita masiku angapo, asilikaliwo analoŵa m’Nyumba ya Ufumu, pamene mpingo wina unali kuchita msonkhano. Analamula mpingo wonsewo—amuna, akazi, ndi ana—kuti atulukemo. Analanda mabaibulo awo nawauza kuti ayende ulendo wapansi kupita kulikulu lawo, kumene anakafunsidwa.

Kuthaŵira ku Greece

Panthaŵi yonseyi, ndinali kusamaliridwa ndi banja lina la Mboni m’dera lakutali ndi kumene kunali kuchitika zinthu zoipazi. Patapita mwezi umodzi ndinasamuka m’dzikomo ndi kupita ku Greece. Nditafika kumeneko, ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova Mulungu ndipo ndinabatizidwa posonyeza kudzipatulirako.

Ku Greece, abale auzimu anandisamalira mwachikondi ndipo panali abale a mitundu yosiyanasiyana—kuphatikizapo Aturki. Ndinazindikira kuona kwa mawu a Yesu akuti: “Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.”—Marko 10:29, 30.

Zaka zitatu zotsatira ndinakhala ku Greece. Ngakhale kuti Atate ndinawalembera kalata maulendo angapo, iwo sanandiyankhe. Patapita nthaŵi ena anandiuza kuti pamene mabwenzi anga anakawachezera ndi kuwafunsa za ine, iwo anali kunena kuti: “Ndilibe mwana amene ali ndi dzina limenelo.”

Kuyanjananso Patapita Zaka Zisanu ndi Chimodzi

Ndinabwerera kukakhala ku Beirut mu 1992, nkhondo itatha. Kudzera mwa bwenzi langa, ndinauza atate anga zoti ndikufuna kubwerera kunyumbako. Iwo anayankha kuti adzandilandira—komatu pokhapokha ngati ndinasiya chikhulupiriro changa. Choncho, ndinali kukhala m’nyumba yalendi kwa zaka zitatu zotsatira. Kenaka, m’November 1995, mosayembekezereka konse Atate anafika kuntchito kwanga napempha kuti aonane ndi ine. Panthaŵiyo ine kunalibe, choncho, iwo anasiya uthenga wakuti anali kundifuna kuti ndipite kunyumba. Poyamba ndinali kuona ngati zonama. Choncho, mwamphwayi, ndinapita kukawaona. Kunali kuyanjananso kokhudza mtima. Iwo ananena kuti salinso wodandaula chifukwa chakuti ndili wa Mboni nanenanso kuti akufuna kuti ndibwerere kunyumba!

Lerolino ndikutumikira monga mkulu wachikristu mumpingo ndiponso mtumiki wa nthaŵi zonse mumpingo wolankhula Chiarmeniya. Nthaŵi zambiri ndimakumana ndi anthu onga atate anga amene amatsutsa anthu a m’banja mwawo chifukwa chakuti anthuwo akufuna kutumikira Yehova. Ndimadziŵa kuti Atate anakhulupirira kwambiri kuti anali kuchita zabwino pondiletsa kulambira kwanga. Baibulo limakonzekeretsa Akristu mwa kunena kuti iwo angakumane ndi chitsutso cha apabanja awo.—Mateyu 10:34-37; 2 Timoteo 3:12.

Ndikuyembekezera kuti tsiku lina atate anga ndi ena onse a m’banja langa adzakhalenso ndi chiyembekezo cha m’Baibulo chonga changa cha dziko labwino limene likudzalo. Panthaŵiyo sikudzakhalanso nkhondo kapena kupululutsana, ndipo anthu sadzapitikitsidwanso kumaiko awo kapena kuzunzidwa chifukwa cha chilungamo. (2 Petro 3:13) Ndiponso panthaŵiyo anthu sadzafunikira kusankha pakati pa zinthu ziŵiri zamtengo wapatali kwa iwo.—Yoperekedwa.

Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena ngati mungakonde kuti wina azibwera kudzachita nanu phunziro la Baibulo laulere la panyumba, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena kukeyala yoyenera ili patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena