Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 9/8 tsamba 30-31
  • Kodi Tiyenera Kumuimba Mlandu Satana Chifukwa cha Machimo Athu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tiyenera Kumuimba Mlandu Satana Chifukwa cha Machimo Athu?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtsutseni Mdyerekezi
  • Mmene ‘Tingamkanizire Mdyerekezi’
  • Nkhondo Yamkati Mwathu
  • Tiyenera Kumavomereza Mlandu
  • Mdani wa Moyo Wosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • “Tsutsani Mdyerekezi” Monga Anachitira Yesu
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kanizani Satana, Ndipo Iye Adzathawa!
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Mumakhulupirira Kuti Mdyerekezi Alikodi?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 9/8 tsamba 30-31

Lingaliro la Baibulo

Kodi Tiyenera Kumuimba Mlandu Satana Chifukwa cha Machimo Athu?

SATANA ndiye anaimbidwa mlandu wa tchimo loyamba la anthu. Hava anati: “Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.” (Genesis 3:13) Kuyambira pamenepo, “njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana” wakhala akuukira anthu, ‘namachititsa khungu maganizo awo’ ndi ‘kunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9; 2 Akorinto 4:4) Palibe munthu amene angalephere kukhudzidwa ndi mphamvu yake, koma kodi zimenezo zikutanthauza kuti sitingamtsutse pofuna kutisonkhezera? Ndipo ngati tachimwa, kodi nthaŵi zonse mlandu ngwake?

Nzoonadi kuti Baibulo limafotokoza kuti Satana ndiyedi ananyenga Hava. (1 Timoteo 2:14) Atanyengedwa, anaganiza kuti angakhale ndi nzeru ngati ya Mulungu nkukhala wodziimira payekha. (Genesis 3:4, 5) Poganizira zimenezo, mkaziyo anachimwa. Komabe, Mulungu anamuimba mlandu iyeyo ndipo anamuweruza kuti afe. Chifukwa? Chifukwa chakuti ngakhale Satana ananama, mkaziyo anadziŵabe lamulo la Mulungu. Iye sanachite kukakamizidwa kusamvera; koma iyeyo ndiye anali woti adzisankhire zochita, akanatha kumtsutsa Satana pamene akumsonkhezera kuchita tchimolo.

Mtsutseni Mdyerekezi

Anthufe tingathe kumtsutsa Mdyerekezi. Aefeso 6:12 amatiuza kuti ‘tikulimbana nawo a uzimu a choipa m’zakumwamba.’ Nzachionekere kuti Mulungu amatiyembekezera kulimbana ndi Satana pamene akufuna kutisonkhezera. Koma kodi munthu angalimbane bwanji ndi Satana limodzi ndi ziŵanda zake pomwe iwowo ali ndi mphamvu yoposa ya anthu? Kodi Mulungu akutipempha kulimbana pankhondo yotiposa usinkhu, nkhondo imene tikudziŵa kuti sitingapambane? Iyayi, chifukwa Mulungu sakutiuza kulimbana ndi Mdyerekezi mwa mphamvu yatokha ayi. Yehova amatipatsa njira zosiyanasiyana zimene tingamtsutsire Mdyerekezi pofuna kutikopa mpaka titapambanadi. Baibulo limatiuza kuti Mdyerekezi ndani, limatiuza mmene amachitira zinthu, ndi mmenenso tingadzichinjirizire.—Yohane 8:44; 2 Akorinto 2:11; 11:14.

Mmene ‘Tingamkanizire Mdyerekezi’

Malemba amatiuza njira ziŵiri zomtsutsira Mdyerekezi. Limatilangiza kuti: “Mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” (Yakobo 4:7) Njira yoyamba pakumvera Mulungu imaphatikizapo kumvera malamulo ake. Tikamazindikira nthaŵi zonse kuti Mulungu aliko, kuzindikiranso ubwino wake, mphamvu ndi ulamuliro wake waukulu, ndi malamulo ake abwino kwambiri tidzapeza mphamvu yomtsutsira Satana. Kupemphera kwa Mulungu mosalekeza nkofunikanso.—Aefeso 6:18.

Tangoganizirani nthaŵi ija pamene Yesu anali kuyesedwa ndi Mdyerekezi. Yesu anakhoza kumtsutsa Mdyerekezi chifukwa anakumbukira malamulo ambiri a Mulungu ndi kugwira mawu ake. Satana ataona kuti walephera kumkopa Yesu kuti achimwe, anamsiya. Chitatha chiyeso chimenecho, Yehova anamlimbikitsa Yesu kudzera mwa angelo ake. (Mateyu 4:1-11) Motero, Yesu analimba mtima nkuwalimbikitsa ophunzira ake kupempha Mulungu ‘kuwalanditsa kwa woipayo.’—Mateyu 6:13.

Si kuti Mulungu amatilanditsa mwa kutitchingira ayi. Koma amatiuza kukulitsa mikhalidwe yaumulungu, yonga choonadi, chilungamo, mtendere, ndi chikhulupiriro. Mikhalidwe imeneyi imachita ngati “zida,” zotithandiza “kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11, 13-18) Choncho, mwa thandizo la Mulungu nkotheka kumgonjetsa Mdyerekezi potiyesa.

Njira yachiŵiri yomwe yatchulidwa pa Yakobo 4:7 ndiyo ‘kukaniza Mdyerekezi.’ Zimenezo zimatanthauza kuchitapo kanthu, kuthaŵa chisonkhezero chake chovulaza. Munthu ayenera kupeŵa mphamvu yake yachinyengo ndi kukana mzimu wake wokonda chuma ndi nkhani zonyansa zimene zili zofala padziko lero. Tikamatsutsa Mdyerekezi moteromo titadziperekanso pamoyo wofuna kukondweretsa Mulungu, ndicho chida champhamvu kwambiri pankhondo yolimbana ndi Satana. Koma kodi machimo onse ndi Satana amene amawachititsa?

Nkhondo Yamkati Mwathu

Wolemba Baibulo Yakobo anafotokoza kuti: “Aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo.” (Yakobo 1:14, 15) Nzachisoni kuti sitingathe kulakiratu zofooka zathu ndi kupanda kwathu ungwiro. (Aroma 5:12) Baibulo limati: “Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.”—Mlaliki 7:20.

Zimenezi sizikutanthauza kuti machimo onse sitingathe kuwapeŵa. Nthaŵi zina, mwa kusankha kwathu kuchita zolakwika, timadzibweretsera tokha ziyeso. Choncho zilibe kanthu kuti chikhumbo choipa chimene tili nacho chayamba chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu kapena tasonkhezeredwa ndi Satana, kaya timachikulitsa kapena kuchikana, zili ndi ife. Nchifukwa chake mtumwi Paulo ananena moyenera kuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”—Agalatiya 6:7.

Tiyenera Kumavomereza Mlandu

Nthaŵi zambiri anthu zimawavuta kuvomereza kuti ngofooka, kuti alephera, kuti alakwa—inde, ndi machimo omwe. (Salmo 36:2) Chinthu china chimene chingatithandize kuvomereza machimo athu ndicho kudziŵa kuti pakali pano Mulungu samatiyembekezera kuchita zinthu monga angwiro. Wamasalmo Davide anati: “Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, Kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.” (Salmo 103:10) Ngakhale kuti Mulungu amakhululukira, amatiyembekezerabe kulimbika nkhondo, kudzilanga tokha polimbana ndi Mdyerekezi pofuna kutikopa ndiponso polimbana ndi uchimo wathu wamkati.—1 Akorinto 9:27.

Tiyenera kumazindikira kuti ngakhale kuti Mulungu amadziŵa kuti Mdyerekezi amasonkhezera zochita zathu ndi kutinso ndiye ali ndi mlandu waukulu wa machimo a anthu, zimenezo sizimatimasula pamlandu ngati tachimwa. Nchifukwa chake Aroma 14:12 amati: “munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.”

Komabe, ‘tikamadana nacho choipa’ ndi ‘kugwirizana nacho chabwino,’ tingachilake choipa. (Aroma 12:9, 21) Mkazi woyamba uja, Hava, analephera kutero ndipo analangidwa chifukwa cha kusamvera kwake; bwenzi atatsutsa nkumvera Mulungu. (Genesis 3:16) Komabe, Mulungu sananyalanyaze mbali imene Mdyerekezi anachita pomnyenga. Mdyerekezi anatembereredwa ndi kuweruzidwa kuti adzawonongedwa kwamuyaya. (Genesis 3:14, 15; Aroma 16:20; Ahebri 2:14) Posachedwapa sitidzafunikiranso kulimbana ndi chisonkhezero chake choipa.—Chivumbulutso 20:1-3, 10.

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Erich Lessing/Art Resource, NY

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena