Dengue—Matenda Otengedwa mwa Kulumidwa
Yolembedwa ndi mtolankhani wa Galamukani! ku Philippines
POPANDA kuuona, udzudzu utera padzanja losafunda la mwana wamng’ono wamkazi. Kachiromboko mwamsanga kakuboola khungu lake ndipo kapsontha magazi ake. Patapita mphindi pang’ono, amayi ake akuyang’ana mwana wawo naona udzudzuwo. Ayesa kuupha, koma uwo wathaŵa kale. Kodi amenewo ndiwo mapeto ake? Mwinamwake si choncho. Udzudzuwo ungakhale utapita, koma kuloŵetsa kwake mlomo m’magazi a mwana kwasiyamo tizirombo tosafunikira timene tingayambitse matenda.
Mkati mwa milungu iŵiri, mwanayo ayamba kumva kuzizira, mutu, maso kupweteka mkati, kuphwanya m’mfundo, ndi kutentha thupi kwambiri. Pamene matendawo akukula, mwanayo akutuluka zotupa zofiira ndipo afooka kwambiri. Iye watenga matenda a dengue, matenda amene amayamba udzudzu utakuluma.
Makamaka ngati mwanayo anadwalapo dengue, matenda akewo angakule kwambiri nkukhala dengue hemorrhagic fever (DHF) yoopsa kwambiri. Nthendayo imachititsa mitsempha yaing’ono m’thupi kukha magazi, amene amadzatulukira pakhungu. Mwinanso angamakhe magazi m’thupi mkati. Popanda mankhwala oyenera, wodwalayo angafooke koopsa ndipo mtima wake ungalephere kukankha magazi, nkumwalira mwamsanga.
Kodi dengue nchiyani kwenikweni? Kodi mungaitenge inunso? Kodi inuyo ndi banja lanu mungadziteteze motani? Tatiyeni tiiyang’anitsitse nthendayi.
Kodi Dengue Nchiyani?
Dengue, yotchedwanso kuti breakbone fever, ndi imodzi mwa nthenda zambiri zimene munthu angatenge atalumidwa ndi udzudzu. Kamene kamayambitsa nthendayi ndi kachirombo kotchedwa vairasi. Udzudzu wonyamula kachiromboka (ndiko kuti, udzudzu umene unalumapo munthu amene ali ndi kachiromboko) umanyamula vairasiyo m’malovu ake. Poluma munthu kuti upsonthe magazi, umalavulira vairasiyo mwa munthu winayo.
Pali mitundu inayi ya kachirombo ka dengue. Munthu akatenga mtundu umodzi sikuti basi sadzatenganso mitundu ina itatuyo. Yemwe anadwalapo mtundu winawo kenako nkulumidwanso ndi udzudzu wonyamula mtundu winanso, angadwale DHF.
“Zigawo Ziŵiri mwa Zisanu za Anthu Padziko” Ali Pangozi
Malinga ndi bungwe loona zaumoyo la World Health Organization (WHO), anthu amene ali pangozi ya nthenda ya dengue ali 2,500,000,000, “zigawo ziŵiri mwa zisanu za anthu padziko.” Magazini ya Asiaweek inati: “Maiko oposa 100 akumadera otentha ndi apafupi ndi maderawo anena kuti kuli matenda a dengue, ndipo chaka chilichonse kumakhala odwala mamiliyoni makumi ambiri, ndipo 95% ya odwalawo ndi ana.”
Sizikudziŵika pamene matendawa anawazindikira nthaŵi yoyamba padziko. Mwina nkhani yonena za “matenda a bondo” ku Cairo mu 1779 ingakhale kuti inkanena dengue. Chiyambire nthaŵiyo, matendawa amveka padziko lonse. Makamaka kuyambira pa Nkhondo Yadziko II, dengue yawononga kwambiri thanzi la anthu, kuyambira ku Southeast Asia. Mitundu yosiyanasiyana ya kachirombo kake inayamba kufalikira, ndipo imeneyi inayambitsa mtundu wina wake woopsa wopangitsa kukha magazi. Buku lofalitsidwa ndi WHO limati: “Matenda oyamba akukha magazi ku Asia anawazindikira ku Manila mu 1954.” Panadzatsatira maiko ena, makamaka Thailand, Vietnam, Malaysia, ndi madera ena apafupi. Matenda oyambirira ameneŵa ku Southeast Asia anapha anthu kuyambira pa 10 mpaka 50 peresenti ya odwala, koma pamene anthu anadziŵa zambiri za matendawo, ziŵerengero zimenezi zinatsika.
Kuyambira m’ma 1960, kunyalanyaza maprogramu a kupha udzudzu wonyamula kachirombowo kwawonjezera kwambiri matenda a dengue. Pamene dengue yafalikira, DHF yafalikiranso. Maiko 9 okha ndiwo anali ndi miliriyo isanafike 1970, koma pofika 1995, chiŵerengero chimenechi chinali chitakwera kufika 41. Bungwe la WHO likuti pachaka odwala DHF pafupifupi 500,000 amagonekedwa m’chipatala.
Ngakhale kuti nthendayi sidziŵika kwambiri m’maiko osakhala m’madera otentha, nthaŵi zina aulendo opita kumadera kumene angatenge nthendayi aitenga ndi kupita nayo kwawo. Mwachitsanzo, chakumapeto kwa 1996, The New York Times inasimba za anthu odwala dengue m’United States—ku Massachusetts, New York, Oregon, ndi Texas.
Kuopsa Kwake kwa DHF
Monga momwe tanenera kale, DHF ndi dengue yamtundu woopsa yoika moyo pangozi. Kuopsa kwake kwina kwa DHF nkwakuti anthu amapusitsidwa nkuganiza kuti matendawo si aakulu. Ambiri amangoyesa kuti ndi chimfine kapena chifuŵa. Komabe, kuchedwa kuchitapo kanthu kungalole matendawo kukula kwambiri kufika poti mlingo wa ma platelet nkutsika kwambiri, kuyamba kukha magazi (mkati mwa thupi kapena m’nkhama, m’mfuno, kapena pakhungu), ndipo mphamvu yokankha magazi kutsika. Wodwalayo angamagwe. Pamene apabanja azindikira kuti matendawo akula kwambiri nkuti munthuyo atafooka kale kodetsa nkhaŵa. Akufulumira kupita naye kuchipatala. Atafika, madokotala akupeza kuti mtima wake ukulephera kukankha magazi. Chifukwa cha kukula kwa ngozi yakeyo, iwo alamula kuti aikidwe madzi m’thupi kudzera m’mitsempha.
Kuteteza Banja Lanu
Kodi chingachitidwe nchiyani pofuna kupeŵa zotsatira zowononga za matendawa? Ngati banja lanu likukhala kudera kumene matenda a dengue ali ofala ndipo wina pabanja thupi lake latentha kwambiri kwa masiku angapo, nkwanzeru kukaonana ndi dokotala. Zimenezi nzofunika makamaka ngati wodwalayo akuonetsa zizindikiro zina za dengue, monga zotupa kapena kupweteka kwa minofu ndi mfundo kapenanso mkati mwa maso.
Dokotala angapime magazi. Nthenda ya dengue yosakhetsa magazi ingalire machiritso osafuna zambiri. Koma ngati popima apeza kuti ndi DHF, dokotala angalimbikitse kuti wodwalayo asamalidwe bwino mwa kumpatsa madzi. Zimenezi zingaphatikizepo madzi amoyo, monga aja amene amapatsa munthu wotseguka m’mimba, kapena ngati zinthu zafika povuta, madzi ompatsira m’mitsempha amtundu wa Ringer’s, saline, kapena ena. Posamalira wodwala wofooka kodetsa nkhaŵa, dokotala angapereke mankhwala othandiza kuwonjezera mphamvu yokankha magazi ndi kubwezeretsa mlingo wake wa ma platelet.
Ngati munthu wataya magazi ambiri, madokotala angafune kumuika magazi. Ena angalimbikitse zimenezi popanda kuganiza za njira zina zimene angagwiritsire ntchito. Komabe, kuwonjezera pakuti nkuswa lamulo la Mulungu, zimenezi zimakhala zosafunikira nthaŵi zambiri. (Machitidwe 15:29) Zochitika zasonyeza kuti kusamalira bwino madzi m’thupi kuchokera pachiyambi pa matendawo kumathandiza kwambiri pakuchiritsa. Kugwirizana kwa wodwalayo ndi dokotala pankhani imeneyi kungathandize kupeŵa mikangano pankhani ya kuika magazi. Zonsezi zikugogomezera kufunika kochitapo kanthu msanga pamene munthu aganiza kuti ali ndi DHF.—Onani bokosi lakuti “Kodi Zizindikiro Zake Nzotani?”
Njira Zopeŵera
Mmodzi mwa onyamula akuluakulu a kachirombo ka dengue ndi udzudzu wamtundu wa Aedes aegypti. Mtundu umenewu ngwochuluka kumadera otentha ndi apafupi nawo kuzungulira dziko lonse. (Onani mapu ali m’nkhani ino.) Udzudzu wa Aedes aegypti umaswana kwambiri m’madera ochulukana anthu. Kuchepetsa udzudzu ndiko imodzi ya njira zoletsera nthendayi.
Kuchepetsa udzudzu padziko lonse si kwapafupi. Komanso, pali zomwe inu mungachite kuti muchepetse nthendayi panyumba panu. Udzudzu waukazi umaikira mazira m’madzi. Mbozi ingakule m’chotengera chilichonse chosunga madzi kwa pafupifupi mlungu umodzi, monga matayala otayidwa, zitini zotha ntchito, mabotolo, kapena zikamba za ngole. Kuchotsa zinthu ngati zimenezi kudzawononga malo oswanira udzudzu. Ndiponso, ndi bwino kuzolitsa zibekete kapena mabwato. Kuchotsa madzi okhalira m’ngalande kumathandizanso. Zofunikanso kudziŵa nzakuti kuchiyambi kwa nyengo ya sukulu ya 1997/98, unduna wa zaumoyo ku Philippines unaletsa kuika zitini za maluŵa m’makalasi chifukwa cha zimenezi.
Wina panyumba atadwala dengue, onetsetsani kuti sakulumidwa ndi udzudzu wina umenenso ungapatsire ena matendawo. Nyumba yotchinga bwino kapena yokhala ndi air-conditioner ingapereke chitetezo.
Bwanji nanga za katemera? Katemera woyenera pakali pano kulibe. Akufufuzafufuza ngati angapange wina, koma vuto lake nlakuti kuti pakhale chitetezo chokwanira, pafunikira katemera wa mitundu yonse inayi ya dengue. Kwenikweni katemera wa mtundu umodzi wokha angapangitse munthu kukhala ndi DHF. Ofufuzawo akukhulupirira kuti katemera wamphamvu mwina adzampeza zaka zisanu mpaka khumi mtsogolo.
Ofufuza ena akhala akuyesa njira ina. Mwa kugwiritsira ntchito njira yotchedwa genetic engineering kusintha majini, iwo akuyembekezera kuletsa kachirombo ka dengue kuti kasamaswane m’malovu a udzudzu. Ngati zimenezi zigwira ntchito malinga ndi mmene akuganizira, udzudzuwo wosinthidwa mwa njira imeneyi udzapatsira ana ake mphamvu yoletsa dengue. Ngakhale kuti pakhala kupita patsogolo ndithu, tionabe mmene zinthu ziti ziyendere.
Pakali pano, zikuoneka kuti sizitheka kuthetseratu matenda a dengue. Koma kusamala kudzakuthandizani inuyo ndi okondedwa anu kupeŵa zovuta za dengue—matenda otengedwa mwa kulumidwa—omwe angawononge moyo wanu.
[Bokosi patsamba 16]
Kodi Zizindikiro Zake Nzotani?
Zizindikiro za matenda a dengue ndi dengue hemorrhagic fever (DHF)
• Kutentha thupi kwadzidzidzi
• Mutu kupweteka kwambiria
• Maso kupweteka mkati
• Mfundo ndi minofu kupweteka
• Anabere kutupa
• Zotupa
• Kutopa
Zizindikiro za DHF yokha
• Kugwa mwadzidzidzi
• Kukha magazi pakhungu
• Kukha magazi mbali zambiri m’thupi
• Khungu lozizira ndi lochita nyatinyati
• Kutakataka
• Kufookeratu thupi mtima ukumagunda pang’ono (dengue shock syndrome)
Musachedwe kukaonana ndi dokotala ngati mwaona zizindikirozo. Ana ndiwo ali pangozi kwambiri
[Mawu a M’munsi]
a Madokotala amanena kuti osamwa asipulini chifukwa angawonjezere kukha kwa magazi.
[Bokosi patsamba 17]
Mawu kwa Apaulendo
Nthaŵi zina, apaulendo opita kuzigawo zotentha amatenga matenda a dengue, koma si ambiri amene amatenga dengue hemorrhagic fever chifukwa mtundu umenewu woopsa wa nthendayi munthu amadwala atatenga matenda a dengue kachiŵiri. Nazi mfundo zomwe zingateteze apaulendo:
• Valani mashati aatali manja ndi matalauza
• Dzolani mafuta opitikitsa udzudzu
• Peŵani madera ochulukana anthu
• Khalani m’nyumba zomwe mungatseke mazenera ake ndi kutsekera udzudzu kunja
• Thupi litayamba kutentha mutabwerera kwanu, uzani dokotala kumene mudapita
[Mapu/Chithunzi patsamba 17]
Madera kumene kwakhala “dengue” posachedwapa
Madera amene ali pangozi yokhala ndi mliri wa “dengue”
Mtundu wa “Aedes aegypti,” udzudzu wonyamula “dengue”
[Mawu a Chithunzi]
Gwero: Centers for Disease Control and Prevention, 1997
© Dr. Leonard E. Munstermann/Fran Heyl Associates, NYC
[Zithunzi patsamba 18]
Malo amene angakhale oswaniranako ndiwo (1) matayala otayidwa, (2) ngalande ya mvula, (3) zitini za maluŵa, (4) zibekete kapena zotengera zina, (5) zitini zotha ntchito, (6) madiramu
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
© Dr. Leonard E. Munstermann/Fran Heyl Associates, NYC